Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khoti Lalikulu Lagamula Kuti Kulambira Koona Kupitirire ‘M’dziko la ku Ararati’

Khoti Lalikulu Lagamula Kuti Kulambira Koona Kupitirire ‘M’dziko la ku Ararati’

Khoti Lalikulu Lagamula Kuti Kulambira Koona Kupitirire ‘M’dziko la ku Ararati’

Bambo wa ana atatu, wa tsitsi la imvi, waimirira m’khoti lalikulu kwambiri la m’dziko lake. Ufulu wake, komanso wa anthu ambiri a chipembedzo chake, ukuopsezedwa. Anthu a m’khotilo akumvetsera pamene iye akugwiritsa ntchito Baibulo kufotokoza zikhulupiriro zake. Kuti timvetsetse mmene mlandu umenewu unabweretsera ufulu wa chipembedzo choona m’dziko limenelo, tiyeni tione kaye zimene zinachititsa kuti zinthu zifike pamenepa.

DZIKO la Armenia lili kum’maŵa kwa dziko la Turkey, ndiponso lili chakum’mwera kwa mtandadza wa mapiri otchedwa Caucasus. M’dzikoli muli anthu opitirira mamiliyoni atatu. Mukakhala mu likulu la dzikoli, Yerevan, mumaona bwino kwambiri nsonga ziŵiri za phiri la Ararati, pamene panatera chingalawa cha Nowa chigumula chitatha, malinga ndi kunena kwa mbiri.​—Genesis 8:4. *

Mboni za Yehova zakhala zikugwira ntchito yawo yachikristu ku Armenia kuyambira mu 1975. Dziko la Armenia litalandira ufulu wake mu 1991 kuchoka ku dziko limene kale linali Soviet Union, linakhazikitsa bungwe loti zipembedzo zizikalembetsako lotchedwa State Council for Religious Affairs. Koma bungwe limeneli nthaŵi zambiri lakana kulemba chipembedzo cha Mboni za Yehova, makamaka chifukwa chakuti siziloŵerera nawo m’ndale zadziko. N’chifukwa chake kuyambira 1991, achinyamata a Mboni opitirira 100 ku Armenia aimbidwa milandu ndipo ambiri a iwo anaikidwa m’ndende chifukwa chokana kuloŵa nawo usilikali potsatira zimene Baibulo limanena.

Bungweli linapempha oimira mbali ya boma ku khoti kuti afufuze ntchito yachipembedzo imene amachita Lyova Margaryan. Iyeyu ndi mkulu wachikristu komanso loya wolimbikira kwambiri amene analembedwa ntchito pa fakitale ina yokonza magetsi. Pamapeto pake, Mbale Margaryan anamuuza kuti walakwira lamulo nambala 244, lomwe ndi lamulo lakalekale limene analitenga ku malamulo a dziko la Soviet Union pansi pa ulamuliro wa Khrushchev. Lamulo limeneli cholinga chake chinali kupondereza, kenaka kuthetseratu gulu la Mboni za Yehova ndi magulu enanso a chipembedzo.

Lamulo limeneli limati n’kulakwira boma kuyambitsa kapena kutsogolera gulu lachipembedzo limene limangonamizira kuti likulalikira zikhulupiriro zachipembedzo, koma limakhala ‘likukopa achinyamata kuti azikapezeka nawo pamisonkhano ya chipembedzo ya gulu losalembetsa ku boma’ ndipo ‘limachititsa otsatira ake kukana kugwira ntchito za boma.’ Kuti anthu am’khulupirire, woimira boma pa mlanduwu anati akunena izi chifukwa pamisonkhano imene Mbale Margaryan amachititsa mu mzinda wa Metsamor pamapezekanso ana aang’ono. Iye anatinso Mbale Margaryan amanyengerera achinyamata a mu mpingo mwake kuti azikana kuloŵa usilikali.

Ayamba Kuzenga Mlanduwo

Mlanduwo unayamba Lachisanu pa July 20, 2001, m’khoti laling’ono la ku Armavir, ndipo jaji amene amatsogolera zonse anali Manvel Simonyan. Unapitirira mpaka mu August. Popereka umboni wawo, ena a ku mbali ya boma pamapeto pake anaulula kuti anthu a m’bungwe la National Security Ministry (limene kale linali KGB) anachita kuwauza zina mwa zimene analemba pa zikalata zawo zoneneza Mbale Margaryan ndiponso anachita kuwakakamiza kuti asaine zikalatazo. Pa nthaŵi ina, mzimayi wina anaulula kuti munthu wina wa udindo wa m’bungwe la Security Ministry anamuuza kuti akaname kuti “Mboni za Yehova zimadana ndi boma lathu ndiponso chipembedzo chathu.” Mzimayiyu anavomera kuti sakudziŵa munthu wa Mboni aliyense koma anangomva pa TV ya boma zoti a Mboni ndi anthu oipa.

Pamene inafika nthaŵi yoti Mbale Margaryan alankhulepo, iye ananena kuti ana aang’ono amene amapezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova amakhala atalolezedwa kubwera ndi makolo awo. Iye anafotokozanso kuti munthu amasankha yekha kuloŵa usilikali kapena kukana. Loya woimira boma anapitiriza kum’funsa Mbale Margaryan mafunso ambirimbiri kwa masiku angapo. Mbale Margaryan anayankha mafunso onse okhudzana ndi chikhulupiriro chake mwachifatse pogwiritsa ntchito Baibulo, ndipo loya woimira bomayo amayang’ana Malembawo m’Baibulo mwake.

Pa September 18, 2001, jaji anagamula kuti Mbale Margaryan “ndi wosalakwa,” ndipo anati ntchito yachipembedzo imene amachita “sinaphwanye lamulo lililonse.” Mu nyuzipepala yotchedwa Associated Press analembamo lipoti lofotokoza zoona zake za mlanduwu. Ilo linati: “M’tsogoleri wa Mboni za Yehova ku Armenia lero wapezeka wosalakwa pa mlandu wolalikira popanda chilolezo komanso kukakamiza achinyamata kuti akane kuloŵa usilikali. Pamapeto pa mlanduwu, umene watha miyezi iŵiri, khotilo lanena kuti panalibe umboni wokwanira woipira m’tsogoleriyo, Levon Markarian [Lyova Margaryan]. Akanapezeka wolakwa akanatha kukhala m’ndende mpaka zaka zisanu. . . . Ngakhale kuti malamulo a dziko la Armenia amapereka ufulu wa chipembedzo, zimavuta kwambiri kuti zipembedzo zatsopano zilembetse kuboma ndipo malamulowa amangokomera chipembedzo chachikulu m’dzikoli cha Armenian Apostolic Church.” Chikalata chimene a bungwe la Organization for Security and Cooperation in Europe (OSCE) anatulutsa pa September 18, 2001, chinati: “Ngakhale kuti ndife osangalala ndi chigamulo chimenechi, ndife okhumudwabe kuti mlandu umenewu unaloledwa poyamba pomwe kuti uchitike.”

Mlanduwo Upitirira

Komabe, maloya oimira boma anakasumanso mlanduwu ku khoti lalikulu, ndipo kumeneko unatha miyezi ina inayi. Kumayambiriro kwa mlanduwo, panthaŵi yoti Mbale Margaryan alankhulepo, jaji mmodzi pagulu lamajaji a mlanduwo anam’funsa funso loyamba. Pamene Mbale Margaryan amati aziyamba kuyankha, jaji wamkulu anam’dula mawu pakamwa n’kum’funsa funso lina. Kuyambira pamenepa, sanamulole Mbale Margaryan kumaliza kuyankha funso n’limodzi lomwe. Kuphatikiza apo, iye sanalembe m’buku mafunso ambiri amene maloya a Mbale Margaryan anam’funsa, ndipo sanafotokoze chifukwa chimene anachitira zimenezi. Mkati mwa mlanduwu, anthu a zipembedzo zina odana ndi Mboni amene anadzaza m’khotimo anakhalira kunyoza Mbale Margaryan. Atatuluka m’khotimo, anaulutsa nkhani zabodza zambiri pa TV. Mwachitsanzo, iwo ananena kuti Mbale Margaryan amalankhula ngati kuti wavomera kale kuti ndi wolakwa.

Mlanduwu utafika pachimake, jaji wamkulu pa majaji atatu a pa mlanduwu anadabwitsa anthu potulutsa kalata yochokera ku bungwe la State Council for Religious Affairs yowalamula maloya aboma kuti ayenera kuchita zotheka kuti Mbale Margaryan zim’vute. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri anthu ochokera m’mayiko ena amene anabwera kudzaonerera mlanduwu chifukwa pamene dziko la Armenia linafunsa kuti likhale nawo mmodzi wa mayiko a m’bungwe la Council of Europe linavomera kuti lili ndi udindo “woonetsetsa kuti matchalitchi kapena mabungwe onse achipembedzo, makamaka amene amatchedwa ‘atsopano,’ akhoza kuchita ntchito zawo za chipembedzo popanda tsankho lililonse.”

M’milungu yotsatira imene mlanduwu umachitika, zinthu sizinali bwino ayi. Anthu odana ndi Mboni anapitirizabe kunyoza komanso kuukira Mboni mkati ndi kunja kwa khotilo. Azimayi a Mboni anamenyedwa mmiyendo, mu nsongolo. Wa Mboni wina atamuukira, sanabwezere komabe anam’menya pa fupa la msana, mpaka anakagonekedwa ku chipatala.

Pa nthaŵi imeneyi, jaji wamkulu watsopano anaikidwa kuti atsogolere mlanduwu. Ngakhale kuti anthu ena m’khotimo amayesetsabe kuwopseza loya wa Mbale Margaryan, jaji wamkuluyu anakhazikitsa bata m’khotimo, mpaka analamula apolisi kuti atulutse mzimayi wina amene ankakuwiza loya wa Mboniyo komanso kunena zinthu zomuopseza.

Autengera ku Khoti Lapamwamba la ku Armenia

Pomalizira pake, pa March 7, 2002, khotili linagamula mogwirizana ndi khoti laling’ono lija. Chodabwitsa n’chakuti, patatsala tsiku limodzi kuti chigamulo chimenechi chiperekedwe, bungwe la State Council for Religious Affairs lija analiphwasula. Kachiŵirinso, maloya a boma anakasumanso mlanduwu, ndipo ulendo uno anakasuma ku khoti lalikulu kwambiri m’dziko la Armenia, khoti la Cassation. Maloya a bomawo anapempha khoti lalikululi kuti liubweze m’mbuyo mlanduwu kuti upitenso ku khoti laling’ono kumene “akapereke chigamulo choti woimbidwa mlanduwu ndi wolakwa.”

Ma jaji 6, otsogozedwa ndi jaji wamkulu Mher Khachatryan, anakumana 11 koloko mmaŵa pa April 19, 2002. M’mawu ake oyamba, mmodzi mwa maloya a boma anati ndi wokwiya kwambiri chifukwa makhoti onse aŵiri aang’ono analephera kum’peza Mbale Margaryan kuti ndi wolakwa. Koma ulendo uno, loya wa bomayu ndi amene anadulidwa mawu pakamwa ndi majaji anayi ndipo anam’funsa mafunso ovuta kuyankha. Jaji mmodzi anakalipira loya wabomayo chifukwa chofuna kuipitsa maganizo a khotilo m’chikalata chake choneneza Mbale Margaryan chimene anatchulamo za ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova komanso ponena kuti Mboni za Yehova sizinalembetse ku boma. Koma zinthu zonsezi sizinali zolakwira lamulo nambala 244 la dziko la Armenia. Jajiyo kenaka ananena kuti zimene ankachita loya wa bomayo kunali “kuzunza pogwiritsa ntchito mlandu.” Jaji wina anatchulapo milandu ingapo ya ku khoti lalikulu la ku Ulaya la European Court imene Mboni za Yehova anazitcha “chipembedzo chodziŵika” chofunika kutetezedwa ndi bungwe loona za ufulu wa anthu la European Convention on Human Rights. Pa nthaŵi imeneyi, wansembe wina anakuwa m’khotimo, n’kunena kuti Mboni za Yehova zikugaŵanitsa mtundu wawo. Khotilo linamulamula kuti akhale chete.

Kenaka majajiwo anamuuza Mbale Margaryan kuti achoke m’gulu mwa anthumo abwere kutsogolo, chinthu chimene khotili silinachitepo n’kale lonse. Mbale Margaryan anapereka umboni wabwino kwambiri wokhudza zimene Mboni za Yehova, monga Akristu, zimachita pa nkhani zosiyanasiyana. (Marko 13:9) Atakakambirana kwa nthaŵi yochepa, majajiwo anabweranso m’khotimo ndipo anagwirizana ndi chigamulo choti “ndi wosalakwa.” Panthaŵi imeneyi, zimachita kuonekeratu kuti Mbale Margaryan tsopano akupumako bwino. M’chikalata chimene analembamo chigamulochi, khotili linati: “Ntchito iyi [ya Lyova Margaryan] sikuphwanya lamulo lililonse pa malamulo amene tili nawo, ndipo mlandu woterewu ndi wosemphana ndi lamulo nambala 23 la malamulo a dziko la Armenia, komanso lamulo nambala 9 limene mayiko anagwirizana pa msonkhano wa European Convention.”

Zimene Zachitika Chifukwa cha Chigamulochi

Mbale Margaryan akanapezeka wolakwa pa mlandu umenewu, zikanachititsa kuti akulu m’mipingo ya m’dziko lonse la Armenia aimbidwe milandu yotereyi. Chiyembekezo chathu n’choti chigamulo chomveka bwino chimene khotili lapereka chipangitsa kuti zimenezi zisachitike. Komanso, akanapeza kuti anali wolakwa, boma likanapeza chonamizira kuti lipitirize kukana kulemba chipembedzo cha Mboni za Yehova. Choncho, ndife oyamikira kwambiri kuona kuti khotili lachotsa chonamizira chimenechi.

Mkupita kwa nthaŵi, tidzaona ngati Mboni za Yehova zopitirira 7,000 zimene zili m’dzikoli adzazilole kulembetsa chipembedzo chawo ku boma. Koma pakadali pano, kulambira koona kukuyendabe bwino ‘m’dziko la ku Ararati.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ichi n’chifukwa china chimene anthu a ku Armenia akamaganiza za phiri la Ararati amangoona ngati lili m’dziko lawo. Kale, Armenia unali ufumu waukulu umene unkafika mpaka ku mapiri ameneŵa. N’chifukwa chake pa Yesaya 37:38, Baibulo lachigiriki la Septuagint, m’malo molemba kuti “dziko la ku Ararati” linangoti “Armenia.” Masiku ano phiri la Ararati lili m’dziko la Turkey, kufupi ndi malire ake a kummaŵa.

[Chithunzi patsamba 12]

Lyova Margaryan pa nthaŵi ya mlandu wake

[Chithunzi patsamba 13]

Mbale Margaryan ndi banja lake