Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Musaope, Kapena Kutenga Nkhaŵa”

“Musaope, Kapena Kutenga Nkhaŵa”

“Musaope, Kapena Kutenga Nkhaŵa”

“Musaope, kapena kutenga nkhawa . . . Yehova ali ndi inu.”​—2 MBIRI 20:17.

1. Kodi uchigawenga umakhudza bwanji anthu, ndipo n’chifukwa chiyani mpake kuti anthu ali ndi mantha?

UCHIGAWENGA! Liwu limeneli limachititsa mantha anthu, kuwapangitsa kuona kuti ndi osatetezeka ndiponso osowa pogwira. Limachititsa anthu kuipidwa, kusasangalala, ndiponso kukwiya. Ndiponso anthu ambiri akuopa kuti uchigawenga udzapulula anthu m’tsogolomu. Mpake kuti anthu akhale ndi mantha otero chifukwa chakuti mayiko ambiri akhala akulimbana ndi uchigawenga wa mtundu uliwonse kwa zaka zambiri koma sanathe kuuthetsa.

2. Kodi Mboni za Yehova zimaona bwanji vuto la uchigawenga, ndipo zimenezi zikubutsa mafunso otani?

2 Komabe, pali chifukwa chomveka choyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino. Mboni za Yehova zimene zikulalikira mwachangu m’mayiko ndi m’madera okwana 234 padziko lonse, zikuyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. M’malo mochita mantha kuti uchigawenga sudzathetsedwa, izo zili ndi chidaliro chonse kuti udzathetsedwa, ndipo zimenezo zichitika posachedwapa. Kodi ndi nzeru kuyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino monga mmene Mboni zimachitira? Kodi ndani angachotse mlili umenewu padziko lapansi, ndipo zingachitike bwanji zimenezo? Popeza mwina chiwawa china chake chatikhudzapo tonsefe, n’koyenera kuona chifukwa chake tingayembekezere kuti zinthu zidzakhala bwino.

3. Kodi n’chiyani chikuchititsa anthu kukhala ndi mantha, ndipo analosera chiyani za nthaŵi yathu ino?

3 Masiku ano, anthu ali ndi mantha ndiponso nkhaŵa pa zifukwa zosiyanasiyana. Taganizirani anthu ambiri amene akulephera kudzisamalira chifukwa chokalamba, anthu amene akufookerafookera chifukwa cha matenda osachiritsika, ndiponso mabanja amene akuvutika kuti apeze zinthu zofunika pa moyo chifukwa cha mavuto a zachuma. Ndiponso, ganizirani kusatsimikizika kwa moyo weniweniwo! Tikhoza kumwalira mwadzidzidzi chifukwa cha ngozi kapena tsoka linalake, zimene zingachititse kuti zonse zimene tinkakonda zithere pomwepo. Mantha ndi nkhaŵa zoterozo, kuphatikizaponso mavuto ambiri okhudza munthu payekha ndiponso kukhumudwitsidwa, zachititsa kuti nthaŵi zathu zino zikhale monga mmene mtumwi Paulo anafotokozera kuti: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.”​—2 Timoteo 3:1-3.

4. Kodi ndi mbali yopatsa chiyembekezo iti imene ikupezeka mu lemba la 2 Timoteo 3:1-3 limene limafotokoza za mavuto okhaokha?

4 Ngakhale kuti lembali likufotokoza za mavuto okhaokha, likuperekanso chiyembekezo. Onani kuti nthaŵi zoŵaŵitsa n’zoti zidzafika mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu la Satana limene lilipoli. Zimenezi zikutanthauza kuti mpumulo uli pafupi ndipo kuti dziko loipali lili pafupi kuloŵedwa m’malo ndi ulamuliro wa Ufumu wangwiro wa Mulungu, umene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuupempherera. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewo ndi boma lakumwamba la Mulungu, limene mneneri Danieli ananena kuti “sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [a anthu] nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44.

Kusaloŵerera M’zinthu za M’dziko kwa Akristu N’kosiyana ndi Uchigawenga

5. Kodi mayiko posachedwapa achita chiyani ndi kuopseza kwa uchigawenga?

5 Kwa zaka zambiri, uchigawenga wapha anthu ambirimbiri. Anthu padziko lonse anazindikira kwambiri kuti uchigawenga ndi woopsa ataona zimene zigaŵenga zinachita ku mizinda ya New York ndi Washington, D.C., pa September 11, 2001. Poona kuti uchigawenga wakula ndiponso kuti ukukhudza dziko lonse, mayiko padziko lonse anagwirizana mwamsanga kuti athane nawo. Mwachitsanzo, pa December 4, 2001, malinga ndi lipoti la nyuzipepala ina, “nduna zoona nkhani za kunja za m’mayiko 55 a ku Ulaya, ku North America ndi ku Central Asia mogwirizana zinakonza mfundo” yoti agwirire ntchito pamodzi. Mkulu wina wa boma la United States anayamikira zimenezi kuti ziwapatsa “mphamvu zatsopano” pa ntchito yawo yothana ndi uchigawenga. Mwadzidzidzi, anthu miyandamiyanda anakhudzidwa ndi zimene magazini ya The New York Times inatcha “kuyambika kwa nkhondo yaikulu.” Sizikudziŵika ngati anthu adzapambana nkhondo imeneyo. Komabe, zotsatira za nkhondo yolimbana ndi uchigawenga imeneyo zachititsa anthu ambiri kukhala ndi mantha ndiponso nkhaŵa, koma osati anthu amene amakhulupirira Yehova.

6. (a) N’chifukwa chiyani nthaŵi zina ena sangamvetse kusaloŵerera m’zinthu za m’dziko kwachikristu kumene Mboni za Yehova zimachita? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa otsatira ake pankhani zoloŵa nawo mu ndale?

6 Mboni za Yehova zimadziŵika bwino kuti siziloŵerera m’nkhani za ndale. Ngakhale kuti anthu ambiri angalolere maganizo a Mboni za Yehova ameneŵa panthaŵi ya mtendere, iwo salolera kwambiri pakachitika zinazake zosayembekezeka. Nthaŵi zambiri, mantha ndi kusadziŵa kuti chichitike n’chiyani kumene kumakhalapo chifukwa cha nkhondo kumachititsa anthu kukhala ndi maganizo okondetsa dziko lawo. Zimenezi zingachititse ena kusamvetsa chifukwa chake munthu wina angakane kuthandizira zimene dziko lawo likuchita. Koma Akristu oona amadziŵa kuti ayenera kumvera lamulo la Yesu lakuti ‘siali a dziko lapansi.’ (Yohane 15:19; 17:14-16; 18:36; Yakobo 4:4) Zimenezi zimatanthauza kuti sayenera kuloŵerera m’nkhani za ndale kapena m’nkhani zina. Mwiniwakeyo Yesu anapereka chitsanzo chabwino. Popeza kuti anali ndi nzeru zangwiro ndi luso losaneneka, iye akanathandiza kwambiri kutukula moyo wa anthu m’nthaŵi yake. Komabe, iye anakana kuloŵerera m’nkhani za ndale. Kuchiyambi kwa utumiki wake, iye anakanitsitsa pamene Satana anati am’patsa ulamuliro pa maufumu onse a dziko lapansi. Kenako iye anathawa pamene anthu anafuna kuti am’patse udindo wa ndale.​—Mateyu 4:8-10; Yohane 6:14, 15.

7, 8. (a) Kodi kusaloŵerera m’nkhani za ndale kwa Mboni za Yehova sikutanthauza chiyani, ndipo chifukwa chiyani? (b) Kodi Aroma 13:1, 2 amaletsa bwanji kulimbana ndi boma mwa kuchita ziwawa?

7 Kusaloŵerera m’zinthu za m’dziko kwa Mboni za Yehova sikukutanthauza kuti izo zimakhalira mbali kapena kugwirizana ndi ziwawa. Zitati zichite zimenezo ndiye kuti zingatsutsane ndi kunena kwawo kuti ndi atumiki a “Mulungu wa chikondi ndi mtendere.” (2 Akorinto 13:11) Izo zaphunzira mmene Yehova amaonera chiwawa. Wamasalmo analemba kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Zimadziŵanso zimene Yesu anauza mtumwi Petro kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.”​—Mateyu 26:52.

8 Ngakhale kuti zochitika m’mbiri zasonyeza kuti Akristu onyenga nthaŵi zambiri agwiritsa ntchito “lupanga,” Mboni za Yehova sizitero. Izo zimapeŵa zimenezo. Mboni zimamvera mokhulupirika lamulo la pa Aroma 13:1, 2, lakuti: “Anthu onse amvere maulamuliro a akulu [olamulira a boma]; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.”

9. Kodi Mboni za Yehova zimathana ndi uchigawenga m’njira ziŵiri ziti?

9 Koma popeza kuti uchigawenga ndi woipa kwambiri, kodi Mboni za Yehova siziyenera kuchita chinachake pofuna kuthana nawo? Ee, ziyenera kutero ndipo zimatero kumene. Choyamba izo sizichita nawo ziwawazo. Chachiŵiri, zimaphunzitsa anthu mfundo zachikristu zomwe anthu akazitsatira zimathetseratu chiwawa chilichonse. * Chaka chatha, Mboni zinathera maola 1,202,381,302 kuthandiza anthu kuphunzira moyo wachikristu woterewu. Kumeneku sikunali kungowononga nthaŵi, chifukwa zotsatira zake zinali zoti anthu okwana 265,469 anabatizidwa monga Mboni za Yehova, motero anasonyeza pamaso pa anthu kuti akukaniratu chiwawa chilichonse.

10. Kodi tingayembekezere chiyani pankhani yochotsa chiwawa chimene chili m’dzikoli masiku ano?

10 Ndiponso, Mboni za Yehova zimadziŵa kuti pazokha sizingathe kuthetsa mavuto pa dziko lonse. N’chifukwa chake zimakhulupirira kwambiri Yehova Mulungu amene angakwanitse kutero. (Salmo 83:18) Anthu ngakhale atayesetsa bwanji, sangathe kuthetsa chiwawa. Wolemba Baibulo wina wouziridwa anatichenjezeratu za nthaŵi yathu ino ya “masiku otsiriza” kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Timoteo 3:1, 13) Poona zimenezi, sitingayembekezere kuti anthu angapambane nkhondo yolimbana ndi mphamvu zoipa. Koma, tingadalire Yehova kuti adzachotseratu chiwawa chonse ndiponso kuti sichidzachitika mpaka kalekale.​—Salmo 37:1, 2, 9-11; Miyambo 24:19, 20; Yesaya 60:18.

Opanda Mantha Ngakhale Ali Pafupi Kuukiridwa

11. Kodi Yehova wachita kale zotani kuti athetse ziwawa?

11 Popeza Mulungu wamtendere amadana ndi chiwawa, tingamvetse chifukwa chake wakonza zoti adzawononge amene amayambitsa ziwawazo, Satana Mdyerekezi. Ndipotu, Iye wachititsa kale Satana kugonjetsedwa mochititsa manyazi ndi mngelo wamkulu, Mikayeli, yemwe ndi Mfumu ya Mulungu yoikidwa kumene, Kristu Yesu. Baibulo limafotokoza zimenezi motere: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka, chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”​—Chivumbulutso 12:7-9.

12, 13. (a) Kodi n’chiyani chinachitika mu 1914? (b) Kodi ulosi wa Ezekieli unaneneratu kuti n’chiyani chidzachitikira amene ali ku mbali ya Ufumu wa Mulungu?

12 Malinga ndi mmene Baibulo limafotokozera, ndiponso zochitika za m’dzikoli, zimasonyeza kuti chaka cha 1914 ndi pamene nkhondo imeneyo inachitika kumwamba. Kuyambira pamenepo, zochitika m’dzikoli zaipiraipira. Pa Chivumbulutso 12:12 pamafotokoza chifukwa chake zili choncho, ponena kuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtundu ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.”

13 N’zomveka kuti Mdyerekezi wasonyeza kwambiri mkwiyo wake makamaka kwa olambira odzozedwa a Mulungu ndi anzawo a “nkhosa zina.” (Yohane 10:16; Chivumbulutso 12:17) Kutsutsa kumeneku kudzafika pachimake posachedwapa pamene Mdyerekezi adzaukira modetsa nkhaŵa onse amene ali kumbali ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu ndiponso amene amaudalira. Kuukira kwakukulu kumeneku anakutchula pa Ezekieli chaputala 38 kuti ndi kuukira kwa “Gogi, wa ku dziko la Magogi.”

14. Kodi Mboni za Yehova zatetezedwa bwanji m’mbuyomu, ndipo kodi zidzakhala choncho nthaŵi zonse?

14 Satana atathamangitsidwa kumwamba, anthu a Mulungu nthaŵi zina atetezedwa ndi atsogoleri ena a ndale poukiridwa ndi Satana, amene awafotokoza mophiphiritsira pa Chivumbulutso 12:15, 16. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza kuti Satana akadzaukira komaliza, palibe gulu la anthu limene lidzateteza anthu amene amakhulupirira Yehova. Kodi zimenezi ziyenera kuchititsa mantha Akristu kapena kuwachititsa kukhala ndi nkhaŵa? Ayi ndithu!

15, 16. (a) Kodi n’chifukwa chiyani zimene Yehova anatsimikizira anthu ake masiku a Yehosafati zikuchititsa Akristu masiku ano kuyembekezera kuti zinthu zidzayenda bwino? (b) Kodi Yehosafati ndi anthuwo anapereka chitsanzo chotani kwa atumiki a Mulungu masiku ano?

15 Mulungu adzakhalira kumbuyo anthu ake monga mmene anachitira ndi mtundu wake panthaŵi ya Mfumu Yehosafati. Timaŵerenga kuti: “Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m’Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhaŵa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. . . . Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhaŵa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.”​—2 Mbiri 20:15-17.

16 Anthu a mu Yuda anawatsimikizira kuti sakanafunikira kumenya nkhondo. Mofananamo, anthu a Mulungu akadzaukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi, sadzatenga zida kuti adziteteze. M’malo mwake, iwo ‘adzaima ndi kupenya chipulumutso cha Yehova.’ Komabe, kuimako sikukutanthauza kuti sadzachita chilichonse, monganso mmene zinalili kuti m’masiku a Yehosafati sikuti anthu a Mulungu anangokhala osachita kanthu ayi. Timaŵerenga kuti: “Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse; ndi okhala m’Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova. . . . Ndipo [Yehosafati] atafunsana ndi anthu, anaika oyimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.” (2 Mbiri 20:18-21) Inde, ngakhale pamene adani anafuna kuwaukira, anthuwo anapitirizabe kutamanda Yehova mwachangu. Zimenezi zikupereka chitsanzo chimene Mboni za Yehova zidzatsatira pamene Gogi adzawaukira.

17, 18. (a) Kodi ndi kulimba mtima kotani kumene Mboni za Yehova zili nako masiku ano pankhani ya kuukira kwa Gogi? (b) Kodi ndi chikumbutso chotani chimene chinaperekedwa kwa Akristu achinyamata posachedwapa?

17 Mboni za Yehova zidzapitiriza kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu mpaka panthaŵi imeneyo ndiponso ngakhale kuukira kwa Gogi kukadzayamba. Zidzapitirizabe kupeza mphamvu ndi chitetezo posonkhana m’mipingo yoposa 94,000 padziko lonse. (Yesaya 26:20) Ndi nthaŵi yabwinotu ino yotamanda Yehova molimba mtima! Inde, kuyembekezera kuti Gogi aukira posachedwa sikuwachititsa kubwerera m’mbuyo chifukwa cha mantha. M’malo mwake, kumawalimbikitsa kuwonjezera nsembe zawo zolemekeza monga momwe angathere.​—Salmo 146:2.

18 Achinyamata ambirimbiri padziko lonse asonyeza bwino kwambiri kulimba mtima kumeneku. Iwo akuchita utumiki wa nthaŵi zonse. Posonyeza kuti kuchita zimenezi ndiko chinthu chabwino kwambiri pa moyo wa munthu, thirakiti lakuti Achinyamata​—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji? linatulutsidwa pa msonkhano wachigawo wa 2002. Akristu achinyamata ndi achikulire omwe akuyamikira kwambiri zikumbutso za panthaŵi yake zimenezo.​—Salmo 119:14, 24, 99, 119, 129, 146.

19, 20. (a) Kodi n’chifukwa chiyani palibe chifukwa choti Akristu achite mantha kapena kuda nkhaŵa? (b) Kodi nkhani yotsatira ichita chiyani?

19 Ngakhale kuti zinthu m’dziko lino sizili bwino, Akristu safunika kuchita mantha kapena kuda nkhaŵa. Akudziŵa kuti Ufumu wa Yehova posachedwapa udzachotsa chiwawa chonse ndipo sichidzakhalaponso. Ndiponso amalimbikitsidwa podziŵa kuti kuuka kwa akufa kudzachititsa anthu ambiri amene anataya miyoyo yawo chifukwa cha chiwawa kukhalanso ndi moyo. Ngakhale kuti zimenezi zidzachititsa ena kukhala ndi mwayi wawo woyamba kuphunzira za Yehova, zidzathandiza ena kupitiriza kudzipereka kwawo pom’tumikira.​—Machitidwe 24:15.

20 Monga Akristu oona, timadziŵa kufunika kosaloŵerera m’zinthu za dzikoli kwa Akristu ndipo ndife otsimikiza mtima kutero. Tikufuna kugwiritsitsa chiyembekezo cha mtengo wapatali chodzatha ‘kuima ndi kupenya chipulumutso cha Yehova.’ Nkhani yotsatira idzalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kutithandiza kudziŵa zochitika masiku ano zimene zikutithandiza kumvetsa pang’ono ndi pang’ono kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Mungaone zitsanzo zina za anthu amene anasiya chiwawa kuti akhale Mboni mu Galamukani! ya August 8, 1991, tsamba 27; ndi Nsanja ya Olonda ya January 1, 1996, tsamba 5; ndi ya August 1, 1998, tsamba 5.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani anthu masiku ano sakuyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino?

• N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zikuyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo?

• Kodi Yehova wachita kale zotani kwa amene amayambitsa chiwawa chonse?

• N’chifukwa chiyani palibe chifukwa choti tichite mantha ndi kuukira kwa Gogi?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kusaloŵerera m’zinthu zadziko kwa Akristu

[Zithunzi patsamba 16]

Mboni zachinyamata zambirimbiri zikuchita utumiki wa nthaŵi zonse mosangalala

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

UN PHOTO 186226/​M. Grafman