Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukuitanidwa Ndipo Tidzakulandirani ndi Manja Aŵiri

Mukuitanidwa Ndipo Tidzakulandirani ndi Manja Aŵiri

Mukuitanidwa Ndipo Tidzakulandirani ndi Manja Aŵiri

MGONERO wa Ambuye, umene Ambuye Yesu Kristu anakhazikitsa zaka zopitirira 2000 zapitazo, sikuti ndi mwambo wamba umene unangochitika kalekale. Mwambo umenewu wakhudza anthu kwambiri chiukhazikitsireni. Anthu ambiri akamaŵerenga m’mauthenga abwino zimene zinachitika usiku umene uja, zimawakhudza kwambiri ndipo n’chifukwa chake amayesetsa kukumbukira mwambo umenewu m’njira zosiyanasiyana.

Zonsezi n’zosadabwitsa, chifukwa Yesu Kristu mwiniwakeyo analamula otsatira ake kuti azikumbukira mwambo umenewu ndipo azichita zimenezi mosadumphitsa. Iye anawauza momveka bwino kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”​—Luka 22:19; 1 Akorinto 11:23-25.

Komabe, kuti chikumbukiro chimenechi chikhaledi chaphindu, m’pofunika kuti munthu amvetsetse bwinobwino tanthauzo lake, mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu, Baibulo, amanena. Kuonjezera apo, m’pofunikanso kudziŵa zimene Baibulo limanena zokhudza tsiku ndi nthaŵi yochitira chikumbutsochi, malo ake, komanso mmene chiyenera kuchitidwira.

Pomvera lamulo la Yesu, Mboni za Yehova pa dziko lonse lapansi zidzakumana Lachitatu madzulo pa April 16, 2003, kuti zidzakumbukire imfa ya Yesu. Imeneyi idzakhala nthaŵi yoti adzasanthule zimene Malemba amanena ndiponso adzakulitse chikhulupiriro ndi chikondi chawo pa Ambuye Yesu Kristu, amene ananena kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mukuitanidwa kuti mudzasonkhane nawo limodzi madzulo amenewo, ndipo tidzakulandirani ndi manja aŵiri. Nanunso mudzalimbitsa chikhulupiriro ndi chikondi chanu pa Yesu Kristu ndi Atate wakumwamba, Yehova Mulungu.