Kuphunzira Chinsinsi Chokwanitsidwa ndi Zimene Tili Nazo
Kuphunzira Chinsinsi Chokwanitsidwa ndi Zimene Tili Nazo
Mtumwi Paulo m’kalata yolimbikitsa Akristu a ku Filipi, anati: “Ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. . . . Konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa.”—Afilipi 4:11, 12.
Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuona zimene anali nazo kukhala zokwanira? Poona kukwera mtengo kwa zinthu ndiponso kusakhazikika kwa chuma masiku athu ano, ndibwino kuti Akristu oona aphunzire kukwanitsidwa ndi zimene ali nazo kuti aike mtima pa ntchito yotumikira Mulungu.
PAULO kumayambiriro kwa kalata imene analemba, anafotokoza ntchito yake imene anali kugwira poyamba imene inali kumuyendera bwino. Iye anati: “Ngati wina yense ayesa kukhulupirira m’thupi, makamaka ineyu; wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israyeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi; monga mwa changu, wolondalonda Eklesia; monga mwa chilungamo cha m’lamulo wokhala wosalakwa ine.” (Afilipi 3:4-6) Komanso, monga Myuda wachangu, Paulo anali kulamulidwa ndi akulu ansembe a ku Yerusalemu ndipo anali kumuthandiza. Zinthu zonsezi zikanamuthandiza kukhala ndi ulamuliro ndi ulemu pa zandale, zachipembedzo, ndiponso mosakayika pa zachuma pakati pa Ayuda.—Machitidwe 26:10, 12.
Komabe, zinthu zinasinthiratu Paulo atakhala mtumiki wachikristu wachangu. Chifukwa cha uthenga wabwino, analolera kusiya ntchito yake imene inali kumuyendera bwinoyo ndiponso zonse zimene poyamba anali kuziona kuti n’zofunika. (Afilipi 3:7, 8) Kodi tsopano akanakwanitsa bwanji kupeza zinthu zofunika pamoyo wake? Kodi anali kulandira malipiro pa utumiki wake? Kodi anapeza bwanji zofuna zake?
Paulo anali kutumikira popanda malipiro. Choncho kuti asalemetse anthu amene anali kuwatumikira, anali kugwira ntchito ndi Akula ndi Priskila yosoka mahema ali ku Korinto, ndipo anali kuchita zinthu zinanso kuti apeze zofunika pamoyo wake. (Machitidwe 18:1-3; 1 Atesalonika 2:9; 2 Atesalonika 3:8-10) Paulo anayenda maulendo atatu ataliatali aumishonale, ndipo anayenderanso mipingo imene inali kufunika kuyenderedwa. Popeza anali wotanganitsidwa kwambiri ndi kutumikira Mulungu, analibe zinthu zambiri. Nthaŵi zambiri abale anali kum’patsa zinthu zimene anali kufunikira. Komabe, nthaŵi zina, chifukwa cha kuvuta kwa zinthu, anali kuvutika ndiponso kusoŵa zinthu. (2 Akorinto 11:27; Afilipi 4:15-18) Ngakhale zinali choncho, Paulo sanadandaulepo za mavuto ake ndipo sanasirire zimene ena anali nazo. Analimbikira kugwira ntchito mofunitsitsa komanso mosangalala kuti Akristu anzake apindule. Ndipotu, ndi Paulo amene anabwereza mawu otchuka a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” Ndi chitsanzotu chabwino kwambiri kwa ife tonse.—Machitidwe 20:33-35.
Tanthauzo Lokwanitsidwa ndi Zimene Tili Nazo
Chinthu chachikulu chimene chinathandiza Paulo kusangalala ndicho kukwanitsidwa ndi zimene anali nazo. Komabe, kodi kukwanitsidwa kumatanthauza chiyani? Kunena mwachidule, kumatanthauza kukhutira ndi zinthu zofunika kwambiri. Pankhani imeneyi, Paulo anauza Timoteo, yemwe anali kuyenda naye mu utumiki kuti: “Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha [“kudzipereka kwa Mulungu pamodzi ndi kukwanitsidwa,” NW] chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zopfunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Timoteo 6:6-8.
Onani kuti Paulo anagwirizanitsa kukwanitsidwa ndi kudzipereka kwa Mulungu. Anazindikira kuti munthu umapeza chimwemwe chenicheni osati chifukwa cha katundu kapena chuma koma chifukwa chodzipereka kwa Mulungu, kutanthauza kuti, kuika patsogolo kutumikira Mulungu. “Zakudya ndi zopfunda” zinali zongom’thandizira kupitirizabe kudzipereka kwa Mulungu. Choncho, chinsinsi chimene chinam’thandiza Paulo kuona zimene anali nazo kukhala zokwanira chinali kudalira Yehova, zivute zitani.
Anthu ambiri masiku ano amakumana ndi mavuto ambiri ndiponso sasangalala chifukwa chakuti sadziŵa chinsinsi chimenechi kapena amachinyalanyaza. M’malo moona zimene ali 1 Timoteo 6:9, 10.
nazo kukhala zokwanira, amakhulupirira ndalama ndi zinthu zimene angagule ndi ndalamazo. Makampani otsatsa malonda, manyuzipepala, mawailesi ndi ma TV amalimbikitsa anthu kuona kuti sangasangalale ngati alibe zinthu zodula ndi zipangizo zapamwamba ndi kuti afunika kuzipeza mofulumira. Mapeto ake, ambiri amakodwa mu msampha wofunafuna ndalama ndi chuma. M’malo mosangalala, “amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.”—Aphunzira Chinsinsi Chake
Masiku ano, kodi n’kothekadi kusangalala uli wodzipereka kwa Mulungu ndi wokwanitsidwa? Inde, n’kotheka. Ndipotu, anthu ambiri masiku ano akuchita zimenezo. Aphunzira chinsinsi chosangalala ndi katundu amene ali naye. Anthuwa ndi Mboni za Yehova, amene adzipatulira kwa Mulungu, kuti achite zofuna zake ndi kuphunzitsa anthu kulikonse cholinga chake.
Mateyu 24:14) Nthaŵi zambiri, moyo wa m’mayiko amene amatumizidwa si wapamwamba monga umene anazoloŵera. Mwachitsanzo, kumayambiriro a 1947 amishonale atafika ku dziko lina la ku Asia, n’kuti mavuto amene anabwera chifukwa cha nkhondo alipobe, ndipo nyumba zambiri zinalibe magetsi. M’mayiko ambiri, amishonale anapeza kuti anthu kumeneko amachapa kumtsinje chovala chimodzichimodzi pathabwa lochapira kapena pamwala osati kuchapa pamakina. Koma anapita kumeneko kukaphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo, choncho anasintha moyo wawo n’kumakhala monga momwe zinthu zinalili kumeneko ndipo anatanganidwa ndi utumiki.
Mwachitsanzo, tamvani za anthu amene adzipereka kuti aphunzitsidwe ndi kuwatumiza monga amishonale m’mayiko achilendo kukalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Ena ayamba utumiki wa nthaŵi zonse kapena asamukira ku madera kumene sikunafike uthenga wabwino. Adulfo wakhala mtumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zoposa 50 m’madera ambiri a ku Mexico. Iye akuti: “Monga mtumwi Paulo, ine ndi mkazi wanga taphunzira kusintha zinthu kuti tizikhala malingana ndi mmene zinthu zilili. Mwachitsanzo, mpingo wina umene tinakayendera unali kutali kwambiri ndi tauni ndiponso msika. Nthaŵi iliyonse ya chakudya, abale zinkawakwanira kudya mkate umodzi ndi kanyama kakhumba ndi mchere ndi kumwa khofi. Ndicho chakudya chimene anali kudya—mikate itatu patsiku. Choncho tinaphunzira kukhala monga mmene abale anali kukhalira. Ndakumana ndi zinthu zambiri ngati zimenezi mu zaka 54 zimene ndakhala ndikutumikira Yehova mu utumiki wa nthaŵi zonse.”
Florentino amakumbukira momwe iye ndi banja lake anasinthira kuyamba moyo wovuta. Iye pokumbukira moyo wake woyambirira akuti: “Bambo anga anali munthu wamalonda wolemera. Anali ndi minda yambiri. Ndimakumbukirabe kuti pakauntala ya golosale yathu panali dilowa, mlifupi linali la masentimita 50 ndipo linali lokuya masentimita 20, ndiponso linali ndi zigawo zinayi. Tinali kuikamo ndalama zimene tapeza patsiku. Pakutha pa tsiku lililonse, linali kudzaza ndi ndalama za siliva ndi za pepala.
“Mwadzidzidzi, chuma chathu chinatha. Tinachoka pa mwanaalirenji kufika posauka. Zonse zinatha kungotsala nyumba yokha. Kuphatikiza apo, mchimwene wanga anachita ngozi ndipo miyendo yake yonse inaferatu. Zinthu zinasintha kwambiri. Ndinali kugulitsa zipatso ndi nyama kwanthaŵi ndithu. Ndinali kukolola nawo thonje, mpesa, ndi nyemba, ndiponso kuthirira mbewu. Anthu ena ankanditi ndine wodziŵa ntchito zonse. Nthaŵi zambiri mayi ankatilimbikitsa potiuza kuti timadziŵa choonadi, chomwe ndi chuma chauzimu chopezeka ndi anthu ochepa okha. Choncho ndinaphunzira kukhala ndi zambiri ndiponso zochepa kapena wopandiratu. Tsopano popeza ndatumikira Yehova mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka pafupifupi 25, ndinganene kuti tsiku lililonse ndimapeza madalitso odziŵa kuti ndinasankha njira yabwino pamoyo—kutumikira Yehova nthaŵi zonse.”
Baibulo limatiuza mosapita m’mbali kuti “maonekedwe a dziko ili apita [“akusintha,” NW].” N’chifukwa chake, limatilimbikitsanso kuti: “Iwo akukondwera, [akhale] monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu; ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa.”—1 Akorinto 7:29-31.
Choncho, ino tsopano ndi nthaŵi yopenda moyo wanu mwachifatse. Ngati muli ndi katundu wochepa, peŵani kuipidwa, ngakhale kuwawidwa mtima ndi kuchita nsanje. Komanso, kaya muli ndi zinthu zochuluka bwanji, ndibwino kuziona moyenera kuti zisakulamulireni. Monga momwe mtumwi Paulo analimbikitsira, ikani chidaliro chanu, osati mu “chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” Mukatero, ndiye kuti inunso munganene kuti mwaphunzira chinsinsi chokwanitsidwa ndi zimene muli nazo.—1 Timoteo 6:17-19.
[Chithunzi patsamba 9]
Paulo anagwira ntchito ndi manja ake kuti asalemetse anthu ena
[Zithunzi patsamba 10]
Anthu ambiri akusangalala ndi moyo ‘wodzipereka kwa Mulungu pamodzi ndi kukwanitsidwa’