N’chifukwa Chiyani Anthu Amazunzidwa pa Zifukwa za Chipembedzo?
N’chifukwa Chiyani Anthu Amazunzidwa pa Zifukwa za Chipembedzo?
KODI mukuvomereza kuti anthu ayenera kuzunzidwa chifukwa cha chipembedzo chawo? Mwina munganene kuti ayi, makamaka ngati zochita za anthu ozunzidwawo sizikusokoneza ufulu wa ena. Komabe, kuzunza anthu chifukwa cha chipembedzo kunayamba kale ndipo kukupitirirabe. Mwachitsanzo, zaka zonse za m’ma 1900, Mboni za Yehova zambiri ku Ulaya ndi m’mayiko ena a padziko lapansi nthaŵi zambiri zinalandidwa ufulu wa kulambira ndiponso zinazunzidwa.
Panthaŵi imeneyi, Mboni za Yehova zinavutika ndi chizunzo chosasimbika chimene chinatenga nthaŵi yaitali m’maulamuliro onse aakulu aŵiri opondereza a ku Ulaya. Kodi zimene anakumana nazo zikutiphunzitsa chiyani za kuzunza anthu chifukwa cha chipembedzo? Ndipo tikuphunzira chiyani ndi mmene anachitira pamene ankavutika?
“Siali a Dziko Lapansi”
Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala anthu omvera malamulo, amtendere ndiponso amakhalidwe abwino. Iwo satsutsa maboma kapena kufuna kukangana nawo, ndiponso sachita zinthu zoyambitsa chizunzo chifukwa chofuna kukhala anthu ofera chikhulupiriro. Akristu ameneŵa satenga nawo mbali m’ndale. Zimenezi ndi zogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “[Otsatira anga] siali a dziko lapansi monga ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Maboma ambiri amadziŵa kuti Mboni sizitenga nawo mbali m’ndale. Koma maulamuliro opondereza salemekeza kwenikweni zimene Baibulo limafuna kuti Akristu sayenera kukhala mbali yadziko.
Chifukwa chimene amachitira zimenezi anachifotokoza pamsonkhano wa ku yunivesite ya Heidelberg, ku Germany, mu November 2000. Msonkhanowo unali ndi mutu wakuti “Kuponderezedwa ndi Kulankhula Molimba Mtima: Mboni za Yehova mu Ulamuliro Wopondereza wa Nazi ndi Chikomyunizimu.” Katswiri wa maphunziro, Dr. Clemens Vollnhals wa bungwe lofufuza za maulamuliro opondereza la Hannah-Arendt-Institute for Research Into Totalitarianism, anati: “Maulamuliro opondereza samasonyeza mphamvu zawo pa zandale zokha. Iwo amafuna munthu kugonjera pachilichonse.”
Akristu oona sangagonjere maboma a anthu pachilichonse chifukwa analumbira kukhala okhulupirika kotheratu kwa Yehova Mulungu yekha. Mboni zimene zikukhala kumene kuli maulamuliro opondereza zaona kuti nthaŵi zina zimene Boma limafuna kuti zichite zimatsutsana ndi zofuna za chikhulupiriro chawo. Kodi iwo amachita chiyani pakakhala kutsutsana koteroko? Nthaŵi zambiri m’mbuyomu, Mboni za Yehova zagwiritsira ntchito mfundo yomwe ophunzira a Yesu Kristu ananena yakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
Mosasamala kanthu za chizunzo chankhanza, Mboni zambiri zatsatirabe chikhulupiriro chawo ndipo sizinatenge nawo mbali m’ndale. Kodi iwo anapirira bwanji? Kodi mphamvu zoti apirire anazipeza kuti? Tiyeni tiwalole aziyankhire okha. Ndipo tiyeni tione zimene ife tonse, Mboni ndiponso omwe sali Mboni, tingaphunzire pa zimene anakumana nazo.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Mboni za Yehova ku Germany zinavutika ndi chizunzo chosasimbika chimene chinatenga nthaŵi yaitali m’maulamuliro onse aŵiri opondereza a zaka za m’ma 1900
[Mawu Otsindika patsamba 4]
“Maulamuliro opondereza samasonyeza mphamvu zawo pa zandale zokha. Iwo amafuna munthu kugonjera pa chilichonse”—Dr. Clemens Vollnhals
[Chithunzi patsamba 4]
Banja la a Kusserow linalandidwa ufulu wawo chifukwa choti sanasiye chikhulupiriro chawo
[Chithunzi patsamba 4]
Johannes Harms anaphedwa m’ndende ya Anazi chifukwa cha chikhulupiriro chake