Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufatsa Ndi Khalidwe Lachikristu Lofunika Kwambiri

Kufatsa Ndi Khalidwe Lachikristu Lofunika Kwambiri

Kufatsa Ndi Khalidwe Lachikristu Lofunika Kwambiri

“Valani . . . chifatso.”​—AKOLOSE 3:12.

1. Kodi n’chiyani chimene chimachititsa kufatsa kukhala khalidwe lochititsa chidwi?

MUNTHU akakhala wofatsa amasangalatsa kukhala naye. Koma Mfumu Solomo yanzeruyo inati “lilime lofatsa lithyola pfupa.” (Miyambo 25:15) Choncho, kufatsa ndi khalidwe lochititsa chidwi chifukwa limaphatikiza kusangalatsa ndi mphamvu.

2, 3. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kufatsa ndi mzimu woyera, ndipo tikambirana chiyani m’nkhani ino?

2 Mtumwi Paulo anatchulapo kufatsa pa m’ndandanda wa “chipatso cha Mzimu,” umene uli pa Agalatiya 5:22, 23. Mawu a Chigiriki amene awamasulira kuti “chifatso” pa vesi 23, nthaŵi zambiri amawamasulira kuti “kudekha” m’Mabaibulo ena. Mfundo ndi yakuti n’kovuta kupeza mawu ofanana ndi mawu a Chigiriki ameneŵa m’zilankhulo zina, chifukwa liwu la Chigiriki kumene kunachokera mawu ameneŵa silifotokoza kufatsa koonekera koma kwa mu mtima, ndiponso silifotokoza khalidwe la munthu, koma mmene maganizo ndi mtima wa munthuyo ziliri.

3 Kuti timvetse bwino tanthauzo ndi phindu la kufatsa, tiyeni tikambirane zitsanzo zinayi za m’Baibulo. (Aroma 15:4) Pamene tikukambirana zitsanzo zimenezi, tiphunzira kuti kodi kufatsa n’chiyani, tingakhale nako bwanji, ndipo tingakuonetse bwanji pa zochita zathu zonse.

“Wa Mtengo Wake Wapatali Pamaso pa Mulungu”

4. Kodi tikudziŵa bwanji kuti Yehova amaona kufatsa kukhala kofunika?

4 Popeza kufatsa ndi mbali ya chipatso cha mzimu wa Mulungu, n’zosadabwitsa kuti Mulungu amasonyeza kwambiri khalidwe limeneli. Mtumwi Petro analemba kuti “mzimu wofatsa ndi wachete” ndi “wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petro 3:4) Ndithudi, kufatsa ndi khalidwe limene Yehova amasonyeza; ndipo amaliona kukhala lofunika kwambiri. Chifukwa cha mfundo imeneyi, n’koyenera kuti atumiki onse a Mulungu akulitse kufatsa. Koma, kodi Mulungu wamphamvuyonse, wokhala ndi Ulamuliro m’chilengedwe chonse, amasonyeza bwanji kufatsa?

5. Kodi tili ndi chiyembekezo chotani chifukwa cha kufatsa kwa Yehova?

5 Anthu aŵiri oyamba, Adamu ndi Hava, mwadala sanamvere lamulo la Mulungu lomveka bwinobwino loti asadye zipatso za mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa. (Genesis 2:16, 17) Zotsatira zake zinali uchimo, imfa, ndiponso kuwonongeka kwa ubwenzi wawo, komanso wa ana awo odzabadwa mtsogolo, ndi Mulungu. (Aroma 5:12) Ngakhale kuti Yehova anali ndi zifukwa zabwino zowalangira, iye sanangowanyanyala ngati kuti sangathenso kuwathandiza ndi kuwaombola. (Salmo 130:3) Mmalo mwake, chifukwa chakuti Yehova ndi wachisomo komanso wosafuna zambiri, zomwe ndi zizindikiro za khalidwe lofatsa, anakonza njira imene anthu ochimwa angafikire kwa iye ndi kuyanjana naye. Inde, kudzera mu mphatso ya nsembe ya dipo la Mwana wake, Yesu Kristu, Yehova amatichititsa kuti tithe kufika ku mpando wake wachifumu wokwezeka mopanda mantha.​—Aroma 6:23; Ahebri 4:14-16; 1 Yohane 4:9, 10, 18.

6. Kodi khalidwe lofatsa linaoneka bwanji pa zimene Mulungu anachita ndi Kaini?

6 Kale kwambiri Yesu asanabwere pa dziko lapansi, kufatsa kwa Yehova kunaonekera pamene Kaini ndi Abele, ana a Adamu, anapereka nsembe kwa Mulungu. Atadziŵa zimene zinali m’mitima yawo, Yehova anakana nsembe ya Kaini koma “anayang’anira” Abele ndi nsembe yake. Chifukwa chakuti Yehova anayang’ana mokondwera pa Abele wokhulupirikayo ndiponso pa nsembe yake, Kaini anakwiya. Nkhani ya m’Baibulo imati: “Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake.” Kodi Yehova anachita chiyani? Kodi anakhumudwa chifukwa cha mtima woipa wa Kaini? Ayi. Mofatsa, anafunsa Kaini chifukwa chimene anakwiyira. Yehova anafotokoza zimene Kaini akanachita kuti ‘alandiridwe.’ (Genesis 4:3-7) Ndithudi, Yehova ndiye mwiniwake wa kufatsa.​—Eksodo 34:6.

Kufatsa Kumakopa Ndiponso Kumatsitsimula

7, 8. (a) Kodi tingamvetse bwanji kufatsa kwa Yehova? (b) Kodi mawu a pa Mateyu 11:27-29 amatisonyeza chiyani za Yehova ndi Yesu?

7 Njira yabwino kwambiri imene ingatithandize kumvetsetsa makhalidwe osayerekezeka a Yehova ndiyo kuphunzira moyo ndi utumiki wa Yesu Kristu. (Yohane 1:18; 14:6-9) Ali ku Galileya pa ulendo wake wachiŵiri wokalalikira, Yesu anachita ntchito zamphamvu zambiri ku Korazini, Betsaida, Kapernao, ndi madera ozungulira. Koma anthu ambiri anali onyada ndi opanda chidwi, ndipo anakana kukhulupirira. Kodi Yesu anachita chiyani? Ngakhale kuti anawakumbutsa mosapita m’mbali zotsatira za kusowa chikhulupiriro kwawo, iye anawamvera chisoni ʽam ha·ʼaʹrets, anthu otsika, anthu wamba amene anali pakati pawo, chifukwa anali anthu omvetsa chisoni mwauzimu.​—Mateyu 9:35, 36; 11:20-24.

8 Zimene Yesu anachita kenako zinasonyeza kuti ‘ankadziŵa Atate’ mokwanira ndipo amawatsanzira. Iye anaitana anthu wamba mokoma mtima kuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” Mawu ameneŵa anali olimbikitsa ndi otsitsimuladi kwa anthu amene anali oponderezedwa! Ndipo ndi olimbikitsa ndiponso otsitsimula ngakhale kwa ife lerolino. Ngati tiyesayesa ndi mtima wonse kuti tikhale ofatsa, tidzakhala pakati pa ‘amene Mwana afuna kuwaululira’ Atate wake.​—Mateyu 11:27-29.

9. Kodi ndi khalidwe liti limene limagwirizana ndi kufatsa, ndipo kodi ndi motani mmene Yesu alili chitsanzo chabwino cha khalidwe limeneli?

9 Khalidwe lina logwirizana kwambiri ndi kufatsa ndi “kudzichepetsa mtima.” Mosiyana ndi kudzichepetsa, kunyada kumayambitsa kudzikweza ndipo nthaŵi zambiri kungachititse munthu kuchitira nkhanza ena mosaganizira. (Miyambo 16:18, 19) Yesu anasonyeza kudzichepetsa nthaŵi yonse ya utumiki wake wa padziko lapansi. Ngakhale pamene analowa mu Yerusalemu atakwera pa bulu masiku asanu ndi atatu asanafe, n’kulandiridwa monga Mfumu ya Ayuda, Yesu anali wosiyana kwambiri ndi olamulira a dziko. Anakwaniritsa ulosi wonena za Mesiya umene Zakariya ananena kuti: “Taona, Mfumu yako idza kwa iwe, Wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.” (Mateyu 21:5; Zekariya 9:9) Mneneri wokhulupirika Danieli anaona m’masomphenya Yehova akupereka ulamuliro kwa Mwana wake. Koma, mu ulosi wam’mbuyo, anafotokoza kuti Yesu ndi “wodzichepetsa mwa anthu onse.” Kufatsa ndi kudzichepetsa zimayenderadi limodzi.​—Danieli 4:17, NW; 7:13, 14.

10. Kodi n’chifukwa chiyani kufatsa kwachikristu sikutanthauza kufooka?

10 Khalidwe losangalatsa kwambiri la kufatsa limene Yehova ndi Yesu amaonetsa limatithandiza kuti tiwayandikire. (Yakobo 4:8) Komatu kufatsa si kufooka. Sizili choncho m’pang’onong’ono pomwe! Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, amasonyeza kuti ali ndi mphamvu zambiri. Mkwiyo wake umayaka kwambiri akaona kupanda chilungamo. (Yesaya 30:27; 40:26) Mofananamo Yesu anasonyeza kuti anali wotsimikiza kuti asagonje, ngakhale pamene amazunzidwa ndi Satana Mdyerekezi. Sanasekerere malonda osavomerezeka amene atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi yake amachita. (Mateyu 4:1-11; 21:12, 13; Yohane 2:13-17) Koma, anakhalabe wofatsa ngakhale kuti ophunzira ake anali ndi zofooka zambiri, ndipo anapirira mofatsa zofooka zawozo. (Mateyu 20:20-28) Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo anakufotokoza bwino kufatsa kuti: “Munthu wodekha amakhala wa mtima wolimba ngati chitsulo.” Choncho, tiyeni tionetse khalidwe lachikristu limeneli la kufatsa.

Wofatsa Kuposa Onse Panthaŵiyo

11, 12. Poona mmene anakulira, kodi n’chiyani chinachititsa kufatsa kwa Mose kukhala kwapadera?

11 Chitsanzo chachitatu chimene tikambirane ndi cha Mose. Baibulo limam’fotokoza kuti anali “wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Mawu ameneŵa analembedwa mouziridwa ndi Mulungu. Kufatsa kwa Mose kunam’chititsa kuti amvere malangizo a Yehova.

12 Mose analeredwa modabwitsa. Yehova anaonetsetsa kuti mwana wa makolo a Chihebri okhulupirika ameneyu asungidwe pa nthaŵi ya chinyengo ndi kuphana. Zaka zake zoyambirira, Mose analeredwa ndi mayi ake, amene anam’phunzitsa mosamalitsa za Mulungu woona, Yehova. Pambuyo pake, Mose anatengedwa kuti akakhale malo amene anali osiyana kwambiri ndi kwawo. Stefano, Mkristu woyambirira kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake anafotokoza kuti, “Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto; [a]nali wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake.” (Machitidwe 7:22) Chikhulupiriro chake chinaonekera pamene anaona nkhanza zimene oyang’anira akapolo a Farao ankachitira abale ake. Chifukwa chakuti anapha Mwaigupto amene anamuona akumenya Mhebri, Mose anathawa kuchoka ku Igupto kupita ku dziko la Midyani.​—Eksodo 1:15, 16; 2:1-15; Ahebri 11:24, 25.

13. Kodi kukhala kwa Mose ku Midyani kwa zaka 40 kunam’khudza motani?

13 Ali ndi zaka 40, Mose anafunika kudzisamalira yekha m’chipululu. Ku Midyani anakumana ndi ana akazi seveni a Rehueli ndipo anawathandiza kutunga madzi omwetsa ziweto zambiri za atate awo. Atabwerera kwawo atsikanawo anauza Rehueli mosangalala kuti “munthu M-aigupto” anawapulumutsa kwa abusa amene ankawavutitsa. Atapemphedwa ndi Rehueli, Mose anakhala ndi banjalo. Mavuto amene anakumana nawo sanam’khumudwitse, ndiponso sanam’lepheretse kusintha moyo wake kuti agwirizane ndi malo ake atsopanowo. Chikhumbo chake chotumikira Yehova sichinazilale. Kwa zaka 40 zambirizo, Mose anaŵeta nkhosa za Rehueli, anakwatira Zipora, analera ana ake amuna, ndipo anakulitsa khalidwe limene anadziŵika nalo. Inde, Mose anaphunzira kufatsa chifukwa cha mavuto.​—Eksodo 2:16-22; Machitidwe 7:29, 30.

14. Fotokozani chimene chinachitika pa nthaŵi imene Mose amatsogolera mtundu wa Israyeli chimene chinaonetsa kufatsa kwake.

14 Yehova atasankha Mose kukhala mtsogoleri wa mtundu wa Israyeli, khalidwe lake la kufatsa linaonekerabe. Mnyamata wina anauza Mose kuti Elidadi ndi Medadi anali kunenera mu msasa, ngakhale kuti iwo panalibe pamene Yehova anapereka mzimu wake kwa amuna aakulu 70 amene anali kudzatumikira monga othandiza Mose. Yoswa anati: “Mose, mfumu yanga, aletseni.” Mofatsa Mose anamuyankha kuti: “Kodi uchita nsanje nawo chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!” (Numeri 11:26-29) Pamenepa kufatsa kunathandiza kuti zinthu zisaipe.

15. Ngakhale kuti Mose anali wopanda ungwiro, kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira chitsanzo chake?

15 Zikuoneka kuti pa nthaŵi ina Mose analephera kukhala wofatsa. Ali ku Meriba, pafupi ndi Kadesi, analephera kupereka ulemu kwa Yehova, Wochita Zozizwitsa. (Numeri 20:1, 9-13) Ngakhale kuti Mose anali wopanda ungwiro, chikhulupiriro chake chosagwederacho chinamulimbikitsa moyo wake wonse, ndipo khalidwe lake lofatsa limatichititsa chidwi lerolino.​—Ahebri 11:23-28.

Kusiyanitsa Nkhanza ndi Kufatsa

16, 17. Kodi tikupeza chenjezo lotani pa nkhani ya Nabala ndi Abigayeli?

16 Chitsanzo chotichenjeza tikuchipeza pa nthaŵi ya Davide, atangofa mneneri wa Mulungu Samueli. Chikukhudza anthu aŵiri okwatirana, Nabala ndi mkazi wake Abigayeli. Anthu aŵiri ameneŵa anali osiyana kwambiri! Pamene Abigayeli anali “wa nzeru yabwino,” mwamuna wake anali “waphunzo ndi woipa machitidwe ake.” Mwamwano Nabala anakana pempho lakuti agaŵire anyamata a Davide zakudya ndi zakumwa, amene anali atathandiza kulondera ziweto zambiri za Nabala kwa akuba. Atakwiya molungama, Davide ndi gulu la anyamata ake anamangirira malupanga awo kuti akamenyane ndi Nabala.​—1 Samueli 25:2-13.

17 Abigayeli atamva zimene zinachitika, mofulumira anakonza mikate, vinyo, nyama, ndi tirigu wokazinga ndi ntchintchi za mphesa ndipo ananyamuka kukakumana ndi Davide. Iye anachonderera Davide kuti: “Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m’makutu anu, nimumvere mawu a mdzakazi wanu.” Mtima wa Davide unatsika pansi atamva kuchonderera kofatsa kwa Abigayeli. Atamvetsera zimene Abigayeli anafotokoza, Davide anati: “Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi.” (1 Samueli 25:18, 24, 32, 33) Nkhanza za Nabala pomalizira pake zinam’bweretsera imfa. Makhalidwe abwino a Abigayeli pomalizira pake anam’bweretsera mwayi wokhala mkazi wa Davide. Kufatsa kwake kumapereka chitsanzo kwa onse amene akutumikira Yehova lerolino.​—1 Samueli 25:36-42.

Yesetsani Kukhala Ofatsa

18, 19. (a) Kodi ndi kusintha kotani kumene kumaonekera tikamayesayesa kukhala ofatsa? (b) Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tidzipende moona mtima?

18 Chotero, kufatsa ndi khalidwe lofunika. Kufatsa si kudekha chabe ayi, koma ndi khalidwe losangalatsa limene limatsitsimula ena. Mwinamwake kale tinkalankhula mwamwano ndiponso kuchita zinthu mwankhanza. Koma titaphunzira Baibulo tinasintha n’kukhala munthu osangalatsa kukhala naye. Paulo analankhula za kusintha kumeneku pamene analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Valani . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.” (Akolose 3:12) Baibulo limayerekezera kusintha kumeneku ndi kusintha kwa zilombo zolusa, monga mmbulu, nyalugwe, mkango, chimbalangondo, ndi mamba n’kukhala nyama zofatsa zoweta monga nkhosa, mwana wa mbuzi, mwana wa ng’ombe, ndi ng’ombe yaikazi. (Yesaya 11:6-9; 65:25) Kusintha kumeneku kumakhala kochititsa chidwi kwambiri ndipo anthu otiona amazizwa. Komabe, ifeyo timadziŵa kuti kusintha kumeneku kumabwera chifukwa cha mzimu wa Mulungu. Mzimu umenewu uli ndi chipatso chapaderadi kwambiri, ndipo kufatsa ndi mbali imodzi ya chipatso chimenechi.

19 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tikasintha ndiponso kudzipatulira kwa Yehova sitifunikiranso kuyesayesa kuti tikhale ofatsa? Kutalitali! Mwachitsanzo, zovala zatsopano zimafunika kuzisamalira nthaŵi zonse kuti zizioneka zoyera ndi zosamalika. Kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kusinkhasinkha pa zitsanzo zimene zimapezeka m’mawuwo kumatithandiza kupendanso moyo wathu. Kodi Mawu a Mulungu, amene ali ngati kalilole, akuulula zotani za inu?​—Yakobo 1:23-25.

20. Kodi tingapambane bwanji posonyeza kufatsa?

20 Mwachibadwa, anthufe tili ndi makhalidwe osiyanasiyana. Atumiki ena a Mulungu savutika kuti aonetse khalidwe la kufatsa pamene ena amavutika. Ngakhale zili choncho, Akristu onse ayenera kukulitsa chipatso cha mzimu wa Mulungu, kuphatikizapo kufatsa. Mwachikondi Paulo analangiza Timoteo kuti: “Nutsate chilungamo, [“Uziyesetsa kukhala ndi moyo wolungama,” Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono] chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.” (1 Timoteo 6:11) Mawu akuti “uziyesetsa” amasonyeza kuti khama n’lofunika. Baibulo lina limamasula mawu olangiza ameneŵa kuti ‘uikirepo mtima.’ (New Testament in Modern English, lomwe anamasulira ndi J. B. Phillips) Ngati muchita khama kusinkhasinkha pa zitsanzo zabwino za m’Mawu a Mulungu, zingasindikizike m’maganizo mwanu, ngati kuti zamera mthupi lanu. Zidzakuumbani ndi kukutsogolerani.​—Yakobo 1:21.

21. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala ofatsa? (b) Kodi tidzakambirana chiyani mu nkhani yathu yotsatira?

21 Mmene timachitira zinthu ndi anthu ena timasonyeza mmene tikupitira patsogolo pa nkhani ya kufatsa. Wophunzira Yakobo anafunsa kuti: “Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.” (Yakobo 3:13) Kodi tingaonetse bwanji khalidwe lachikristu limeneli m’banja, mu utumiki wachikristu, ndi mu mpingo? Nkhani yotsatirayi ili ndi malangizo othandiza.

Kubwereza

• Kodi mwaphunzira chiyani za kufatsa pa chitsanzo cha

• Yehova?

• Yesu?

• Mose?

• Abigayeli?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala ofatsa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anayanja nsembe ya Abele?

[Chithunzi patsamba 17]

Yesu anasonyeza kuti kufatsa ndi kudzichepetsa zimayenderana

[Chithunzi patsamba 18]

Mose anasonyeza chitsanzo chabwino cha kufatsa