Zimene Mbalame Zingatiphunzitse
Zimene Mbalame Zingatiphunzitse
“YANG’ANIRANI mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?” (Mateyu 6:26) Yesu Kristu ananena mawu ameneŵa mu ulaliki wake wotchuka pamene anali m’mphepete mwa phiri pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Anthu amene anamva mawu ameneŵa si otsatira ake okha ayi. Anthu ambiri amene akanatha kudzakhala ophunzira ake ochokera m’madera onse a dzikolo anali pamenepo. Ambiri a iwo anali anthu osauka amene anabweretsa anthu odwala kuti Yesu awachiritse.—Mateyu 4:23–5:2; Luka 6:17-20.
Atatha kuchiritsa odwala onsewo, Yesu anayamba kuphunzitsa zinthu zofunika kwambiri zauzimu. Chimodzi mwa zinthu zimene anaphunzitsa ndi mawu amene atchulidwa pamwambawo.
Mbalame zakumwamba zakhalapo kwa nthaŵi yaitali. Zina mwa izo zimadya tizilombo, pamene zina zimadya zipatso ndi njere. Ngati Mulungu amaonetsetsa kuti mbalame zizikhala ndi zakudya zochuluka choncho, ndithudi angathe kuthandiza atumiki ake kupeza chakudya cha tsiku lililonse. Angachite zimenezi mwa kuwathandiza kupeza ntchito kuti azilandira ndalama zogulira chakudya. Kapena angawathandize kuti azilima okha chakudya chawo. Pa nthaŵi ya masoka, Mulungu angapangitse anthu okhala nawo pafupi ndi mabwenzi kugaŵana ndi anthu osoŵa chakudya chilichonse chimene angakhale nacho.
Palinso zinthu zina zambiri zimene tingaphunzire mwa kuyang’anitsitsa moyo wa mbalame. Mulungu polenga mbalame anazipatsa nzeru zodabwitsa zopangira zisa zolereramo ana awo. Onani mitundu iŵiri ya zisa. Chithunzi chimene chili kumanzereku ndi cha chisa cha mbalame imene ili m’gulu la namzeze wa ku Africa kuno. Chisacho chimamangidwa pamwala kapena pakhoma la nyumba. Denga la chisa choterocho limakhala mwala wina umene uli pamwamba pake, kapena, monga tikuonera m’chithunzichi, malata a nyumba. Pansi pa chisacho pamakhala timibulu ting’onoting’ono ta dothi tomatirirana timene timaoneka ngati kapu. Mbalame zonse ziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zimagwira ntchito molimbika kufunafuna timibulu ta matope ndipo zingatenge nthaŵi yopitirira mwezi umodzi zisanamalize kumanga chisacho. Kenaka, zimaika udzu ndi nthenga m’kati mwa chisamo. Zonse ziŵiri zimathandizana kudyetsera ana. Chimene chikuoneka pansipa ndi chisa cha tchete. Mbalame yojijirika imeneyi ya kuno ku Africa imamanga chisa chake pogwiritsa ntchito udzu kapena masamba a zomera zina. Imatha kumaliza kumanga chisa tsiku limodzi lokha, ndipo imatha kumanga zisa zopitirira 30 m’nyengo imodzi yokha!
Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati Mulungu amapatsa mbalame luso loterolo komanso zida zambiri choncho zomangira zisa, ndithudi angathandize atumiki ake kupeza pokhala. Komabe, Yesu anasonyeza kuti kenakake kakufunika ngati tikufuna kuti Mulungu atithandize kupeza zinthu zofunikira. Yesu analonjeza kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Koma mwina mungadabwe kuti, ‘Kodi kufunafuna Ufumu choyamba kumatanthauza chiyani?’ A Mboni za Yehova, amene amafalitsa magazini ino, adzakhala okondwa kuyankha funso limenelo.