Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ndi Mwambo Chabe Kapena N’kupereka Ziphuphu?

Kodi ndi Mwambo Chabe Kapena N’kupereka Ziphuphu?

Kodi ndi Mwambo Chabe Kapena N’kupereka Ziphuphu?

KUMAKOLEJI ena ku Poland, ana a sukulu amasonkha ndalama n’kugulira aphunzitsi awo mphatso, n’cholinga chofuna kukhoza bwino mayeso. N’zosadabwitsa kuti zimenezi zinam’vuta kwambiri mtsikana wachikristu wotchedwa Katarzyna. Iye anadzifunsa kuti: “Kodi ndipereke nawo ndalamazo kapena ndisapereke?” Anzake anamuuza kuti: “Umenewu ndi mwambo wofala. Suluza kanthu kalikonse, koma ungapeze zambiri, ndiye ukukayika chifukwa chiyani?”

“Ndiyenera kuvomereza kuti m’chaka changa choyamba chamaphunziro, ndinapereka nawo ndalamazo,” akutero Katarzyna. “Pambuyo pake m’pamene ndinadzazindikira kuti pochita zimenezi, ndalimbikitsa kupereka ziphuphu, kumene Baibulo limaletsa.” Anakumbukira malemba amene amasonyeza kuti Yehova amadana kwambiri ndi kupereka ziphuphu. (Deuteronomo 10:17; 16:19; 2 Mbiri 19:7) Katarzyna akuti: “Ndinazindikira kuti kugonjera mabwenzi ako n’kosavuta. Ndinaganiza bwino za zimenezi, ndipo chiyambireni pamenepo, sindichita nawonso mwambo umenewu.” Kwa zaka zitatu zapitazi, ngakhale kuti anzake ankamuseka, iye anatha kuwafotokozera ena a iwo kuti iye sasonkha nawo ndalama zokagulira “mphatso” zimenezi chifukwa amakhulupirira zimene zili m’Baibulo.

Ena anamunena Katarzyna kuti ndi wodzikonda komanso wosaganizira ena. “Ena a iwo mpaka pano sindigwirizana nawobe,” iye akutero. “Koma ambiri amandilemekeza chifukwa cha mfundo zanga, ndipo zimenezi zimandisangalatsa.” Katarzyna anadziŵika ngati wa Mboni za Yehova, anthu amene amatsatira mfundo za Baibulo m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.