Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?

Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?

Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?

TINENE kuti simungathe kuŵerenga mawu amene ali patsamba lino. Ndiponso simutha kulankhula chinenero cha boma cha dziko lanu. Komanso simutha kulodza dziko lanu pa mapu osonyeza dziko lonse lapansi. Kodi mungamve bwanji? Ana osaŵerengeka adzakula ali otere. Bwanji mwana wanu?

Kodi mwana wanu ayenera kumapita kusukulu? M’mayiko ambiri, muli lamulo loti mwana aliyense ayenera kuphunzira kupulayimale ndi kusekondale kaya akufuna kapena sakufuna ndipo nthaŵi zambiri amaphunzira ulere. Pangano loona za ufulu wa mwana lakuti Convention on the Rights of the Child, limati kupita ku sukulu ndi ufulu wofunika kwambiri. Ndi mmenenso chimanenera chikalata chofotokoza za ufulu wa anthu cha Universal Declaration of Human Rights. Koma m’mayiko ena, sukulu si yaulere ndipo makolo angavutike kuti apeze ndalama zolipirira. Tiyeni tiione nkhaniyi monga mmene akuionera makolo achikristu amene akufuna kuti ana awo akhale ophunzira, kaya mwa kupita ku sukulu kapena mwa njira zina.

Zitsanzo za M’Baibulo za Anthu Ophunzira

Atumiki a Mulungu ambiri amene awatchula m’Baibulo ankatha kuŵerenga ndi kulemba. Petro ndi Yohane, atumwi a Yesu, anali asodzi achiyuda koma analemba mabuku a m’Baibulo m’Chigiriki osati m’chinenero chawo cha ku Galileya. * Makolo awo mwachionekere anaonetsetsa kuti ana awo aphunzira. Olemba Baibulo ena ofanana ndi ameneŵa anali Davide yemwe anali woŵeta nkhosa, Amosi yemwe anali mlimi, ndi Yuda, mbale wa Yesu yemwe ayenera kuti anali kalipentala.

Yobu ankatha kuŵerenga ndi kulemba, ndipo buku la m’Baibulo limene lili ndi dzina lake limasonyeza kuti ankadziŵa sayansi. Ayeneranso kuti anali ndi luso la zolembalemba, chifukwa mawu ake amene ali m’buku la Yobu analembedwa mwandakatulo. Ndipo timadziŵa kuti Akristu oyambirira anali ophunzira chifukwa chakuti pali mapale olembedwapo notsi za Malemba zimene akuziganizira kuti ndi za Akristuwo.

Maphunziro Ndi Ofunika Kwambiri kwa Akristu

Akristu onse afunika kupita patsogolo pa kudziŵa kwawo Baibulo ngati akufuna kusangalatsa Mulungu. (Afilipi 1:9-11; 1 Atesalonika 4:1) Kuŵerenga mwakhama Malemba ndiponso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo kungathandize kuti munthu apite patsogolo mwauzimu. Popeza Mulungu wapereka Mawu ake olembedwa, amayembekezera olambira ake kukhala ophunzira mmene angathere. Kuŵerenga Baibulo molimvetsa kumathandiza kuti kukhale kosavuta kutsatira malangizo ake. Ngakhale kuti tingafunike kuŵerenga zigawo zina maulendo angapo kuti timvetse mfundo zake ndi kuzisinkhasinkha.​—Salmo 119:104; 143:5; Miyambo 4:7.

Chaka chilichonse, anthu a Yehova amalandira nkhani zambiri zolembedwa zothandiza kwambiri, ndipo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi amene amayang’anira ntchito imeneyi. (Mateyu 24:45-47) Mabuku ndi magazini amenewo amafotokoza nkhani zokhudza banja, miyambo, chipembedzo, sayansi, ndi nkhani zina zambiri. Chofunika kwambiri n’chakuti amakhala ndi malangizo a m’Malemba pankhani zauzimu. Ngati ana anu sangathe kuŵerenga, nkhani zofunika kwambiri zidzawapita.

Kuphunzira mbiri ya anthu n’kofunika kwambiri chifukwa kumatithandiza kumvetsetsa chifukwa chake tifunikira Ufumu wa Mulungu. Kudziŵako za jogalafe n’kofunikanso. Baibulo limatchula malo ambiri, monga Israyeli, Igupto, ndi Girisi. Kodi mwana wanu angathe kulodza malo ameneŵa pa mapu osonyeza dziko lonse? Kodi angathe kupeza pamene pali dziko lake? Kusadziŵa mapu kukhozanso kulepheretsa munthu kuchita zambiri potumikira m’gawo limene wapatsidwa.​—2 Timoteo 4:5.

Maudindo Mumpingo

Akulu achikristu ndi atumiki otumikira ali ndi ntchito zambiri zimene zimafuna kuŵerenga. Mwachitsanzo, pali nkhani zofunika kuzikonzekera zokakamba ku misonkhano ya mpingo. Pamafunika kusunga kaundula wa mabuku ndi magazini ndiponso zopereka. Ngati munthu sanaphunzire, zingamuvute kwambiri kusamalira ntchito zimenezi moyenera.

Antchito odzipereka amatumikira pa nyumba za Beteli padziko lonse. Kuti antchito ameneŵa azilankhulana bwino ndi kugwira ntchito zawo, monga kumasulira mabuku ndi kukonza makina, ayenera kutha kuŵerenga ndi kulemba chinenero cha boma cha m’dziko limene akukhalalo. Kuti ana anu adzakhale ndi mwayi wotumikira ngati umenewu, afunika kuphunzira. Kodi ndi zifukwa zinanso zabwino ziti zimene mwana wanu afunikira kupita kusukulu?

Umphaŵi Ndiponso Kukhulupirira Malodza

Anthu aumphaŵi angasoŵe pogwira nthaŵi zina. Komabe nthaŵi zina, kuphunzira mokwanira kungatithandize ife ndi ana athu kupeŵa mavuto obwera chifukwa chosaphunzira. Anthu ambiri osaphunzira amavutika kwambiri kupeza zofunika pa moyo. Ana ndiponso ngakhale makolo nthaŵi zina amamwalira chifukwa chakuti ndalama zochepa zimene amapeza n’zosakwanira kuti apezere chithandizo cha mankhwala. Anthu amene anangophunzira pang’ono kapena sanaphunzire n’komwe nthaŵi zambiri amavutika ndi matenda a kusoŵa zakudya m’thupi ndipo amakhala m’nyumba zosaoneka bwino. Maphunziro kapena ngakhale kudziŵa chabe kulemba ndi kuŵerenga kungathandize m’mbali zimenezi.

Kuphunzira kumachepetsanso kukonda kukhulupirira malodza. N’zoona kuti ophunzira ndi osaphunzira omwe amakhulupirira malodza. Koma osaphunzira angakhale osavuta kupusitsidwa ndi kudyeredwa masuku pamutu kusiyana ndi ophunzira, chifukwa sangaŵerenge nkhani zimene zimavumbula chinyengo choterocho. Motero, iwo amakonda kukhulupirira kwambiri malodza ndi kukhulupirira kuti sing’anga wamizimu angachiritse mozizwitsa.​—Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8.

Cholinga cha Maphunziro Sikungopeza Ntchito Kokha

Anthu ambiri amaganiza kuti cholinga chachikulu cha maphunziro n’choti azidzapeza ndalama. Komatu, anthu ena ophunzira sali pantchito kapena sapeza ndalama zambiri zogulira zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Chifukwa cha zimenezi, makolo ena angaganize kuti kutumiza ana kusukulu n’kopanda phindu. Koma phindu la sukulu sindilo lakuti munthu azidzapeza ndalama basi ayi. Imathandiza ana kukonzekera mbali zina zonse za moyo. (Mlaliki 7:12) Ngati munthu angathe kulankhula, kuŵerenga, ndi kulemba m’chinenero cha boma cha dziko limene akukhala, kulankhulana ndi ogwira ntchito kuchipatala, akuluakulu a boma, kapena ogwira ntchito ku banki kumakhala kosavuta, ngati chinthu wamba, m’malo mochititsa mantha.

M’madera ena, ana osaphunzira angaperekedwe kwa munthu wina kuti awaphunzitse ntchito yomanga nyumba, usodzi, kusoka, kapena ntchito zina. Kuphunzira ntchito n’kwabwino, koma ngati ana ameneŵa sanapite kusukulu mwina sadzadziŵa kuŵerenga ndi kulemba molondola. Mosakayika, iwo angapeŵe kudyeredwa masuku pamutu ndiponso angakhale ndi moyo wosangalatsa akanakhala kuti anayamba aphunzira kusukulu ndiyeno n’kuphunzira ntchitoyo.

Yesu wa ku Nazarete anali kalipentala ndipo mwachionekere atate ake omulera, Yosefe, anam’phunzitsa ntchitoyo. (Mateyu 13:55; Marko 6:3) Yesu ankadziŵanso kulemba ndi kuŵerenga, chifukwa ngakhale pamene anali ndi zaka 12, anatha kukambirana bwino kwambiri ndi anthu ophunzira pakachisi. (Luka 2:46, 47) Kwa Yesu, kuphunzira ntchito sikunadodometse maphunziro ena.

Kodi Ana Aakazi Aziphunziranso?

Makolo nthaŵi zina amatumiza ana awo aamuna kusukulu koma osati ana aakazi. Mwina makolo ena amaganiza kuti kuphunzitsa ana awo aakazi kumafuna ndalama zambiri ndiponso amakhulupirira kuti atsikana angathandize kwambiri mayi awo ngati akhala pakhomo tsiku lonse. Koma kusaphunzira kungalepheretse mwana wanu wamkazi kuchita zinthu zina. Kabuku ka bungwe loona za ana la United Nations Children’s Fund (UNICEF) kanati: “Kufufuza kumene kwachitika nthaŵi zambiri kukusonyeza kuti kuphunzitsa atsikana ndi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zothetsera umphaŵi.” (Poverty and Children: Lessons of the 90s for Least Developed Countries) Atsikana ophunzira amakhala okonzeka kuthana ndi mavuto pa moyo wawo ndi kusankha zochita mwanzeru, ndipo motero amathandiza ena onse m’banjamo.

Atafufuza za imfa za ana ku Benin, West Africa, anapeza kuti mwa ana 1,000 alionse a amayi osaphunzira, ana 167 amamwalira asanakwanitse zaka zisanu, pamene kwa amayi amene anamaliza sukulu kusekondale, ana 38 mwa ana 1,000 alionse ndi amene amamwalira. Bungwe la UNICEF linati: “Motero, kuphunzira kumachepetsa imfa za ana pamene kusaphunzira kumachititsa kuti imfa za ana zichuluke ku Benin, monga mmenenso zilili padziko lonse.” Ndiyetu, kuphunzitsa ana anu aakazi kuli ndi phindu lochuluka.

Kodi Makalasi Ophunzitsa Kulemba ndi Kuŵerenga Ndi Okwanira?

Mboni za Yehova zimakhala ndi makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga pakafunikira kutero kwa anthu a mumpingo amene sangathe kuŵerenga. * Dongosolo labwino limeneli limathandiza anthu kuphunzira kuŵerenga, nthaŵi zambiri m’chinenero chawo. Kodi makalasi ameneŵa ayenera kutenga malo a sukulu? Kodi muyenera kuyembekezera kuti mpingo uphunzitse mwana wanu ngakhale ngati sukulu zimene angathe kumapita zilipo?

Ngakhale kuti makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga ndi dongosolo labwino limene mipingo ya Mboni za Yehova imachita, makalasiŵa ndi a anthu achikulire osaphunzira amene sanapite ku sukulu ali ana. Mwina makolo awo sankadziŵa kufunika kophunzira, kapena sukuluzo kunalibe. Anthu oterowo angathandizidwe mwa kukhala nawo m’makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerengaŵa amene amachitika m’mipingo. Koma makalasi ameneŵa sayenera kutenga malo a sukulu ndipo sanawakonze kuti aziphunzitsa maphunziro a kupulayimale. Maphunziro monga sayansi, masamu, ndi histole saphunzitsa m’makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerengaŵa. Koma maphunziro ameneŵa amaphunzitsidwa kusukulu zimene ana amapitako.

Ku Africa, makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga nthaŵi zambiri amachitika m’zinenero za mafuko a dzikolo ndipo ndi nthaŵi zochepa zimene amachitika m’chinenero cha boma cha dzikolo. Koma maphunziro a kusukulu nthaŵi zambiri amachitika m’chinenero cha boma. Zimenezi zimathandiza anawo kupeza phindu lina chifukwa mabuku ambiri ndi zinthu zina zofunika kuŵerenga zimalembedwa m’chinenero cha bomacho. Ngakhale kuti makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba a mpingo angawonjezere pa maphunziro a kusukulu a anawo, sangaloŵe m’malo mwake. Motero, ngati n’kotheka, kodi si bwino kuti ana azipita kusukulu?

Udindo wa Makolo

Amuna amene amatsogolera popereka zosoŵa zauzimu za mpingo ayenera kukhala Akristu achitsanzo chabwino. Ayenera kuweruza “bwino” nyumba yawo ndi ana awo. (1 Timoteo 3:4, 12) Kuweruza “bwino” kungaphatikizepo kuchita zonse zotheka pothandiza ana athu kuti adzapeŵe mavuto m’tsogolo.

Mulungu wapereka udindo waukulu kwa makolo achikristu. Ayenera kulera ana awo motsatira Mawu ake ndi kuwathandiza kukhala ‘okonda kudziŵa.’ (Miyambo 12:1; 22:6; Aefeso 6:4) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Ana athu ayeneranso kupeza maphunziro oyenera.

Nthaŵi zina sukulu sizitha kuphunzitsa bwino ana chifukwa cha kuchulukana, kusoŵa ndalama zoyendetsera sukulu, kapena kusasangalala kwa aphunzitsi omwe amalandira ndalama zochepa kwambiri. Motero, n’kofunika kuti makolo azionetsetsa zimene ana awo akuphunzira kusukulu. Ndi bwino kudziŵana ndi aphunzitsi awo, makamaka kumayambiriro kwa teremu iliyonse, ngakhale kuwafunsa malangizo awo a mmene anawo angakhalire ana a sukulu abwino. Zimenezi zingachititse aphunzitsiwo kuona kuti amalemekezedwa ndipo zingawalimbikitse kuchita khama kwambiri kuti aphunzitse bwino anawo.

Maphunziro ndi ofunika kwambiri kuti mwana akule bwino. Lemba la Miyambo 10:14 limati: “Anzeru akundika zomwe adziŵa.” Zimenezi zimakhaladi choncho makamaka ngati munthu wadziŵa za m’Baibulo. Anthu a Yehova, kaya achichepere kapena achikulire, ayenera kudziŵa zambiri kuti athandize ena mwauzimu ndiponso kuti ‘adzionetsere kwa Mulungu ovomerezeka, antchito opanda chifukwa cha kuchita manyazi, olunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15; 1 Timoteo 4:15) Motero, kodi ana anu ayenera kupita kusukulu? Mosakayika mungavomereze kuti ayeneradi kutero, ngakhale kuti zambiri zidzadalira zinthu zomwe zingatheke m’dziko lanu. Koma makolo achikristu afunika kuyankha funso lofunika kwambiri ili lakuti, ‘Kodi ana anga ayenera kuphunzira?’ Kodi simukuvomereza kuti yankho lake liyenera kukhala inde wamphamvu mosaganizira kuti kaya mukukhala kuti?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Chinenero chawo mwina chinali Chialamu cha ku Galileya kapena kalankhulidwe kena ka Chihebri. Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, masamba 144 mpaka 146 lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 12, 13]

NGATI N’ZOSATHEKA KUPITA KU SUKULU

Nthaŵi zina n’zosatheka kupita ku sukulu. Mwachitsanzo, magazini ya Refugees inati mwana mmodzi yekha mwa ana asanu amene ali oyenerera kupita ku sukulu ndi amene amapita ku sukulu m’misasa ya othaŵa kwawo. Nthaŵi zina, sukulu zimakhala zotseka kwanthaŵi yaitali chifukwa chakuti aphunzitsi anyanyala ntchito. Mu dera lina sukulu zingakhale kutali kapena sizingapezeke n’komwe. Kuzunzidwa kwa Akristu kungapangitse kuti ana achotsedwe sukulu.

Kodi mungathandize bwanji ana anu ngati zinthu zili choncho? Kodi mungachite chiyani ngati muli ndi ana angapo ndipo mukukhala ku dera limene ndalama zolipirira sukulu zapangitsa kukhala kosatheka kuti ana anu onse apite ku sukulu? Kodi mungakwanitse kulipirira mwana mmodzi kapena aŵiri sukulu popanda kuwononga moyo wawo wauzimu? Ngati ndi choncho, ana amene amapita kusukuluwo angathe kuthandiza ana anu ena zimene akuphunzira kusukuluko.

M’mayiko ena muli maphunziro omwe amawatcha kuti apanyumba. * Pa maphunziro ameneŵa, nthaŵi zambiri kholo limodzi limathera maola angapo kuphunzitsa mwana tsiku lililonse. M’nthaŵi za makolo akale, makolo zinawayendera bwino zedi pophunzitsa ana awo. Zikuoneka kuti chifukwa chakuti makolo anamuphunzitsa bwino, Yosefe mwana wa Yakobo anatha kuyang’anira anthu ena ali wamng’ono.

Ndondomeko ya maphunziro, kapena kuti zimene ana amakaphunzira kusukulu, ingakhale yovuta kuipeza m’malo onga m’msasa wa othaŵa kwawo, koma makolo angathe kugwiritsira ntchito mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova monga gwero la malangizo. Mwachitsanzo, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lingakhale lothandiza pophunzitsa ana anu aang’ono. Magazini ya Galamukani! imakhala ndi nkhani zambiri zosiyanasiyana. Buku lakuti Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?, lingagwiritsidwe ntchito pophunzitsa nkhani zokhudza sayansi. Yearbook ya Mboni za Yehova ili ndi mapu aang’ono osonyeza dziko lonse lapansi ndipo imafotokoza zamoyo wa anthu ndiponso ntchito yolalikira m’mayiko osiyanasiyana.

Zingakuyendereni bwino kwambiri ngati mukonzekera bwino ndiponso mufotokoza malangizowo moti anawo amva malinga ndi msinkhu wawo. Ngati apitiriza kuŵerenga ndi kuphunzira, iwo sadzavutika kuzoloŵera mwayi wopita ku sukulu ukadzapezeka. Mwakuyambirira ndiponso kuyesetsa, mungathandize ana anu kukhala ophunzira bwino. Ndipo zimenezitu zingakhale zopindulitsa kwambiri!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 40 Onani nkhani yakuti “Home Schooling​—Is It for You?” mu Galamukani! yachingelezi ya April 8, 1993, masamba 9-12.

[Chithunzi]

Kodi mungachite chiyani ngati kumene mukukhala n’koti ana anu sangathe kumapita ku sukulu?