Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Ndachitako Popititsa Patsogolo Ntchito ya Padziko Lonse Yophunzitsa Baibulo

Zimene Ndachitako Popititsa Patsogolo Ntchito ya Padziko Lonse Yophunzitsa Baibulo

Mbiri ya Moyo Wanga

Zimene Ndachitako Popititsa Patsogolo Ntchito ya Padziko Lonse Yophunzitsa Baibulo

YOSIMBIDWA NDI ROBERT NISBET

Mfumu Sobhuza II ya ku Swaziland inatilandira bwino ku nyumba yake yachifumu ndili ndi mng’ono wanga George. Munali m’chaka cha 1936, koma mpaka lero ndimakumbukirabe bwinobwino zimene tinakambirana. Kuti ndithe kucheza ndi mfumu kwa nthaŵi yaitali motere n’chifukwa cha mbali imene ndakhala nayo kwa nthaŵi yaitali pa ntchito yaikulu yophunzitsa Baibulo. Panopa ndili ndi zaka 95 ndipo ndimasangalala ndikaganiza za mbali imene ndachitako pa ntchito imeneyi, imene inandipititsa ku makontinenti asanu.

ZONSEZI zinayamba mu 1925 pamene bambo wina wogulitsa tiyi, dzina lake Dobson anayamba kubwera kunyumba kwathu ku Edinburgh, Scotland. Ndinali nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 ndipo ndinali kuphunzira ntchito ya mu famase. Ngakhale kuti ndinali ndikadali wamng’ono, ndinkada nkhaŵa ndi mmene nkhondo ya dziko lonse ya 1914 mpaka 1918 inasinthira mabanja a anthu komanso maganizo awo a za chipembedzo. Ulendo wina a Dobson atabwera, anatisiyira buku lakuti The Divine Plan of the Ages. Zimene buku limeneli linafotokoza zoti kuli Mlengi wanzeru amene ali ndi “zolinga” zotsimikizika zinali zomveka ndiponso zogwirizana ndi mtundu wa Mulungu amene ine ndinkafuna kumulambira.

Patangopita nthaŵi yochepa, ine ndi amayi tinayamba kusonkhana ndi Ophunzira Baibulo, monga mmene Mboni za Yehova zinkadziŵikira nthaŵi imeneyo. Mu September 1926, tonse ine ndi amayi tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova poyera mwa kubatizidwa m’madzi pa msonkhano wachigawo ku Glasgow. Aliyense wopita kokabatizidwa anam’patsa mkanjo wokhala ndi zingwe zomangira mu akakolo ku miyendo kwake kuti avale pamwamba pa zovala zimene timavala posambira masiku onse. M’masiku amenewo, kumeneku ndiye amati kuvala kwaulemu pa mwambo wofunika kwambiri umenewu.

M’masiku oyambirira amenewo, panali zinthu zambiri zimene sitimazimva molondola. Anthu ambiri mu mpingo, ngati si onse kumene, ankakondwerera Khirisimasi. Ochepa chabe ndi amene ankapita m’munda kukalalikira. Panali ngakhale akulu ena amene ankaletsa ntchito yogaŵira mabuku Lamlungu, n’kumanena kuti kumeneku n’kuswa Sabata. Koma nkhani za mu Nsanja ya Olonda za mu 1925 zinayamba kufotokoza momveka bwino malemba ngati Marko 13:10 “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.”

Kodi ntchito yolalikira padziko lonse imeneyi ikanatheka bwanji? Pa ulendo wanga woyamba kuchita nawo ntchito yolalikira khomo ndi khomo, ndinangomuuza mwininyumbayo kuti ndikugulitsa mabuku a Mawu a Mulungu abwino kwambiri n’kumusonyeza buku la Zeze wa Mulungu, limene limafotokoza ziphunzitso zofunika teni za m’Baibulo ndipo limaziyerekezera ndi zingwe teni pa zeze. Kenaka, tinapatsidwa khadi lochitira umboni, pamene analembapo umboni wachidule kwambiri woti mwininyumba aŵerenge. Tinagwiritsanso ntchito nkhani zojambulidwa za mphindi zinayi ndi theka zimene mawu ake tinkawaulutsira pa galamafoni yonyamula m’manja. Magalamafoni oyambirira anali olemera kwambiri ukawanyamula, koma kenaka anayamba kupanga opepukirako, ndipo ena a iwo amatha kulankhula ukawaika choimirira.

Kuyambira mu 1925 mpaka zaka za m’ma 1930, aliyense ankangolalikira m’njira imene akuganiza kuti n’jolondola. Kenaka m’zaka zoyambirira za m’ma 1940, m’mipingo yonse anayambitsamo Sukulu ya Teokalase. Anatiphunzitsa kuti tizilalikira mbiri ya Ufumu kwa anthu polankhula pamaso m’pamaso ndi aliyense amene akufuna kumvetsera. Tinaphunziranso kufunika kochititsa maphunziro a Baibulo a panyumba kwa anthu omvetsera. Kunena kwina tinganene kuti kumeneku kunali kuyambika kwa ntchito yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse imene ilipo leroyi.

Mbale Rutherford Anandilimbikitsa

Chifukwa chakuti ndimafuna kuchita zambiri pa ntchito yophunzitsayi, ndinalembetsa utumiki wa nthaŵi zonse wa upainiya mu 1931. Ndinayenera kuyamba pamapeto pa msonkhano wina wachigawo ku London. Koma tsiku lina tikupuma panthaŵi ya chakudya cha masana pa msonkhanowu, mbale Joseph Rutherford, amene amayang’anira ntchitoyi pa nthaŵi imeneyo, anandipempha kuti alankhule nane. Amafuna kuti mpainiya mmodzi apite ku Africa. “Kodi ungafune kupitako?” anandifunsa. Ngakhale kuti anandidzidzimutsa nayo nkhani imeneyi, ndinathabe kuyankha molimba mtima kuti “Inde, ndipita.”

M’masiku amenewo, cholinga chathu chinali choti tigaŵe mabuku ambiri ofotokoza Baibulo monga mmene tingathere, ndipo zimenezi zinatipangitsa kuti tizingokhalira kuyendayenda. Ndinalimbikitsidwa kukhala wosakwatira, monga mmene abale ambiri okhala ndi udindo woyang’anira ntchitoyi analiri m’masiku amenewo. Gawo langa linayambira ku Cape Town, kum’mwera kwenikweni kwa Africa, ndipo linafika kummaŵa kwa kontinentiyi, kuphatikizapo tizilumba ta mphepete mwa nyanja ya Indian Ocean. Kuti ndikafike kumadzulo kwa gawo langali ndinkadutsa mu mchenga wotentha wa m’chipululu cha Kalahari mpaka kukafika pamene panayambira mtsinje wa Nile ku nyanja ya Victoria. Ine pamodzi ndi mnzanga amene ndinali naye tinafunikira kukhala m’dziko lililonse la mu Africa limene linali m’gawo lalikulu limeneli kwa miyezi sikisi kapena kuposa.

Makatoni 200 a Chuma Chauzimu

Nditafika ku Cape Town, anandionetsa makatoni 200 a mabuku, oti apite kummaŵa kwa Africa. Mabukuwo anali m’zinenero zinayi za ku Ulaya ndi zinenero zinayi za ku Asia, koma panalibe mabuku a m’zinenero za ku Africa. Nditafunsa kuti zinatheka bwanji kukhala ndi mabuku onsewo ine n’sanafike n’komwe, anandiuza kuti mabuku ameneŵa anayenera kutengedwa ndi Frank ndi Gray Smith, apainiya aŵiri amene anali atangopita kumene ku Kenya. Koma atangofika kumene ku Kenyako, onse anadwala malungo, ndipo mwachisoni, Frank anamwalira.

Ngakhale kuti zimenezi zinandipatsa maganizo, sizinandibwezere m’mbuyo. Ine ndi mnzanga David Norman tinachoka ku Cape Town pa sitima yapamadzi n’kuyenda ulendo wa makilomita 5000 kupita ku gawo lathu loyamba, ku Tanzania. Munthu wina wogwira ntchito yothandiza anthu za maulendo anatisungira mabuku athu ku Mombasa, m’dziko la Kenya ndipo amatitumizira mabukuwo kulikonse kumene tapita tikawafuna. Poyamba, tinalalikira m’gawo la malonda, m’masitolo ndi m’maofesi, m’tauni iliyonse. Pa gulu la mabuku athuwo tinali ndi mipukutu yokhala ndi mabuku 9 ndi timabuku 11. Mipukuti imeneyi anthu anayamba kuitcha mipukutu ya utawaleza chifukwa chakuti mabukuwa anali a mitundu yosiyanasiyana.

Kenaka tinaganiza kuti tipite ku Zanzibar, umene unali mtunda wa makilomita 30 kuchoka ku gombe la kummaŵa. Kwa zaka mazana ambiri, ku Zanzibar kunali kuchimake kwa malonda a ukapolo, koma kunalinso kotchuka chifukwa cha malonda a timaluŵa tina tonunkhiritsa zakudya, timene fungo lake linali ponseponse m’taunimo. Zinali zovuta kuti tidziŵe kumene tikupita, chifukwa tauniyo anangoimanga popanda dongosolo lililonse. Misewu inali yokhotakhota mosokoneza kwambiri, ndipo nthaŵi zambiri timangosochera. Hotela imene timagonamo inali yabwino ndithu, kungoti zitseko zake zinali zokhomerera ndi zitsulo ndipo zipupa zake zinali zokhuthala kwambiri moti imangooneka ngati ndende. Komabe, zinthu zinatiyendera bwino kumeneko moti tinasangalala kwambiri kuona Aluya, Amwenye ndi ena akulandira mabuku athu mwansangala.

Masitima, Maboti ndi Magalimoto

Kuyenda kummaŵa kwa Africa masiku amenewo kunali kovuta. Mwachitsanzo, tsiku lina tikuyenda pa sitima ya pamtunda kuchoka ku Mombasa kupita ku dera la kumapiri ku Kenya, sitima yathu inaima chifukwa tinakumana ndi dzombe lambiri. Dzombe linali waa ponseponse, ndi panjanji ya sitima pomwe, moti sitimayo imaterereka kwambiri chifukwa magudumu ake samatha kugwirana ndi njanjiyo. Panalibe kuchitira mwina koma kutsuka njanjiyo ndi madzi otentha ochokera m’sitimamo sitimayo ikamayandikira kuli dzombeko. Tinayenda pang’onopang’ono chonchi, mpaka kukafika kumene kunalibe dzombe. Tinayamba kupumako bwino pamene sitimayo inafika ku madera okwera kumene kumadutsa kamphepo kozizira bwino!

Tinkatha kufika mosavutikira ku madera a ku gombe la nyanja pa sitima ndi boti, koma kuti tikafike ku madera a kumidzi timafunikira galimoto. Ndinasangala kwambiri mchimwene wanga George atabwera kudzagwira nane ntchito limodzi, chifukwa tinatha kugula galimoto yaikulu ya mtundu wa bokosi bode koma yotseka pamwamba kumbuyo kwakeku. M’galimotoyi tinatha kuikamo bedi, ndipo inali ndi khitchini, posungira katundu, komanso mawindo oti udzudzu sungalowe. Pa denga pake tinaikapo zokuzira mawu. Chifukwa chokhala ndi galimoto yotereyi, tinkatha kukalalikira khomo ndi khomo masana, kenako n’kuitana anthu kuti adzamvere nkhani madzulo, imene timakambira pamsika. Nkhani imene tinkakonda kuiulutsa inali ya mutu wakuti, “Kodi Helo N’ngotentha?” Pa nthaŵi ina tinayenda ulendo wa makilomita 3000 pa “nyumba yoyenda” imeneyi kuchokera ku South Africa kupita ku Kenya. Pa nthaŵi imeneyi tinali osangalala chifukwa tinali ndi timabuku tosiyanasiyana m’zinenero za ku Africa, ndipo anthu anali okondwa kwambiri polandira timabuku timeneti.

Kwa ife, chinthu china chosangalatsa pa maulendo ngati ameneŵa chinali kuona nyama zambiri zakutchire za ku Africa. N’zosachita kufunsa kuti kukada tinkakhala mkati mwa galimotoyo kuti tisajiŵe, koma zinali zinthu zolimbitsa chikhulupiriro chathu kwambiri kuona nyama zambirimbiri chotero zolengedwa ndi Yehova zili kwawo ku tchire.

Ayamba Kudana Nafe

Tinafunikira kukhala osamala kuti tipewe nyama zakutchirezo. Koma iyi inali nkhani yochepa poyerekezera ndi zimene tinayenera kuchita tikakumana ndi akuluakulu a boma ena komanso atsogoleri a chipembedzo amene anayamba kudana ndi ntchito yathu yolakira Ufumu mochita kuonekeratu. Vuto limodzi limene tinakumana nalo linali lokhudza munthu wina wochita zinthu monyanyira amene anadzipatsa dzina loti Mwana Lesa, kutanthauza kuti “Mwana wa Mulungu,” ndi gulu lake lotchedwa Kitawala, dzina limene vuto lake limatanthauzanso kuti “Watchtower.” Kwa kanthaŵi ndithu ife tisanafike, munthu ameneyu anapha anthu ambiri m’madzi, ponamizira kuti akuwabatiza. Kenako anamumanga ndi kumupha pomudula mutu. Pambuyo pa zimenezi ndinakhala ndi mwayi wolankhula ndi munthu amene anapha Mwana Lesa n’kumufotokozera kuti Mwana Lesayo sanali wa gulu la Watch Tower Society.

Tinavutikanso kwambiri chifukwa cha azungu amene samasangalala ndi ntchito yathu yophunzitsa, poopa kuti iwaonongera bizinesi. Munthu wina woyang’anira malo osungiramo katundu anadandaula kuti: “Ngati azungu azikhalabe m’dziko lino, n’kofunika kuti anthu akudawa asadziŵe mmene tikuwaponderezera powalipira ndalama zochepa kwambiri akamatigwirira ntchito.” Pa zifukwa zomwezo, mwini wa kampani ina yokumba golide anandithamangitsa mu ofesi mwake mwachipongwe. Kenaka anandiperekeza mpaka ku msewu atakwiya kwambiri.

Zikuoneka kuti chidani chochokera kwa amalonda ndi achipembedzo chimenechi n’chimene chinapangitsa boma la Rhodesia (limene panopa ndi Zimbabwe) kutilamula kuti tichoke m’dzikomo. Ife tinakadandaula za chigamulo chimenechi, ndipo anatilola kuti tikhoza kukhala, koma tisamalalikire kwa anthu akuda. Chifukwa chimene mkulu wa boma wina anapereka chinali choti mabuku athu “anali osayenerana ndi maganizo a anthu akuda.” Koma m’mayiko ena, ntchito yathu yophunzitsa anthu inayenda bwinobwino osaletsedwa, ndipo ena amakondwera nayo kumene. Dziko limodzi mwa mayiko oterewa linali Swaziland.

Mfumu Inatilandira Bwino ku Swaziland

Swaziland ndi dziko laling’ono lodzilamulira lokha lalikulu ma sikweya kilomita 17, 364 ndipo lili mkati mwa South Africa. Kumeneku n’kumene tinakumana ndi mfumu yodziŵa bwino kulankhula, Mfumu Sobhuza II, imene yatchulidwa koyambirira kwa nkhani kuja. Mfumuyi imalankhula chingelezi chabwino kwambiri chifukwa inaphunzira ku yunivesite ya ku Britain. Chifukwa inavala zovala wamba, inatipangitsa kuti tikhale omasuka ndithu.

Zimene tinakambirana zinali zokhudzana ndi dziko lapansi la paradaiso limene Mulungu akukonzera anthu olungama. Ngakhale kuti nkhani imeneyi inalibe nayo chidwi, panali nkhani ina imene imaiganizira kwambiri. Mfumuyi imafunitsitsa kutukula miyoyo ya anthu osauka ndi osaphunzira. Iyo imadana kwambiri ndi amishonale a matchalitchi ena achikristu chadziko amene amangofuna kuti matchalitchi awo azikula, koma samafuna kuphunzitsa anthu awo. Koma mfumuyi imadziŵa za ntchito imene ena mwa apainiya athu amachita, ndipo inatiyamikira chifukwa cha ntchito yathu yophunzitsa Baibulo, makamaka chifukwa timachita ntchito imeneyi popanda malipiro komanso mosapempha chinthu china chilichonse.

Ntchito Yophunzitsa Baibulo Iyamba Kuthamanga

Mu 1943 sukulu yophunzitsa amishonale ya Watchtower Bible School of Gilead inakhazikitsidwa. Inalimbikitsa kubwereranso paliponse pamene pali anthu omvetsera, mmalo mongolimbikira kugaŵa mabuku ofotokoza Baibulo. Mu 1950, ine ndi George anatiitana kuti tikaphunzire nawo kalasi ya nambala 16 ya sukulu ya Gileadi. Uku n’kumene ndinakumana koyamba ndi Jean Hyde, mlongo wakhama kwambiri wa ku Astralia amene anatumizidwa kukachita ntchito ya umishonale ku Japan titamaliza sukulu ya Gileadi. M’masiku amenewo, anthu ambiri ankakhalabe osakwatira, choncho kudziŵana kwathu sikunapite patali.

Titamaliza maphunziro athu a Gileadi, ine ndi George anatitumiza ku Mauritius, chimene chili chilumba cha m’nyanja ya Indian Ocean, kuti tikachiteko umishonale. Tinapalana ubwenzi ndi anthu akumeneko, tinaphunzira chinenero chawo, ndipo tinachita nawo maphunziro a Baibulo ambiri. Pambuyo pake, mchimwene wanga wam’ngono William ndi mkazi wake Muriel, nawonso anachita maphunziro a Gilead. Kenaka anawatumiza ku gawo langa lakale, ku Kenya.

Zaka eyiti zinadutsa mofulumira, ndiye kenako ndinakumananso ndi Jean Hyde pa msonkhano wa mayiko ku New York mu 1958. Ubwenzi wathu unayambiranso ndipo tinagwirizana zoti tikwatirane. Gawo langa analisintha ndipo ndinachoka ku Mauritius kupita ku Japan kumene ine ndi Jean tinakwatirana mu 1959. Kenako tinayamba ntchito yosangalatsa kwambiri yochita umishonale ku Hiroshima kumene panthaŵi imeneyo kunali mpingo umodzi wokha. Lero mu mzinda umenewu muli mipingo 36.

“Sayonara” Japan

Patapita nthaŵi, tonse aŵiri tinayamba kuvutika kwambiri kuti tichite ntchito yathu yaumishonale chifukwa cha kudwala, choncho pamapeto pake tinafunikira kuchoka ku Japan ndipo tinakakhala kwawo kwa Jean ku Astralia. Tsiku limene tinachoka ku Hiroshima linali tsiku lomvetsa chisoni kwambiri. Pa siteshoni yokwerera sitima tinanena kuti “sayonara” kapena kuti, tsalani bwino, kwa anzathu onse a pamtima.

Panopa takhazikika kuno ku Australia ndipo timayesetsa monga momwe tingathere kutumikira Yehova mu mpingo wa Armidale, umene uli m’chigawo cha New South Wales, ngakhale kuti panopa sitingathe kuchita zambiri. Zakhaladi zinthu zosangalatsa kwambiri kugawana chuma cha choonadi chachikristu ndi anthu ambiri kwa zaka pafupifupi 80! Ndaona mmene ntchito yophunzitsa Baibulo yakulira modabwitsa ndipo ndaona ndi maso angawa zinthu zambiri zauzimu zochititsa chidwi zikuchitika. Palibe munthu payekha kapena gulu la anthu limene linganene kuti ndilo lachititsa zinthu zimenezi. Zoonadi, kuti tigwiritse ntchito mawu amene wa masalmo ananena, “ichi chidzera kwa Yehova; n’chodabwitsa ichi pamaso pathu.”​—Salmo 118:23.

[Chithunzi patsamba 28]

Mchimwene wanga George ali pa galimoto yathu imene tinkagonamonso

[Chithunzi patsamba 28]

Ine ndili ku nyanja ya Victoria

[Chithunzi patsamba 29]

Ana a sukulu a ku sekondale amene anadzamvetsera nkhani ya onse ku Swaziland mu 1938

[Zithunzi patsamba 30]

Ndili ndi Jean paukwati wathu mu 1959 komanso masiku ano