Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Imani ndi Kupenya Chipulumutso cha Yehova!

Imani ndi Kupenya Chipulumutso cha Yehova!

Imani ndi Kupenya Chipulumutso cha Yehova!

“Chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu.”​—2 MBIRI 20:17.

1, 2. N’chifukwa chiyani kuukira kwa “Gogi, wa ku dziko la Magogi” kumene kuchitike posachedwapa n’kwakukulu kuposa kuukira kwa zigaŵenga kokhudza dziko lonse?

ANTHU ena amati uchigawenga n’kuukira dziko lonse, ndiponso kuukira chitukuko. M’pomveka kuti kuukira kumeneku sikuyenera kuonedwa mopepuka. Komabe, pali kuukira kwina kwakululu kumene anthu padziko lapansi akungokuganizira pang’ono kapenanso sakukuganizira n’komwe. Kodi n’kuukira kotani kumeneko?

2 Kumeneku n’kuukira kwa “Gogi, wa ku dziko la Magogi,” kumene Baibulo limafotokoza mu Ezekieli chaputala 38. Kodi n’kukokomeza zinthu kunena kuti kuukira kumeneku n’kwakukulu kuposa kuukira kwa zigaŵenga kokhudza mayiko onse? Ayi, chifukwa chakuti Gogi adzaukira boma lakumwamba la Mulungu osati maboma a anthu. Komabe, mosiyana ndi anthu amene amangothana pang’ono chabe ndi kuukiridwa kwa maboma awo, Mlengi angathane kotheratu ndi kuukira koopsa kwa Gogi.

Kuukira Boma la Mulungu

3. Kodi olamulira a dziko lapansi auzidwa kuchita chiyani kuyambira mu 1914, ndipo kodi achita bwanji?

3 Kulimbana pakati pa Mfumu ya Mulungu imene ikulamulira tsopano ndi dongosolo loipa la Satana kwakhala kukuchitika kuyambira pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914. Panthaŵi imeneyo, olamulira a anthu anadziŵitsidwa kuti ayenera kugonjera Wolamulira amene Mulungu anamusankha. Koma iwo akana kutero, monga mmene zinaloseredwa kale kuti: “Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti, tidule zomangira zawo, titaye nsinga zawo.” (Salmo 2:1-3) Kutsutsa ulamuliro wa Ufumu kudzafika pachimake panthaŵi ya kuukira kwa Gogi wa ku Magogi.

4, 5. Kodi anthu angalimbane bwanji ndi boma lakumwamba losaoneka la Mulungu?

4 Tingadabwe kuti anthu angalimbane bwanji ndi boma lakumwamba losaoneka. Baibulo limafotokoza kuti boma limeneli lapangidwa ndi “zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, ogulidwa kuchokera kudziko,” pamodzi ndi “Mwanawankhosayo,” Kristu Yesu. (Chivumbulutso 14:1, 3; Yohane 1:29) Popeza n’lakumwamba, boma latsopanolo limatchedwa “kumwamba kwatsopano,” pamene nzika zake zimene zidzakhala pa dziko lapansi moyenera zimatchedwa “dziko latsopano.” (Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13) Ambiri mwa olamulira anzake a Kristu a 144,000 anamwalira ali okhulupirika. Motero iwo anatsimikizira kuti anali oyenerera kuyamba ntchito yawo yatsopano yotumikira kumwamba.

5 Komabe, otsalira ochepa a 144,000 akadali padziko lapansi. Mwa anthu oposa 15,000,000 amene anapezeka pa phwando la Mgonero wa Ambuye mu 2002, anthu 8,760 okha ndi amene anasonyeza kuti anasankhidwa kukagwira ntchito ya kumwamba imeneyi. Aliyense amene amayerekeza kuukira otsalira oyembekezera kukalamulira nawo mu Ufumuwo kwenikweni amaukira Ufumu wa Mulungu.​—Chivumbulutso 12:17.

Mfumu Igonjetsa Komaliza

6. Kodi Yehova ndi Kristu amaona bwanji kutsutsidwa kwa anthu a Mulungu?

6 Zimene Yehova adzachitira anthu otsutsa Ufumu wake wokhazikitsidwa zinaloseredwa motere: “Wokhala m’mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. Pomwepo adzalankhula nawo mu mkwiyo wake, nadzawaopsa m’ukali wake; koma Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” (Salmo 2:4-6) Tsopano nthaŵi yafika yoti Kristu, molangizidwa ndi Yehova, “alakike [“agonjetse komaliza,” NW].” (Chivumbulutso 6:2) Kodi Yehova amaona bwanji kutsutsidwa kwa anthu ake pa nthaŵi ya kugonjetsa komaliza? Amaona kuti akutsutsa iyeyo ndiponso Mfumu yake imene ikulamulira. Yehova anati: “Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso [langa, NW].” (Zekariya 2:8) Ndiponso Yesu ananena mwamphamvu kuti amaona zimene anthu akuchitira abale ake odzozedwa kuti akumuchitira iye ndipo zimene alephera kuwachitira abale akewo ndiye kuti alephera kumuchitira iye.​—Mateyu 25:40, 45.

7. N’chifukwa chiyani Gogi akukwiyira a “khamu lalikulu” amene awafotokoza pa Chivumbulutso 7:9?

7 N’zoona kuti amene akuthandiza kwambiri otsalira odzozedwa, Gogi adzawakwiyira monga akuchitira kwa odzozedwawo. Anthu ameneŵa amene akuyembekezera kudzakhala ena mwa anthu a “dziko latsopano” la Mulungu, ndiwo “khamu lalikulu” limene laitanidwa ‘kuchokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ (Chivumbulutso 7:9) Ameneŵa akuwafotokoza kuti “akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera.” Motero, Mulungu ndi Kristu Yesu akukondwera nawo. Atatenga “makhwatha a kanjedza m’manja mwawo,” akutamanda Yehova monga Wolamulira woyenera wa chilengedwe chonse, amene ulamuliro wake ukuimiridwa ndi ulamuliro wa Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu, “Mwanawankhosa wa Mulungu.”​—Yohane 1:29, 36.

8. Kodi kuukira kwa Gogi kudzapangitsa Kristu kuchita chiyani, ndipo padzakhala zotsatira zotani?

8 Kuukira kwa Gogi kudzapangitsa Mfumu yoikidwayo kuchitapo kanthu ndi kumenya nkhondo ya Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Anthu amene akana kugonjera ulamuliro wa Yehova adzawonongedwa. Koma amene apirira chizunzo chifukwa cha kukhulupirika kwawo ku Ufumu wa Mulungu, adzapeza mpumulo wosatha. Mtumwi Paulo pofotokoza zimenezi analemba kuti: “[Ichi] ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukaŵerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zoŵaŵa; popeza n’kolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.”​—2 Atesalonika 1:5-8.

9, 10. (a) Kodi Yehova anawathandiza bwanji Ayuda kugonjetsa gulu lankhondo lochititsa mantha? (b) Kodi Akristu masiku ano ayenera kupitiriza kuchita chiyani?

9 Panthaŵi ya chisautso chachikulu chimene chidzafika pachimake pa Armagedo, Kristu adzalimbana ndi mphamvu zoipa zonse. Koma otsatira ake sadzafunikira kumenya nkhondo, monganso mmene anthu a mu ufumu wa mafuko aŵiri wa Yuda sanafunikire kumenya nkhondo zaka zambirimbiri zapitazo. Nkhondoyo inali ya Yehova, ndipo iye anachititsa Ayudawo kupambana. Nkhaniyo imati: “Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m’phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha. Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m’phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwawononga psiti; ndipo atatha okhala m’Seiri, anasandulikirana kuwonongana. Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kuchipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo ili ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.”​—2 Mbiri 20:22-24.

10 Zinachitika monga mmenedi Yehova ananeneratu kuti: “Si kwanu kuchita nkhondo.” (2 Mbiri 20:17) Zimenezi zikupereka chitsanzo choti Akristu adzatsatire Yesu Kristu ‘akamadzagonjetsa komaliza.’ Pakadali pano, akupitiriza kulimbana ndi mphamvu zoipa pogwiritsa ntchito zida zauzimu osati zida zenizeni za nkhondo. Mwa kuchita zimenezi, iwo ‘ndi chabwino, akugonjetsa choipa.’​—Aroma 6:13; 12:17-21; 13:12; 2 Akorinto 10:3-5.

Ndani Adzatsogolera Kuukira kwa Gogi?

11. (a) Kodi ndi magulu ati amene Gogi adzawagwiritsa ntchito poukira? (b) Kodi kukhala tcheru mwauzimu kumafuna chiyani?

11 Gogi wa ku Magogi ndiye Satana Mdyerekezi pa malo ake onyozeka kuyambira mu 1914. Iye monga cholengedwa chauzimu, sangaukire mwachindunji, m’malo mwake adzagwiritsa ntchito magulu a anthu kuchita ntchito yake. Kodi magulu a anthu ameneŵa adzakhala ati? Baibulo silikutifotokozera mwatsatanetsatane, komabe limatisonyeza zinthu zina zimene zingatithandize kudziŵa kuti maguluwo adzakhala ati. Pamene zinthu zikuchitika m’dzikoli pokwaniritsa maulosi a Baibulo, pang’onompang’ono tidzamvetsa bwinobwino. Anthu a Yehova amapeŵa nkhambakamwa koma amakhala atcheru mwauzimu, akumaona zochitika za ndale ndi zachipembedzo zimene zikusonyeza kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo.

12, 13. Kodi mneneri Danieli analosera bwanji kuukiridwa komaliza kwa anthu a Mulungu?

12 Mneneri Danieli anafotokoza zambiri zokhudza kuukiridwa komaliza kwa anthu a Mulungu, pamene analemba kuti: “Adzatuluka iye [mfumu ya kumpoto] ndi ukali waukulu kupha ndi kuwononga konse ambiri. Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika.”​—Danieli 11:44, 45.

13 M’nthaŵi za m’Baibulo, “nyanja yamchere” inali Nyanja Yaikulu, kapena kuti nyanja ya Mediterranean, ndipo “phiri lopatulika” linali Ziyoni, limene Yehova anati: “Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” (Salmo 2:6; Yoswa 1:4) Motero, mwauzimu, dera la “pakati pa nyanja ya mchere ndi phiri lopatulika” likuimira malo auzimu a Akristu odzozedwa omwe zinthu zikuwayendera bwino kwambiri. Iwo salinso m’nyanja ya anthu amene apatuka kwa Mulungu, ndipo akuyembekezera kudzalamulira pamodzi ndi Kristu Yesu mu Ufumu wakumwamba. Mwachionekere, atumiki odzozedwa a Mulungu pamodzi ndi anzawo okhulupirika a khamu lalikulu, adzaukiridwa mwankhanza ndi mfumu ya kumpoto pokwaniritsa ulosi wa Danieli.​—Yesaya 57:20; Ahebri 12:22; Chivumbulutso 14:1.

Kodi Atumiki a Mulungu Adzachita Bwanji?

14. Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene anthu a Mulungu adzachita akadzaukiridwa?

14 Kodi atumiki a Mulungu adzafunika kuchita chiyani akadzaukiridwa? Pa mbali imeneyinso, zimene mtundu wa Mulungu m’masiku a Yehosafati unachita zikupereka chitsanzo. Onani kuti anthuwo analamulidwa kuchita zinthu zitatu: (1) kuchirimika, (2) kuima, ndi (3) kupenya chipulumutso cha Yehova. Kodi anthu a Mulungu masiku ano adzatsatira bwanji mawu ameneŵa?​—2 Mbiri 20:17.

15. Kodi kuchirimika kwa anthu a Yehova kukutanthauza chiyani?

15 Kuchirimika: Anthu a Mulungu adzachirimikabe kukhala ku mbali ya Ufumu wa Mulungu popanda kugwedezeka. Adzapitirizabe kuchirimika pa kusaloŵerera kwawo m’zinthu za m’dzikoli monga Akristu. Adzakhala “okhazikika, osasunthika” potumikira Yehova mokhulupirika ndipo adzapitiriza kutamanda Yehova pamaso pa anthu chifukwa cha kukoma mtima kwake kwachikondi. (1 Akorinto 15:58; Salmo 118:28, 29) Pakalipano ngakhalenso m’tsogolo, palibe chiyeso chimene chidzawachititsa kusiya kuchirimika kumeneku kumene Mulungu akukondwera nako.

16. Kodi atumiki a Yehova adzaima motani?

16 Kuima: Atumiki a Yehova sadzayesera kudzipulumutsa okha koma adzadalira Yehova ndi mtima wawo wonse. Ndi iye yekha amene angathe kupulumutsa atumiki ake m’chipwirikiti cha dzikoli, ndipo walonjeza kuti adzatero. (Yesaya 43:10, 11; 54:15; Maliro 3:26) Kudalira Yehova kudzaphatikizapo kudalira njira yamakono yooneka ndi maso imene iye wakhala akuigwiritsa ntchito kwa zaka zambiri pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Panthaŵi imeneyo, kuposa ndi kale lonse, Akristu oona adzafunika kudalira kwambiri olambira anzawo amene akutsogolera movomerezedwa ndi Yehova ndiponso Mfumu yake imene ikulamulira. Amuna okhulupirika ameneŵa adzatsogolera anthu a Mulungu. Kunyalanyaza malangizo awo kudzabweretsa tsoka.​—Mateyu 24:45-47; Ahebri 13:7, 17.

17. N’chifukwa chiyani atumiki okhulupirika a Mulungu adzaona chipulumutso cha Yehova?

17 Kupenya chipulumutso cha Yehova: Chipulumutso chidzakhala mphoto ya onse amene akuchirimika pa kukhulupirika kwawo kwachikristu ndiponso amene akudalira Yehova kuti adzawawombola. Iwo adzalengeza mmene angathere kufika kwa tsiku la Yehova la chiweruzo mpaka nthaŵi yomaliza. Chilengedwe chonse chiyenera kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu woona ndipo kuti iye ali ndi atumiki okhulupirika padziko lapansi. Sipadzakhalanso kusagwirizana kumene kwakhalapo nthaŵi yaitali pankhani yoti Yehova ndiye woyenerera kulamulira chilengedwe chonse.​—Ezekieli 33:33; 36:23.

18, 19. (a) Kodi nyimbo yachipambano imene ili mu Eksodo chaputala 15 ikusonyeza bwanji mmene adzamvera anthu amene adzapulumuka kuukira kwa Gogi? (b) Kodi anthu a Mulungu ayenera kuchita chiyani pakalipano?

18 Anthu a Mulungu atapezanso mphamvu, adzaloŵa m’dziko latsopano, akufunitsitsa kuimba nyimbo yachipambano, monga mmene Aisrayeli akale anachitira atawomboledwa pa Nyanja Yofiira. Poyamikira Yehova kosatha chifukwa chowateteza, iwo, aliyense payekha ndiponso monga gulu, adzabwereza mawu akale aŵa akuti: “Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu. . . . Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova. . . . Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani. Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira inu; mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu. . . . Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwa mphamvu yanu mudawalondolera njira yakumka pokhala panu poyera. . . . Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la choloŵa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, Malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika. Yehova adzachita ufumu nthaŵi yomka muyaya.”​—Eksodo 15:1-19.

19 Popeza kuti tsopano chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha n’chotsimikizika kuposa kale lonse, ndi nthaŵi yabwino kwambiri kuti atumiki a Mulungu asonyeze kudzipereka kwawo kwa Yehova ndi kutsimikizanso mtima kumutumikira monga Mfumu yawo yosatha.​—1 Mbiri 29:11-13.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani Gogi adzaukira odzozedwa ndi a nkhosa zina?

• Kodi anthu a Mulungu adzachirimika bwanji?

• Kodi kuima kukutanthauza chiyani?

• Kodi anthu a Mulungu adzaona bwanji chipulumutso cha Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Yehova anathandiza Yehosafati ndi anthu ake kupambana popanda anthuwo kumenya nawo nkhondo

[Chithunzi patsamba 20]

Odzozedwa ndi a nkhosa zina pamodzi akukhalira mbali ulamuliro wa Yehova

[Chithunzi patsamba 22]

Mofanana ndi Aisrayeli akale, anthu a Mulungu posachedwapa adzaimba nyimbo yachipambano