‘Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino’
‘Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino’
ANTHU ambiri amaona kuti ayenera kutsatira chikumbumtima chawo posankha zochita. Koma kuti chikumbumtima chathu chititsogolere moyenera, chimafunika kuchiphunzitsa bwino kuti chizisiyanitsa zabwino ndi zoipa, ndipo tiyenera kumaonetsetsa mmene chikutitsogolerera.
Taonani nkhani ya mwamuna wina dzina lake Zakeyu, nkhani imene inalembedwa m’Baibulo. Iye anali kukhala ku Yeriko, anali mkulu wa okhometsa misonkho ndipo anali wolemera. Zakeyu anavomereza kuti anapeza chuma chake mwa kulanda ena, khalidwe limene linapangitsa anthu anzake kuvutika. Kodi chikumbumtima cha Zakeyu chinamuvutitsa chifukwa cha zinthu zoipa zimene anali kuchitazo? Ngati chinatero, ndiye kuti mwachionekere anali kuchinyalanyaza.—Luka 19:1-7.
Komano panachitika zinthu zina zimene zinachititsa Zakeyu kusintha khalidwe lake. Yesu atapita ku Yeriko, Zakeyu, yemwe anali wamfupi, anafuna kumuona koma sanathe kutero chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Motero, iye anathamanga kupitirira khamulo n’kukakwera mumtengo kuti amuone bwinobwino. Yesu atachita chidwi ndi zimene Zakeyu anachita, anamuuza kuti adzakhala mlendo kunyumba kwake. Zakeyu anamulandira mlendo wake wapaderayo mosangalala.
Zimene Zakeyu anaona ndi kumva pamene anali kucheza ndi Yesu zinamukhudza mtima ndipo zinamuchititsa kusintha khalidwe lake. Iye analengeza kuti: “Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogaŵika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndim’bwezera kanayi.”—Luka 19:8.
Chikumbumtima cha Zakeyu chinaphunzitsidwa ndipo anachimvera ndi kuchitsatira. Zotsatira zake zinali zabwino kwambiri. Tangoganizani mmene Zakeyu anamvera pamene Yesu anamuuza kuti: “Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi!”—Luka 19:9.
Chimenechi ndi chitsanzo cholimbikitsa kwambiri. Chikusonyeza kuti zilibe kanthu kuti khalidwe lathu n’lotani, tikhoza kusintha. Mofanana ndi Zakeyu, tingamvere mawu a Yesu amene ali m’Baibulo, ndi kumatha kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Ndiyeno, monga mmene mtumwi Petro analimbikitsira, ‘tingakhale ndi chikumbumtima chabwino.’ Tingamvere chikumbumtima chathu chimene tachiphunzitsa ndipo tingachite zabwino.—1 Petro 3:16.