Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Umphaŵi Udzatha?

Kodi Umphaŵi Udzatha?

Kodi Umphaŵi Udzatha?

“TAONA, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza,” inatero mfumu yanzeru Solomo ya ku Israyeli wakale. (Mlaliki 4:1) Mosakayikira, anthu ambiri otsenderezedwa amene iye anali kunena, analinso amphaŵi.

Sikuti ndi ziŵerengero zokha za ndalama zimene anthu amawononga pa tsiku zimene zimasonyeza kuti anthuwo ndi amphaŵi. Malinga n’kuŵerengera kumene a World Bank anachita mu June 2002, “akuti mu 1998 anthu pafupifupi 1,200,000,000 padziko lonse ankagwiritsa ntchito ndalama zosakwana dola imodzi pa tsiku . . . ndipo anthu pafupifupi 2,800,000,000 ankagwiritsa ntchito ndalama zosakwana madola aŵiri pa tsiku.” Anatinso ngakhale kuti ziŵerengero zimenezi n’zotsika poziyerekezera ndi za m’mbuyomo, “n’zapamwamba kwambiri tikatengera ndi mmene anthu akuvutikira.”

Kodi umphaŵi udzatha? Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti: “Osauka muli nawo pamodzi ndi inu nthaŵi zonse.” (Yohane 12:8) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti umphaŵi ndi mavuto ake sizidzatha? Sizikutanthauza zimenezo. Ngakhale kuti Yesu sanalonjeze otsatira ake kuti onse adzakhala olemera, tisawatenge mawu akeŵa kuti akutanthauza kuti osauka zinthu sizidzawayendera bwino m’tsogolo.

Ngakhale kuti anthu ayesetsa ndiponso ngakhale zimene amalonjeza zothetsa umphaŵi zalephereka, Mawu a Mulungu, Baibulo, amatitsimikizira kuti posachedwapa sipadzakhala anthu osoŵa. Ndipotu, Yesu anauza “anthu osauka Uthenga Wabwino.” (Luka 4:18) Uthenga wabwino umenewu unalinso ndi lonjezo lakuti umphaŵi udzathetsedwa. Izi zidzachitika Ufumu wa Mulungu ukadzakonza zinthu padziko lapansi kukhala zabwino.

Si mmene dzikoli lidzasinthire! Mfumu yakumwamba Yesu Kristu “adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” Inde, “adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.”​—Salmo 72:13, 14.

Pofotokoza za nthaŵi imeneyo, Mika 4:4 amati: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse amene akuvutitsa anthu, ngakhale matenda ndi imfa. Mulungu ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’​—Yesaya 25:8.

Mungatsimikizire kuti malonjezo ameneŵa adzachitika chifukwa ndi ouziridwa ndi Mulungu mwiniyo. Bwanji osapenda umboni wotsimikizira kuti maulosi a Baibulo ndi odalirika?

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

FAO photo/​M. Marzot