Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Ufumu Choyamba Ndiwo Moyo Wabwino ndi Wosangalatsa

Kufunafuna Ufumu Choyamba Ndiwo Moyo Wabwino ndi Wosangalatsa

Mbiri ya Moyo Wanga

Kufunafuna Ufumu Choyamba Ndiwo Moyo Wabwino ndi Wosangalatsa

YOSIMBIDWA NDI JETHA SUNAL

Titatha kudya chakudya cha m’maŵa, tinamva pa wailesi akulengeza kuti: “Mboni za Yehova n’zosaloledwa mwa lamulo ndipo ntchito yawo yaletsedwa.”

MUNALI mu 1950, ndipo atsikana anayife, tili ndi zaka za m’ma 20, tinali kutumikira monga amishonale a Mboni za Yehova m’dziko la Dominican Republic. Tinali titakhala m’dzikoli kwa chaka chimodzi.

Utumiki wa umishonale sikuti unali ntchito imene ndinkafuna pamoyo wanga. N’zoona kuti ndili wamng’ono ndinkapita ku tchalitchi. Komabe, bambo anga, anasiya kupita kutchalitchi m’kati mwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Mu 1933, patsiku limene ndinaloŵa Tchalitchi cha Episikopo, bishopu anangoŵerenga lemba limodzi m’Baibulo, n’kuyamba kukamba nkhani zandale. Izi zinakwiyitsa kwambiri mayi anga moti kuyambira pompo analeka kupita kutchalitchi.

Moyo Wathu Unasintha

Makolo anga, a William Karl Adams ndi a Mary anali ndi ana asanu. Ana aamuna anali Don, Joel, ndi Karl. Mng’ono wanga Joy ndi amene anali womaliza, ndipo ine ndinali mwana wachisamba. Ndiyenera kuti ndinali ndi zaka 13, pamene tsiku lina pochokera ku sukulu ndinapeza mayi akuŵerenga kabuku kosindikizidwa ndi Mboni za Yehova. Kanali ndi mutu wakuti, The Kingdom, the Hope of the World. Iwo anandiuza kuti: “Ichi ndiye choonadi.”

Mayi ankatiuza tonse zimene anali kuphunzira m’Baibulo. Mwa zonena ndi zochita zawo, anakhomereza mwa ife kufunika kwa uphungu wa Yesu wakuti: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.”​—Mateyu 6:33.

Nthaŵi zonse sindinkafuna kumvetsera. Nthaŵi ina ndinanena kuti: “Mayi, muleke kundilalikira, apo ayi sindipukuta mbale.” Komabe, anapitiriza mwaluso kutiuza uthenga. Nthaŵi zonse ankatenga ana tonse popita ku maphunziro a Baibulo amene ankachitikira m’nyumba ya Clara Ryan, yemwe ankakhala pafupiko ndi nyumba yathu ku Elmhurst, m’chigawo cha Illinois, m’dziko la United States.

Clara ankaphunzitsanso kuimba piyano. Chaka chilichonse ophunzira ake pochita chionetsero cha zimene aphunzira, iye ankapezerapo mwayi kunena za Ufumu wa Mulungu ndi chiyembekezo cha chiukiriro. Chifukwa chakuti ndinkakonda nyimbo, popeza ndinaphunzira kuimba vayolini ndili ndi zaka zisanu ndi ziŵiri , ndinkamvetsera zimene Clara ankanena.

Posakhalitsa anafe tinayamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo ndi mayi kudera la kumadzulo kwa Chicago. Unali ulendo wautali wa pabasi ndi wa pagalimoto, koma unali mbali ya maphunziro athu oyambirira a zimene zimafunika pofunafuna Ufumu choyamba. Mu 1938, patatha zaka zitatu mayi atabatizidwa, ndinapita nawo ku msonkhano wa Mboni za Yehova ku Chicago. Uwu unali umodzi mwa mizinda 50 imene anailunzanitsa ndi telefoni yomvetsera ku wailesi pa msonkhanowu. Zimene ndinamva kumeneko zinandikhudza mtima.

Komabe, ndinkakondanso kwambiri nyimbo. Ndinamaliza sukulu ya sekondale mu 1938, ndipo bambo anakonza zoti ndikaphunzire kuimba pa sukulu ya American Conservatory of Music ku Chicago. Choncho m’zaka ziŵiri zotsatira, ndinaphunzira nyimbo, ndinaimba m’magulu a oimba aŵiri, ndipo ndinaganiza zogwira ntchito imeneyi.

Amene ankandiphunzitsa kuimba vayolini, a Herbert Butler, anasamuka ku Ulaya kupita ku United States. Choncho ndinawapatsa kabuku kakuti Refugees, * ndi maganizo akuti aŵerenga. Anaŵerengadi, ndipo mlungu wotsatira atamaliza kundiphunzitsa anati: “Jetha, umaimba bwino, ndipo utapitiriza maphunziro ako, ungadzapeze ntchito m’gulu la oimba pa wailesi kapena yophunzitsa nyimbo.” Ndipo atagwira kabuku kamene ndinawapatsa kaja anatinso: “Koma ndikuganiza kuti mtima wako uli apa. Bwanji osakonza zoti imeneyi ikhale ntchito yamoyo wako wonse?”

Ndinaganizira zimenezo mofatsa. M’malo mopitiriza kuphunzira pa sukulu ija, ndinavomera zimene mayi anandipempha zopita ku msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Detroit, ku Michigan, mu July 1940. Tinakakhala m’matenti pamalo pamene panali nyumba zoyenda nazo ndi matenti ambiri. Ndipotu, ndinapita ndi vayolini yanga yomwe, ndipo ndinaimba nawo m’gulu la anthu oimba nyimbo zamalimba pamsonkhano. Ndipo pamalo anyumba zoyenda nazowo, ndinakumana ndi apainiya ambiri (olengeza anthaŵi zonse). Onse anali osangalala kwambiri. Ndinaganiza zobatizidwa ndi kulembetsa utumiki wa upainiya. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kupitiriza utumiki wa nthaŵi zonse kwa moyo wanga wonse.

Ndinayamba kuchita upainiya m’tauni ya kwathu. Kenako, ndinakatumikira ku Chicago. Mu 1943, ndinasamukira ku Kentucky. Chaka chimenecho m’chilimwe, titatsala pang’ono kuchita msonkhano wachigawo, ndinalandira kalata yondiitana kukaphunzira nawo m’kalasi lachiŵiri pa Sukulu ya Gileadi, kuti ndikaphunzire za ntchito ya umishonale. Maphunzirowo anali oti ayamba mu September 1943.

Panthaŵi yamsonkhano wachigawo m’chilimwe chimenecho, ndinakakhala kunyumba ya Mboni imene inandipatsa zovala zilizonse za mwana wake wamkazi zimene ndinkafunikira. Mwana wakeyo anakaloŵa usilikali, ndipo anauza mayi akewo kuti apatse anthu ena zinthu zake zonse. Kwa ine, zinthu zimenezi zinakwaniritsa lonjezo la Yesu lakuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Miyezi isanu imene ndinali ku Gileadi inatha mofulumira, ndipo nditamaliza mu January 31, 1944, ndinayembekeza mwachidwi kulandira utumiki wa umishonale.

Nawonso Anasankha Utumiki wa Nthaŵi Zonse

Mayi analembetsa utumiki wa upainiya mu 1942. Panthaŵiyo, azichimwene anga atatu ndi mng’ono wanga anali akadali pa sukulu. Nthaŵi zambiri mayi anali kukumana nawo akaŵeruka kusukulu ndipo ankawatenga mu utumiki wa kumunda. Anawaphunzitsanso kugwira ntchito za pakhomo. Nthaŵi zambiri mayi ankagona mochedwa chifukwa chosita zovala ndi kugwira ntchito zina zofunika kuti masana adzapite ku utumiki.

Mu January 1943, ndikuchita upainiya ku Kentucky, mchimwene wanga Don anayambanso upainiya. Bambo anakwiya nazo zimenezi, popeza ankafuna kuti ana awo onse adzapite ku koleji, monga iwo ndi mayi anachitira. Don atachita upainiya kwa zaka pafupifupi ziŵiri, anaitanidwa kukapitiriza utumiki wake wa nthaŵi zonse monga mmodzi mwa anthu ogwira ntchito palikulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.

Joel anayamba upainiya mu June 1943 akukhalabe kunyumba. Panthaŵi imeneyo anayesetsa kulimbikitsa bambo kupita ku msonkhano wachigawo koma sanaphule kanthu. Komabe, Joel atayesetsa kufuna anthu oti aziphunzira nawo Baibulo panyumba m’gawolo koma osaphula kanthu, bambo anavomera kuti aziwaphunzitsa pogwiritsa ntchito buku lakuti “The Truth Shall Make You Free.” Ankayankha mafunso mosavuta, koma ankalimbikira kuti Joel apereke umboni wa m’Malemba wa zimene bukulo linali kunena. Izi zinam’thandiza Joel kupanga choonadi cha Baibulo kukhala chakechake.

Joel ankaganiza kuti bungwe loona ngati munthu sakuyenerera kulembetsa usilikali la Selective Service Board limene linati Don akuyenerera kusaloŵa usilikali popeza ndi mtumiki lichitanso chimodzimodzi kwa iye. Koma bungwelo litaona kuti Joel anali mnyamata kwambiri, linakana kumutenga ngati mtumiki ndipo anamutumizira kalata yoti akayambe ntchitoyi. Atakana kukayamba ntchitoyo, bungwelo linati akufunika kumangidwa. Apolisi a FBI atam’gwira, anakhala masiku atatu mu ndende ya Cook County.

Bambo anapereka nyumba yathu monga chikole kuti amutulutse pa belo. Ndiyeno anachita zomwezo kwa Mboni zachinyamata zimene zinali ndi mlandu wofananawo. Bambo anakwiya kwambiri chifukwa cha mmene nkhaniyi inayendera mwachinyengo, ndipo anapita ndi Joel ku Washington, D.C., kukayesa kuchita apilo. Mapeto ake, Joel anamuika m’gulu la atumiki, ndipo mlandu wake unatha. Bambo anga anandilembera kalata ndili ku ntchito yanga ya umishonale kuti: “Ndikuganiza kuti tiyenera kuthokoza Yehova chifukwa cha kupambana kumeneku!” Chakumapeto kwa August 1946, nayenso Joel anaitanidwa kukakhala m’gulu la anthu ogwira ntchito ku likulu ku Brooklyn.

Nthaŵi zambiri Karl akakhala patchuti, ankachita upainiya asanamalize sukulu ya sekondale kumayambiriro kwa 1947 ndipo atamaliza anayamba utumiki wa upainiya wokhazikika. Nthaŵi imeneyo bambo anali kudwaladwala, choncho Karl anawathandiza kuyendetsa bizinesi yawo kwa nthaŵi yochepa, asanapite kukachita upainiya ku malo ena. Kumapeto kwa 1947, Karl anayamba kutumikira pamodzi ndi Don ndi Joel ku malikulu a ku Brooklyn monga wa m’banja la Beteli.

Joy atamaliza sukulu ya sekondale, anayamba upainiya. Ndiyeno mu 1951, anapitanso kukatumikira ndi azichimwene ake ku Beteli. Ankagwira ntchito yoyeretsa zipinda ndiponso ku Dipatimenti Yolembetsa Masabusikiripishoni. Mu 1955 anakwatiŵa ndi Roger Morgan, wa m’banja la Beteli. Patatha zaka zisanu ndi ziŵiri , anafuna zobereka ana, ndipo anachoka pa Beteli. M’kupita kwa nthaŵi, anabereka ana aŵiri, amene akutumikiranso Yehova.

Pamene ana onse anali mu utumiki wa nthaŵi zonse, mayi analimbikitsa kwambiri bambo, moti anapatulira moyo wawo kwa Yehova ndipo anabatizidwa mu 1952. Kwa zaka 15, mpaka pamene anamwalira, anali aluso kwambiri popeza njira zouzira ena choonadi cha Ufumu, ngakhale kuti ankalephera kuchita zambiri chifukwa chodwala.

Mayi anasiya upainiya kwa kanthaŵi chifukwa cha kudwala kwa bambo, ndiyeno atayambiranso kuchita upainiyawo anapitiriza mpaka pamene iwo anamwalira. Analibe galimoto; komanso sankayendetsa njinga. Mayiwa omwe anali aafupi, ankayenda kulikonse, nthaŵi zambiri kumidzi, kukachititsa maphunziro a Baibulo.

Mu Utumiki wa Umishonale

Titamaliza sukulu ya Gileadi, kagulu kathu kanakachita upainiya kumpoto kwa mzinda wa New York City kwa chaka chimodzi mpaka pamene tinapeza zikalata zoyendera. Kenako, mu 1945 tinanyamuka kupita ku gawo lathu ku Cuba, kumene tinakazoloŵera pang’onopang’ono moyo watsopano. Anthu anali kulabadira uthenga wathu, ndipo patapita nthaŵi pang’ono tonse tinali ndi maphunziro ambiri a Baibulo. Tinatumikira kumeneko kwa zaka zingapo. Ndiyeno anatitumiza ku dziko la Dominican Republic. Tsiku lina ndinakumana ndi mzimayi amene anandipempha kuti ndikaonane ndi kasitomala wake, mzimayi wachifalansa dzina lake Suzanne Enfroy, amene ankafuna kuti athandizidwe kumvetsa Baibulo.

Suzanne anali Myuda, ndipo Hitler ataukira France, mwamuna wake anamusamutsira dziko lina pamodzi ndi ana awo aŵiri. Suzanne mofulumira anauza anthu ena zinthu zimene anali kuphunzira. Koyamba analankhula ndi mzimayi amene anandiuza kuti ndikaonane naye uja, kenako kwa Blanche, mnzake wa ku France. Onse analimbikira mpaka anabatizidwa.

Suzanne anandifunsa kuti: “Kodi ndingatani kuti ndithandize ana anga?” Mwana wake wamwamuna anali kuphunzira udokotala, ndipo mwana wake wamkazi anali kuphunzira kuvina gule wina wotchedwa ballet, poyembekezera kukavina ku holo ya Radio City Music Hall ku New York. Suzanne ankawatumizira Nsanja za Olonda ndi Galamukani! mwezi uliwonse. Chifukwa cha zimenezi, mwana wamwamuna wa Suzanne ndi mkazi wake, ndi mchemwali wa mkaziyo amene anabadwa naye mapasa anakhala Mboni. Mwamuna wa Suzanne, Louis, ankaopa chifukwa chakuti mkazi wake anali kuphunzira ndi Mboni za Yehova popeza boma la dziko la Dominican Republic n’kuti litaletsa ntchito yathu. Koma banja lonse litasamukira ku United States, iyenso mapeto ake anakhala Mboni.

Tinaletsedwa Koma Tinatumikirabe

Ngakhale kuti ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Dominican Republic patangopita nthaŵi pang’ono tili kumeneko mu 1949, tinatsimikiza mtima kumvera Mulungu monga Wolamulira koposa anthu. (Machitidwe 5:29) Tinapitiriza kufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba mwa kulengeza uthenga wake wabwino, monga momwe Yesu analamulira otsatira ake kuchita. (Mateyu 24:14) Komabe, tinaphunzira kukhala “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda” pochita ntchito yathu yolalikira. (Mateyu 10:16) Mwachitsanzo, vayolini yanga inandithandiza kwambiri. Ndinkaitenga pochititsa maphunziro a Baibulo. Ophunzira anga sanakhale oimba vayolini koma mabanja ambiri anakhala atumiki a Yehova.

Ataletsa ntchito yathu, atsikana anayife, ine, Mary Aniol, Sophia Soviak, Edith Morgan, anatisamutsa m’nyumba ya amishonale ya ku San Francisco de Macorís kupita kunyumba ya amishonale imene inali pa nthambi ku Santo Domingo, ku likulu la dzikoli. Koma mwezi uliwonse, ndinkapita ku gawo lathu limene anatipatsa poyamba kukaphunzitsa nyimbo. Zimenezi zinandipangitsa kutengera abale athu achikristu chakudya chauzimu m’chikwana cha vayolini ndiponso kukatenga malipoti a ntchito yawo yolalikira.

Pamene abale a ku San Francisco de Macorís anamangidwa ku Santiago chifukwa cha kusaloŵerera m’zinthu za dziko monga Akristu, ndinapemphedwa kukawapatsira ndalama ndiponso kukakhala kotheka mabaibulo, komanso kutenga mauthenga opita ku mabanja awo. Ku ndende ya ku Santiago, alonda ataona chikwama cha vayolini nditakolekera pamkono, anafunsa kuti, “Ichi ndi chantchito yanji?” Ndinayankha kuti, “Kuti ndikawasangalatse.”

Mwa nyimbo zimene ndinkaimba panali imene Mboni ina inalemba ili ku msasa wa chibalo wa Anazi. Nyimbo imeneyo tsopano ndi nambala 29 mu buku la nyimbo la Mboni za Yehova. Ndinkaiimba kuti abale athu amene anali m’ndende aphunzire kuiimba.

Ndinamva kuti Mboni zambiri anazisamutsira ku famu ya Trujillo, mtsogoleri wa boma. Ndinamva izi pafupi ndi msewu wa basi. Choncho cha kumasana, nditatsika basi ndinafunsa mmene ndingayendere kuti ndikafike kumeneko. Mwiniwake wa golosale inayake yaing’ono analoza mapiri angapo ndipo anati andibwereka kavalo wake ndiponso andipatsa mnyamata kuti andilondolere ndikasiya vayolini yanga ngati chikole kuti ndibwereranso.

Titapitirira zitunda zimenezo, tinawoloka mtsinje tonse titakwera kavaloyo iye n’kumasambira. Kumeneko tinaona gulu la mbalame zotchedwa zinkhwe, zomwe nthenga zake zobiriŵira ndiponso za bluu zimawonekera bwino padzuŵa. Zinali zokongola zedi! Ndinapemphera kuti: “Zikomo kwambiri Yehova, pozipanga mbalamezi kukhala zokongola kwambiri.” Kenako, cha m’ma 4 koloko yamadzulo, tinafika pa famuyo. Msilikali amene anali kuyang’anira pamenepo anandikomera mtima kulankhula ndi abalewo, ndipo anandilola kuwapatsa zonse zimene ndinawabweretsera, ngakhale ka Baibulo kakang’ono.

Pobwerera, ndinapemphera njira yonse, popeza tsopano kunali kutada. Ndinakafikanso pa golosale ija, titanyowa ndi mvula. Popeza basi yotsiriza patsikuli inali itapita, ndinapempha mwini golosaleyo kuti andiimitsire galimoto ikamadutsa. Kodi zikanakhala bwino kukwera galimoto imene munali amuna aŵiri? M’modzi mwa iwo anandifunsa kuti: “Kodi umam’dziŵa Sophie? Ankaphunzira ndi mchemwali wanga.” Ndinadziŵa kuti Yehova wayankha pemphero langa! Anayenda nane bwinobwino mpaka ku Santo Domingo.

Mu 1953, ndinali pa gulu la anthu a ku Dominican Republic amene anapezeka pa msonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova ku Yankee Stadium ku New York. Banja lathu lonse linali kumeneko, ndi bambo anga omwe anali konko. Litatha lipoti la mmene ntchito yolalikira inali kuyendera ku Dominican Republic, ine ndi mmishonale mnzanga Mary Aniol, tinali ndi kambali pa pulogalamupo yosonyeza momwe tinkachitira ulaliki ntchito yathu italetsedwa.

Chimwemwe Chapadera M’ntchito Yoyendayenda

Chaka chimenecho m’chilimwe, ndinakumana ndi Rudolph Sunal, amene anakhala mwamuna wanga chaka chotsatira. Banja lawo linakhala Mboni ku Allegheny, Pennsylvania, nkhondo yoyamba ya padziko lonse itangotha kumene. Atakhala m’ndende chifukwa chosatenga mbali m’zinthu za dziko monga Mkristu panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, anayamba utumiki wa pa Beteli ku Brooklyn, New York. Titangokwatirana kumene, anapemphedwa kuyendera mipingo monga woyang’anira woyendayenda. Kwa zaka 18 zotsatira, ndinkayenda naye mu ntchito yadera.

Utumiki wathuwu unali kutifikitsa ku Pennsylvania, West Virginia, New Hampshire, ndi Massachusetts, ndiponso malo ena. Nthaŵi zambiri tinkakhala m’nyumba za abale athu achikristu. Tinasangalala kwambiri kuwadziŵa bwino ndiponso kutumikira nawo limodzi Yehova. Nthaŵi zonse kutikonda ndi kutichereza kwawo kunali kochokera pansi pamtima ndiponso kwenikweni. Joel atakwatira Mary Aniol, amene anali mmishonale mnzanga, anakhala zaka zitatu mu ntchito yoyendayenda, kuyendera mipingo ku Pennsylvania ndi Michigan. Kenako mu 1958, Joel anapemphedwa kukhala m’banja la Beteli kachiŵirinso, panthaŵi ino ali ndi Mary.

Karl anali atakhala pa Beteli zaka pafupifupi zisanu ndi ziŵiri pamene anatumizidwa ku ntchito yadera kwa miyezi ingapo kuti akaphunzire zina. Kenako anakhala mlangizi pa Sukulu ya Gileadi. Mu 1963 anakwatira Bobbie, amene anatumikira mokhulupirika pa Beteli mpaka pamene anamwalira mu October 2002.

Don pa zaka zambiri zimene wakhala pa Beteli, nthaŵi zambiri amapita m’mayiko ena kukathandiza anthu ogwira ntchito pa maofesi a nthambi ndiponso amene ali mu utumiki wa umishonale. Utumiki wake wamufikitsa ku mayiko a Asia, ku Africa, ku Ulaya ndi m’mayiko osiyanasiyana a ku America. Nthaŵi zambiri Dolores yemwe ndi mkazi wokhulupirika wa Don, amayenda naye limodzi.

Zinthu Zinasintha Pamoyo Wathu

Bambo anamwalira atadwala kwa nthaŵi yaitali, koma asanamwalire anandiuza kuti anali osangalala kwambiri kuti tinasankha kutumikira Yehova Mulungu. Anati talandira madalitso ambiri zedi kuposa amene tikanakhala nawo ngati tikanapita kukaphunzira ku koleji monga momwe iwo ankafuna. Nditatha kuthandiza mayi kulongedza katundu kuti asamukire kumalo oyandikana ndi mng’ono wanga, Joy, ine ndi mwamuna wanga tinavomera kukachita upainiya ku New England kuti tikakhale pafupi ndi mayi ake, amene panthaŵiyo ankafunika thandizo lathu. Mayi ake atamwalira, mayi anga anakhala nafe zaka 13. Ndiyeno pa January 18, 1987, anamaliza ntchito yawo ya pa padziko lapansi ali ndi zaka 93.

Nthaŵi zambiri anzawo akamawayamikira kuti anaphunzitsa ana awo onse kukonda ndi kutumikira Yehova, mayi ankayankha modzichepetsa kuti: “Zinangochitika kuti ndinapeza ‘nthaka’ yabwino.” (Mateyu 13:23) Ndi dalitso zedi kuti tinali ndi makolo oopa Mulungu amene anapereka chitsanzo chabwino pankhani yachangu ndi kudzichepetsa.

Kuikabe Ufumu Poyamba

Tapitiriza kuika Ufumu wa Mulungu poyamba pamoyo wathu ndipo tayesetsanso kugwiritsira ntchito uphungu wa Yesu wogaŵana ndi ena. (Luka 6:38; 14:12-14) Chotsatira chake n’chakuti, Yehova watipatsa mowolowa manja zosoŵa zathu. Moyo wathu wakhala wabwino ndi wosangalatsa.

Ine ndi Rudy sitinasiyebe kukonda nyimbo. Timasangalala kwambiri anthu ena amene amakondanso nyimbo akabwera kunyumba kwathu kudzacheza madzulo ndipo timaimbira pamodzi zida zathu. Koma kuimba nyimbo si ntchito yanga. Changokhala chinthu china chosangalatsa pamoyo wanga. Tsopano ine ndi mwamuna wanga timasangalala kuona zipatso za utumiki wathu wa upainiya, anthu amene tawathandiza kwa zaka zapitazi.

Ngakhale kuti ndikudwaladwala, ndinganene kuti moyo wanga wakhala wosangalatsa ndi wabwino kwambiri kwa zaka zoposa 60 zimene ndakhala mu utumiki wa nthaŵi zonse. Tsiku lililonse ndikadzuka, ndimathokoza Yehova chifukwa choyankha pemphero langa pamene ndinkayamba utumiki wanga wa nthaŵi zonse zaka zambiri zapitazo, ndipo ndikuganiza kuti, ‘Tsopano, kodi ndingafunefune bwanji Ufumu choyamba lero?’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma anasiya kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 24]

Banja lathu mu 1948 (kuyambira kumanzere kupita kumanja): Joy, Don, mayi, Joel, Karl, ine, ndi bambo

[Chithunzi patsamba 25]

Mayi anapereka chitsanzo chabwino pokhala achangu mu utumiki

[Chithunzi patsamba 26]

Karl, Don, Joel, Joy, ndi ine masiku ano, patapita zaka zoposa 50

[Chithunzi patsamba 27]

Kumanzere kupita kumanja: Ine, Mary Aniol, Sophia Soviak, ndi Edith Morgan amishonale ku dziko la Dominican Republic

[Chithunzi patsamba 28]

Ndili ndi Mary (kumanzere) ku Yankee Stadium, mu 1953

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili ndi mwamuna wanga pamene anali mu ntchito yadera