Kodi Chitonthozo Chenicheni Chingapezeke Kuti?
Kodi Chitonthozo Chenicheni Chingapezeke Kuti?
“Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu . . . wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”—2 AKORINTO 1:3, 4.
1. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse anthu kufunitsitsa chitonthozo?
MATENDA opuwalitsa ziwalo angampangitse munthu kudziona kuti moyo wake wawonongekeratu. Zivomezi, mikuntho, ndi njala zimachititsa anthu kukhala pa umphaŵi wadzaoneni. Nkhondo ingaphe wachibale wathu, ingawonongetse nyumba zathu, kapena ingapangitse anthu kuthaŵa m’nyumba zawo. Chinyengo chingapangitse anthu kuona kuti kulibe kumene angapeze thandizo. Amene amakhudzidwa ndi mavuto ameneŵa amafunitsitsa chitonthozo. Nanga kodi chingapezeke kuti?
2. N’chifukwa chiyani chitonthozo chimene Yehova amapereka n’chapadera?
2 Anthu ndiponso mabungwe ena amayesetsa kupereka chitonthozo. Anthu amayamikira kwambiri akauzidwa mawu osonyeza chifundo. Kupereka zinthu zofunika kwambiri pamoyo wa munthu kumathandiza pa mavuto akanthaŵi a anthuwo. Koma ndi Yehova yekha, Mulungu woona, amene angachotse mavuto onse ndi kupereka thandizo limene likufunika kwambiri kuti mavuto ameneŵa asadzachitikenso. Baibulo limafotokoza za iye kuti: “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.” (2 Akorinto 1:3, 4) Kodi Yehova amatitonthoza bwanji?
Kuthana ndi Chimene Chinayambitsa Mavuto
3. Kodi chitonthozo chimene Mulungu amapereka chimathandiza bwanji kuthana ndi chimene chinayambitsa mavuto amene anthu amakumana nawo?
3 Anthu onse ndi opanda ungwiro chifukwa cha tchimo la Adamu, ndipo zimenezi n’zimene zimayambitsa mavuto ambirimbiri amene mapeto ake ndi imfa. (Aroma 5:12) Zinthu zanyanyira chifukwa chakuti Satana Mdyerekezi ndi “mkulu wa dziko ili lapansi.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) Yehova anachita zambiri osati kungomva kokha chisoni chifukwa cha mavuto amene amachitikira anthu. Anatumiza Mwana wake wobadwa yekha monga dipo kudzawombola anthu, ndipo Iye anatiuza kuti tingamasuke ku zotsatira za tchimo la Adamu ngati tikhulupirira Mwana Wake. (Yohane 3:16; 1 Yohane 4:10) Mulungu ananeneratunso kuti Yesu Kristu, amene wapatsidwa ulamuliro wonse kumwamba ndi padziko lapansi, adzawononga Satana ndi dongosolo lake lonse loipa.—Mateyu 28:18; 1 Yohane 3:8; Chivumbulutso 6:2; 20:10.
4. (a) Kodi Yehova wapereka chiyani kuti atilimbikitse kudalira zimene walonjeza zobweretsa mpumulo? (b) Kodi Yehova watithandiza bwanji kuzindikira nthaŵi imene adzabweretsa mpumulo?
4 Potilimbikitsa kudalira malonjezo ake, Mulungu Yoswa 23:14) Analembanso m’Baibulo nkhani ya zimene anachita kuti apulumutse atumiki ake ku zinthu zimene n’zosatheka kuti anthu adzipulumutse okha. (Eksodo 14:4-31; 2 Mafumu 18:13–19:37) Ndipo Yehova kudzera mwa Yesu Kristu, anasonyeza kuti cholinga chake chimaphatikizapo kuchiritsa anthu “zofooka zonse,” ngakhale kuukitsa akufa. (Mateyu 9:35; 11:3-6) Kodi zonsezi zidzachitika liti? Poyankha funso limeneli, Baibulo limafotokoza zimene zidzachitike m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu lino, miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano la Mulungu zisanafike. Zimene Yesu anafotokoza n’zimene zikuchitika masiku athu ano.—Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5.
analemba umboni wokwanira zedi wosonyeza kuti chilichonse chimene amanena chimachitikadi. (Kutonthoza Anthu Amene Ali M’mavuto
5. Kodi Yehova potonthoza Aisrayeli akale, anali kuwalimbikitsa kuganiza za chiyani?
5 Pa zimene Yehova anachitira Aisrayeli akale, timaphunzirapo momwe anawatonthozera panthaŵi ya mavuto. Iye anawakumbutsa kuti iye ndi Mulungu wotani. Zimenezi zinawalimbikitsa kudalira malonjezo ake. Yehova anapangitsa aneneri ake kufotokoza momveka bwino mmene Mulungu woona komanso wamoyo amasiyanira ndi mafano, amene sakanatha kudzithandiza okha kapena kuthandiza amene anali kuwalambira. (Yesaya 41:10; 46:1; Yeremiya 10:2-15) Yehova pomuuza Yesaya kuti, “Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga,” anali kulimbikitsa mneneri wakeyu kugwiritsa ntchito mafanizo ndiponso kufotokoza ntchito Zake za chilengedwe kuti agogomezera ukulu wa Yehova monga Mulungu woona yekha.—Yesaya 40:1-31.
6. Kodi nthaŵi zina Yehova ankasonyeza bwanji nthaŵi imene alanditse anthu?
6 Panthaŵi ina, Yehova anatonthoza anthu ake mwa kuwauza nthaŵi yeniyeni imene adzawalanditsa, kuti kaya achita zimenezo posachedwa kapena patenga nthaŵi yaitali. Nthaŵi yolanditsa Aisrayeli amene anali kuponderezedwa ku Igupto itayandikira, iye anawauza kuti: “Watsala mliri umodzi ndidzam’tengera Farao, ndi Aigupto; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno.” (Eksodo 11:1) Mitundu itatu itagwirizana kugonjetsa Yuda m’masiku a Mfumu Yehosafati, Yehova anawauza kuti Iye adzachitapo kanthu “mawa.” (2 Mbiri 20:1-4, 14-17) Koma zowalanditsa ku Babulo, Yesaya analemba kutatsala zaka pafupifupi 200 kuti zichitike, ndipo zochitika zina zinanenedwa kudzera mwa Yeremiya kutatsala zaka pafupifupi 100 kuti alanditsidwe. Maulosi amenewo analimbikitsa kwambiri atumiki a Mulungu nthaŵi yoti alanditsidwe itayandikira.—Yesaya 44:26–45:3; Yeremiya 25:11-14.
7. Kodi ndi chiyani chimene nthaŵi zambiri chinali kupezeka m’malonjezo a chipulumutso, ndipo kodi zimenezi zinakhudza bwanji anthu okhulupirika mu Israyeli?
7 N’zochititsa chidwi kuti nthaŵi zambiri malonjezo amene anatonthoza anthu a Mulungu Yesaya 53:1-12) Zimenezi zinathandiza anthu okhulupirika m’mibadwo yambiri, kuyembekezera zabwino pamene anali kukumana ndi mavuto ochuluka. Pa Luka 2:25, timaŵerenga kuti: “Onani, m’Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, anali kulindira matonthozedwe a Israyeli [kubwera kwa Mesiya]; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.” Simeoni ankadziŵa zimene Malemba ananena zakuti kudzabwera Mesiya, ndipo kuyembekezera kukwaniritsidwa kwa zimenezi kunakhudza moyo wake. Sankadziŵa mmene zidzachitikire, ndipo anamwalira asanaone chipulumutso chimene chinanenedwacho chikuchitika, koma anasangalala ataona Amene anali kudzasonyeza kuti ndi njira ya Mulungu ya “chipulumutso.”—Luka 2:30.
anali ndi mfundo zokhudza Mesiya. (Anawatonthoza Kudzera mwa Kristu
8. Kodi thandizo limene Yesu anapereka linasiyana bwanji ndi limene anthu ambiri ankafuna?
8 Pamene Yesu Kristu anali kuchita utumiki wake padziko lapansi, si nthaŵi zonse zimene anali kuthandiza anthu momwe iwo anali kufunira. Ena ankalakalaka Mesiya woti awamasule ku ulamuliro wa Ufumu wa Roma. Koma Yesu sanasinthe ndale; anawauza ‘kupatsa kwa Kaisara zake za Kaisara.’ (Mateyu 22:21) Cholinga cha Mulungu chinaphatikizapo zambiri osati kungomasula anthu ku ulamuliro wa ndale. Anthu ankafuna kumulonga Yesu ufumu, koma iye anati ‘akapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28; Yohane 6:15) Siinali nthaŵi yoti alongedwe ufumu, ndipo Yehova ndi amene akanam’patsa mphamvu zolamulira osati khamu la anthu losasangalalalo.
9. (a) Kodi ndi uthenga wotonthoza uti umene Yesu analalikira? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kufunika kwa uthengawo pa mavuto amene anthu anali kukumana nawo paokhapaokha? (c) Kodi utumiki wa Yesu unayala maziko a chiyani?
9 Chitonthozo chimene Yesu anapereka chinali mu “Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” Umenewu unali uthenga umene Yesu analalikira kulikonse kumene anali. (Luka 4:43) Iye anatsindika kufunika kwa uthenga umenewu pa mavuto amene anthu amakumana nawo tsiku ndi tsiku mwa kusonyeza chimene iye monga Wolamulira Waumesiya adzachitira anthu. Iye anapatsa anthu amene anali kuvutika chifukwa chatsopano chokhalira ndi moyo mwa kuchiritsa anthu akhungu ndi osalankhula (Mateyu 12:22; Marko 10:51, 52), kuchiritsa opuwala ziwalo (Marko 2:3-12), kuchiritsa Aisrayeli anzake amene anali kudwala matenda oipa kwambiri (Luka 5:12, 13), ndiponso kuchiritsa matenda ena aakuluakulu. (Marko 5:25-29) Anatonthoza kwambiri mabanja olira mwa kuukitsa ana awo amene anamwalira. (Luka 7:11-15; 8:49-56) Iye anasonyeza kuti anali ndi mphamvu zoletsa namondwe wamkulu ndiponso zodyetsa khamu lalikulu la anthu. (Marko 4:37-41; 8:2-9) Komanso, Yesu anawaphunzitsa mfundo zofunika kuzitsatira pamoyo wawo zowathandiza kuthana bwinobwino ndi mavuto amene analipo ndiponso zimene zikanawathandiza kuyembekezera ulamuliro wolungama wa Mesiya. Chotero pamene Yesu anali kuchita utumiki wake, anatonthoza anthu amene anali kumumvetsera mwa chikhulupiriro komanso anayala maziko olimbikitsira anthu kwa zaka zina zambiri.
10. Kodi ndi zinthu ziti zimene n’zotheka chifukwa cha nsembe ya Yesu?
10 Patatha zaka zoposa 60 Yesu atapereka moyo wake nsembe ndiponso ataukitsidwira kumoyo wakumwamba, mtumwi Yohane anauziridwa kulemba kuti: “Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:1, 2) Timatonthozedwa kwambiri chifukwa cha phindu la nsembe yangwiro ya Yesu. Timadziŵa kuti machimo athu angakhululukidwe, tingakhale ndi chikumbumtima choyera, ubale wabwino ndi Mulungu, ndiponso chiyembekezo cha moyo wosatha.—Yohane 14:6; Aroma 6:23; Ahebri 9:24-28; 1 Petro 3:21.
Mzimu Woyera Umatonthoza
11. Kodi ndi chotonthoza china chiti chimene Yesu analonjeza asanafe?
11 Yesu ali ndi atumwi ake usiku womaliza asanafe imfa yake ya nsembe, anawauza chinthu china chimene Atate ake akumwamba akonza kuti chiwatonthoze. Yesu anati: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina [wotonthoza; Chigiriki, pa·raʹkle·tos], kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi.” Yesu anawatsimikizira kuti: “Nkhosweyo, Mzimu Woyera, . . . adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” (Yohane 14:16, 17, 26) Kodi mzimu woyera unawatonthoza bwanji kwenikweni?
12. Kodi ntchito ya mzimu woyera monga wokumbutsa ophunzira a Yesu inathandiza bwanji kutonthoza anthu ambiri?
12 Atumwiwo anaphunzira zinthu zambiri kwa Yesu. Mwachionekere sakanaiŵala nthaŵi imene anali ndi Yesu, koma kodi akanakumbukiradi zimene iye ananena? Kodi sakanaiwala malangizo ofunika amenewo popeza anali anthu oti sakanatha kukumbukira zinthu mwangwiro? Yesu anawatsimikizira kuti mzimu woyera ‘udzawakumbutsa iwo zinthu zonse zimene ananena kwa iwo.’ N’chifukwa chake, patatha zaka pafupifupi zisanu ndi zitatu Yesu atamwalira, Mateyu anatha kulemba Uthenga Wabwino woyamba, womwe analembamo za Ulaliki wa pa Phiri wogwira mtima wa Yesu, mafanizo ake ambiri okhudza Ufumu, ndiponso nkhani yake yatsatanetsatane ya chizindikiro cha kukhalapo kwake. Patatha zaka zoposa 50, mtumwi Yohane anatha kulemba nkhani yodalirika yodzadza ndi mfundo zosiyanasiyana za zimene zinachitika m’masiku angapo omalizira a moyo wa Yesu padziko lino lapansi. Nkhani zouziridwa zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri mpaka masiku athu ano!
13. Kodi mzimu woyera unali mphunzitsi kwa Akristu oyambirira motani?
13 Kuphatikiza pa kukumbutsa ophunzira mawu a Yesu, mzimu woyera unawaphunzitsa ndi kuwathandiza kumvetsa mokwanira cholinga cha Mulungu. Yesu akadali ndi ophunzira ake, anawauza zinthu zimene panthaŵiyo sanazimvetse bwinobwino. Koma patapita nthaŵi, chifukwa cha mzimu woyera, Yohane, Petro, Yakobo, Yuda ndi Paulo anamveketsa zochitika zina zokhudza cholinga cha Mulungu. Choncho mzimu woyera unali ngati mphunzitsi, zimene zinapereka umboni waukulu wakuti Mulungu anali kuwatsogolera.
14. Kodi mzimu woyera unathandiza bwanji anthu a Yehova?
14 Mphamvu zozizwitsa za mzimu zinathandizanso kuonetsa kuti Mulungu waleka kuyanja mtundu wa Israyeli ndipo akuyanja mpingo wachikristu. (Ahebri 2:4) Chipatso cha mzimu umenewo pa moyo wa anthu chinalinso chinthu chofunika kwambiri pofuna kuzindikira amene analidi ophunzira a Yesu. (Yohane 13:35; Agalatiya 5:22-24) Ndipo mzimu unalimbikitsa anthu a mumpingo umenewo kukhala mboni zolimba mtima ndi zopanda mantha.—Machitidwe 4:31.
Kuthandizidwa Pamene Anali M’mavuto Aakulu
15. (a) Kodi Akristu akumana ndi mavuto otani kale ndi masiku ano? (b) N’chifukwa chiyani nthaŵi zina anthu amene amalimbikitsa ena amafunika kulimbikitsidwa?
15 Anthu onse amene ali odzipereka ndi okhulupirika kwa Yehova, amakumana ndi chizunzo chinachake. (2 Timoteo 3:12) Komabe, Akristu ambiri akumana ndi mavuto aakulu zedi. M’nthaŵi zathu zino, ena avutitsidwa ndi magulu achiŵembu ndiponso aikidwa m’misasa yophera anthu, m’ndende, ndi m’misasa imene amagwira ntchito ya kalavula gaga kumene anali kuwachitira zinthu zosayenera anthu. Maboma azunza kwambiri, kapena alola anthu achipongwe kuchitira Akristu zachiwawa popanda kulangidwa. Komanso, Akristu avutika kwambiri ndi matenda aakulu kapena mavuto aakulu a m’banja. Nayenso Mkristu wokhwima mwauzimu amene amathandiza okhulupirira anzake ambiri kuthana ndi mavuto, angakumanenso ndi mavuto. Pachifukwa chimenechi, amene amalimbikitsa anzakeyo angafunikenso kulimbikitsidwa.
16. Pamene Davide anali m’mavuto aakulu, kodi anathandizidwa bwanji?
16 Pamene Mfumu Sauli ankasakasaka Davide kuti amuphe, Davide anadalira Mulungu kukhala Mthandizi wake. Iye anapempha kuti: “Imvani pemphero langa, Mulungu . . . ndithaŵira ku mthunzi wa mapiko anu.” (Salmo 54:2, 4; 57:1) Kodi Davide anathandizidwa? Inde. Panthaŵi imeneyo, Yehova anatuma mneneri Gadi ndi Abyatara wansembe, kukalangiza Davide ndiponso anatuma Yonatani mwana wa Sauli kukam’limbikitsa. (1 Samueli 22:1, 5; 23:9-13, 16-18) Yehova analolanso Afilisti kuukira dzikolo, choncho anamuchititsa Sauli kusiya kusakasaka Davide kuti alimbane ndi adaniwo.—1 Samueli 23:27, 28.
17. Kodi Yesu anapempha ndani thandizo pamene anali pa mavuto aakulu?
17 Yesu Kristu nayenso anakumana ndi mavuto aakulu, mapeto a moyo wake wa padziko lapansi atayandikira. Ankadziŵa bwino momwe zochita zake zidzakhudzira dzina la Atate wake wakumwamba ndiponso mmene zidzakhudzira tsogolo la anthu onse. Iye anapemphera mochokera pansi pa mtima, mpaka kufika “pokhala Iye m’chipsinjo.” Mulungu anaonetsetsa kuti Yesu walandira thandizo limene anali kufunikira panthaŵi yovuta imeneyo.—Luka 22:41-44.
18. Kodi Mulungu anatonthoza bwanji Akristu oyambirira amene anazunzidwa kwabasi?
18 Mpingo utayambika m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Akristu anazunzidwa kwabasi, moti onse anabalalitsidwa mu Yerusalemu Ahebri 10:34; Aefeso 1:18-20) Iwo akupitiriza kulalikira, anaona umboni wakuti mzimu wa Mulungu unali nawo, ndipo zimene zinawachitikirazo zinawonjezera chisangalalo chawo.—Mateyu 5:11, 12; Machitidwe 8:1-40.
kupatulapo atumwi okha. Amuna ndi akazi anali kutengedwa m’nyumba zawo. Kodi Mulungu anawatonthoza bwanji? Anawatonthoza ndi lonjezo la m’Mawu ake lakuti anali ndi “chuma choposa chachikhalire,” cholowa chosakanika chokakhala kumwamba ndi Kristu. (19. Ngakhale kuti Paulo anazunzidwa kwambiri, kodi anachiona bwanji chitonthozo chimene Mulungu amapereka?
19 Patapita nthaŵi, Saulo (Paulo), amene ankazunza kwambiri, nayenso anazunzidwa chifukwa tsopano anali Mkristu. Pa Chisumbu cha Kupro, panali munthu wamatsenga amene anayesa kusokoneza utumiki wa Paulo mwa kugwiritsa ntchito chinyengo ndi kupotoza zinthu. Ku Galatiya, Paulo anaponyedwa miyala ndi kumusiya ali thapsa poganiza kuti wafa. (Machitidwe 13:8-10; 14:19) Ku Makedoniya anakwapulidwa. (Machitidwe 16:22, 23) Iye atavutitsidwa ndi khamu la anthu achiwawa ku Efeso, analemba kuti: “Tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu; koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha.” (2 Akorinto 1:8, 9) Koma m’kalata yomweyo, Paulo analemba mawu otonthoza amene ali mu ndime yachiŵiri ya m’nkhani ino.—2 Akorinto 1:3, 4.
20. Kodi tidzakambirana chiyani mu nkhani yotsatira?
20 Kodi mungatani kuti mugwire nawo ntchito yotonthoza imeneyi? Masiku ano, pali anthu ambiri amene amafunika kuwatonthoza pamene ali ndi chisoni, mwina chifukwa cha mavuto amene agwera anthu ambiri kapena chifukwa cha mavuto amene agwera iwo okha basi. Mu nkhani yotsatira, tidzakambirana momwe tingaperekere chitonthozo m’mbali zonsezi.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani chitonthozo cha Mulungu chimaposa chitonthozo china chilichonse?
• Kodi ndi chitonthozo chotani chimene chinaperekedwa kudzera mwa Kristu?
• Kodi mzimu woyera unasonyeza bwanji kuti unali wotonthoza?
• Perekani zitsanzo za chitonthozo chimene Mulungu anapereka pamene atumiki ake anali pamavuto aakulu.
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 15]
Baibulo limatisonyeza kuti Yehova anapereka chitonthozo mwa kulanditsa anthu ake
[Zithunzi patsamba 16]
Yesu anapereka chitonthozo mwa kuphunzitsa, kuchiritsa, ndi kuukitsa akufa
[Chithunzi patsamba 18]
Yesu analandira thandizo kuchokera kumwamba