Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Okhazikika Kuti Mudzapambane pa Mpikisano wa Moyo

Khalani Okhazikika Kuti Mudzapambane pa Mpikisano wa Moyo

Khalani Okhazikika Kuti Mudzapambane pa Mpikisano wa Moyo

KODI mungakwere chiyani ngati mukufuna kudutsa panyanja poti pali namondwe? Kodi mungakwere kabwato kakang’ono kosalimba, kapena mungakwere sitima yolimba, yomangidwa bwino? Mosakayikira mungasankhe sitimayo, chifukwa ingathe kudutsa namondweyo mosavutikira.

Pamene tikuyenda m’dziko longa namondwe komanso loopsali, timakumana ndi mavuto ambiri othetsa nzeru. Achinyamata, mwachitsanzo, nthaŵi zina angakhale osokonezeka ndiponso ankhaŵa chifukwa cha mfundo ndi masitayelo zosokoneza za dzikoli. Anthu amene angoyamba posachedwapa moyo wachikristu angakhale okayikakayikabe. Ngakhale ena amene ali okhazikika ndipo atumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri angakhale ali pa chiyeso chifukwa zimene akhala akuyembekezera sizinakwaniritsidwebe zonse.

Kumva moteromo si kwachilendo. Atumiki okhulupirika a Yehova monga Mose, Yobu ndi Davide anathedwapo nzeru pa nthaŵi ina. (Numeri 11:14, 15; Yobu 3:1-4; Salmo 55:4) Komabe, moyo wawo umasonyeza kuti anali anthu odzipereka kwa Mulungu mokhazikika. Chitsanzo chawo chabwino chimatilimbikitsa kuti tikhalenso okhazikika, koma Satana Mdyerekezi akufuna kuti atisocheretse n’kutichotsa pa mpikisano wa moyo wosatha. (Luka 22:31) Choncho, kodi tingakhale bwanji olimba, “okhazikika m’chikhulupiriro”? (1 Petro 5:9) Ndipo kodi tingalimbikitse bwanji okhulupirira anzathu?

Yehova Akufuna Kuti Tikhale Okhazikika

Ngati tikhala okhulupirika kwa Yehova, iye nthaŵi zonse adzatithandiza kuti tikhale okhazikika. Wamasalmo Davide anakumana ndi mavuto ambiri, koma anadalira Mulungu ndipo n’chifukwa chake anatha kuimba kuti: “[Yehova] anandikweza kunditulutsa m’dzenje la chitayiko, ndi m’thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.”​—Salmo 40:2.

Yehova amatipatsa mphamvu yomenyera“nkhondo yabwino ya chikhulupiriro” kuti ‘tigwire moyo wosatha.’ (1 Timoteo 6:12) Amatipatsanso zonse zimene tikufunikira kuti tikhale olimba ndiponso kuti tipambane pa nkhondo yathu yauzimu. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake ‘kulimbika mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake,’ ndiponso anawauza kuti ‘avale zida zonse za Mulungu, kuti adzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.’ (Aefeso 6:10-17) Koma kodi ndi zinthu zotani zimene zingatigwetse? Ndipo kodi tingalimbane nazo bwanji zimenezo?

Chenjerani ndi Zinthu Zimene Zingakugwetseni

Ndi chinthu chanzeru kukumbukira kuti: Zimene timasankha m’kupita kwa nthaŵi zingatithandize kapena kutilepheretsa kukhala Akristu olimba. Achinyamata ayenera kusankha chochita pa nkhani ya ntchito imene adzagwire, maphunziro owonjezereka, ndi ukwati. Anthu achikulire angafunike kusankha chochita pa nkhani ya kusamuka kukakhala kwina, kapena kuloŵa ntchito ina kuonjezera pa imene ali nayo kale. Tsiku lililonse timasankha chochita pa nkhani ya mmene tigwiritsire ntchito nthaŵi yathu komanso pa zinthu zina zambiri. Kodi n’chiyani chimene chidzatithandiza kusankha mwanzeru kuti tikhale atumiki a Mulungu olimba? Munthu wina amene wakhala Mkristu kwa nthaŵi yaitali anati: “Ndikamasankha zochita ndimapempha Yehova kuti andithandize. Ndimakhulupirira kuti n’kofunika kumvera ndi kugwiritsa ntchito malangizo amene amaperekedwa m’Baibulo, pa misonkhano yachikristu, ndi akulu, komanso m’mabuku ofotokoza Baibulo.”

Pamene tikusankha zochita, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi zaka zisanu kapena khumi zikubwerazi, ndidzakhala wosangalala chifukwa cha zinthu zimene ndikusankha panozi, kapena zidzandibweretsera mavuto? Kodi ndimaonetsetsa kuti zinthu zimene ndikusankha zisandigwetse mwauzimu koma zindithandize kupita patsogolo?’​—Afilipi 3:16.

Anthu ena obatizidwa akhala ndi moyo wosalimba mwauzimu chifukwa chogonja atayesedwa kapena chifukwa chakuti analola kufika poti anatsala pang’ono kuphwanya malamulo a Mulungu. Anthu ena amene anachotsedwa mu mpingo chifukwa chosalapa machimo awo ayesetsa kuti abwezeretsedwe, koma atangobwezeretsedwa achotsedwanso. Nthaŵi zina zimenezi zachitika patangotha kanthaŵi kochepa chabe, chifukwa cha tchimo lomwelomwelo. Kodi chingakhale chifukwa chakuti sanapemphere kwa Mulungu kuti awathandize kuti ‘adane nacho choipa n’kugwirizana nacho chabwino’? (Aroma 12:9; Salmo 97:10) Tonsefe tiyenera ‘kulambula misewu yolunjika yoyendamo mapazi athu.’ (Ahebri 12:13) Choncho, tiyeni tione mfundo zina zimene zingatithandize kuti tikhale olimba mwauzimu.

Khalani Okhazikika mwa Kuchita Ntchito Zachikristu

Njira imodzi imene ingatithandize kuti tisachepetse liŵiro lathu pa mpikisano wathu wa moyo ndiyo kukhala ndi zambiri zochita pa ntchito yolalikira Ufumu. Zoonadi, utumiki wathu wachikristu ndi njira yabwino kwambiri yothandizira mitima yathu ndi maganizo athu kukhala pa kuchita chifuniro cha Mulungu komanso pa mphotho ya moyo wosatha. Pa nkhani imeneyi, Paulo analimbikitsa Akorinto kuti: “Abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) “Kukhazikika” kumatanthauza ‘kulimba mosagwedezeka.’ “Kusasunthika” kungatanthauze ‘kusalola kuti nangula wanu amasuke.’ Choncho, kukhala wotanganidwa mu utumiki wathu kungachititse moyo wathu wachikristu kukhala wolimba. Ngati tithandiza anthu ena kuti am’dziŵe Yehova, moyo wathu umakhala watanthauzo komanso wachimwemwe.​—Machitidwe 20:35.

Pauline, Mkristu amene watha zaka zopitirira 30 akuchita umishonale komanso utumiki wa nthaŵi zonse wosiyanasiyana, akunena kuti: “Utumiki umanditeteza chifukwa ndikamalalikira ena m’pamene ndimatsimikizadi kuti ndili ndi choonadi.” Timakhalanso otsimikiza choncho tikamachita ntchito zosiyanasiyana zachikristu, monga kupezeka pa misonkhano yolambira ndi kuchita phunziro laumwini la Baibulo mwakhama.

Kukhala Olimba Chifukwa cha Abale Achikondi

Kukhala m’gulu la padziko lonse la olambira oona kungatilimbitse kwambiri. Ndi dalitso lalikulu kukhala pakati pa abale achikondi a padziko lonse ameneŵa! (1 Petro 2:17) Ndipo ngakhale ifeyo tikhoza kulimbitsanso okhulupirira anzathu.

Taganizirani ntchito zothandiza zimene munthu wolungama Yobu ankachita. Ngakhale Elifazi, amene anali wotonthoza wabodza, anavomereza kuti: “Mawu ako anachirikiza iye amene akadagwa, walimbitsanso maondo otewa.” (Yobu 4:4) Kodi ife timathandiza anzathu? Aliyense wa ife ali ndi udindo wothandiza abale ndi alongo athu auzimu kuti apirire potumikira Mulungu. Tikamachita nawo zinthu, tizichita mogwirizana ndi mawu aŵa: “Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo agwedegwede.” (Yesaya 35:3) Choncho, bwanji osakhala n’cholinga cholimbikitsa Mkristu mnzanu mmodzi kapena aŵiri nthaŵi iliyonse imene mwakumana? (Ahebri 10:24, 25) Mawu owalimbikitsa ndi owayamikira chifukwa chopitirizabe kusangalatsa Yehova angawathandize kuti akhale okhazikika kuti adzapambane pa mpikisano wa moyo.

Akulu achikristu angachite zambiri mwa kulimbikitsa anthu atsopano. Angachite izi mwa kuwauzako nzeru yothandiza ndi malangizo abwino a m’Malemba komanso mwa kupita nawo limodzi mu utumiki wa kumunda. Mtumwi Paulo ankalimbikitsa ena paliponse pamene wapeza mpata. Analakalaka kuona Akristu a ku Roma kuti awathandize kukhala olimba mwauzimu. (Aroma 1:11) Anaona abale ndi alongo ake okondedwa a ku Filipi ngati “chimwemwe . . . ndi korona” wake ndipo anawalimbikitsa kuti: “Chirimikani motere mwa Ambuye.” (Afilipi 4:1) Atamva kuti abale ake ku Tesalonika akuvutika, Paulo anatumiza Timoteo kuti ‘akawakhazikitse ndi kuwatonthoza, kuti wina asasunthike ndi zisautso.’​—1 Atesalonika 3:1-3.

Mtumwi Paulo ndi Petro anaona ndi kuyamikira khama la olambira anzawo. (Akolose 2:5; 1 Atesalonika 3:7, 8; 2 Petro 1:12) Nafenso tiyeni tiziona, osati kufooka kwa abale athu, koma makhalidwe awo abwino komanso kuyesayesa kwawo kuti akhale okhazikika komanso kuti alemekeze Yehova.

Ngati timangoona zolakwika zokhazokha kapena kumangodzudzula abale athu, mwina mosadziŵa tingapangitse ena mwa iwo kuvutika kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Ndi bwino kumakumbukira kuti abale athu ndi “okambululudwa ndi omwazikana” m’dziko la masiku anoli! (Mateyu 9:36) Sikulakwa iwo akamafuna kutonthozedwa ndi kutsitsimulidwa mu mpingo wachikristu. Choncho, tiyeni tonsefe tiyesetse kulimbikitsa okhulupirira anzathu ndi kuwathandiza kuti akhale okhazikika.

Nthaŵi zina, ena angatichitire zinthu zimene zingatifooketse. Kodi tidzalola kuti mawu kapena kanthu kopweteka kamene munthu wina watichitira katibweze m’mbuyo pa utumiki wathu kwa Yehova? Tiyeni tisalole kuti munthu wina aliyense atisunthe!​—2 Petro 3:17.

Malonjezo a Mulungu Amatithandiza Kukhala Olimba

Yehova watilonjeza tsogolo labwino kwambiri mu ulamuliro wa Ufumu wake, ndipo chifukwa cha lonjezolo tili ndi chiyembekezo chimene chimatithandiza kukhala okhazikika. (Ahebri 6:19) Ndipo chikhulupiriro chimene tili nacho choti Mulungu nthaŵi zonse amakwaniritsa malonjezo ake chimatithandiza ‘kudikira, kuchirimika m’chikhulupiriro.’ (1 Akorinto 16:13; Ahebri 3:6) Chikhulupiriro chathu chingayesedwe tikamaona ngati ena mwa malonjezo a Mulungu akuchedwa kukwaniritsidwa. Choncho, n’kofunika kwambiri kuti tipeŵe kusocheretsedwa ndi ziphunzitso zonyenga zimene zingatitayitse chiyembekezo chathu.​—Akolose 1:23; Ahebri 13:9.

Chitsanzo choipa cha Aisrayeli amene anawonongeka chifukwa chosakhulupirira malonjezo a Yehova chiyenera kukhala chenjezo kwa ife. (Salmo 78:37) Mosiyana ndi iwowo, tiyeni tikhale okhazikika, ndipo titumikire Mulungu tikudziŵa kuti nthaŵi yatsala pang’ono masiku otsiriza ano. Mbale wina amene wakhala mkulu kwa zaka zambiri anati: “Tsiku lililonse ndimachita zinthu ngati kuti tsiku lalikulu la Yehova likubwera maŵa.”​—Yoweli 1:15.

N’zoona, tsiku lalikulu la Yehova latsala pang’ono kufika. Komabe, ngati tiyandikana ndi Mulungu sitiyenera kuopa kanthu kalikonse. Ngati titsatira kwambiri mfundo zake zolungama, komanso ngati tikhala okhazikika, tikhoza kupambana pa mpikisano wa moyo wosatha!​—Miyambo 11:19; 1 Timoteo 6:12, 17-19.

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi mukuchita zonse zimene mungathe kuti muthandize Akristu anzanu kukhala okhazikika?

[Mawu a Chithunzi patsamba 21]

The Complete Encyclopedia of Illustration/​J. G. Heck