Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi Chapamwamba Kwambiri

Chikondi Chapamwamba Kwambiri

Chikondi Chapamwamba Kwambiri

NTHAŴI zambiri m’Malemba Achigiriki Achikristu, kapena kuti Chipangano Chatsopano, pamene timapeza liwu loti “chikondi” alimasulira kuchokera ku liwu lachigiriki lakuti a·gaʹpe.

Pofotokoza tanthauzo la liwu limenelo, buku la Insight on the Scriptures * limati: “[Chikondi cha a·gaʹpe] sindicho kutengeka mtima, kumene munthu amakhala nako chifukwa cha kugwirizana kwake ndi munthu winayo, monga mmene anthu amaganizira nthaŵi zambiri, koma ndi chikondi cha makhalidwe abwino chimene munthu amakhala nacho pochivomereza monga mfundo yofunika, kuona kuti ndi udindo wake kutero, ndiponso kuti ndi khalidwe lofunika, kufunira zabwino munthu wina malinga ngati zili zoyenera. (Chikondi cha) a·gaʹpe chimachititsa munthu kusonyeza chikondi ngakhale pamene pali udani. Sichimalola udani kupangitsa munthu kulephera kutsatira mfundo zabwino zachikhalidwe mwa kubwezera choipa.”

Chikondi cha a·gaʹpe chingaphatikizeponso malingaliro amphamvu. Mtumwi Petro analangiza kuti: ‘Mukhale nacho chikondano [a·gaʹpe] chenicheni mwa inu nokha.’ (1 Petro 4:8) N’chifukwa chake, tinganene kuti chikondi cha a·gaʹpe chimakhudza mtima ndiponso maganizo. Bwanji osapenda malemba amene amasonyeza mphamvu ndi ukulu wa chikondi chapamwamba chimenechi? Malemba otsatirawa angakhale othandiza: Mateyu 5:43-47; Yohane 15:12, 13; Aroma 13:8-10; Aefeso 5:2, 25, 28; 1 Yohane 3:15-18; 4:16-21.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.