Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Asanaphunzire ndi Ataphunzira Moyo Wake Unasinthiratu

Asanaphunzire ndi Ataphunzira Moyo Wake Unasinthiratu

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa inu”

Asanaphunzire ndi Ataphunzira Moyo Wake Unasinthiratu

SIMMENE moyo wa Matsepang unalili wosasangalatsa ndiponso wopanda tanthauzo! Mtsikana ameneyu kwawo kunali ku Lesotho, dziko limene lili mkatikati mwa dziko la South Africa. Matsepang anali Mkatolika. Koma m’malo mom’phunzitsa kuyandikira kwa Mulungu, avirigo kwa zaka zambiri anali kumunyengerera ndi ndalama kuti achite naye zachiwerewere.

Chifukwa cha zimenezi, Matsepang anakhumudwa ndi zipembedzo ndipo sanakhulupirire kuti kuli Mlengi wachikondi amene amaganizira kwambiri anthu amene anawalenga. Chifukwa cha kunyalanyazidwa ndiponso kuzunzidwa, Matsepang anali kuvutika mtima kwambiri ndipo ankadziona kuti anali wopandiratu ntchito. Atakula anali waukali ndiponso wamtopola kwambiri. Izi zinam’pangitsa kuchita zinthu zaupandu.

Patapita nthaŵi Matsepang analoŵa m’gulu la zigaŵenga zimene zinkabera anthu okwera sitima. Ndiyeno anagwidwa n’kumulamula kuti akhale m’ndende ku South Africa. Kenako, anamutumiza kwawo, ku Lesotho, kumene anapitiriza khalidwe lake laupandu, lauchidakwa, lachiwawa, ndiponso lachiwerewere.

Atathedwa nzeru, Matsepang anapemphera kwambiri kwa Mulungu kuti amuthandize. Iye analonjeza kuti: “Mulungu, ndikapulumuka, ndidzachita zomwe ndingathe kukutumikirani.”

Posakhalitsa, amishonale a Mboni za Yehova anam’fikira Matsepang. Anamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo. Akuphunzira, anazindikira kuti Mulungu amaganizira ndiponso amakonda anthu. Ndipotu, anazindikira kuti Satana, ‘atate wa bodza,’ amagwiritsa ntchito njira zamachenjera ndi zonyenga kulimbikitsa anthu ena kudziona kuti ndi opanda ntchito ndiponso kuwapangitsa kukhulupirira kuti Yehova sangawakonde n’komwe.​—Yohane 8:44; Aefeso 6:11.

Mosiyana ndi zimenezi, Matsepang anasangalala kwambiri ataphunzira kuti tingadzione kukhala ofunika ngati tilapa machimo amene tinachita, kupempha Mulungu kutikhululukira, ndi kuyesetsa kumukondweretsa. Anathandizidwa kuzindikira kuti “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu” ndipo amationa mwanjira yosiyana kwambiri ndi mmene ife timadzionera.​—1 Yohane 3:19, 20.

Matsepang anasangalala kuŵerenga mawu a wamasalmo Davide akuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi [“woswanyika,” NW].” (Salmo 34:18) Pokhala ndi “mzimu woswanyika,” iye anazindikira kuti Yehova sataya atumiki ake, ngakhale ngati ena mwa iwo akuvutika maganizo kapena kudziona kuti ndi osafunika. Zinamukhudza mtima ataphunzira kuti Mulungu amasamalira nkhosa zake zonse ndipo amazithandiza pamavuto. (Salmo 55:22; 1 Petro 5:6, 7) Chimene chinamukhudza mtima kwambiri ndi mawu akuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”​—Yakobo 4:8.

Patapita kanthaŵi, mphamvu ya Mawu a Mulungu, Baibulo, inayamba kuonekera pamoyo wa Matsepang. Anayamba kufika pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse ndipo anasiya makhalidwe ake osagwirizana ndi Malemba. Ndiyeno? Saganizanso kuti Mulungu sangamukonde ndi kumuyanja. Kuchokera pamene anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova, wagwiritsa ntchito maola ambirimbiri pantchito yachikristu monga wolengeza uthenga wabwino wa Ufumu. Ngakhale kuti amavutika mtima chifukwa cha mmene moyo wake unalili m’mbuyo, Matsepang tsopano ali ndi moyo wachimwemwe ndi watanthauzo. Ndi umbonitu waukulu umenewu wosonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu yosintha moyo wa anthu.​—Ahebri 4:12.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Mulungu, ndikapulumuka, ndidzachita zomwe ndingathe kukutumikirani”

[Bokosi patsamba 9]

Mfundo za M’Baibulo Zikugwira Ntchito

Zina mwa mfundo za m’Baibulo zimene zathandiza anthu amene anazunzidwa ndi izi:

Pondichulukira zolingalira [“nkhaŵa,” NW] zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu [Mulungu] zikondweretsa moyo wanga.” (Salmo 94:19) “Zotonthoza” za Yehova zopezeka m’Mawu ake zimalimbikitsa kwambiri. Kuzilingalira pamene tikusinkhasinkha ndiponso popemphera kumathandiza kuchepetsa nkhaŵa ndipo kumalimbikitsa kukhulupirira Mulungu monga Bwenzi lomvetsa zinthu.

“[Yehova] achiritsa osweka mtima, namanga mabala awo.” (Salmo 147:3) Ngati timayamikira chifundo cha Yehova ndi zimene wakonza zophimba machimo athu mwa nsembe ya dipo ya Yesu, tingalankhule ndi Mulungu molimba mtima popanda kuziimbanso mlandu. Izi zingatilimbitse mtima ndi kutipatsa mtendere wambiri wa m’maganizo.

“Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine [Yesu Kristu] koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.” (Yohane 6:44) Mwa mzimu wake woyera ndi mwa ntchito yolalikira Ufumu, Yehova mwiniyo amatikokera kwa Mwana wake ndipo amatipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha.