Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Anthu Ogwiritsa Ntchito Chinenero Chapadera ku Korea

Kuthandiza Anthu Ogwiritsa Ntchito Chinenero Chapadera ku Korea

Kuthandiza Anthu Ogwiritsa Ntchito Chinenero Chapadera ku Korea

ANTHU achidwi kwambiri koma osalongolola anasonkhana pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova m’chilimwe cha 1997. Umenewu unali msonkhano woyamba wa anthu ogontha ndi anthu omva movutikira ku Korea. Anthu amene anabwera anakwana 1,174. Msonkhano wonsewo, kuphatikizapo nkhani, kufunsana, ndi seŵero, zinachitika m’Chinenero cha Manja cha ku Korea ndipo anaonetsa zimenezi pa vidiyo yaikulu imene inkaoneka bwinobwino munthu akakhala paliponse mu Nyumba ya Msonkhanoyo. Pamenepa panali pakaindeinde pa ntchito yakhama imene anthu ongodzipereka ambiri anachita kwa zaka zambiri.

Nthaŵi idzafika m’dziko lapansi la paradaiso pamene “makutu a ogontha adzatsegulidwa.” (Yesaya 35:5) Kuti adzasangalale ndi moyo m’Paradaiso ameneyo, aliyense, kuphatikizapo anthu ogontha, ayenera choyamba kuloŵa m’paradaiso wauzimu, kapena kuti m’moyo wabwino wauzimu wa anthu a Mulungu achimwemwe. Ayenera kudzipatulira ndi kubatizidwa kukhala Mboni za Yehova, zophunzitsidwa ndi iye.​—Mika 4:1-4.

Zinayamba Pang’onopang’ono

Ngakhale kuti ntchito yochepa yolalikira inali kuchitika pakati pa anthu ogontha m’ma 1960, kuyambira m’ma 1970 ndi pamene ena a iwo anayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova ku Seoul, likulu la dziko la Korea. Mbale wachikristu amene ankatha kulemba mwamsanga ankalemba pa bolodi mfundo zazikulu za nkhanizo, kuphatikizapo malemba a Baibulo amene aŵerengedwa.

Mu 1971 mu mzinda wa Taejon, wa Mboni wina amene anali ndi mwana wamwamuna wogontha anayamba kum’phunzitsa mwana wakeyo ndi anzake ogontha uthenga wa Ufumu. Masiku ano, pali anthu achangu angapo amene akuthandiza kwambiri m’gawo la chinenero cha manja amene anachokera m’gulu limenelo.​—Zekariya 4:10.

Achinyamata Adzipereka ndi Mtima Wonse

Pofuna kuthandiza anthu ogontha kuti adziŵe Yehova ndi Yesu kuti akhale pa njira yopita ku moyo, panafunika anthu ena ongodzipereka kuti achite ntchito imeneyi mwakhama. (Yohane 17:3) Kuti achite zimenezi, anthu angapo a Mboni za Yehova aphunzira chinenero cha manja ndipo adalitsidwa chifukwa pali zinthu zosangalatsa zambiri zimene zawachitikira.

Mnyamata wina wa zaka 15 dzina lake Park In-sun anaganiza zophunzira chinenero cha manja. Kuti achite zimenezi, anakaloŵa ntchito ku fakitale kumene anthu ogontha 20 amagwirakonso ntchito. Kwa miyezi isanu ndi itatu iye anagwira ntchito limodzi ndi anthu ogonthaŵa kuti aphunzire chinenero chawo komanso adziŵe mmene amaganizira. Chaka chotsatira, iye anakhala mpainiya wokhazikika, kapena kuti wolengeza Ufumu wa nthaŵi zonse, ndipo ankalalikira kwa kagulu ka anthu ogontha amene ankasangalatsidwa ndi choonadi cha Baibulo. Kaguluko kanakula mwamsanga, ndipo pasanapite nthaŵi yaitali anthu 35 anayamba kubwera ku misonkhano patsiku Lamlungu.​—Salmo 110:3.

Kenako, kwa nthaŵi yoyamba ku Seoul, misonkhano yachikristu yogwiritsa ntchito chinenero cha manja chokha inakhazikitsidwa. Mbale Park In-sun anatumikira monga mpainiya wapadera m’gulu limeneli, ndipo linakula mwamsanga. Panthaŵi imeneyi n’kuti akuchidziŵa bwino kwambiri chinenero cha manja. Miyezi ina ankachititsa maphunziro a Baibulo a panyumba 28 ndi anthu ogontha. Ambiri a ameneŵa anapita patsogolo ndipo anakhala a Mboni za Yehova.

Chifukwa cha ntchito imene anthu odzipereka a khama ameneŵa anagwira, mpingo wa chinenero cha manja woyamba unakhazikitsidwa ku Seoul mu October 1976, ndipo unali ndi ofalitsa 40 ndi apainiya okhazikika aŵiri. Zimenezi zinachititsa kuti ntchito imeneyi ikule m’mizinda ina ya ku Korea. Anthu ogontha ambiri anali kulakalaka uthenga wabwino ndipo anali kudikira kuti munthu wina adzawayendere.

Kugwira Ntchito Pakati pa Anthu Ogontha

Mwina mungadabwe kuti kodi anthu ogonthawo anawapeza bwanji. Ambiri a iwo anapezeka chifukwa chouzana okhaokha. Komanso a Mboni anapita kwa anthu ogulitsa mpunga m’masitolo, ndipo iwo anapereka mayina ndi maadiresi a anthu ogontha. Anthu ena ogwira ntchito za boma anathandizanso popereka mayina ndi maadiresi a anthu ogonthawa. Ntchito yolalikira m’gawo la anthu ogontha inayenda bwino kwambiri moti, patapita nthaŵi, mipingo inayi ya chinenero cha manja inakhazikitsidwa. Akristu ambiri achinyamata analimbikitsidwa kuphunzira chinenero cha manja.

Apainiya apadera amene anaphunzira chinenero cha manja anatumizidwa ndi ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kuti akatumikire ku mipingo imeneyi. Posachedwapa, anthu omaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki atumizidwa ku mipingo imeneyi ndipo alimbikitsa mipingoyi mwauzimu.

Pali zovuta zimene zimafunika kuzigonjetsa. Kulalikira m’gawo limeneli kumafuna khama kuti munthu amvetse chikhalidwe cha anthu ogontha. Anthu ogontha akafuna kunena zimene akuganiza, sapita m’mbali, ndipo akafuna kuchita kanthu sachita mokayikira. Zimenezi nthaŵi zina zimadabwitsa anthu, ndipo zingayambitse kusemphana maganizo. Komanso, Mboni zikamachititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu ogontha, zimafunika kuwathandiza kuti adziŵe bwino chinenero chawo cha manja komanso kuwalimbikitsa kuti paokha aziŵerenga ndi kuphunzira mwakhama.

M’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku, anthu ogontha amakumana ndi mavuto amene anthu ambiri sawadziŵa. Kuti amvane ndi anthu ogwira ntchito za boma, kapena zachipatala, komanso kuti achite ntchito zina ndi zina zosavuta za malonda, nthaŵi zambiri zimawavuta. Chifukwa chakuti Mboni zochokera m’mipingo yapafupi zimawathandiza mwachikondi, anthu ogonthaŵa apeza ubale weniweni mu mpingo wachikristu.​—Yohane 13:34, 35.

Phindu la Kulalikira Mwamwayi

Mu mzinda waukulu wa Pusan, umene uli ku gombe la nyanja kum’mwera kwa dziko la Korea, wa Mboni wina anakumana ndi anthu ogontha aŵiri amene analemba pa kapepala kuti: “Timakonda Paradaiso. Tikufuna kudziŵa malemba amene amafotokoza za moyo wosatha.” Mbaleyu analemba adiresi yawo ndipo anawauza kuti adzawayendera. Atapita, anakapeza chipinda chodzaza ndi anthu ogontha akudikira kumva uthenga wa Ufumu. Zimenezi zinam’limbikitsa kuyamba kuphunzira chinenero cha manja. Pasanapite nthaŵi yaitali, ku Pusan anakhazikitsako mpingo wa chinenero cha manja.

Mbale wina wa mu mpingo umenewu anaona anthu aŵiri ogontha akulankhulana m’chinenero cha manja ndipo anapita pomwepo. Atamva zoti anthuŵa anali kuchokera ku msonkhano wachipembedzo, anawaitanira ku Nyumba ya Ufumu 2 koloko masana tsiku lomwelo. Anthuwo anabweradi, ndipo phunziro la Baibulo linayambika. Patangopita nthaŵi yochepa, anthu aŵiriŵa anapita ku msonkhano wachigawo limodzi ndi anzawo ogontha 20. Pa gulu limenelo, anthu angapo adzipatulira kwa Yehova. Aŵiri tsopano ndi akulu ndipo mmodzi ndi mtumiki wotumikira m’mipingo ya chinenero cha manja.

Khama Lipindula

Chifukwa chakuti anthu ena ogontha amakhala kutali ndi mpingo wina uliwonse wa chinenero cha manja, pamafunika khama komanso kudzipereka pofuna kupatsa anthu ameneŵa chakudya chauzimu chochokera m’Baibulo mokhazikika. Mwachitsanzo, mwamuna wina wa zaka 31 anali msodzi pa chilumba china. Anamva za uthenga wa m’Baibulo kwa wamng’ono wake, amene anali atalankhulana ndi Mboni za Yehova. Chifukwa chofuna kuthetsa njala yake yauzimu, msodzi wogonthayo anayenda ulendo wa makilomita 16 pa bwato kupita ku Tongyoung City, ku gombe la kum’mwera kwa Korea. Anachita zimenezi kuti akakumane ndi mpainiya wapadera wa mu mpingo wa chinenero cha manja wa ku Masan City. Lolemba lililonse, mpainiya wapadera ameneyu ankayenda ulendo wa makilomita 65 kuti akachititse phunziro la Baibulo ndi msodzi wogonthayo.

Kuti akasonkhane nawo tsiku Lamlungu ku Masan City, wophunzira Baibulo wogonthayo anali kuyenda ulendo wa makilomita 16 pa bwato, kenaka n’kukwera basi n’kuyenda makilomita 65. Khama lake linapindula. Patangotha miyezi yochepa yokha, anadziŵa bwino chinenero cha manja kuposa kale, anaphunzira zilembo zina za mu alifabeti ya chinenero cha ku Korea, ndipo, koposa zonse, anaphunzira njira yokhayo imene angakhalire bwenzi la Yehova. Atazindikira kufunika kwa misonkhano komanso kulalikira mokhazikika, anasamuka n’kukakhala kumene kunali mpingo wa chinenero cha manjawo. Kodi zimenezi zinali zosavuta kuchita? Ayi. Kuti achite zimenezi, anafunika kusiya ntchito yake yausodzi imene inkam’bweretsera ndalama zofika madola 3,800 a ku United States pa mwezi, koma anapindula chifukwa cha khama lakelo. Atapita patsogolo m’choonadi, anabatizidwa ndipo panopa akutumikira Yehova mosangalala limodzi ndi banja lake.

Ntchito Yomasulira Mawu Anthu Ogontha

Nthaŵi zambiri anthu amamva uthenga wabwino wa Ufumu ukulankhulidwa pakamwa. Komabe, pofuna kuti uthenga wochokera m’Mawu a Mulungu ukhale wolondola, pamafunika kuti ziphunzitso za m’Baibulo zikhale m’njira inayake yokhalitsa. N’chifukwa chake m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, mabuku ndi makalata analembedwa ndi akulu odziŵa bwino zinthu. (Machitidwe 15:22-31; Aefeso 3:4; Akolose 1:2; 4:16) Masiku ano, chakudya chauzimu chochuluka chaperekedwa pogwiritsa ntchito mabuku ndi zofalitsa zina zachikristu. Zimenezi azimasulira m’zinenero zambiri, kuphatikizapo zinenero za manja zosiyanasiyana. Kuti amasulire m’Chinenero cha Manja cha ku Korea, ku ofesi ya nthambi kuli dipatimenti yomasulira mawu m’chinenero cha manja. Dipatimenti yokonza mavidiyo imatulutsa mavidiyo a chinenero cha manja. Zimenezi zimapereka chakudya chauzimu kwa ofalitsa uthenga wabwino ogontha komanso anthu achidwi m’mipingo ya chinenero cha manja ya m’dziko lonse la Korea.

Ngakhale kuti anthu ambiri aphunzira chinenero cha manja ndipo athandiza nawo potulutsa mavidiyo, nthaŵi zambiri amene amamasulira bwino kwambiri ndi anthu amene makolo awo ali ogontha. Anthu ameneŵa aphunzira chinenero cha manja kuyambira ali makanda. Anthu otereŵa amagwiritsa ntchito zizindikiro za manja zolondola, komanso amathandiza kuti tanthauzo ndi kufunika kwa uthengawo kuonekere chifukwa cha mmene amagwiritsira ntchito manja ndi nkhope zawo. Zimenezi zimathandiza kuti uthengawo um’fike munthu pa mtima.

Monga tanenera muja, misonkhano ikuluikulu ya chinenero cha manja ikuchitika mokhazikika tsopano ku Korea. Kuti zimenezi zitheke, pamafunika kugwira ntchito mwakhama komanso ndalama zambiri. Komabe, anthu amene amabwera ku misonkhano imeneyi amayamikira kwambiri. Misonkhanoyi ikatha, ambiri amakhalabe pompo, ndipo amafuna kupitirizabe kucheza mosangalala ndi kukambirana za chakudya chauzimu chabwino kwambiri chimene alandira. Zoonadi, kuthandiza anthu m’gulu lapadera limeneli kuli ndi mavuto ake, koma n’kwaphindu chifukwa kumabweretsa madalitso auzimu.

[Chithunzi patsamba 10]

Mavidiyo a chinenero cha manja opangidwa ku Korea: “Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?,” “Kuyamikira Choloŵa Chathu Chauzimu,” Zitsanzo Zotichenjeza M’nthaŵi Yathu,” ndi “Lemekezani Ulamuliro wa Yehova”

[Zithunzi patsamba 10]

Zithunzi zitatuzi. Pamunsipa: Akukonza vidiyo ya chinenero cha manja ku nthambi ya ku Korea. Kulamanjaku pamwamba: Akupanga zizindikiro za manja za mawu a ziphunzitso za Mboni; gulu limene limamasulira mawu m’chinenero cha manja. Kulamanjaku pamunsi: Kum’kumbutsa munthu amene akugwiritsa ntchito chinenero cha manja nthaŵi yokonza vidiyo