Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Limbikani, Ine Ndaligonjetsa Dziko Lapansi”

“Limbikani, Ine Ndaligonjetsa Dziko Lapansi”

“Limbikani, Ine Ndaligonjetsa Dziko Lapansi”

TSIKU limene Yesu anafa linayamba Lachinayi dzuŵa litaloŵa, pa March 31, mu 33 C.E. Tsikulo linali la 14 pamwezi wachiyuda wa Nisani. Usiku umenewu, Yesu ndi atumwi ake anasonkhana m’chipinda chapamwamba cha nyumba ya ku Yerusalemu kuchita Paskha. Yesu akukonzekera “kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate,” anasonyeza kuti anakonda atumwi ake mpaka chimaliziro. (Yohane 13:1) Anasonyeza motani? Mwa kuwaphunzitsa mfundo zabwino, powakonzekeretsa zinthu za m’tsogolo.

Usiku womwewo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Limbikani, Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.” (Yohane 16:33, Chipangano chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Kodi iye anali kutanthauza chiyani ndi mawu olimbikitsa ameneŵa? Mbali ina, anali kutanthauza kuti: ‘Sindinakwiye ndi mphamvu zoipa za m’dzikoli kapena kubwezera. Sindinalole kuti dziko lapansi lisinthe makhalidwe anga. Inunso mungachite chimodzimodzi.’ Zimene Yesu anaphunzitsa atumwi ake okhulupirika m’maola omaliza amenewo a moyo wake padziko lapansi zikawathandizanso kugonjetsa dziko lapansi.

Ndani angatsutse zoti masiku ano kuipa n’kochuluka m’dzikoli? Kodi timatani anthu akamachita zachinyengo kapena chiwawa chosasimbika? Kodi zimatipangitsa kusunga chakukhosi kapena timafuna kubwezera zomwezo? Kodi kuipa kwa makhalidwe kumatikhudza bwanji? Kuphatikiza pamenepa, ndife opanda ungwiro ndiponso timakonda kuchita zoipa, choncho timalimbana ndi zinthu ziŵiri: dziko loipali ndi zilakolako zathu zoipa. Kodi tingayembekezeredi kupambana popanda thandizo la Mulungu? Kodi tingalipeze bwanji thandizo lake? Kodi ndi makhalidwe ati amene tifunika kukhala nawo kuti tigonjetse zilakolako za thupi? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tione zimene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake okondedwa pa tsiku lomaliza la moyo wake padziko lapansi.

Gonjetsani Kunyada mwa Kukhala Odzichepetsa

Mwachitsanzo, onani kuipa kwa kunyada, kapena kuti kudzikuza. Ponena za zimenezi, Baibulo limati: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” (Miyambo 16:18) Malemba amatilangizanso kuti: “Ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.” (Agalatiya 6:3) Inde, kunyada ndi kowononga komanso konyenga. Tingachite bwino kudana ndi “kunyada, ndi kudzikuza.”​—Miyambo 8:13.

Kodi atumwi a Yesu anali ndi vuto lonyada ndi lodzikuza? Panthaŵi ina, anakangana okhaokha za amene anali wamkulu. (Marko 9:33-37) Panthaŵi inanso, Yakobo ndi Yohane anapempha malo apamwamba mu Ufumu. (Marko 10:35-45) Yesu anafuna kuthandiza ophunzira ake kuthetsa khalidwe limeneli. Chotero akudya chakudya cha Paskha, anaimirira, n’kudzimangirira chopukutira m’chuuno, n’kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake. Phunziro limene anafuna kuti iwo atolepo linali loonekeratu. Yesu anati: “Ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.” (Yohane 13:14) Tiyenera kukhala odzichepetsa m’malo mokhala onyada.

Komabe, si kophweka kugonjetsa kunyada. Nthaŵi ina madzulo omwewo Yesu atam’chotsa Yudasi Isikarioti, amene anali pafupi kum’pereka, panabuka mkangano waukulu pakati pa atumwi 11 aja. Nkhani yake? Kufuna kudziŵa yemwe anali wamkulu pakati pawo. M’malo mowakalipira, apanso Yesu anagogomezera moleza mtima kufunika kotumikirana. Iye anati: “Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino. Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.” Powakumbutsa za chitsanzo chake, ananenanso kuti: “Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.”​—Luka 22:24-27.

Kodi atumwiwo anatola mfundo yake? Zikuoneka choncho. Patapita zaka, mtumwi Petro analemba kuti: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) N’kofunika kwambiri kuti ifenso tigonjetse kunyada mwa kukhala odzichepetsa. Tingachite bwino kusatanganidwa kwambiri ndi kufunafuna kutchuka, ulamuliro kapena udindo. Baibulo limati: “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” (Yakobo 4:6) Mwambinso wanzeru wakale umati: “Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”​—Miyambo 22:4.

Kodi Tingagonjetse Bwanji Udani?

Onaninso khalidwe lina lofala m’dzikoli​—udani. Udani ukuoneka kuti uli ponseponse ndipo umayamba ndi zinthu ngati mantha, umbuli, tsankho, kuponderezana, chinyengo, kukonda dziko, fuko kapena mtundu wako. (2 Timoteo 3:1-4) Udani unalinso wofala m’masiku a Yesu. Ayuda anali kuda anthu okhometsa msonkho ndi kuwapatula. Ayuda sanali kuyenderana ndi Asamariya. (Yohane 4:9) Ndipo Akunja, kapena kuti amene sanali Ayuda, analinso kudedwa ndi Ayuda. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, njira yolambirira imene Yesu anayambitsa inali yolandira anthu a mitundu yonse. (Machitidwe 10:34, 35; Agalatiya 3:28) Choncho, chifukwa chowakonda, anawapatsa ophunzira ake chinthu china chatsopano.

Yesu ananena kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” Iwo anafunika kuphunzira kusonyeza chikondi chimenechi, n’kuona iye anapitiriza kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Lamuloli linali latsopano chifukwa chakuti limafuna zoposa ‘kungokonda mnansi wako monga udzikonda wekha.’ (Levitiko 19:18) Mwanjira yanji? Yesu anafotokozera zimenezi mwa kunena kuti: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:12, 13) Ophunzirawo anayenera kukhala ofunitsitsa kupereka moyo wawo weniweniwo chifukwa cha ena.

Kodi anthu opanda ungwiro angathetse bwanji udani woipa kwambiri pamoyo wawo? Mwa kukhala ndi chikondi chodzimana m’malo mwa udani. Anthu ambiri oona mtima ochokera m’mafuko onse, chikhalidwe, zipembedzo ndi magulu a ndale osiyanasiyana, akuchita zimenezi. Tsopano akusonkhanitsidwa m’gulu la anthu ogwirizana, osadana, kupanga ubale wapadziko lonse wa Mboni za Yehova. Amatsatira mawu ouziridwa a mtumwi Yohane akuti: “Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziŵa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.” (1 Yohane 3:15) Akristu oona saloŵerera nkhondo iliyonse komanso amayesetsa kwambiri kusonyezana chikondi.

Komabe, kodi tiyenera kuwaona bwanji anthu amene si okhulupirira anzathu amene mwina amatida? Yesu ali pamtengo wozunzirapo anapempherera anthu amene anali kumuphawo. Anati: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.” (Luka 23:34) Pamene anthu audani anam’ponya miyala wophunzira Stefano mpaka kumupha, mawu omaliza amene iye ananena anali akuti: “Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili.” (Machitidwe 7:60) Yesu ndi Stefano anafunira zabwino ngakhale anthu amene anali kuwada. Analibe nawo chifukwa m’mitima yawo. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Tichitire onse chokoma.”​—Agalatiya 6:10.

‘Wothandiza Nthaŵi Yonse’

Msonkhano umene anachita ndi atumwi ake 11 okhulupirika uli m’kati, Yesu anawauza kuti pakapita nthaŵi pang’ono sakhala nawonso. (Yohane 14:28; 16:28) Koma anawatsimikizira kuti: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina [“wothandiza wina,” NW] kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse.” (Yohane 14:16) Wothandiza amene analonjezayo ndi mzimu woyera wa Mulungu. Unali kudzawaphunzitsa zinthu zakuya za m’Malemba ndiponso kuwakumbutsa zimene Yesu anawaphunzitsa mu utumiki wake padziko lapansi.​—Yohane 14:26.

Kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji masiku ano? Chabwino, Baibulo ndi Mawu ouziridwa a Mulungu. Amuna amene anagwiritsidwa ntchito kunena maulosi ndi kulemba Baibulo anali “ogwidwa ndi Mzimu Woyera.” (2 Petro 1:20, 21; 2 Timoteo 3:16) Kuphunzira kwathu Malemba ndi kugwiritsira ntchito zimene tikuphunzirazo kumatithandiza kukhala odziŵa zinthu, anzeru, omvetsa bwino zinthu, aluntha, ozindikira. Kodi pamenepa sindife okonzekera bwino kulimbana ndi mavuto a m’dziko loipali?

Mzimu woyera ndi wothandiza m’njira inanso. Mzimu woyera wa Mulungu ndi mphamvu yothandiza kwambiri. Imathandiza anthu amene imawalamulira kusonyeza makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Baibulo limati: “Chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” Kodi ameneŵa si makhalidwe enieniwo amene timafunika kuti tigonjetse zilakolako za thupi zimene zimatsogolera ku chiwerewere, ndewu, kaduka, kupsa mtima, ndi zinthu zangati zimenezo?​—Agalatiya 5:22, 23.

Mwa kudalira mzimu wa Mulungu, tingalandirenso “mphamvu yoposa yachibadwa,” kuti tithane ndi mavuto alionse kapena kuvutika maganizo. (2 Akorinto 4:7, NW) Ngakhale kuti mzimu woyera sungachotse mayesero ndi zokopa, ungatithandize kwambiri kupirira zimenezi. (1 Akorinto 10:13) Mtumwi Paulo anati: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Mulungu amapereka mphamvu imeneyo mwa mzimu wake woyera. Tiyeneratu kuyamikira kwambiri mzimu woyera! Amaupereka kwa anthu amene ‘amakonda Yesu ndi kusunga malamulo ake.’​—Yohane 14:15.

“Khalani M’chikondi Changa”

Usiku wake womaliza padziko lino lapansi, Yesu anauzanso atumwi ake kuti: “Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga.” (Yohane 14:21) Iye anawapempha kuti: “Khalani m’chikondi changa.” (Yohane 15:9) Kodi kukhala m’chikondi cha Atate ndi Mwana kumatithandiza bwanji polimbana ndi zilakolako zathu zoipa ndi dziko loipali?

Kodi tingagonjetsedi makhalidwe oipa popanda chifukwa chotichititsa zimenezo? Kodi pangakhale chifukwa china kusiyapo kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu ndi Mwana wake? Ernesto, * mnyamata wina amene anamenyera nkhondo kwambiri kuti asiye kukonda chiwerewere kumene anayamba ali wamng’ono, anati: “Ndinkafuna kusangalatsa Mulungu, ndipo ndinaphunzira m’Baibulo kuti sakonda khalidwe lomwe ndinali nalo. Choncho ndinaganiza zosintha khalidwe langa kuti ndizitsatira malangizo a Mulungu. Tsiku lililonse, ndinkalimbana ndi maganizo oipa amene anali kundibwerera kwambiri m’maganizo. Koma ndinatsimikiza mtima kuti ndipambana nkhondo imeneyi basi, ndipo ndinapempha Mulungu kosalekeza kuti andithandize. Patatha zaka ziŵiri mbali yaikulu ya nkhondoyi inatha, ngakhale kuti ndimadziletsabe kwambiri.”

Pankhani yolimbana ndi dzikoli, onani pemphero lomaliza limene Yesu anapemphera asanachoke m’chipinda chapamwamba cha ku Yerusalemu. Popempherera ophunzira ake, anati kwa Atate wake: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Sali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:15, 16) Mawu olimbikitsa bwanji! Yehova amasunga amene amawakonda ndipo amawalimbikitsa pamene akusiyana ndi dzikoli.

“Khulupirirani”

Kutsatira malamulo a Yesu kungatithandizedi kupambana polimbana ndi dziko loipali ndiponso zilakolako zathu zoipa. Komabe, ngakhale kuti kupambana n’kofunika, sikungachotse dzikoli kapena uchimo umene timabadwa nawo. Koma tisataye mtima.

Baibulo limati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Yesu anapereka moyo wake kupulumutsa “yense wakukhulupirira Iye” ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16) Choncho, pamene tikupitiriza kudziŵa zambiri ponena za zimene Mulungu amafuna ndi zolinga zake, tiyeni titsatire malangizo a Yesu akuti: ‘Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.’​—Yohane 14:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 Si dzina lake lenileni.

[Chithunzi pamasamba 6, 7]

Yesu anapempha atumwi ake kuti: “Khalani m’chikondi changa”

[Chithunzi patsamba 7]

Posachedwapa tidzamasukadi ku uchimo ndi mavuto ake