Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Onetsani ‘Kufatsa Konse pa Anthu Onse’

Onetsani ‘Kufatsa Konse pa Anthu Onse’

Onetsani ‘Kufatsa Konse pa Anthu Onse’

“Uwakumbutse iwo . . . akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.”​—TITO 3:1.

1. N’chifukwa chiyani si kwapafupi nthaŵi zonse kuonetsa kufatsa?

MTUMWI Paulo analemba kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Atumiki onse a Mulungu lerolino amayesetsa kwambiri kumvera langizo limeneli. N’zoona kuti kuchita zimenezi n’kovuta, chifukwa tinatengera kudzikonda ndi makhalidwe amene sagwirizana ndi chitsanzo cha Kristu kwa makolo anthu oyambawo. (Aroma 3:23; 7:21-25) Ngakhale zili choncho, tonsefe tikhoza kukwanitsa kuonetsa kufatsa ngati titachita khama. Koma kudalira khama lathu lokha sikokwanira. N’chiyaninso chikufunika?

2. Kodi tingaonetse bwanji “chifatso chonse pa anthu onse”?

2 Kufatsa kumene Mulungunso amaonetsa ndi mbali ya chipatso cha mzimu woyera. Tikamagonjera kwambiri ku mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito imeneyi, m’pamenenso chipatso chake chizionekera kwambiri mwa ife. Pokhapokha ngati titatero m’pamene tingaonetse ‘chifatso chonse’ kwa aliyense. (Tito 3:2) Tiyeni tione mmene tingatsatirire chitsanzo cha Yesu kuti anthu onse amene timacheza nawo ‘apeze mpumulo.’​—Mateyu 11:29; Agalatiya 5:22, 23.

M’banja

3. Kodi ndi khalidwe liti m’banja limene limasonyeza mzimu wa dziko?

3 Mbali imodzi imene kufatsa kuli kofunika ndi m’banja. Malinga n’kunena kwa Bungwe la World Health Organization, chiwawa chochitika m’banja chimaika pangozi yaikulu moyo wa azimayi, kuposa mmene ngozi zapamsewu ndi matenda a malungo zimachitira tikaziphatikiza. Mwachitsanzo mu mzinda wa London, ku England, milandu yachiwawa 25 mwa milandu 100 iliyonse imene amakanena ku polisi imakhala ya m’banja. Nthaŵi zambiri apolisi amakumana ndi anthu amene amafotokoza maganizo awo ‘mwachiwawa ndi mwamwano.’ Choipa kwambiri n’chakuti, okwatirana ena alola “chizondi,” kuwononga ubwenzi wawo. Limeneli ndi khalidwe lomvetsa chisoni la “mzimu wa dziko” ndipo ndi losavomerezeka m’mabanja achikristu.​—Aefeso 4:31, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono; 1 Akorinto 2:12.

4. Kodi kufatsa kungachititse banja kukhala lotani?

4 Kuti tigonjetse zizolowezi za dziko, tikufunika mzimu wa Mulungu. “Pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Chikondi, chifundo, kudziletsa, ndi kuleza mtima, zimalimbitsa mgwirizano wa mwamuna ndi mkazi opanda ungwiro. (Aefeso 5:33) Kufatsa kumachititsa panyumba kuti pazisangalatsa kukhalapo, kusiyana ndi mmene pamakhalira ngati pali kulongolola, kumene kukuchititsa mabanja ambiri kukhala osasangalala. Zimene munthu amanena n’zofunika, koma njira imene wafotokozera zinthuzo ndi imene imasonyeza mtima wake. Nkhaŵa ndi madandaulo zikafotokozedwa mofatsa zimachepetsa kusagwirizana. Mfumu Solomo yanzeruyo inalemba kuti: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.”​—Miyambo 15:1.

5. Kodi kufatsa kungathandize bwanji banja la anthu osiyana zipembedzo?

5 Kufatsa n’kofunika kwambiri makamaka m’banja limene muli anthu a zipembedzo zosiyana. Kufatsa kukamayendera limodzi ndi khalidwe la chifundo, kungakopere anthu otsutsa kwa Yehova. Petro analangiza akazi achikristu kuti: “Mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu. Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golidi, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.”​—1 Petro 3:1-4.

6. Kodi kuonetsa kufatsa kungalimbitse bwanji ubwenzi wa makolo ndi ana?

6 Ubwenzi wapakati pa makolo ndi ana ungawonongeke, makamaka ngati sakukonda Yehova. Koma mabanja onse achikristu afunika kuonetsa khalidwe la kufatsa. Paulo analangiza azibambo amene ali makolo kuti: “Musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Ngati m’banja muli khalidwe la kufatsa, ubwenzi wabwino umene uli pakati pa makolo ndi ana umalimbitsidwa. Pokumbukira zakale zokhudza abambo ake, Dean, mmodzi wa ana asanu anati: “Abambo anali munthu wofatsa. Sindikukumbukira kuti ndinakanganapo nawo ngakhale pamene ndinali mnyamata. Nthaŵi zonse anali ofatsa, ngakhale pamene ndawakwiyitsa. Nthaŵi zina ankandiuza kuti ndipite kuchipinda changa, nthaŵi zina ankandimana zinthu zina, koma sitinakanganepo. Sikuti anali bambo athu chabe. Iwo analinso bwenzi lathu, ndipo sitinkafuna kuwakhumudwitsa.” Kufatsa kumathandizadi kulimbitsa ubwenzi wa makolo ndi ana.

Mu Utumiki Wathu

7, 8. N’chifukwa chiyani kuonetsa khalidwe la kufatsa mu utumiki n’kofunika?

7 Mbali ina imene kufatsa n’kofunika ndi mu utumiki wakumunda. Pamene tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, timakumana ndi anthu a khalidwe losiyanasiyana. Ena amamvetsera mosangalala uthenga wopatsa chiyembekezo umene timawatengera. Ena, pazifukwa zosiyanasiyana, satilandira bwino. Pamenepa m’pamene khalidwe la kufatsa lija limakhala lothandiza kwambiri kuti tikwanitse ntchito yathu yolalikira mpaka ku malekezero a dziko lapansi.​—Machitidwe 1:8; 2 Timoteo 4:5.

8 Mtumwi Petro analemba kuti: “Mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Chifukwa chakuti timatenga Kristu kukhala Chitsanzo chathu, timasamala kuti tionetse kufatsa ndi ulemu pamene tikulalikira kwa amene amalankhula monyoza. Kusonyeza khalidwe limeneli nthaŵi zambiri kumakhala ndi zotsatirapo zabwino kwambiri.

9, 10. Fotokozani zimene zinachitika zosonyeza kufunika kwa kufatsa mu utumiki wakumunda.

9 Pamene mkazi wa Keith anayankha atamva kugogoda pa khomo la nyumba yawo, Keith anangokhala m’nyumbamo. Atadziŵa kuti mlendoyo anali wa Mboni za Yehova, mkazi wa Keith anadzudzula Mbonizo mokwiya kuti zimachitira ana nkhanza. Mbaleyo anadekha. Mofatsa, anayankha kuti: “Pepani kuti mukuganiza chotero. Kodi ndingakuonetseni zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira?” Nthaŵi yonseyi n’kuti Keith akumvetsera kukambiranako ndipo tsopano anabwera pachitsekopo kudzamuuza mbale uja kuti azipita.

10 Kenaka, banjali linayamba kudziimba mlandu chifukwa chochitira nkhanza mlendo wawo uja. Kufatsa kwake kunawakhudza mitima. Iwo anadabwa chifukwa patapita mlungu umodzi mbale uja anafikanso, ndipo Keith ndi mkazi wake anamulola kufotokoza zimene amakhulupirira kuchokera m’Malemba. Iwo anati: “Zaka ziŵiri zotsatira, tinamvetsera kwambiri zimene Mboni zina zinkanena.” Anavomera kuphunzira Baibulo, ndipo pomalizira pake onse anabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova. Zinalitu zosangalatsa kwa Mboni imene inalalikira koyamba kwa Keith ndi mkazi wake! Patapita zaka, wa Mboni uja anakumana ndi banjali ndipo anapeza kuti tsopano anali mbale ndi mlongo wake wauzimu. Kufatsa kumathandizadi.

11. Kodi kufatsa kungathandize bwanji munthu kuvomera choonadi chachikristu?

11 Zimene anakumana nazo Harold ali msilikali zinam’khumudwitsa ndiponso kum’chititsa kukayikira ngati Mulungu aliko. Ngozi yapamsewu imene anachititsa dalaivala woledzera inamulemalitsa ndipo inangowonjezera mavuto ake. Mboni za Yehova zitafika panyumba yake, Harold anazilamula kuti zisamabwerenso. Koma tsiku lina, wa Mboni wina dzina lake Bill ananyamuka kuti akakumane ndi munthu wachidwi amene ankakhala khomo lachitatu kuchokera pa khomo la Harold. Mwangozi, Bill anagogoda pakhomo la Harold. Pamene Harold, amene ankayendera ndodo ziŵiri, anatsegula chitseko, Bill mofulumira anapepesa, n’kum’fotokozera kuti anali ndi cholinga chogogoda khomo lina la pafupi naye. Kodi Harold anachita chiyani? Zimene Bill samadziŵa n’zoti, Harold anaona nkhani ina pa TV imene inkaonetsa Mboni zikugwira ntchito pamodzi kuti zimange Nyumba ya Ufumu pa nthaŵi yochepa. Atachita chidwi ndi anthu ambiri akugwira ntchito mogwirizana, anasintha maganizo ake okhudza Mboni. Atachitanso chidwi ndi kupepesa kwa Bill kochokera pansi pa mtima, ndiponso khalidwe lake losangalatsa ndi kufatsa kwake, Harold anaganiza zovomera kuti azicheza ndi Mboni. Anaphunzira Baibulo n’kupita patsogolo, ndipo anakhala mtumiki wa Yehova wobatizidwa.

Mu Mpingo

12. Kodi ndi makhalidwe ati a kudziko amene anthu a mu Mpingo wachikristu ayenera kuyesetsa kupeŵa?

12 Mbali yachitatu imene kufatsa n’kofunika ndi mumpingo wachikristu. Kukangana n’kofala lerolino m’dzikoli. Kutsutsana, kukangana, kulimbana ndilo khalidwe la anthu amene amakhala ndi moyo wakudziko. Nthaŵi zina, makhalidwe akudziko ameneŵa amalowa mu mpingo wachikristu ndipo amachititsa kulimbana ndi kukangana. Abale amaudindo amamva chisoni akamathetsa nkhani zimenezi. Komabe, kukonda Yehova ndiponso abale awo kumawalimbikitsa kuthandiza ochimwawo kuti alape ndi kubwerera.​—Agalatiya 5:25, 26.

13, 14. Kodi pangakhale zotsatira zotani ngati “[ti]langiza iwo akutsutsana mofatsa”?

13 M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Paulo ndi mnzake Timoteo anakumana ndi mavuto ambiri kuchokera kwa ena mu mpingo. Paulo analangiza Timoteo kuti adziteteze kwa abale amene ankafanana ndi zotengera “zopanda ulemu.” Paulo anati: “Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.” Tikakhalabe ofatsa ngakhale pamene ena akutiputa, zimachititsa amene tikusiyana nawo maganizo kuti aganizenso mofatsa. Pomalizira pake, mwina Yehova ‘angawapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi’ monga momwe Paulo akupitirizira kulemba. (2 Timoteo 2:20, 21, 24, 25) Onani kuti Paulo akusonyeza kuti kudekha ndi kudziletsa zimayenderana ndi kufatsa.

14 Zimene Paulo ankachita zinali zogwirizana ndi zimene ankalalikira. Pochita zinthu ndi “atumwi oposatu” mu mpingo wa ku Korinto, analimbikitsa abale kuti: “Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Kristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu.” (2 Akorinto 10:1; 11:5) Paulo anatsanziradi Kristu. Onani kuti anadandaulira abale ameneŵa “mwa kufatsa” kwa Kristu. Motero anapeŵa khalidwe lodzitukumula ndi lolamula. Mawu ake olimbikitsa mosakayikira anagwira mtima amene anali ndi mitima yomvera mu mpingo. Anathandiza kulimbikitsa maubwenzi ndi kukhazikitsa mtendere ndiponso mgwirizano mu mpingo. Kodi limeneli si khalidwe limene tonsefe tingayesetse kutengera? Akulu makamaka ayenera kutengera chitsanzo cha Kristu ndi Paulo.

15. N’chifukwa chiyani kufatsa kuli kofunika popereka uphungu?

15 Udindo wothandiza ena sikuti umangokhalapo pamene mtendere ndi mgwirizano mu mpingo ukusokonezeka. Abale amafunika kuwatsogolera mwachikondi kusagwirizana kusanayambe. Paulo analimbikitsa kuti: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo.” Koma kodi tim’bweze motani? “Mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.” (Agalatiya 6:1) Kukhalabe ndi “mzimu wa chifatso” si chinthu chapafupi nthaŵi zonse, makamaka chifukwa chakuti Akristu onse, kuphatikizapo akulu, amavutika ndi zizolowezi zobwera chifukwa cha uchimo. Ngakhale zili choncho, kudzichepetsa kwa wopereka uphungu n’kumene kudzathandiza wochimwa kuti asakumve kuwawa kusinthako.

16, 17. Kodi n’chiyani chimene chingathandize munthu amene akulimbalimba pamene tikupereka uphungu?

16 Liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “mubweze” lingatanthauzenso kubwezeretsa mafupa osweka m’chimake, zimene ndi zopweteka kwambiri. Dokotala wabwino amene akubwezeretsa fupa losweka m’chimake amalankhula molimbikitsa ndi mokoma mtima za ubwino wochita zimenezi. Kudekha kwake kumalimbikitsa. Kunena mawu ochepa asanayambe ntchito yake kumachepetsa ululu wosanenekawo. Mofananamo, kubweza kwauzimu kungakhale kopweteka. Koma kufatsa kungathandize wochimwa kulandira uphunguwo mosavuta, n’kukhazikitsa ubale wabwino, komanso kum’thandiza kuti asinthe njira yake. Ngakhale kuti poyamba angakhale akukana uphungu, kufatsa kwa amene akumuthandiza kungathetse kulimbalimba kwa wochimwa kuti atsatire malangizo ogwira mtima a m’Malemba.​—Miyambo 25:15.

17 Pamene tikupatsa ena uphungu kuti awongolere, pali vuto lakuti angaone ngati tikuwaimba mlandu. Wolemba wina anafotokoza zimenezi motere: “Tikamadzudzula ena m’pamene timafunika kufatsa kwambiri chifukwa chakuti pa nthaŵi imeneyi zimakhala zosavuta kulankhula mwaukali.” Kukulitsa kufatsa, kumene kumayambira pa kudzichepetsa, kungathandize mlangizi wachikristu kupeŵa msampha umenewu.

“Pa Anthu Onse”

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani kungakhale kovuta kwa Akristu kuonetsa kufatsa pochita zinthu ndi akuluakulu a boma? (b) N’chiyani chingathandize Akristu kuonetsa kufatsa kwa olamulira, ndipo pangakhale zotsatira zotani?

18 Mbali imodzi imene anthu ambiri amavutika kuti aonetse kufatsa ndi pamene akuchita zinthu ndi akuluakulu a boma. N’zoona kuti mmene anthu ena amaudindo amachitira zinthu, amasonyeza nkhanza ndiponso kusaganizira ena. (Mlaliki 4:1; 8:9) Komabe, kukonda kwathu Yehova kungatithandize kuzindikira ulamuliro wake waukulu ndi kupereka kwa akuluakulu a boma ulemu wowayenera. (Aroma 13:1, 4; 1 Timoteo 2:1, 2) Ngakhale pamene anthu amene ali pa maudindo aakulu akulepheretsa kulambira kwathu Yehova poyera, mosangalala timapeza njira zimene tingaperekere nsembe zoyamika.​—Ahebri 13:15.

19 Mulimonse mmene zingakhalire, sitikangana nawo koma timayesetsa kukhala omvetsa zinthu, mosanyalanyaza mfundo zolungama. Mwanjira imeneyi, abale anthu akutha kuchita utumiki wawo m’maiko 234 pa dziko lonse. Timamvera uphungu wa Paulo wakuti “agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino; asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.”​—Tito 3:1, 2.

20. Kodi pali madalitso otani kwa amene akuonetsa kufatsa?

20 Onse amene amaonetsa kufatsa adzasangalala ndi madalitso ochuluka. Yesu anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Kwa abale a Kristu odzozedwa, kukhalabe wofatsa kumawabweretsera chisangalalo ndi mwayi wodzalamulira nawo mu Ufumu wa dziko lonse lapansi. Ndipo a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” akupitirizabe kuonetsa kufatsa ndipo akuyembekezera moyo m’dziko lapansi la Paradaiso. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16; Salmo 37:11) Tikuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri kutsogoloku! Choncho, tiyeni tisanyalanyaze zimene Paulo anakumbutsa Akristu a ku Efeso kuti: ‘Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nawo, ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso.’​—Aefeso 4:1, 2.

Kubwereza

• Kodi ndi madalitso otani amene amabwera chifukwa choonetsa kufatsa

• m’banja?

• mu utumiki wakumunda?

• mu mpingo?

• Kodi ndi madalitso otani amene alonjezedwa kwa anthu ofatsa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Kufatsa ndi kofunika makamaka m’banja la anthu a zipembedzo zosiyana

[Chithunzi patsamba 21]

Kufatsa kumalimbitsa banja

[Chithunzi patsamba 23]

Yankhani mofatsa ndiponso mwaulemu

[Chithunzi patsamba 24]

Kufatsa kwa wopereka uphungu kungathandize wochimwa