‘Solomo Sanavala Monga Limodzi la Ameneŵa’
‘Solomo Sanavala Monga Limodzi la Ameneŵa’
MALUŴA a kuthengo ngati amene mukuwaona patsamba lino, sasoŵa m’mphepete mwa misewu kum’mwera kwa Africa. Dzina la maluŵa ameneŵa ndi cosmos ndipo anachokera ku dera lina la ku America. Maluŵa okongola ameneŵa angatikumbutse zimene Yesu anaphunzitsa. Omvera ake ambiri anali osauka, ndipo anali kudera nkhaŵa kwambiri zinthu zofunika pamoyo wawo, chakudya ndi zovala.
Yesu anafunsa kuti: “Muderanji nkhaŵa ndi chovala? Tapenyetsani maluŵa a kuthengo, makulidwe awo; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa.”—Mateyu 6:28, 29.
Anthu apereka maganizo osiyanasiyana pankhani ya mtundu wa maluŵa a kuthengo amene Yesu anali kunena. Komabe, Yesu anawayerekezeranso ndi maudzu wamba, ponena kuti: “Koma ngati Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi maŵa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono?”—Mateyu 6:30.
Ngakhale kuti maluŵa a cosmos si ochokera ku Israyeli, amatsimikizira mfundo imene Yesu anali kuphunzitsa. Kaya kuwaonera patali kapena pafupi kwambiri, ndi okongola mogometsa ndipo akatswiri a zojambulajambula amawakonda zedi. Ndithudi, Yesu sanakokomeze ponena kuti, “angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa.”
Kodi pankhaniyi tikuphunzirapo chiyani masiku ano? Anthu amene amatumikira Mulungu angatsimikizire kuti adzawathandiza kupeza zinthu zofunika pamoyo wawo ngakhale panthaŵi zamavuto. Yesu anafotokoza kuti: “Tafunafunani Ufumu [wa Mulungu], ndipo izi [monga chakudya ndi zovala zomwe timafunikira] adzakuwonjezerani.” (Luka 12:31) Inde, kufunafuna Ufumu wa Mulungu kumatipindulitsa kwambiri. Koma kodi mumadziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ndi chiyani komanso kuti udzawachitira chiyani anthu? Mboni za Yehova zidzasangalala kukuthandizani kudziŵa mayankho a mafunsoŵa kuchokera m’Baibulo.