Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukoma Mtima Kwachikondi N’kofunika Bwanji?

Kodi Kukoma Mtima Kwachikondi N’kofunika Bwanji?

Kodi Kukoma Mtima Kwachikondi N’kofunika Bwanji?

BAIBULO limati: “Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima [“kwachikondi,” NW] kwake.” (Miyambo 19:22) Zoona, kukomera anthu mtima chifukwa chowakonda n’kofunikadi zedi. Komabe, m’Baibulo mawu akuti “kukoma mtima kwachikondi” amatanthauza kukomera anthu mtima chifukwa choti mumadziŵana nawo kale, mwina chifukwa chakuti winayo anakukomeraninso mtima m’mbuyomo. Choncho, kumaphatikizapo kukhulupirika.

Mfumu Yoasi ya Yuda inalephera kusonyeza khalidwe labwino limeneli. Inali ndi zifukwa zambiri zothokozera kwambiri amalume ake, a Yehoyada, ndi adzakhali ake. Yoasi asanathe chaka chimodzi atabadwa, agogo ake aakazi oipa mtima anadziika okha kukhala mfumukazi ndipo anapha azichimwene ake onse a Yoasi, amene anali pamzera wodzaloŵa ufumu. Komabe, analephera kupha Yoasi wakhandayo, chifukwa chakuti adzakhali ake ndi amalume ake anamubisa kwambiri. Iwo anamuphunzitsanso Chilamulo cha Mulungu. Yoasi ali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, amalume ake anagwiritsa ntchito udindo wawo monga mkulu wansembe kupha mfumukazi yoipa mtimayo n’kumulonga Yoasi ufumu.​—2 Mbiri 22:10–23:15.

Yoasi wamng’onoyo analamulira bwino zedi monga mfumu mpaka pamene amalume ake anamwalira. Ndiyeno atamwalira amalume akewo, Yoasi anayamba kulambira mafano. Mulungu anatuma Zekariya, amene anali mwana wa Yehoyada, kukachenjeza Yoasi kusiya zochita zake za mpatukozo. Yoasi anam’ponya miyala Zekariya. Koma ndiye sanakhulupiriketu ku banja limene linamusamalira zedi!​—2 Mbiri 24:17-21.

Baibulo limati: “Mfumu Yoasi sanakumbukira zokoma [“kukoma mtima kwachikondi,” NW] anam’chitirazi atate wake [a Zekariya], koma anapha mwana wake.” Zekariya ali pafupi kufa anati: “Yehova achipenye, nachifunse.” Mogwirizana ndi mawu a Zekariya, Yoasi anadwala mwakayakaya ndipo anyamata ake anamupha.​—2 Mbiri 24:17-25.

M’malo mokhala ngati Mfumu Yoasi, onse amene amatsatira langizo lotsatirali zinthu zidzawayendera bwino zedi m’tsogolo. Langizoli limati: “Chifundo [“kukoma mtima kwachikondi,” NW] ndi choonadi zisakusiye . . . Motero udzapeza chisomo . . . pamaso pa Mulungu ndi anthu.”​—Miyambo 3:3, 4.