Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mverani Zimene Mzimu Ukunena!

Mverani Zimene Mzimu Ukunena!

Mverani Zimene Mzimu Ukunena!

“Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.”​—CHIVUMBULUTSO 3:22.

1, 2. Kodi m’mauthenga onse a Yesu opita ku mipingo isanu ndi iŵiri yotchulidwa m’buku la Chivumbulutso muli langizo lotani?

ATUMIKI a Yehova ayenera kumvera mawu a Yesu Kristu ouziridwa ndi mzimu opita ku mipingo isanu ndi iŵiri yotchulidwa m’buku la m’Baibulo la Chivumbulutso. Ndipo m’mauthenga onseŵa muli langizo loti: “Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.”​—Chivumbulutso 2:7, 11, 17, 29; 3:6, 13, 22.

2 Takambirana kale mauthenga a Yesu kwa angelo, kapena oyang’anira, a ku Efeso, Smurna, ndi Pergamo. Kodi zimene ananena mouziridwa ndi mzimu woyera ku mipingo inayi yotsalayo zingatipindulitse bwanji?

Kwa Mngelo wa ku Tiyatira

3. Kodi mzinda wa Tiyatira unali kuti, ndipo unkatchuka makamaka chifukwa chopanga chiyani?

3 “Mwana wa Mulungu” anayamikira ndi kudzudzula mpingo wa ku Tiyatira. (Ŵerengani Chivumbulutso 2:18-29.) Mzinda wa Tiyatira (umene tsopano umatchedwa Akhisar) unamangidwa m’mbali mwa mtsinje waung’ono wothira mu mtsinje wa Gediz (umene kale unali kutchedwa Hermus) kumadzulo kwa Asia Minor. Mzindawu unkatchuka ndi ntchito za manja. Anthu opanga utoto kumeneko ankagwiritsa ntchito chitsamba chinachake kuti apange mlangali kapena chibakuwa chotchuka kwambiri. Lidiya, amene anakhala Mkristu pa ulendo wa Paulo wopita ku Filipi ku Greece anali “wakugulitsa chibakuwa, wakumudzi wa Tiyatira.”​—Machitidwe 16:12-15.

4. Kodi mpingo wa ku Tiyatira anauyamikira chifukwa chiyani?

4 Yesu anayamikira mpingo wa ku Tiyatira chifukwa cha ntchito zake zabwino, chikondi, chikhulupiriro, ndi kupirira kwake, ndi ntchito zake mu utumiki. Inde, ‘ntchito zake zotsiriza zinali zochuluka koposa zoyambazo.’ Komabe, ngakhale tili ndi mbiri yabwino, tiyenera kukhalabe osamala za makhalidwe athu.

5-7. (a) Kodi “mkazi Yezebeli” anali ndani, ndipo n’chiyani chimene anthu anafunika kuchita polimbana ndi khalidwe lake? (b) Kodi uthenga wa Kristu ku mpingo wa ku Tiyatira umathandiza akazi oopa Mulungu kuchita chiyani?

5 Mpingo wa ku Tiyatira unkalekerera kupembedza mafano, ziphunzitso zonyenga, ndi chiwerewere. Pakati pawo panali “mkazi Yezebeli,” amene mwina linali gulu la akazi a khalidwe ngati la Yezebeli, Mfumu yaikazi yoipa ya Ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi. Akatswiri ena akunena kuti ‘aneneri aakazi’ a ku Tiyatira anayesera kunyengerera Akristu kuti azilambira milungu yaimuna ndi yaikazi ya timabungwe ta zamalonda, komanso kuti azichita nawo mapwando amene kunali kupezeka zakudya zoperekedwa nsembe ku mafano. Masiku ano, mkazi amene akuganiza kuti ndi mneneri asayese kusocheretsa ena mu mpingo wachikristu!

6 Yesu anali pafupi ‘kum’ponya mkazi Yezebeli pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m’chisautso chachikulu, ngati salapa ndi kuleka ntchito zake.’ Oyang’anira sayenera kumvera m’pang’onong’ono pomwe ziphunzitso ndi njira zoipa zoterozo, ndipo Mkristu aliyense safunika kuchita chiwerewere chenicheni kapena chauzimu kapena kupembedza mafano kuti aone kuti “zakuya za Satana” n’zoipadi. Ngati timvera chenjezo la Yesu, ‘tidzagwira chimene tili nacho,’ ndipo tchimo silidzatilamulira pakati pathu. Chifukwa chakuti anakana khalidwe loipa, zilakolako zoipa, ndi zolinga zosemphana ndi Mulungu, odzozedwa oukitsidwa amalandira “ulamuliro wa pa amitundu” ndipo limodzi ndi Kristu adzaphwanya amitunduwo. Mipingo ya masiku ano ili ndi nyenyezi zophiphiritsira, ndipo odzozedwa adzapatsidwa “nyenyezi yonyezimira ya nthanda,” Mkwati, Yesu Kristu, akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba.​—Chivumbulutso 22:16.

7 Mpingo wa ku Tiyatira anauchenjeza kuti usalekerere khalidwe loipa la akazi ampatuko. Uthenga wouziridwa ndi mzimu umene Kristu anapereka ku mpingowu umathandiza akazi oopa Mulungu masiku ano kuti azichita zinthu zogwirizana ndi malo amene Mulungu anawapatsa. Sayesa kulamulira amuna kapena kunyengerera abale kuti achite chiwerewere chauzimu kapena chenicheni. (1 Timoteo 2:12) M’malo mwake, akazi ameneŵa amapereka chitsanzo chabwino pochita ntchito zabwino komanso utumiki, zimene zimatamanda Mulungu. (Salmo 68:11; 1 Petro 3:1-6) Ngati mpingo utchinjiriza zinthu zimene uli nazo, zinthu monga ziphunzitso ndi khalidwe loyera, komanso utumiki wamtengo wapatali wa Ufumu, ndiye kuti Kristu pobwera adzaupatsa mphotho yabwino kwambiri, osati kuupha.

Kwa Mngelo wa ku Sarde

8. (a) Kodi mzinda wa Sarde unali kuti, ndipo unali mzinda wotani? (b) N’chifukwa chiyani mpingo wa ku Sarde unafunika kuuthandiza?

8 Mpingo wa ku Sarde unafunika kuuthandiza mwamsanga chifukwa unali wakufa mwauzimu. (Ŵerengani Chivumbulutso 3:1-6.) Mzinda wa Sarde unali pamtunda wa pafupifupi makilomita 50 kummwera kwa Tiyatira, ndipo unali mzinda wotukuka. Ntchito za malonda, nthaka ya chonde ya m’deralo, nsalu zaubweya ndi makalapeti aubweya amene ankapanga, zinapangitsa kuti mzindawu ukhale wolemera ndipo pa nthaŵi ina unali ndi anthu pafupifupi 50,000. Malinga ndi zimene wolemba mbiri Josephus ananena, mu mzinda wa Sarde munali Ayuda ambiri m’zaka 100 zomalizira za m’ma B.C.E. Pakati pa nyumba zophwasuka zimene zili mu mzindawu pali sunagoge ndi kachisi wa Artemi, mulungu wamkazi wa ku Efeso.

9. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuchita ngati sitichita utumiki wathu ndi mtima wonse?

9 Kristu anauza mngelo wa mpingo wa ku Sarde kuti: “Ndidziŵa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.” Bwanji ngati ifeyo timadziŵika kuti tili maso mwauzimu koma nkhani yochita nawo utumiki wosiyanasiyana wachikristu sitikhudza, ndipo sitichita utumiki wathu ndi mtima wonse, komanso utumikiwo ‘ukufuna kufa’ mwauzimu? Pamenepo tiyenera ‘kukumbukira umo tinalandirira ndi kumvera’ uthenga wa Ufumu, ndipo tiyambirenso kuchita khama mu utumiki wopatulika. Ndiponso, tiyenera kuyamba kupita ku misonkhano yonse yachikristu ndipo tizichita nawo zinthu zochitika pa misonkhano imeneyi ndi mtima wonse. (Ahebri 10:24, 25) Kristu anachenjeza mpingo wa ku Sarde kuti: “Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthaŵi yake ndidzadza pa iwe.” Kodi zimenezi zikutikhudzanso masiku ano? Posachedwapa adzatifunsa ndipo tidzafunikira kuyankha.

10. Ngakhale zinthu zitakhala ngati mmene zinalili ku Sarde, kodi Akristu oŵerengeka akhozabe kukhala otani?

10 Ngakhale zinthu zitakhala ngati mmene zinalili ku Sarde, pangakhalebe oŵerengeka ‘amene sadetsa zovala zawo ndipo angayende ndi Kristu m’zoyera; chifukwa ali oyenera.’ Nthaŵi zonse amadziŵika kuti ndi Akristu, ndipo amakhala osadetsedwa, opanda banga lililonse la dzikoli pa khalidwe lawo kapena chipembedzo chawo. (Yakobo 1:27) N’chifukwa chake Yesu ‘sadzafafaniza ndithu mayina awo m’buku la moyo, ndipo adzavomereza mayina awo pamaso pa Atate wake, ndi pamaso pa angelo.’ Akadzauzidwa kuti ndi oyenera kuyenda ndi Kristu, anthu a gulu la mkwatibwi wake odzozedwa adzavala bafuta wonyezimira woti mbu, amene akuimira ntchito zolungama za anthu oyera a Mulungu. (Chivumbulutso 19:8) Chifukwa chakuti akudziŵa kuti kumwamba kuli mwayi wapadera wa utumiki umene ukuwadikira, amakhala ndi mphamvu zoti agonjetsere dzikoli. Anthu amene akuyembekezera moyo wosatha wa padziko lapansi nawonso ali ndi madalitso amene akuwadikira. Nawonso mayina awo amalembedwa m’buku la moyo.

11. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tayamba kugona mwauzimu?

11 Palibe aliyense wa ife amene angafune kukhala ngati mpingo wa ku Sarde, umene moyo wake wauzimu unali womvetsa chisoni. Koma bwanji ngati taona kuti tayamba kugona mwauzimu? Tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti zinthu zitiyendere bwino. Mwina tayamba kukopeka ndi njira zoipa kapena tayamba kuphonya misonkhano komanso kuchita zochepa chabe mu utumiki wathu. Tiyeni timupemphe Yehova kuti atithandize popemphera ndi mtima wonse. (Afilipi 4:6, 7, 13) Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kuphunzira Malemba ndi mabuku a “mdindo wokhulupirika” kudzatithandiza kuti tikhale maso mwauzimu. (Luka 12:42-44) Tikatero tidzakhala ngati anthu a ku Sarde amene anali ovomerezeka pamaso pa Kristu, ndipo tidzalimbikitsa okhulupirira anzathu.

Kwa Mngelo wa ku Filadelfeya

12. Kodi zinthu zinali bwanji ku Filadelfeya wakale pa nkhani ya chipembedzo?

12 Yesu anayamikira mpingo wa ku Filadelfeya. (Ŵerengani Chivumbulutso 3:7-13) Mzinda wa Filadelfeya (umene tsopano umatchedwa Alasehir) unali wolemera komanso unali likulu la dera lopanga vinyo kumadzulo kwa Asia Minor. Moti mulungu wake wamkulu anali Dionisiyo, mulungu wa vinyo. Zikuoneka ngati Ayuda a ku Filadelfeya anayesayesa kuti anyengerere Akristu achiyuda kuti asasiye miyambo ina ya m’Chilamulo cha Mose, kapena kuti ayambirenso kuchita miyambo imeneyi, koma analephera.

13. Kodi Kristu wagwiritsa ntchito motani “chifungulo cha Davide”?

13 Kristu ali ndi “chifungulo cha Davide,” kutanthauza kuti zinthu zonse za Ufumu zili m’manja mwake ndipo iye ndi amene akuyang’anira banja la chikhulupiriro. (Yesaya 22:22; Luka 1:32) Yesu anagwiritsa ntchito chifungulo chimenecho, kapena kuti kiyi, kutsegulira Akristu a ku Filadelfeya wakale ndi kwina mwayi wogwira nawo ntchito zokhudzana ndi Ufumu. Chiyambire 1919, watsegulira “mdindo wokhulupirika” “khomo lalikulu” la mwayi wolalikira za Ufumu limene palibe munthu wotsutsa angalitseke. (1 Akorinto 16:9; Akolose 4:2-4) Komabe, khomo la ntchito zokhudzana ndi Ufumu n’lotsekeka kwa anthu amene ali “m’sunagoge wa Satana,” chifukwa sali Aisrayeli auzimu.

14. (a) Kodi Yesu anaulonjeza chiyani mpingo wa ku Filadelfeya? (b) Kodi tingatani kuti tisagwe pa “nthaŵi ya kuyesedwa”?

14 Yesu analonjeza Akristu ku Filadelfeya wakale kuti: “Popeza unasunga mawu a chipiriro changa, inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthaŵi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi.” Kulalikira kumafunika kupirira kofanana ndi kumene Yesu anasonyeza. Iye sanagonjere adani ake, koma anapitiriza kuchita chifuniro cha Atate wake. N’chifukwa chake Kristu anaukitsidwa n’kupatsidwa moyo wosafa kumwamba. Ngati sitisiya kulambira Yehova kumene tinasankha ndipo ngati tisonyeza kuti tili kumbali ya Ufumu mwa kulalikira uthenga wabwino, sitidzagwa pa nthaŵi ya mayeso ino, “nthaŵi ya kuyesedwa.” Tidzapitiriza ‘kugwira chimene tili nacho’ chochokera kwa Kristu mwa kuyesetsa kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Kuchita zimenezi kudzapangitsa odzozedwa kulandira korona wakumwamba wamtengo wapatali kwambiri, ndipo anzawo okhulupirika adzalandira moyo wosatha padziko lapansi.

15. Kodi anthu amene adzakhale ‘mizati ya m’Kachisi wa Mulungu’ ayenera kukhala otani?

15 Yesu akupitiriza kunena kuti: “Iye wakulakika, ndidzam’yesa iye mzati wa m’Kachisi wa Mulungu wanga, . . . ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m’Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.” Oyang’anira odzozedwa ayenera kuchirikiza kulambira koona. Iwo ayenera kulalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso kukhala oyera mwauzimu nthaŵi zonse kuti akhalebe oyenera kukaloŵa nawo mu “Yerusalemu watsopano.” Zimenezi n’zofunika ngati akufuna kudzakhala mizati m’kachisi wakumwamba waulemerero, ndiponso ngati akufuna kudzatenga dzina la mzinda wa Mulungu monga nzika zake zakumwamba, komanso ngati akufuna kudzakhala ndi dzina la Kristu monga mkwatibwi wake. Komanso, ayenera kukhala ndi makutu oti “amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.”

Kwa Mngelo wa ku Laodikaya

16. Kodi Laodikaya unali mzinda wotani?

16 Kristu anadzudzula mpingo wodzidalira kwambiri wa ku Laodikaya. (Ŵerengani Chivumbulutso 3:14-22.) Mzinda wa Laodikaya unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 150 kummaŵa kwa mzinda wa Efeso, ndipo unali m’chigwa cha chonde cha mtsinje wa Lycus pamphambano pa misewu imene amalonda ambiri anali kudutsamo. Mzindawu unali wolemera kwambiri ndipo unali ndi mafakitale komanso mabanki ambiri. Zovala zopangidwa ndi ubweya wakuda wa mu mzindawu zinali zodziŵika kwambiri. Chifukwa chakuti mu mzindawu ndi mmene munali sukulu ya zamankhwala yotchuka kwambiri, mwina n’kumene kunachokera mankhwala a maso a ufa otchedwa Frugiya. Asclepius, mulungu wa mankhwala, anali mmodzi mwa milungu yake yaikulu. Zikuoneka kuti ku Laodikaya kunali Ayuda ambiri ndipo ena mwa iwo akuoneka ngati anali olemera ndithu.

17. Kodi n’chifukwa chiyani Alaodikaya anadzudzulidwa?

17 Polankhula ku mpingo wa ku Laodikaya kudzera mwa “mngelo” wake, Yesu akulankhula mosonyeza kuti ali ndi ulamuliro monga “mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu.” (Akolose 1:13-16) Alaodikaya anadzudzulidwa chifukwa sanali ‘ozizira kapena otentha’ mwauzimu. Chifukwa anali ofunda chabe, Kristu anati adzawalavula m’kamwa mwake. Sizinali zovuta kwa iwo kumvetsetsa mfundo imeneyi. Mu mzinda wapafupi nawo wa Herapoli munali akasupe a madzi otentha, pamene mu mzinda wa Kolose munali madzi ozizira. Chifukwa chakuti madzi opita ku Laodikaya anali kuyenda ulendo wautali m’mapaipi, mwachidziŵikire anali kufika mu mzindawo ali ofunda. Mbali ina ya ulendowo madziwo amadutsa m’ngalande. Akamayandikira ku Laodikaya, anali kudutsa m’miyala yobooledwa pakati imene amaimatirira pamodzi.

18, 19. Kodi masiku ano Akristu amene ali ngati a ku Laodikaya angathandizidwe bwanji?

18 Anthu amene ali ngati Alaodikaya masiku ano sakhala otentha moti n’kutenthetsako anzawo kapena ozizira moti n’kutsitsimulako anzawo. Monga madzi ofunda, adzalavulidwa! Yesu safuna kuti anthu ameneŵa azim’lankhulira, monga ‘akazembe odzozedwa m’malo mwa Kristu.’ (2 Akorinto 5:20, NW) Ngati salapa, adzataya mwayi wawo wolalikira za Ufumu. Alaodikaya anali kufuna chuma cha padziko lapansi ndipo ‘sanadziŵe kuti anali atsoka, ndi ochititsa chifundo, ndi osauka, ndi akhungu, ndi ausiwa.’ Kuti anthu amene ali ngati Alaodikaya masiku ano achotse kusauka, khungu, ndi usiwa wawo wauzimu, ayenera kugula kwa Kristu “golidi woyengeka,” woimira chikhulupiriro choyesedwapo, komanso “zovala zoyera” zoimira chilungamo, ndi “mankhwala opaka m’maso” amene amathandiza munthu kuti aziona bwino mwauzimu. Oyang’anira achikristu amafuna kuthandiza anthu ameneŵa kuti azindikire kusauka kwawo kwauzimu, kuti asinthe n’kukhala “olemera ndi chikhulupiriro.” (Yakobo 2:5; Mateyu 5:3) Kuphatikiza apo, oyang’anira ayenera kuwathandiza kuthira “mankhwala opaka m’maso,” kuti akhulupirire ndi kutsata zimene Yesu amaphunzitsa, uphungu wake, chitsanzo chake, ndiponso kuti akhale ndi mtima wofanana ndi wa Yesuyo. Ameneŵa ndiwo mankhwala othetsa “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, [ndi] matamandidwe a moyo.”​—1 Yohane 2:15-17.

19 Yesu amadzudzula ndi kulanga anthu onse amene amawakonda. Oyang’anira amene ali pansi pake ayenera kuchita chimodzimodzi, koma mwachikondi. (Machitidwe 20:28, 29) Alaodikaya anafunika ‘kuchita changu, n’kutembenuka mtima,’ mwa kusintha maganizo ndi moyo wawo. Choncho, kodi ena a ife tazoloŵera moyo umene umachititsa kuti utumiki wathu wopatulika kwa Mulungu ukhale ngati chinthu chosafunika kwenikweni? Ngati ndi choncho, tiyeni ‘tigule mankhwala opaka m’maso kwa Yesu’ kuti tizitha kuona kufunika kochita changu pofuna Ufumu choyamba.​—Mateyu 6:33.

20, 21. Kodi ndani amene akulabadira akamva ‘kugogoda’ kwa Yesu masiku ano, ndipo kodi akuyembekezera chiyani mtsogolo?

20 “Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mawu anga nakatsegula pakhomo, ndidzaloŵa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine,” akutero Kristu. Nthaŵi zambiri Yesu ankaphunzitsa zinthu zauzimu akamadya chakudya. (Luka 5:29-39; 7:36-50; 14:1-24) Panopa akugogoda pakhomo pa mipingo yokhala ngati ya ku Laodikaya. Kodi anthu a m’mipingo yotereyi adzayankha akamva kugogodako, n’kuyambanso kumukonda Yesu, kumulandira pakati pawo, n’kumulola kuti awaphunzitse? Ngati atatero, Kristu adzadya nawo limodzi ndipo iwo adzapindula kwambiri mwauzimu.

21 Masiku ano, a “nkhosa zina” akulola Yesu kuloŵa mophiphiritsira, ndipo zimenezi zidzawabweretsera moyo wosatha. (Yohane 10:16; Mateyu 25:34-40, 46) Kristu adzapereka mwayi kwa wodzozedwa aliyense wolakika, woti ‘akhale pansi ndi iye pa mpando wachifumu wake, monga iyenso analakika, ndipo anakhala pansi ndi Atate wake pa mpando wachifumu Wake.’ Inde, Yesu akulonjeza wodzozedwa wolakika aliyense kuti adzamupatsa mphotho yaikulu kwambiri yoti adzakhale pa mpando wachifumu pamodzi naye kudzanja lamanja la Atate wake kumwamba. Ndipo a nkhosa zina olakika akuyembekezera kudzakhala nawo m’dziko lapansi losangalatsa kwambiri nthaŵi imene Ufumu uzidzalamulira.

Zimene Tonsefe Tingaphunzirepo

22, 23. (a) Kodi Akristu onse angapindule bwanji ndi mawu a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri? (b) Kodi titsimikize mtima kuchita chiyani?

22 Mosakayikira, Akristu onse angapindule ndi mawu a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asia Minor. Mwachitsanzo, akulu achikristu amayamikira anthu ndi mipingo imene ikuchita bwino zinthu zauzimu ngati mmene Kristu anachitira poyamikira anthu amene anayenera kuwayamikira. Ngati okhulupirira anzawo ali ofooka penapake, akulu amawathandiza kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba kuti alimbe. Ngati tonsefe, mwamsanga komanso ndi pemphero, tigwiritsa ntchito mfundo zosiyanasiyana za uphungu umene Kristu anapereka ku mipingo isanu ndi iŵiri ija, tidzapindula nthaŵi zonse. *

23 Masiku otsiriza ano si nthaŵi yoti tizidzidalira, kukonda chuma, kapena kuchita chinthu china chilichonse chimene chingatipangitse kuti tisatumikire Mulungu ndi mtima wonse. Choncho, mipingo yonse ipitirize kuwala ngati zoikapo nyali zimene Yesu akuzisunga pamalo pake. Monga Akristu okhulupirika, tiyeni tionetsetse kuti nthaŵi zonse tizimvetsera pamene Kristu akulankhula komanso tizimvera zimene mzimu ukunena. Tikatero, tidzakhala osangalala mpaka kalekale monga onyamula kuunika ndipo tidzabweretsa ulemerero kwa Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 Mavesi amene ali pa Chivumbulutso 2:1 mpaka 3:22 akufotokozedwanso m’chaputala 7 mpaka chaputala 13 cha buku la Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi “mkazi Yezebeli” anali ndani, ndipo n’chifukwa chiyani akazi oopa Mulungu samutsanzira?

• Kodi zinthu zinali bwanji mu mpingo wa ku Sarde, ndipo tingachite chiyani kuti tisakhale ngati Akristu ambiri akumeneko?

• Kodi Yesu anaulonjeza chiyani mpingo wa ku Filadelfeya, ndipo kodi zimenezi zimatikhudza bwanji masiku ano?

• Kodi n’chifukwa chiyani Alaodikaya anadzudzulidwa, koma kodi Akritu achangu masiku ano akuyembekezera chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Tiyenera kupeŵa njira zoipa za “mkazi Yezebeli”

[Zithunzi patsamba 18]

Yesu watsegulira otsatira ake “khomo lalikulu” lotsogolera ku ntchito zokhudzana ndi Ufumu

[Chithunzi patsamba 20]

Kodi mumamulandira Yesu ndi kumumvera?