Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
“Yehova wandidzoza ine . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.”—YESAYA 61:1, 2.
1, 2. Kodi tiyenera kutonthoza ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?
YEHOVA, Mulungu wachitonthozo chonse chenicheni, amatiphunzitsa kuti tizikhudzidwa ena akamavutika. Amatiphunzitsa ‘kulimbikitsa amantha mtima [“ovutika maganizo,” NW]’ ndi kutonthoza onse olira. (1 Atesalonika 5:14) Olambira anzathu akafunikira thandizo limeneli, timawathandiza. Timasonyezanso chikondi kwa anthu amene si Mboni zinzathu, ngakhale anthu amene sanasonyezepo kuti amatikonda.—Mateyu 5:43-48; Agalatiya 6:10.
2 Yesu Kristu anaŵerenga lamulo laulosi ili n’kunena kuti linali kunena za iye: “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima; . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.” (Yesaya 61:1, 2; Luka 4:16-19) Akristu odzozedwa a masiku ano azindikira kwa nthaŵi yaitali kuti lamulo limeneli limawakhudza iwonso, ndipo “nkhosa zina” zimawathandiza mosangalala kugwira ntchito imeneyi.—Yohane 10:16.
3. Kodi tingawathandize bwanji anthu akamafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti mavuto azichitika?”
3 Pakachitika masoka anthu amasweka mitima, * Komabe, monga poyambira, ena atonthozeka kungoona kokha m’Baibulo mawu monga amene ali pa Yesaya 61:1, 2, popeza amasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu atonthozedwe.
ndipo nthaŵi zambiri amafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti mavuto azichitika?” Baibulo limayankha momveka bwino funso limeneli. Komabe, zingatenge nthaŵi kuti munthu amene sanaphunzirepo Baibulo amvetsetse yankho la funsoli. Tingapeze thandizo m’mabuku a Mboni za Yehova.4. Kodi Mboni ya ku Poland inathandiza bwanji mwana wasukulu wina amene anali kuvutika maganizo, ndipo kodi nkhani imeneyi ingakuthandizeni bwanji kuthandiza ena?
4 Achinyamata ndi achikulire omwe, amafunika chitonthozo. Mtsikana wina wa ku Poland amene ankavutika kwambiri maganizo anafunsa mnzake malangizo. Mnzakeyo, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, atamufunsa zina ndi zina mwachikondi, anazindikira kuti mafunso ndiponso kusamvetsetsa zinthu zina n’kumene kunali kumusoŵetsa mtendere mtsikanayo. Mtsikanayo anati: “N’chifukwa chiyani pakuchitika zinthu zoipa zambiri? N’chifukwa chiyani anthu amavutika? N’chifukwa chiyani mng’ono wanga ndi wopuwala? N’chifukwa chiyani ndimadwala mtima? Kutchalitchi kwathu amati ndi mmene Mulungu wafunira kuti zikhalire. Koma ngati ndi choncho, ndisiya kumukhulupirira!” Mboniyo inapemphera kwa Yehova cha mumtima ndipo inati: “Ndasangalala kuti wandifunsa zimenezi. Ndiyesetsa kukuthandiza.” Mtsikana wa Mboniyo anamuuza kuti iyenso ali mwana sanali kumvetsetsa zinthu zina ndipo Mboni za Yehova n’zimene zinamuthandiza. Iye anafotokoza kuti: “Ndinaphunzira kuti si Mulungu amene amapangitsa kuti anthu azivutika. Iye amakonda anthu, amawafunira zabwino, ndipo posachedwapa asintha zinthu kwambiri padziko lapansili. Matenda, mavuto a ukalamba, ndi imfa zidzatha, ndipo anthu omvera adzakhala kosatha padziko lapansi pompano.” Anamuŵerengera mtsikanayo Chivumbulutso 21:3, 4; Yobu 33:25; Yesaya 35:5-7 ndi Yesaya 65:21-25. Atakambirana kwanthaŵi yaitali, mtsikanayo anaonekeratu kuti mtima wake wakhala pansi, ndipo anati: “Tsopano ndadziŵa cholinga cha moyo wanga. Kodi ndingadzakupezenso?” Anayamba kuphunzira naye Baibulo kaŵiri pamlungu.
Tonthozani Ena ndi Chitonthozo Chimene Mulungu Amapereka
5. Kodi posonyeza chisoni, n’chiyani chingathandize kwambiri kuwatonthoza?
5 Tikafuna kutonthoza ena, mawu achisoni amakhaladi oyenera. Timayesetsa kumusonyeza munthu amene ali ndi chisoniyo mwa mawu ndi mmene tikulankhulira kuti zatikhudza zedi zimene zamuchitikirazo. Kuti tichite zimenezi tifunika kulankhula zogwira mtima. Baibulo limatiuza kuti ‘mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.’ (Aroma 15:4) Pachifukwa chimenechi, ngati n’koyenera tingafotokoze kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndipo tingawasonyeze m’Baibulo mmene udzathetsere mavuto a masiku ano. Ndiyeno tingafotokoze chifukwa chake uli chiyembekezo chodalirika. Tikatero, tidzawatonthoza.
6. Kodi tiyenera kuthandiza anthu kudziŵa chiyani kuti apindule kwambiri ndi chitonthozo cha m’Malemba?
6 Kuti munthu apindule kwambiri ndi chitonthozo chathu, afunika kudziŵa Mulungu woona, kuti ndi Munthu wamtundu wanji, ndiponso kudalirika kwa malonjezo ake. Tikafuna kuthandiza
munthu amene salambira Yehova, ndibwino kufotokoza mfundo izi. (1) Chilimbikitso cha m’Baibulo chimachokera kwa Yehova, Mulungu woona. (2) Yehova ndi Wamphamvuyonse, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. Iye ndi Mulungu wachikondi ndiponso wokoma mtima kwambiri ndi wachoonadi. (3) Tingalimbikitsidwe kupirira mavuto ngati tiyandikira kwa Mulungu mwa kudziŵa zolondola za m’Mawu ake. (4) M’Baibulo muli malemba onena za mavuto enieni amene anthu osiyanasiyana anakumana nawo.7. (a) Kodi n’chiyani chimene chingachitike chifukwa chogogomezera kuti chitonthonzo chimene Mulungu amapereka “chichuluka mwa Kristu”? (b) Kodi mungatonthonze bwanji amene akudziŵa kuti wakhala akuchita zoipa?
7 Ena atonthoza mwauzimu anthu amene ali ndi chisoni mwa kuŵerenga 2 Akorinto 1:3-7 kwa amene amalidziŵa bwino Baibulo. Pochita zimenezi, agogomezera mawu akuti “chitonthozo chathu chichuluka mwa Kristu.” Lemba limeneli lingathandize munthu kuona kuti Baibulo ndi kuchimake kwa chitonthozo kumene akufunika kuikirako mtima kwambiri. Lembali lingakhalenso poyambira kukambirana zambiri, mwina panthaŵi ina. Ngati munthu akuona kuti mavuto ake akuchitika chifukwa cha zoipa zimene wachita, tingamuuze popanda kumuŵeruza, kuti n’zotonthoza kudziŵa zimene zili pa 1 Yohane 2:1, 2 ndi pa Salmo 103:11-14. Mwa kuchita zimenezi, timatonthozadi ena ndi chitonthozo chimene Mulungu amapereka.
Kutonthoza Amene Akuvutika ndi Chiwawa Kapena Mavuto Azachuma
8, 9. Kodi chitonthozo chingaperekedwe bwanji moyenera kwa anthu amene akuvutika ndi chiwawa?
8 Anthu ambirimbiri akuvutika ndi chiwawa—kaya chochitika chifukwa cha uchigawenga wa m’dera limene akukhala kapena nkhondo. Kodi tingawatonthoze bwanji?
9 Akristu oona amasamala kuti zonena kapena zochita zawo zisasonyeze kukondera gulu lina la ndale kapena anthu ena m’nkhondo zadziko. (Yohane 17:16) Koma amagwiritsa ntchito bwino Baibulo posonyeza kuti zinthu zoipa zimene zikuchitikazi sizidzakhala zikuchitika mpaka kalekale. Angaŵerenge Salmo 11:5 kuti asonyeze momwe Yehova amaonera anthu okonda chiwawa kapena angaŵerenge Salmo 37:1-4 kuti asonyeze kuti Mulungu amalimbikitsa kusabwezera koma kukhulupirira iye. Mawu a pa Salmo 72:12-14 amasonyeza momwe Solomo Wamkulu, Yesu Kristu, amene tsopano akulamulira monga Mfumu kumwamba, amaonera anthu osalakwa amene akuvutika ndi chiwawa.
10. Ngati mwakhala zaka zambiri m’dziko lankhondo, kodi malemba ali m’ndimeyi angakutonthozeni bwanji?
10 Anthu ambiri avutika ndi nkhondo zambiri pamene magulu andale anali kulimbirana ulamuliro. Amangoganiza kuti nkhondo ndiponso mavuto amene amakhalapo chifukwa cha nkhondoyo ndiye moyowo. Chinthu chimene amaona kuti chingathandize kuti zinthu ziwayendere bwino n’kusamukira dziko lina. Koma ambiri sakwanitsa kuchita zimenezi, ndipo anthu ena amene ayesa kuchita zimenezi ataya moyo wawo poyesa kutero. Amene amakafikadi ku dziko lina nthaŵi zambiri amaona kuti asiyanadi ndi mavuto ena koma apezanso ena. Mungagwiritse ntchito lemba la Salmo 146:3-6 pothandiza anthu oterewa kuika chiyembekezo chawo pa chinthu china chodalirika kwambiri osati kusamuka. Ulosi wa pa Mateyu 24:3, 7, 14 kapena 2 Timoteo 3:1-5 ungawathandize kumvetsa vutolo mokwanira ndiponso tanthauzo la zimene zikuwachitikira, kuti tikukhala kumapeto a dongosolo la zinthu la kale lino. Mawu monga a pa Salmo 46:1-3, 8, 9 ndi Yesaya 2:2-4 angawathandize kuzindikira kuti palidi chiyembekezo chakuti m’tsogolo tidzakhala mumtendere.
11. Kodi ndi malemba ati amene anatonthoza mayi wina wa ku West Africa, ndipo n’chifukwa chiyani?
11 Panthaŵi yankhondo yosatha ku West Africa, mkazi wina anathawa kwawo asilikali akulakatitsa zipolopolo. Anali ndi mantha kwambiri, sankasangalala, ndiponso anakhumudwa zedi. Patapita nthaŵi, banja lake likukhala m’dziko lina, mwamuna wake anaganiza zowotcha mtchato wawo, n’kumuthamangitsa ngakhale kuti anali woyembekezera pamodzi ndi mwana wawo wamwamuna wa zaka 10. Mwamunayo anali ndi cholinga choti aloŵe unsembe. Mboni zitamuŵerengera mkaziyo Afilipi 4:6, 7 ndi Salmo 55:22, ndiponso nkhani za m’Malemba za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! anapeza chitonthozo ndi cholinga pamoyo wake.
12. (a) Kodi Malemba amathandiza bwanji anthu amene ali ndi mavuto aakulu azachuma? (b) Kodi Mboni ina ku Asia inathandiza bwanji kasitomala wake?
12 Mavuto azachuma asokoneza moyo wa anthu ambiri. Nthaŵi zina zimenezinso zimachitika chifukwa cha nkhondo ndiponso mavuto amene amakhalapo chifukwa cha nkhondoyo. Nthaŵi zina, mfundo zopanda nzeru zoyendetsera boma komanso dyera ndi chinyengo cha anthu amaulamuliro zawonongetsa ndalama zonse zimene anthu anasunga ndipo anthuwo akakamizika kusiya katundu wawo. Ena sanakhalepo ndi katundu wambiri. Anthu onseŵa angatonthozedwe mwa kudziŵa kuti Mulungu amatsimikizira kuti adzathandiza anthu amene amamukhulupirira ndipo walonjeza kubweretsa dziko lolungama mmene anthu adzasangalala ndi ntchito ya manja awo. (Salmo 146:6, 7; Yesaya 65:17, 21-23; 2 Petro 3:13) Pamene Mboni ina ku dziko lina la ku Asia inamva kasitomala wake akudandaula kwambiri za mmene chuma chikuyendera kumeneko, inamufotokozera kuti zimene zikuchitika kumeneko ndi zina za zinthu zimene zikuchitikanso padziko lonse. Kukambirana naye Mateyu 24:3-14 ndi Salmo 37:9-11 kunachititsa kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo nthaŵi zonse.
13. (a) Anthu akakhumudwa ndi malonjezo abodza, kodi tingawathandize bwanji pogwiritsa ntchito Baibulo? (b) Ngati anthu amaona kuti mavuto ndi umboni wakuti kulibe Mulungu, kodi mungayese bwanji kukambirana nawo?
13 Anthu akavutika zaka zambiri kapena akakhumudwa ndi malonjezo abodza, angakhale ngati Aisrayeli ku Igupto amene “chifukwa cha kuwawa,” sanamvere. (Eksodo 6:9) Zikatero, zingathandize kwambiri kuwasonyeza njira zimene Baibulo lingawathandizire kuthana bwinobwino ndi mavuto amene alipowa ndi kupeŵa mavuto amene amawononga mosayenerera moyo wa anthu ambiri. (1 Timoteo 4:8b) Ena angaone mavuto amene akukumana nawo monga umboni wakuti kulibe Mulungu kapena kuti sawaganizira. Mungakambirane nawo malemba oyenera kuti muwathandize kuzindikira kuti Mulungu wapereka thandizo koma anthu ambiri amalikana.—Yesaya 48:17, 18.
Kutonthoza Anthu Amene Akuvutika ndi Mikuntho ndi Zivomezi
14, 15. Kodi Mboni za Yehova zinasonyeza bwanji chikondi pamene tsoka linakhumudwitsa zedi anthu ambiri?
14 Masoka angagwe chifukwa cha mkuntho, chivomezi, moto, kapena kuphulika kwa mabomba. Chisoni chingakhale ponseponse. Kodi mungatani kuti mutonthoze anthu amene apulumuka pa masokaŵa?
15 Anthu akufunika kudziŵa kuti pali amene amawaganizira. Zigawenga zitaukira dziko lina, anthu ambiri anakhumudwa zedi. Anthu ambiri anataya achibale awo, anthu amene anali kuwapezera zofunika pamoyo, ndiponso anzawo. Ena ntchito yawo inatha, kapena analibe chilichonse chimene chikanawathandiza kukhala ndi moyo wabwino. Mboni za Yehova zinathandiza anthu a m’madera awo, kuwamvera chisoni chifukwa cha zinthu zambiri zimene zinawonongeka ndiponso kuwauza mawu otonthoza a m’Baibulo. Anthu ambiri anayamikira chikondi cha Mbonizo.
16. Kutagwa tsoka ku chigawo china cha ku El Salvador, n’chifukwa chiyani utumiki wa kumunda wa Mboni za kumeneko unali kuyenda bwino kwambiri?
16 Ku dziko la El Salvador kutachitika chivomezi chachikulu mu 2001, kunabwera matope ambiri okokoloka amene anapha anthu ambiri. Mnyamata wina wa zaka 25 amene amayi ake anali Mboni pamodzi ndi aphwake aŵiri a chibwenzi chake anafa. Amayi a mnyamatayo ndi chibwenzi chakecho nthaŵi yomweyo anatanganidwa mu utumiki wa kumunda. Anthu ambiri ankawauza kuti ndi Mulungu amene anatenga anthu amene anamwalirawo kapena kuti Mulungu anafuna kuti zimenezi zichitike. Mbonizo zinkagwira mawu a pa Miyambo 10:22 posonyeza kuti Mulungu safuna kuti tizimva chisoni. Anaŵerenga Aroma 5:12 kuti asonyeze kuti imfa inabwera ndi tchimo la munthu, osati kuti Mulungu anafuna kuti anthu azifa. Anasonyezanso uthenga wotonthoza wopezeka pa Salmo 34:18, Salmo 37:29, Yesaya 25:8, ndi Chivumbulutso 21:3, 4. Anthu anamvetsera ndi mtima wonse, makamakanso chifukwa chakuti akazi aŵiri ameneŵa anataya achibale awo patsoka limeneli, ndipo anayambitsa maphunziro ambiri a Baibulo.
17. Panthaŵi yatsoka, kodi tingathandize bwanji?
17 Pakagwa tsoka, mungapeze munthu amene akufunika chithandizo mwamsanga. Mwina pangafunike kuitana dokotala, kumuthandiza munthuyo kupita ku chipatala, kapena kuchita china chilichonse chotheka kuti apeze chakudya ndi pogona. Ku Italy mu 1998 kutagwa tsoka lotere, wolemba nkhani wina anaona kuti Mboni za Yehova “zimathandiza mogwira mtima, kuwathandiza anthu amene akuvutika, mosayang’ana kuti ndi a chipembedzo chiti.” M’madera ena, zochitika zimene zinanenedwa kuti zidzachitika m’masiku otsiriza zikubweretsa mavuto aakulu. M’madera amenewo, Mboni za Yehova zimatchula maulosi a Baibulo, ndipo amatonthoza anthu ndi lonjezo la m’Baibulo lakuti Ufumu wa Mulungu udzabweretsa moyo wabwino kwa anthu.—Miyambo 1:33; Mika 4:4.
Kutonthoza Anthu Amene Wina M’banja Mwawo Wamwalira
18-20. M’banja mukachitika maliro, kodi munganene kapena kuchita chiyani kuti muwatonthoze?
18 Tsiku lililonse anthu ambiri amalira chifukwa cha imfa ya munthu amene amamukonda. Mungakumane ndi anthu amene akulira maliro mu utumiki wachikristu kapena pochita zinthu zina zatsiku ndi tsiku. Kodi munganene kapena kuchita chiyani chimene chingawatonthoze?
19 Kodi munthuyo akuoneka kuti ali ndi chisoni chachikulu? Kodi m’nyumba mwawo muli achibale ambiri achisoni? Mungafune kunena zambiri, koma m’pofunika kusamala. (Mlaliki 3:1, 7) Mwina chimene chingakhale choyenera kuchita ndi kupepesa, kusiya chofalitsa choyenera chothandiza kuphunzira Baibulo (bulosha, magazini, kapena thirakiti), n’kudzabweranso patapita masiku angapo kudzaona ngati mungawathandize zina n’zina. Panthaŵi ina yabwino, apempheni kukambirana nawo mfundo zina zolimbikitsa za m’Baibulo. Zimenezi zingakhazike mtima pansi anthuwo ndiponso kuwachiritsa. (Miyambo 16:24; 25:11) Simungaukitse akufa monga anachitira Yesu. Koma mungakambirane nawo zimene Baibulo limanena za chimene chimachitikira anthu akufa, ngakhale kuti imeneyi sinthaŵi yabwino kutsutsa maganizo olakwika. (Salmo 146:4; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Mungaŵerenge pamodzi malonjezo a m’Baibulo onena za kuuka kwa akufa. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Mungakambirane tanthauzo la zimenezi, mwina mungachite zimenezi pogwiritsa ntchito nkhani ya m’Baibulo yonena za munthu amene anauka kwa akufa. (Luka 8:49-56; Yohane 11:39-44) Ndiponso gogomezerani makhalidwe a Mulungu wachikondi amene amatipatsa chiyembekezo chimenechi. (Yobu 14:14, 15; Yohane 3:16) Fotokozani mmene mfundo zimenezi zakuthandizirani ndiponso chifukwa chake mumazidalira.
20 Kumuitanira munthu amene akulira maliro ku Nyumba ya Ufumu kungamuthandize kudziŵa anthu amene amakondadi anzawo ndiponso amene amadziŵa kulimbikitsana. Mkazi wina wa ku Sweden anapeza kuti zimenezi n’zimene wakhala akufunafuna kwa moyo wake wonse.—Yohane 13:35; 1 Atesalonika 5:11.
21, 22. (a) Kodi tifunika kutani kuti tipereke chitonthozo? (b) Kodi mungatonthoze bwanji munthu amene amawadziŵa bwino kale Malemba?
21 Mukadziŵa kuti munthu wina ali ndi chisoni, kaya wa mu mpingo wachikristu kapena ayi, kodi nthaŵi zina mumasoŵa chonena kapena chochita? Mawu achigiriki amene nthaŵi zambiri m’Baibulo amawamasulira kuti “chitonthozo” kwenikweni amatanthauza kuti “kumuitanira wina pafupi ndi iwe.” Kukhala wotonthoza weniweni kumatanthauza kuti mukhale pafupi ndi anthu amene ali pachisoni.—Miyambo 17:17.
22 Nanga bwanji ngati munthu amene mukufuna kutonthoza amadziŵa kale zimene Baibulo limanena pankhani ya imfa, dipo, ndi kuuka kwa akufa? Wokhulupirira mnzake akapezekapo n’chitonthozo pachokha. Ngati akufuna kulankhula, mvetserani mwatcheru. Musaganize kuti muyenera kukamba nkhani. Ngati malemba angaŵerengedwe, aoneni monga mawu a Mulungu amene amalimbikitsa nonsenu. Sonyezani chikhulupiriro cholimba chimene nonse muli nacho pankhani ya kudalirika kwa zimene malemba akulonjeza. Mwa kusonyeza chifundo cha Mulungu ndiponso mwakukambirana mfundo zamtengo wapatali za m’Mawu a Mulungu, mungathandize anthu amene ali ndi chisoni kupeza chitonthozo ndi mphamvu kwa “Mulungu wa chitonthozo chonse,” Yehova.—2 Akorinto 1:3.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Onani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha mutu 8, Kukambitsirana za m’Malemba tsamba 183 mpaka 187 ndiponso, tsamba 222 mpaka 229; onaninso buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You?, mutu 10; ndi bulosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
Kodi Mukutipo Bwanji?
• Kodi anthu ambiri amaimba mlandu ndani chifukwa cha mavuto, ndipo tingawathandize bwanji?
• Kodi tingachite chiyani kuti tithandize ena kupindula mokwanira ndi chitonthozo cha m’Baibulo?
• Ndi zinthu ziti zikupangitsa anthu kukhala ndi chisoni m’dera lanu, ndipo mungawatonthoze bwanji?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 23]
Kukambirana uthenga wotonthoza weniweni panthaŵi ya mavuto
[Mawu a Chithunzi]
Refugee camp: UN PHOTO 186811/J. Isaac
[Chithunzi patsamba 24]
Kupezekapo kokhako kwa mnzake n’chitonthozo kale