Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anapambana Chizunzo

Anapambana Chizunzo

Anapambana Chizunzo

FRIEDA JESS anabadwa mu 1911 ku Denmark, ndiyeno anasamuka kumeneku ndi makolo ake kupita ku Husum, mzinda wa kumpoto kwa Germany. Patapita zaka anayamba kugwira ntchito ku Magdeburg, ndipo mu 1930 anabatizidwa kukhala Wophunzira Baibulo, monga momwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira. Hitler anayamba kulamulira mu 1933, ndipo kwa Frieda kulamulira kumeneku kunali chiyambi cha zaka 23 za kunzunzidwa osati ndi boma limodzi lopondereza koma aŵiri.

Mu March 1933 boma la Germany linachita chisankho. Katswiri wa mbiri ya kale, Dr. Detlef Garbe ndiponso woyang’anira malo okumbukira za chizunzo a Neuengamme pafupi ndi Hamburg, anati: “A chipani cha Nazi anafuna kukakamiza anthu ambiri kusankha Adolf Hitler yemwe anali mkulu wa boma ndiponso mtsogoleri wawo.” Mboni za Yehova zinatsatira malangizo a Yesu akuti sayenera kutenga mbali m’ndale ndiponso kusakhala “a dziko lapansi,” chotero sanachite nawo chisankhocho. Kodi chotsatira chake chinali chiyani? Mboni zinaletsedwa.​—Yohane 17:16.

Frieda anapitirizabe kuchita ntchito yake yachikristu mobisa, ngakhale kuthandiza kusindikiza magazini ya Nsanja ya Olonda. Iye anati: “Magazini ena ankawaloŵetsa mobisa m’misasa yachibalo kupatsa okhulupirira anzathu.” Iye anagwidwa mu 1940 ndipo anaimbidwa mlandu ndi a Gestapo, ndiyeno anaikidwa m’ndende m’chipinda chayekha kwa miyezi ingapo. Kodi anapirira bwanji? Iye anati: “Pemphero linali pothaŵirapo panga. Ndinkayamba kupemphera m’maŵa kwambiri ndipo ndinkapemphera nthaŵi zambiri patsiku. Pemphero linandipatsa mphamvu ndipo linandithandiza kuti ndisakhale ndi nkhaŵa kwambiri.”​—Afilipi 4:6, 7.

Frieda anatulutsidwa, koma mu 1944 a Gestapo anam’gwiranso. Panthaŵiyi anam’lamula kukhala m’ndende ya ku Waldheim zaka zisanu ndi ziŵiri. Frieda akupitiriza kuti: “Alonda a kundende anandiika kuti ndizigwira ntchito ndi akazi ena m’chipinda chochapira. Nthaŵi zambiri ndinkakhala ndi wandende mnzanga wochokera ku Czechoslovakia, chotero ndinkalankhula naye kwambiri za Yehova ndi zokhudza chikhulupiriro changa. Kukambirana kumeneku kunandilimbikitsa.”

Kumasulidwa Koma Kwanthaŵi Yochepa

Mu May 1945, asilikali a Soviet anamasula akaidi ku ndende ya Waldheim, ndipo Frieda anali ndi ufulu wobwerera ku Magdeburg ndiponso kuyamba utumiki wake koma kwanthaŵi yochepa. Kudedwa kwa Mboni kunayambiranso, koma tsopano ndi akuluakulu a m’madera amene boma la Soviet linkalamulira. A Gerald Hacke a bungwe lofufuza za maulamuliro opondereza la Hannah-Arendt-Institute for Research Into Totalitarianism anati: “Mboni za Yehova zinali gulu limodzi pamagulu ochepa a anthu omwe anazunzidwa mosalekeza ndi maulamuliro opondereza ku Germany.”

N’chifukwa chiyani kudedwa kunayambanso? Nkhani yaikulu yomwe inachititsanso kudedwaku inali kusatenga nawo mbali m’ndale kwa Akristu. Mu 1948, dziko la East Germany linachita chisankho, chimene anthu anasankha mwachindunji ndipo monga momwe Hacke anafotokozera, “chochititsa chachikulu [cha chizunzo cha Mboni za Yehova] chinali chakuti izo sizinachite nawo chisankhocho.” Mu August 1950, Mboni za Yehova zinaletsedwa m’dziko la East Germany. Ambiri anamangidwa, kuphatikizapo Frieda.

Frieda anapitanso kukhoti ndipo analamulidwa kukhala m’ndende zaka zisanu ndi chimodzi. “Panthaŵiyi ndinali ndi okhulupirira anzanga ndipo kucheza nawo kunathandiza kwambiri.” Atatulutsidwa mu 1956, anasamukira ku West Germany. Frieda tsopano ali ndi zaka 90 ndipo akukhala ku Husum, akutumikirabe Mulungu woona, Yehova.

Frieda anazunzidwa zaka 23 ndi maulamuliro aŵiri opondereza. “A Nazi anafuna kuwononga moyo wanga, a Komyunizimu anafuna kuthetsa kulimbika mtima kwanga. Kodi n’kuti kumene ndinapeza mphamvu? Chizoloŵezi cha kuphunzira bwino Baibulo nthaŵi imene ndinali paufulu, kupemphera nthaŵi zonse pamene ndinali m’ndende m’chipinda chandekha, kugwirizana ndi okhulupirira anzanga ngati kunali kotheka ndiponso kuuza ena zikhulupiriro zanga ndikangopeza mpata.”

Ulamuliro wa Chifasizimu ku Hungary

Dziko lina kumene Mboni za Yehova zinadedwa kwa zaka zambiri ndi ku Hungary. Ena anazunzidwa osati ndi maulamuliro opondereza aŵiri koma atatu. Mmodzi mwa anthu amene anazunzidwa ndi Ádám Szinger. Ádám anabadwa mu 1922 ku Paks m’dziko la Hungary, ndipo anakulira m’chipembedzo cha chipulotesitanti. Mu 1937 Ophunzira Baibulo ena anafika panyumba ya Ádám ndipo nthaŵi yomweyo anachita chidwi ndi uthenga wawo. Zimene anaphunzira m’Baibulo zinam’tsimikizira kuti ziphunzitso za ku tchalitchi chake sizinali za m’Baibulo. Chotero anachoka mu Tchalitchi cha chipulotesitanti ndi kugwirizana ndi Ophunzira Baibulo mu utumiki wawo.

Ulamuliro wa chifasizimu unali kukula ku Hungary. Nthaŵi zambiri, apolisi ankaona Ádám akulalikira kunyumba ndi nyumba ndipo ankam’gwira kuti am’fufuze mwa kum’funsa mafunso. Kuvutitsa Mboni kunakulirakulira ndipo mu 1939 ntchito yawo inaletsedwa. Mu 1942, Ádám anagwidwa, ndi kum’pititsa kundende ndipo anamenyedwa modetsa nkhaŵa. Kodi n’chiyani chinam’thandiza kupirira kuvutika ndiponso kupirira miyezi imene anakhala m’ndende munthu woti anali ndi zaka 19? Iye anati: “Nthaŵi imene ndinali kunyumba, ndinkaphunzira Baibulo mosamalitsa ndipo ndinamvetsa bwino zolinga za Yehova.” Nthaŵi imene Ádám anamasulidwa kundende m’pamene anabatizidwa kukhala Mboni ya Yehova. Anabatizidwa usiku mu August 1942, m’mtsinje umene unali pafupi ndi nyumba yake.

Kukhala Kundende ku Hungary Kenako Kupita Kumsasa Wachibalo ku Serbia

Panthaŵi imeneyi, nkhondo yapadziko lonse ili m’kati, dziko la Hungary linagwirizana ndi dziko la Germany kulimbana ndi dziko la Soviet Union, ndipo cha kumapeto kwa 1942, Ádám anauzidwa kuloŵa usilikali. Iye anati: “Ndinawauza kuti sindingaloŵe usilikali chifukwa cha zimene ndinaphunzira m’Baibulo. Ndinafotokoza chifukwa chake ndinalibe mbali.” Iye analamulidwa kukhala m’ndende zaka 11. Koma Ádám sanakhalitse kwambiri ku Hungary.

Mu 1943 Mboni za Yehova zokwana 160 anazisonkhanitsa kuchokera kumadera osiyanasiyana, anazikweza mabwato ndipo anazitumiza ku Serbia kudzera pa mtsinje wa Danube. Ádám anali pagulu limeneli. Ku Serbia andende ameneŵa tsopano anali kulamulidwa ndi ulamuliro wachitatu wa Hitler. Anawatsekera m’msasa wachibalo ku Bor ndipo anawakakamiza kugwira ntchito m’migodi ya kopa. Pafupifupi chaka chimodzi chitapita, anawatumizanso ku Hungary, kumene Ádám anamasulidwa ndi asilikali a Soviet m’chilimwe cha mu 1945.

Dziko la Hungary mu Ulamuliro wa Chikomyunizimu

Koma ufuluwo unali wanthaŵi yochepa. Kumapeto kwa ma 1940, olamulira achikomyunizimu ku Hungary analetsa ntchito ya Mboni za Yehova, monga mmene olamulira achifasizimu anachitira nkhondo isanayambe. Mu 1952, Ádám, yemwe tsopano anali ndi zaka 29, ndipo anali ndi mkazi ndi ana aŵiri, anamangidwa ndi kuimbidwa mlandu atakananso kuloŵa usilikali. Ádám anafotokozera khothi kuti: “Si kuyamba kuti ine ndikane kuloŵa usilikali. Nkhondo ili m’kati, ndinapita kundende ndipo anandithamangitsira ku Serbia pachifukwa chomwechi. Ndikukana kuloŵa usilikali chifukwa cha chikumbumtima changa. Ndine Mboni ya Yehova ndipo sinditenga nawo mbali m’ndale.” Ádám analamulidwa kukhala m’ndende zaka zisanu ndi zitatu, patapita nthaŵi anachotsera zaka kukhala zinayi.

Ádám ankamudabe mpaka kudzafika pakati pa ma 1970, zaka zoposa 35 kuchokera nthaŵi yoyamba imene Ophunzira Baibulo anafika panyumba ya makolo ake. Nthaŵi yonseyi, makhoti asanu ndi limodzi anamulamula kukhala m’ndende zaka 23 ndipo anaikidwa m’ndende ndi m’misasa yosachepera khumi. Iye anapirira chizunzo chosalekeza m’maulamuliro atatu, wa chifasizimu ku Hungary nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse isanachitike, wa Nazi ku Serbia ndiponso wa chikomyunizimu ku Hungary panthaŵi imene dziko la America linali paudani waukulu ndi dziko la Soviet Union.

Ádám akukhalabe kwawo ku Paks ndipo akutumikira Mulungu mokhulupirika. Kodi anali ndi mphamvu zapadera zimene zinam’chititsa kupirira kwambiri mavuto? Ayi. Iye akuti:

“Kuphunzira Baibulo, pemphero ndi kugwirizana ndi okhulupirira anzanga zinali zofunika kwambiri. Koma ndifuna kunenanso zinthu zina ziŵiri. Choyamba, Yehova ndiye Gwero la mphamvu. Kukhala naye paubwenzi wapamtima kunandithandiza kwambiri kukhalabe ndi moyo. Ndipo chachiŵiri, ndinkakumbukirabe mawu a pa Aroma chaputala 12, amene amati: ‘Musabwezere choipa.’ Chotero sindinasunge chakukhosi. Nthaŵi zambiri ndinali ndi mwayi wobwezera anthu amene anandizunza, koma sindinatero. Tisagwiritsire ntchito mphamvu zimene Yehova watipatsa kuti tibwezere choipa pa choipa.”

Kutha kwa Chizunzo Chonse

Frieda ndi Ádám tsopano atha kulambira Yehova popanda chopinga. Komano, kodi zimene anakumana nazo zikusonyeza chiyani za kuzunza anthu chifukwa cha chipembedzo? Zikusonyeza kuti kuzunza kotero sikungapambane, makamaka ngati amene akuzunzidwa ndi Akristu oona. Ngakhale kuti kuzunza Mboni za Yehova kunawononga chuma chambiri ndiponso kunachititsa kuvutika kwambiri, sikunakwaniritse cholinga chake. Masiku ano, Mboni za Yehova zikuchulukana kwambiri ku Ulaya kumene maulamuliro aakulu aŵiri opondereza panthaŵi ina ankalamulira.

Kodi Mboni zinachita bwanji pozunzidwa? Monga mmene nkhani ya Frieda ndi Ádám yasonyezera, iwo anagwiritsira ntchito malangizo a m’Baibulo akuti: “Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.” (Aroma 12:21) Kodi chabwino chingagonjetsedi choipa? Inde, ngati n’chogwirizana ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. Kupambana chizunzo kwa Mboni za Yehova ku Ulaya kunali kupambana kwa mzimu wa Mulungu, kusonyeza mphamvu yochita chabwino imene imakhalapo chifukwa cha chikhulupiriro chimene mzimu woyera umabala mwa Akristu odzichepetsa. (Agalatiya 5:22, 23) M’dziko lino lachiwawa, zimenezi ndi phunziro limene onse afunika kuliganizira kwambiri.

[Zithunzi patsamba 5]

Frieda Jess (tsopano ndi Frieda Thiele) panthaŵi imene anamangidwa ndiponso masiku ano

[Zithunzi patsamba 7]

Ádám Szinger panthaŵi imene anaikidwa m’ndende ndiponso masiku ano