Nthaŵi Imene Kulalikira Kumakhaladi Kosaiŵalika
Nthaŵi Imene Kulalikira Kumakhaladi Kosaiŵalika
“Dzuŵa linaomba kwambiri. Njira ya m’mapiri inaoneka ngati yosatha. Titagonjetsa zopinga zambiri, pomalizira pake tinafika kumene tinali kupita: ku mudzi womwe unali kutali kwambiri. Pamene tinagogoda pa khomo loyamba n’kutilandira bwino kwambiri, kutopa konse kunasanduka chimwemwe chokhachokha. Pofika madzulo, tinali titagaŵira mabuku onse omwe tinabwera nawo ndipo tinayambitsa maphunziro a Baibulo angapo. Anthu ake ndi ofunitsitsa kuphunzira. Tsopano tinafunika kupita, koma tinalonjeza kuti tidzabweranso.”
GULU lina la apainiya ku Mexico limakumana ndi zochitika ngati zimenezi nthaŵi zambiri. Apainiyawo ndi ofunitsitsa kukwaniritsa nawo mwachangu lamulo limene Yesu Kristu anapatsa ophunzira ake lakuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Ku Mexico, makonzedwe apadera olalikira otchedwa maulendo a apainiya anapangidwa ndi cholinga chofikira magawo omwe sanagaŵiridwe mpingo uliwonse ndipo motero sanali kulandira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi zambiri, magawo ameneŵa amakhala a kutali kapena ovuta kufikako. Mipingo yakutali yokhala ndi gawo lalikulu kwambiri lolalikiramo imalandiranso thandizo.
Kuti ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ione gawo la dzikolo kumene apainiya azikalalikirako pamaulendo awo, imapenda zosoŵa za gawolo. * Akachita zimenezi, magulu a apainiya apadera amawatumiza kukalalikira m’gawolo. Amawapatsa galimoto zoyenda nazo m’misewu yokumbika, yosakonzedwa bwino. Nthaŵi zina galimoto zimenezi amazigwiritsira ntchito kusungiramo mabuku ndiponso kugonamo pakafunikira kutero.
Kuyankha Pempho Mofunitsitsa
Kuyambira mu October 1996, olalikira uthenga wabwino ena anapemphedwa kuchita nawo ntchito imeneyi, kuti aziyendera limodzi ndi apainiya apadera. Ofalitsa Ufumu limodzinso ndi apainiya okhazikika amene ali ofunitsitsa kutumikira kumene olalikira ali ochepa, anachita nawo ntchito imeneyi panthaŵi zosiyanasiyana. Ena anawatumiza ku mipingo yomwe ili m’njira kuti asamalire gawolo ndiponso kukulitsa chidwi chimene anapeza. Ofalitsa ndiponso apainiya achinyamata ambiri avomereza pempho limeneli ndipo apindula ndi zokumana nazo zolimbikitsa kwambiri.
Mwachitsanzo, Abimael, Mkristu wachinyamata amene ankagwira ntchito ku kampani ya mafoni a m’manja ndiponso ankalandira ndalama zambiri, anafuna kuchita nawo ntchito yolalikira ku magawo akutali ameneŵa. Pamene om’lemba ntchito anadziŵa kuti afuna kusiya ntchito, anam’kweza pantchito ndiponso kuwonjezera malipiro ake. Anzake a kuntchito analimbikira kumuuza kuti unali mwayi wapadera ndipo n’kupanda nzeru kukana mwayi umenewu. Komabe, Abimael anatsimikiza mtima kuchirikiza makonzedwe apadera a kulalikira kwa miyezi itatu. Atasangalala ndi utumiki umenewu, Abimael anasankha kukhaliratu m’mpingo wa kutali kumene ofalitsa Ufumu anali ochepa. Iye tsopano akugwira ntchito yosadya nthaŵi kwambiri ndiponso waphunzira kukhala ndi moyo wosalira zambiri.
Chochitika china ndi cha Julissa amene ankayenda pa basi maola 22 kuti akafike kumene kunali gawo lake. Pa mbali yomaliza ya ulendo
wake, basi yomalizira patsikulo inam’siya. Komabe, panali galimoto yomwe inkanyamula antchito. Julissa analimba mtima kuwapempha kuti am’tengeko. N’zomveka kuti anali ndi mantha chifukwa anali mkazi yekha pakati pa amuna ambiri. Pamene anayamba kulalikira kwa mwamuna wachinyamata, anazindikira kuti mwamunayo anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Julissa anati: “Kuwonjezera pamenepa, ndinapezanso kuti woyendetsa galimotoyo anali mkulu ku mpingo umene ananditumiza.”Okalamba Alalikira Nawo
Komabe, ntchito imeneyi si ya achinyamata okha. Adela, mlongo wokalamba, nthaŵi zonse ankafuna kuthera nthaŵi yochuluka m’ntchito yolalikira. Iye anapeza mwayi pamene anapemphedwa kuchita nawo ntchito yapadera yolalikira imeneyi. Iye anati: “Ndinasangalala kwambiri ndi utumiki wanga moti ndinapempha akulu m’mpingo kuti andilole kukhaliratu. Ndikusangalala chifukwa choti ngakhale ndine wokalamba, Yehova akundigwiritsirabe ntchito.”
Mofananamo, a Martha a zaka 60 anadzipereka kuchita nawo ntchito imeneyi chifukwa cha kuyamikira kwawo Yehova ndiponso kukonda anthu anzawo. Poona kuti kutalika kwa ulendowo ndiponso kuvuta kwa kayendedwe m’gawolo kunapangitsa gulu lawo kuti lisafikire anthu onse, iwo anagula galimoto yoti apainiya azigwiritsira ntchito. Galimoto imene mlongoyu anagula inapangitsa kuti azilalikira gawo lalikulu ndiponso kulalikira choonadi cha Baibulo kwa anthu ambiri.
Zotsatira Zosangalatsa
Cholinga cha anthu amene anatenga nawo mbali m’makonzedwe apadera olalikira ameneŵa chinali choti ‘aphunzitse anthu.’ Pambali imeneyi, zotsatirapo zakhala zabwino kwambiri. Anthu akutali alandira choonadi chopulumutsa moyo cha m’Baibulo. (Mateyu 28:19, 20) Anthu ambiri ayamba kuphunzira Baibulo. Anthu ameneŵa amaphunzitsidwa ndi ofalitsa a m’deralo kapena olengeza amene akhaliratu m’gawolo. Nthaŵi zina, magulu a ofalitsa alinganizidwa ndipo nthaŵi zina, mipingo yaing’ono yapangidwa.
Magdaleno ndi anzake anali kugwiritsira ntchito zoyendera za onse popita ku gawo lakutali limene anagaŵiridwa. Popita kumeneko, anagwiritsira ntchito mwayi kulalikira woyendetsa galimoto. “Mwamunayu anatiuza kuti mlungu wathawu Mboni zina zinafika kunyumba kwake iye kulibe. Atabwerera kunyumba, a m’banja lake anamuuza zimene anauzidwa.
Tinamuuza kuti sitinachokere pafupi koma tinachokera ku madera osiyanasiyana a dzikoli n’cholinga choti tithandize makonzedwe apadera olalikira ndiponso ife tonse tinalipira ndalama zanthu kuti tifike kuno. Zimenezi zinam’sangalatsa ndipo anatiuza kuti adzayamba kuphunzira Baibulo limodzi ndi banja lake mlungu womwewo. Iye anathandiza nawo ntchitoyi mwa kutinyamula ulere paulendowu.”Magdaleno anasangalalanso kwambiri chifukwa cha chidwi cha anthu ku mapiri a Chiapas. “Ine ndi mkazi wanga tinali ndi mwayi wolalikira uthenga wa Ufumu gulu la achinyamata 26 a mpingo wa Presbyterian. Iwo onse anamvetsera mwachidwi kwa mphindi 30. Iwo anatenga mabaibulo awo ndipo tinawalalikira bwino kwambiri za zolinga za Yehova. Anthu ambiri ali ndi Baibulo lawolawo la chinenero cha Tzeltal.” Maphunziro a Baibulo ambiri opita patsogolo anayambidwa.
Chitsutso Chinachepa Mphamvu
Dera lina ku Chiapas linali lisanalalikidwe uthenga wa m’Baibulo kwa zaka zoposa ziŵiri chifukwa cha anthu ena otsutsa. Teresa, mlaliki wanthaŵi zonse, anaona kuti Mboni zina zinali ndi mantha kulalikira m’mudzi umenewo. “Abalewo anadabwa kuona kuti anthuwo anali ofunitsitsa kumvetsera. Titamaliza kulalikira, mvula yambiri inayamba kugwa. Pofuna malo ousirapo mvula, tinafika panyumba ya munthu wina yemwe anatilandira bwino wotchedwa Sebastián, ndipo anatilola kuloŵa m’nyumba kuti tisanyowe. Titaloŵa m’nyumba, ndinam’funsa ngati ena anam’fikirapo kale. Atanena kuti ayi, ndinayamba kum’lalikira ndiponso kuphunzira naye Baibulo mwa kugwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Titamaliza kuphunzira, Sebastián anatichonderera kwambiri kuti tizabwerenso kudzaphunzira naye.”
Gulu lina la apainiya amene anapita ku Chiapas anati: “Tinali ndi zotsatirapo zabwino chifukwa Yehova anatithandiza. Mlungu woyamba, tinayambitsa maphunziro 27, mlungu wachiŵiri, tinaitanira anthu kudzaonera vidiyo yakuti The Bible—Its Power in Your Life. Panapezeka anthu okwana 60. Onse anasangalala kuonera vidiyo imeneyi. Pomaliza, tinalinganiza kuyambitsa phunziro la Baibulo la kagulu. Modabwitsa, magulu aŵiri ophunzira anapangidwa m’mudzi umenewu.
“Titamaliza kulalikira gawo limene anatigaŵira, tinabwerera ku mudziwo kukalimbikitsa anthu achidwi ndiponso kuona mmene magulu a phunziro la Baibulo anali kuchitira. Tinawaitanira ku msonkhano wa onse ndiponso ku Phunziro la Nsanja ya Olonda. Komabe, tinalibe
malo aakulu oti n’kuchitirapo misonkhano. Munthu yemwe anapereka nyumba yake kuchitirapo phunziro la gulu analoza malo amene anali kuseli kwa nyumba yake ndipo anati: ‘Tingachitire misonkhano pamalo ameneŵa.’”Mlungu umenewo apainiya omwe anatichezera limodzinso ndi anthu achidwi anatithandiza kukonza malowo kuti tizichitirapo misonkhano. Pa msonkhano woyamba panali anthu okwana 103. Tsopano anthu 40 akuphunzira Baibulo m’mudzi umenewu.
“Chokumana Nacho Chosangalatsa”
Kuwonjezera pa zotsatirapo zabwino kwambiri m’ntchito yolalikira, amene achita nawo ntchito yolengeza imeneyi apindula kwambiri. María, mpainiya wachitsikana amene anachita nawo imodzi ya ntchito zimenezi, anafotokoza maganizo ake kuti: “Chinali chokumana nacho chosangalatsa kwambiri pa zifukwa ziŵiri. Chimwemwe changa pantchito yolalikira chinawonjezeka, ndipo ubwenzi wanga ndi Yehova unalimba. Nthaŵi ina pamene tinali kukwera phiri, tinatopa kwambiri. Titapempha Yehova kutithandiza, zomwe mawu a pa Yesaya 40:29-31 amanena zinatichitikira: ‘Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu.’ Motero tinafika kumene tinali kupita ndipo tinachititsa maphunziro ndi anthu amene anatilandira mosangalala kwambiri.”
Claudia, mpainiya winanso wachitsikana wa zaka 17, anati: “Ndapindula kwambiri. Ndaphunzira kukhala waluso kwambiri mu utumiki ndipo zimenezi zandipatsa chisangalalo chachikulu ndiponso zandichititsa kukhala ndi zolinga zauzimu. Ndiponso ndakhwima mwauzimu. Kunyumba, amayi ankandichitira zinthu zonse. Tsopano, popeza kuti ndadziŵa zambiri, ndikutha kuchita zinthu mwanzeru. Mwachitsanzo, ndinali wovuta kwambiri pankhani yakadyedwe. Komano popeza kuti ndinafunika kusintha kuti ndithe kudya zakudya za m’madera osiyanasiyana amene ndinali, sindidandaulanso za chakudya. Utumiki umenewu wandithandiza kukhala ndi mabwenzi abwino kwambiri. Tinkagaŵana zonse zimene tinali nazo ndipo tinkathandizana.”
Kututa Kosangalatsa
Kodi zotsatirapo za kuyesayesa kwapadera kumeneku n’zotani? Kuchiyambi kwa chaka cha 2002, apainiya pafupifupi 28,300 anachita nawo maulendo a apainiya ameneŵa. Iwo anachititsa maphunziro a Baibulo oposa 140,000 ndipo anathera maola oposa 2 miliyoni m’ntchito yolalikira. Kuti athandize anthu kuphunzira Baibulo, iwo anagaŵira mabuku oposa 121,000 ndi magazini pafupifupi 730,000. Si zachilendo kwa apainiya kuchititsa maphunziro a Baibulo 20 kapena kuposapo.
Anthu omwe anakomeredwa mtima chonchi anayamikira kwambiri chifukwa cha kuyesetsa kwapadera kumeneku powafikira ndi uthenga wa m’Baibulo. Ngakhale kuti anali osauka, ambiri anaumiriza ofalitsa kuti alandire zopereka. Mkazi wina wa zaka 70 yemwe anali wosauka, nthaŵi zonse anali kupatsa apainiya chinachake akam’chezera. Ngati akana kulandira iye anali kulira. Banja lina losauka linauza olengeza a nthaŵi zonse kuti nkhuku inaikira mazira oti awapatse ndipo linawauza kutenga mazirawo.
Chofunika kwambiri n’choti, anthu oona mtima ameneŵa anayamikiradi zinthu zauzimu. Mwachitsanzo, mayi wachitsikana anali kuyenda kwa maola atatu ndi theka kuti akapezeke pamisonkhano yachikristu ndipo sanali kuiphonya. Pamene woyang’anira woyendayenda anali kuchezera mpingo, wokalamba wina wachidwi anali kuyenda maola aŵiri kuti akalandire malangizo a m’Baibulo ngakhale kuti anali ndi vuto la miyendo. Ena amene sanali kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba anafuna kuphunzira kuti apindule kwambiri ndi maphunziro a Baibulo. Iwo adalitsidwa kwambiri chifukwa cha kuyesetsa kwawo.
M’buku la Machitidwe, Luka anafotokoza masomphenya amene mtumwi Paulo anaona, kuti: “Panali munthu wa ku Makedoniya alinkuimirira, nam’dandaulira kuti, Muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.” Paulo anavomera pempho limeneli. Masiku ano, m’magawo akutali a ku Mexico, ambiri asonyeza mzimu wofananawo, iwo adzipereka kuti alalikire uthenga wabwino “kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:8; 16:9, 10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 M’chaka chaposachedwapa, mipingo ya Mboni za Yehova sinali kulalikira mokhazikika malo oposa 8 peresenti a gawo lonse la ku Mexico. Zimenezi zikutanthauza kuti pali anthu oposa 8,200,000 amene akukhala mu madera mmene kulalikira kuli kochepa.
^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 9]
Mboni zambiri ku Mexico zatenga nawo mbali m’makonzedwe apadera olalikira