Kodi N’chiyani Chinaichitikira?
Kodi N’chiyani Chinaichitikira?
NOFI ndi No ndi mayina a m’Baibulo a mizinda ya Memphis ndi Thebes imene nthaŵi ina yake inali malikulu otchuka kwambiri a Igupto. Mzinda wa Nofi (Memphis) unali pamtundu wa makilomita 23 kumwera kwa Cairo, kumadzulo kwa mtsinje wa Nile. Koma nthaŵi ina, Memphis sanalinso likulu la Igupto. Pofika kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1400 B.C.E., Igupto anali ndi likulu latsopano, lotchedwa No (Thebes), limene linali pamtundu wa makilomita pafupifupi 500 kumwera kwa Memphis. Mmodzi mwa akachisi ambiri amene anawonongedwa ku Thebes anali kachisi wa Kanaki, amene anthu amati inali nyumba yaikulu kwambiri ya mizati imene sinamangidweponso. Thebes ndi kachisi wake wa Kanaki anazipatulira pa kulambira Amoni, mulungu wamkulu wa Aigupto.
Kodi Baibulo linalosera zotani zokhudza Memphis ndi Thebes? Ilo linalengeza kuti Farao wa ku Igupto ndi milungu yake idzalangidwa, makamaka mulungu wamkulu, “Amoni wa No.” (Yeremiya 46:25, 26) Namtindi wa anthu olambira amene anali kupita kumeneko ‘adzalikhidwa.’ (Ezekieli 30:14, 15) Ndipo zinachitikadi zimenezo. Zimene zatsala pa kulambira kwa Amoni ndi zotsalira za kachisi amene anawonongedwa. Tauni ya makono ya Luxor ili pa mbali ina ya pomwe kale panali mzinda wa Thebes, ndipo palinso midzi ina ing’onoing’ono pabwinjalo.
Nawo mzinda wa Memphis, wangotsala ndi manda okha. Katswiri wa maphunziro a Baibulo, Louis Golding, anati: “Kwa zaka zambiri Aluya amene anagonjetsa Aigupto anagwiritsa ntchito zinthu zambiri za pa bwinja la Memphis kukhala miyala yomangira nyumba ya ku likulu lawo [la Cairo] kutsidya lina la mtsinjewo. Dothi la mumtsinje wa Nile ndiponso zimene omanga achiluya anachita zinapangitsa kuti mtunda wa makilomita ambiri m’kati mwa dera la mzinda wakalewo pasaoneke mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa dothi lakuda la pamaloŵa.” Inde, monga mmene Baibulo linaloserera, Memphis anakhala “bwinja . . . mulibenso wokhalamo.”—Yeremiya 46:19.
Zimenezi ndi zitsanzo ziŵiri chabe mwa zitsanzo zambiri zimene zimasonyeza kuti maulosi a Baibulo ndi olondola kwambiri. Kuwonongedwa kwa Thebes ndi Memphis kumatipatsa zifukwa zokwanira zokhulupirira maulosi a Baibulo amene sanakwaniritsidwe.—Salmo 37:10, 11, 29; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3-5.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Photograph taken by courtesy of the British Museum