“Sindinkadziŵa Zambiri za Mulungu”
“Sindinkadziŵa Zambiri za Mulungu”
MWAMUNA wina amene akukhala ku Kerala, m’dziko la India analemba kuti: “Chaka chapitachi, Mboni za Yehova zakhala zikundiyendera kudzandiuza uthenga wabwino kwambiri wa Ufumu wa Mulungu. Ndakhala ndili Mkatolika kwa zaka zisanu ndi zitatu, koma sindinkadziŵa zambiri za Mulungu. M’chaka chimenechi chokha, ndaphunzira zambiri. Ndasangalala kwambiri kudziŵa kuti Nsanja ya Olonda imafalitsidwa m’zinenero 139 [tsopano 146]. N’zodabwitsa kuti anthu a zinenero zonse akuzindikira uthenga wa Mulungu.”
Ngakhale kuti anthu ambiri anzeru zadziko amati n’zosatheka kumudziŵa Mulungu, mtumwi Paulo anasonyeza bwinobwino kuti n’zotheka kumudziŵa Mulungu. Polankhula ndi gulu la anthu a ku Atene, limene ena mwa iwo anali kulambira pa guwa la nsembe lopatulidwa kwa “MULUNGU WOSADZIŴIKA,” iye anati: “Chimene muchipembedza osachidziŵa, chimenecho ndichilalikira kwa inu. Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo . . . apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.”—Machitidwe 17:23-26.
Paulo anapempha anthuwo kuti afufuze kuti am’dziŵe Mlengi, popeza “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Mboni za Yehova zidzasangalala kukuthandizani kudziŵa Mulungu woona ndi makhalidwe ake abwino kwambiri.