Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupatsa Kumene Kumasangalatsa Mulungu

Kupatsa Kumene Kumasangalatsa Mulungu

Kupatsa Kumene Kumasangalatsa Mulungu

YESU ndi ophunzira ake anali akudya chakudya chokoma ku Betaniya ndi anzawo apamtima angapo, monga Maria, Marita, ndiponso Lazaro yemwe anangoukitsidwa kumene. Mariya atatenga muyeso umodzi wa mafuta odula ndi kudzoza mapazi a Yesu, Yudase Isikariote anakwiya ndipo ananena mawu amene anali kukhosi kwake. Iye anadandaula kuti: “Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi malupiya atheka mazana atatu [pafupifupi malipiro a munthu a chaka chonse], ndi kupatsidwa kwa osauka?” Nthaŵi yomweyo anthu enanso anadandaula chimodzimodzi.​—Yohane 12:1-6; Marko 14:3-5.

Komabe, Yesu anayankha kuti: “Mlekeni. . . . Pakuti muli nawo aumphaŵi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.” (Marko 14:6-9) Atsogoleri achipembedzo achiyuda ankaphunzitsa kuti kupereka zinthu zothandiza anthu osoŵa ndi khalidwe labwino komanso munthu angakhululukidwe machimo. Koma Yesu anasonyeza kuti kupatsa kumene kumasangalatsa Mulungu si kuthandiza osoŵa kudzera m’mabungwe okha basi.

Kuona mwachidule momwe kupatsa kunkachitikira mu mpingo woyambirira wachikristu kutisonyeza njira zina zabwino zimene tingasonyezere kuganizira ena ndiponso kuti kupatsa kwathu kusangalatse Mulungu. Kutisonyezanso kupatsa kumene kumapindulitsa kwambiri.

‘Patsani Mphatso Zachifundo’

Panthaŵi zingapo Yesu analimbikitsa ophunzira ake ‘kupatsa mphatso zachifundo.’ (Luka 12:33) Komabe Yesu anachenjeza kuti azipeŵa kudzionetsera kumene kunali kuchitika n’cholinga chotamanda woperekayo m’malo motamanda Mulungu. Iye anati: “Pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamawomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m’masunagoge, ndi m’makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu.” (Mateyu 6:1-4) Potsatira langizo limeneli, Akristu oyambirira ankapeŵa kudzionetsera kumene atsogoleri achipembedzo odziona ngati opembedza kwambiri a m’nthaŵi yawo anali kuchita ndipo anasankha kuthandiza anthu osoŵa mwa kuwatumikira kapena kuwapatsa mphatso mwachinsinsi.

Mwachitsanzo, pa Luka 8:1-3 timauzidwa kuti Mariya Magadalene, Yohana, Susana, ndi anthu ena anagwiritsa ntchito “chuma chawo” mosadzionetsera kutumikira Yesu ndi atumwi ake. Ngakhale kuti amuna ameneŵa sanali osauka, anasiya zinthu zimene zinkawathandiza kupeza zofunika pamoyo wawo pofuna kuthera mphamvu zawo zonse mu utumiki. (Mateyu 4:18-22; Luka 5:27, 28) Akazi ameneŵa kwenikweni anatamanda Mulungu, chifukwa chothandiza amuna ameneŵa kumaliza ntchito imene Mulungu anawapatsa. Ndipo Mulungu anayamikira akazi ameneŵa mwa kusunga mu Baibulo nkhani yonena za kupatsa ndi kuchitira anthu chifundo kumene anasonyeza, kuti anthu a mibadwo yonse ya m’tsogolo adzaŵerenge.​—Miyambo 19:17; Ahebri 6:10.

Dorika anali mkazi winanso amene “anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo.” Ankasokera zovala akazi amasiye osauka ku mudzi wakwawo wa Yopa umene unali m’mphepete mwa nyanja. Sitikudziŵa ngati ankagula zonse zofunika pa zimene anali kusokazo kapena ankangowathandiza ntchito yosoka yokha. Komabe, ntchito yake yabwino inapangitsa kuti anthu amene anali kuwathandizawo amukonde, pamodzinso ndi Mulungu amene anadalitsa kukoma mtima kwake.​—Machitidwe 9:36-41.

N’Kofunika Kukhala ndi Cholinga Choyenera

Kodi n’chiyani chinalimbikitsa anthu ameneŵa kupatsa? Sikuti chinali chifukwa cha chifundo chimene ankakhala nacho akapemphedwa kuti athandize. Ankadziŵa kuti kunali koyenera tsiku lililonse kuchita zimene angathe pothandiza amene anali paumphaŵi, kudwala, kapena pamavuto ena. (Miyambo 3:27, 28; Yakobo 2:15, 16) Uku ndiko kupatsa kumene kumasangalatsa Mulungu. Kumachitika kwenikweni chifukwa chokonda kwambiri Mulungu ndi kufunitsitsa kutsanzira chifundo chake ndi kuwolowa manja kwake.​—Mateyu 5:44, 45; Yakobo 1:17.

Mtumwi Yohane anagogomezera mfundo yofunika kwambiri imeneyi pankhani yopatsa pamene anafunsa kuti: “Iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pom’mana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?” (1 Yohane 3:17) Yankho lake n’lachidziŵikire. Kukonda Mulungu kumalimbikitsa anthu kuthandiza anthu osoŵa. Mulungu amayamikira ndi kudalitsa anthu amene mofanana ndi iye, amasonyeza mtima wopatsa. (Miyambo 22:9; 2 Akorinto 9:6-11) Kodi masiku ano timaona kupatsa kwamtundu umenewu? Tamvani zimene zinachitika posachedwapa mu mpingo wina wa Mboni za Yehova.

Mayi wina wachikristu yemwe ndi wokalamba nyumba yake inkafunika kukonza zinthu zambiri. Mayiyu ankakhala yekha ndipo analibe achibale oti angamuthandize. Zaka zonsezo, m’nyumba yake anali kuchitiramo misonkhano yachikristu, ndipo nthaŵi zambiri ankadya chakudya chake ndi aliyense amene walola akamuitanira. (Machitidwe 16:14, 15, 40) Anthu a mumpingo wake ataona vuto lakelo, anagwirizana zoti athandize. Ena anapereka ndalama, ena anathandiza ntchito yeniyeniyo. Mapeto angapo a sabata, anthu ogwira ntchito odziperekawo anaika denga, anamanga chipinda china chosambiramo, anaika pulasitala ndi kupenta nsanja yoyamba yonse, ndipo anaika makabati atsopano ku khichini. Kupatsa kwawo kunasangalatsa mayiyo komanso kunagwirizanitsa kwambiri anthu a mumpingowo ndipo kunachititsa chidwi anthu oyandikana nawo monga chitsanzo cha mmene Akristu oona amapatsira.

Pali njira zambiri zimene tingathandizire ena. Kodi sitingacheze ndi mwana wamasiye? Kodi sitingakagulire zinthu kapena kusokera chinthu mkazi wamasiye wachikulire amene timamudziŵa? Kodi sitingapatse chakudya kapena kumpatsa ndalama munthu wosoŵa ndalama? Sikuti zimadalira kukhala wolemera kuti tithandize ena. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chim’soŵa.” (2 Akorinto 8:12) Koma kodi Mulungu amavomereza kupatsa kwa mtundu umenewu basi, kopatsa anthuwo mwachidunji? Ayi.

Bwanji Zothandiza Anthu Ambiri?

Nthaŵi zina kuthandiza patokha kumakhala kosakwanira. Ndipotu, Yesu ndi ophunzira ake anali ndi thumba la ndalama zothandizira osoŵa, ndipo ankalandira ndalama kwa anthu achifundo amene anali kukumana nawo mu ntchito yawo. (Yohane 12:6; 13:29) Mofananamo, mpingo wa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino unkatolera ndalama pakafunika kutero ndipo unkakonza zothandiza anthu ambiri.​—Machitidwe 2:44, 45; 6:1-3; 1 Timoteo 5:9, 10.

Nthaŵi ina imene zimenezi zinafunika inali cha m’ma 55 C.E. Mipingo ya ku Yudeya inali paumphaŵi, mwina chifukwa cha njala yaikulu imene inagwa kumeneko. (Machitidwe 11:27-30) Mtumwi Paulo, popeza nthaŵi zonse ankaganizira za amphaŵi, anapempha mipingo mpaka ya ku Makedoniya kuti ithandize. Iye anasonkhanitsa ndalama ndipo anatuma amuna oyenerera kukatula ndalamazo. (1 Akorinto 16:1-4; Agalatiya 2:10) Iye ndiponso ena amene anali kugwira nawo ntchitoyo sanali kulipidwa pantchito yawo.​—2 Akorinto 8:20, 21.

Mboni za Yehova masiku ano zimakhalanso chire kuthandiza pakagwa tsoka. Mwachitsanzo, m’chilimwe cha 2001, chifukwa cha mvula ya mkuntho, madzi anasefukira ku Houston, mu chigawo cha Texas, m’dziko la United States of America. Nyumba za Mboni zokwana 723 zinawonongeka, zina pang’ono pamene zina zinawonongeka kwambiri. Komiti ya akulu oyenerera achikristu, yoyang’anira zopereka thandizo inakhazikitsidwa mwamsanga kuti ifufuze zimene anthu anali kusoŵa ndi kukapereka ndalama zoti zithandize Mboni za kumeneko kuthana ndi vutolo ndiponso kukonzetsera nyumba zawo. Antchito odzipereka a m’mipingo yapafupi anagwira ntchito yonse. Mboni ina inayamikira kwambiri thandizo limene inalandira moti kampani ya inshuwalansi itangom’patsa ndalama zoti akonzetsere nyumba yake, iye anapereka ndalamazo ku thumba la ndalama zothandizira anthu kuti zithandizenso anthu ena ovutika.

Komabe, pankhani yopereka ndalama ku mabungwe othandiza anthu osoŵa, tifunika kusamala pamene tikulingalira zimene tapemphedwa kuchita. Mabungwe ena amafuna ndalama zambiri zolipirira amene akuyendetsa mabungwewo kapena zogwiritsa ntchito pa ndaŵala zopempha thandizolo. Zimenezi zimapangitsa kuti pa ndalama zimene apeza, n’zochepa zimene zimagwiradi ntchito yake. Miyambo 14:15 amati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Choncho ndi nzeru kuiona nkhaniyo mosamala.

Kupatsa Kumene Kumapindulitsa Kwambiri

Pali kupatsa kumene kuli kofunika kwambiri kuposa kuthandiza anthu osoŵa powapatsa zinthu. Yesu anali kunena zimenezi pamene wolamulira wachinyamata, wachuma anamufunsa zimene afunika kuchita kuti akalandire moyo wosatha. Yesu anamuuza kuti: “Pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphaŵi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.” (Mateyu 19:16-22) Onani kuti Yesu sanangoti, ‘Kapatse aumphaŵi ndipo udzapeza moyo wosatha.’ Koma anatinso, “Ukadze kuno, unditsate.” M’mawu ena tinganene kuti, ngakhale kuti ntchito zachifundo n’zabwino ndiponso n’zothandiza, kukhala wophunzira wa Kristu kumafuna zambiri.

Chofunika kwambiri kwa Yesu chinali kuthandiza ena mwauzimu. Atatsala pang’ono kuphedwa, anamuuza Pilato kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Ngakhale kuti Yesu ankakonda kuthandiza amphaŵi, kuchiritsa odwala, ndiponso kudyetsa anjala, koposa zonse anaphunzitsa ophunzira ake kulalikira. (Mateyu 10:7, 8) Ndipotu, pa zimene anawalangiza komalizira pali lamulo lakuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.”​—Mateyu 28:19, 20.

Ndi zoona kuti kulalikira sikungathetse mavuto onse padziko lapansi. Komabe, kuuza anthu amitundu yonse uthenga wabwino wa Ufumu kumapangitsa Mulungu kutamandidwa chifukwa chakuti kulalikira kumakwaniritsa zimene Mulungu amafuna ndipo kumatsegulira anthu amene amalandira uthenga wa Mulungu njira yopezera madalitso osatha. (Yohane 17:3; 1 Timoteo 2:3, 4) Bwanji osamvetsera Mboni za Yehova zikafikanso panyumba panu? Zimabwera ndi mphatso yauzimu. Ndipo zimadziŵa kuti ndicho chinthu chabwino koposa chimene angakupatseni.

[Zithunzi patsamba 6]

Pali njira zambiri zosonyezera kuganizira ena

[Chithunzi patsamba 7]

Kulalikira kwathu uthenga wabwino kumasangalatsa Mulungu ndipo kumatsegula njira yopezera madalitso osatha