Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira Ena Kumachepetsa Mavuto

Kutumikira Ena Kumachepetsa Mavuto

Mbiri ya Moyo Wanga

Kutumikira Ena Kumachepetsa Mavuto

YOSIMBIDWA NDI JULIÁN ARIAS

Mu 1988, ndili ndi zaka 40, ntchito imene ndinali kugwira inaoneka ngati sidzatha. Ndinali mkulu wa kampani ina m’chigawo china cha dziko la Spain. Kampaniyi inali ndi nthambi zake m’mayiko ambiri. Chifukwa cha ntchito imene ndinali kugwira, anandipatsa galimoto yapamwamba, malipiro abwino kwambiri, ndi ofesi yapamwamba m’kati mwa mzinda wa Madrid, ku Spain. Eni a kampaniyo anasonyezanso kuti ankafuna kudzandisankha kukhala mkulu wa kampaniyi m’dziko lonselo. Sindinazindikire kuti moyo wanga unatsala pang’ono kusintha kwambiri.

TSIKU lina m’chaka chimenecho, dokotala wanga anandiuza kuti ndinali ndi matenda osachiritsika okhudza ubongo otchedwa multiple sclerosis. Ndinakhumudwa kwambiri. Kenako, nditaŵerenga zimene matenda ameneŵa angachite kwa munthu, ndinachita mantha. * Zinaoneka kuti ndikhala ndi vuto losatha kwa moyo wanga wonse. Kodi ndikanasamalira bwanji mkazi wanga, Milagros, ndi mwana wanga wa zaka zitatu, Ismael? Kodi tikanachita bwanji ndi vuto limeneli? Pamene ndinali kuganizirabe mayankho a mafunso ameneŵa, panabwera vuto linanso lopweteka kwambiri.

Patatha pafupifupi mwezi umodzi dokotala wanga atandidziŵitsa za matendawa, abwana anga anandiitanira mu ofesi yawo n’kundidziŵitsa kuti kampaniyo inkafuna anthu amene anali ndi “chithunzi chabwino.” Ndipo munthu amene anali ndi matenda osachiritsika, ngakhale anali atangoyamba kumene, sakanakhala ndi chithunzi choterocho. Motero, nthaŵi yomweyo abwana angawo anandichotsa ntchito. Mosayembekezeka, ntchito yanga inatha!

Ndinkayesetsa kusonyeza kulimba mtima ndikakhala ndi banja langa, koma ndinkafuna kukhala pandekha, kuti ndiganizire mavuto anga atsopanowa, ndiponso kuganizira tsogolo langa. Ndinayesetsa kulimbana ndi kuvutika maganizo kumene kunali kukulirakulira. Chimene chinandipweteka kwambiri n’chakuti mosayembekezeka ndinakhala wopanda phindu ku kampani imene ndinali kugwirako ntchito.

Kupeza Mphamvu M’kufooka

Mwamwayi, m’nthaŵi yovuta kwambiri imeneyi, panali magwero osiyanasiyana amene ndinali kupezako mphamvu. Zaka 20 zinthu zimenezi zisanachitike, ndinakhala wa Mboni za Yehova. Motero, ndinapemphera moona mtima kwa Yehova za maganizo anga ndi kusatsimikizira kwanga za tsogolo. Mkazi wanga yemwenso ndi wa Mboni za Yehova, anandilimbikitsa kwambiri, pamodzinso ndi anzanga ena apamtima amene kukoma mtima ndi chifundo chawo zinandithandiza kwambiri.​—Miyambo 17:17.

Kuganizira kuti ndili ndi udindo kwa anthu ena kunathandizanso. Ndinafuna kulera bwino mwana wanga, kumuphunzitsa, kucheza naye, ndi kumuphunzitsa ntchito yolalikira. Motero, sindinataye mtima. Ndiponso, ndinali mkulu mu mpingo wina wa Mboni za Yehova, ndipo abale ndi alongo anga achikristu ankafuna thandizo langa. Ngati ndikanalolera kuti mavuto angawa afooketse chikhulupiriro changa, kodi ndikanakhala chitsanzo chotani kwa ena?

Mosapeweka, moyo wanga unasintha pankhani ya thanzi ndiponso pankhani ya zachuma. M’njira zina kusinthaku kunali koipa pamene m’njira zina kunali kwabwino. Ndinamumvapo dokotala akunena kuti: “Nthenda siwononga munthu, koma imangomusintha.” Ndipo ndaona kuti kusintha sikumangokhala koipa kokhakokha.

Choyamba, “munga m’thupi” langa unandithandiza kumvetsa bwino matenda a anthu ena ndi kuwamvera chisoni. (2 Akorinto 12:7) Ndinamvetsa bwino kwambiri kuposa kale lonse mawu amene ali pa Miyambo 3:5 akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” Koposa zonse, mavuto angawa anandithandiza kudziŵa zinthu zofunika kwambiri pamoyo ndiponso zimene zimapatsa chisangalalo chenicheni komanso kudziona kuti ndine wofunika. Panali zambiri zimene ndikanathabe kuchita m’gulu la Yehova. Ndinamvetsa tanthauzo lenileni la mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Moyo Watsopano

Nditangopezeka ndi matenda angawo, ndinaitanidwa ku maphunziro a nthaŵi yochepa ku Madrid kumene Akristu odzipereka anaphunzitsidwa kuti azikhazikitsa mgwirizano pakati pa madokotala ndi odwala awo omwe ndi Mboni. Kenako, anthu odziperekawo analinganizidwa n’kukhala m’Makomiti Olankhulana ndi Chipatala. Kwa ine, maphunziro ameneŵa anachitika pa nthaŵi yake. Ndinapeza ntchito yabwino imene inali kudzandibweretsera chimwemwe chachikulu kuposa ntchito iliyonse yolipidwa.

Kumaphunziroko tinaphunzira kuti Makomiti Olankhulana ndi Chipatala amene anangokhazikitsidwa kumenewo anali oti aziyendera zipatala, kulankhula ndi madokotala, ndi kulankhula kwa anthu ogwira ntchito zachipatala, ndipo zonsezi cholinga chake chinali chakuti pakhale mgwirizano ndiponso kuti pasamakhale mikangano. Makomitiwo amathandiza Mboni zinzawo kupeza madokotala omwe amalola kupanga maopaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Inde, popeza sindinali dokotala, panali zambiri zoti ndiphunzire zokhudza mawu amene amagwiritsa ntchito pa zamankhwala, malamulo a zamankhwala, ndi kayendetsedwe ka zipatala. Komabe, maphunzirowa anandisintha kwambiri, anandikonzekeretsa ntchito yatsopano imene inandisangalatsa.

Kuyendera Zipatala Kumandisangalatsa

Ngakhale kuti matenda angawo anali kundipundula mosalekeza ndiponso pang’onopang’ono, ntchito yanga monga wa mu Komiti Yolankhulana ndi Chipatala inakula. Ndinalandira penshoni chifukwa cholumala, motero ndinali ndi nthaŵi yambiri yochezera zipatala. Ngakhale kuti nthaŵi zina pankakhala zokhumudwitsa, kuyendera zipatala kumeneku kunakhala kosavuta ndiponso kopindulitsa kwambiri kuposa mmene ndinkaganizira. Ngakhale kuti tsopano nthaŵi zonse ndimakhala pa njinga ya olumala, zimenezi sizindidodometsa kwambiri. Ndimapita limodzi ndi wa m’komiti mnzanga nthaŵi zonse. Ndiponso, madokotala anazoloŵera kulankhula ndi anthu amene ali pa njinga za olumala, ndipo nthaŵi zina amaoneka kuti amamvetsera mwaulemu kwambiri akamaona khama langa powayendera.

M’zaka khumi zimene zapitazi, ndayendera madokotala ambirimbiri. Ena anali okondwa kutithandiza ngakhale poyamba penipeni. Dr. Juan Duarte, dokotala wa opaleshoni ya mtima ku Madrid amene amakonda kulemekeza chikumbumtima cha wodwala, anathandiza mwamsanga. Kuyambira pamenepo, iye wachita maopaleshoni oposa 200 kwa odwala omwe ndi Mboni a m’madera ambiri a ku Spain popanda kugwiritsa ntchito magazi. M’zaka zimenezi madokotala ambiri ayamba kuchita opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Kuwayendera kwathu nthaŵi zonse kwathandizira pa mbali imeneyi, koma ntchitoyi yayenda bwinonso chifukwa cha kupita patsogolo kwa zamankhwala ndiponso zotsatira zabwino zimene zakhalapo chifukwa cha opaleshoni yosagwiritsa ntchito magazi. Ndipo tikukhulupirira kuti Yehova wadalitsa khama lathu.

Ndalimbikitsidwa kwambiri makamaka ndi mmene anachitira madokotala ena a opaleshoni ya mtima ya ana. Kwa zaka ziŵiri tinayendera gulu lina la madokotala aŵiri a opaleshoni ndi akatswiri awo ogonetsa tulo. Tinawapatsa mabuku a zamankhwala ofotokoza zimene madokotala ena akuchita pa mbali imeneyi. Khama lathu linapindula mu 1999 pa Msonkhano wa Zamankhwala wa Opaleshoni ya Mtima ya Ana. Madokotala a opaleshoni aŵiriwo, amene anatsogoleredwa bwino kwambiri ndi dokotala wa opaleshoni wogwirizanika wa ku England, anachita opaleshoni yovuta kwambiri kwa mwana wa Mboni amene kachiwalo kake kamene kamateteza magazi kubwerera ku mtima kanafunika kukakonza. * Ndinasangalala pamodzi ndi makolo a mwanayo pamene mmodzi mwa madokotala a opaleshoniwo anatuluka m’chipinda chochitira opaleshoni kudzatiuza kuti opaleshoniyo yayenda bwino ndipo chikumbumtima cha banjalo chalemekezedwa. Tsopano madokotala aŵiri ameneŵa nthaŵi zonse amalandira odwala omwe ndi Mboni a m’madera onse a dziko la Spain.

Chimene chimandisangalatsa kwambiri pa zochitika zimenezi ndicho kuzindikira kuti ndingathandize abale anga achikristu. Nthaŵi zambiri, akamafuna a m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala, imakhala kuti ndi nthaŵi yovuta kwambiri pa moyo wawo. Amakhala kuti akufunika kuchitidwa opaleshoni, ndipo madokotala a chipatala cha m’dera lawo sakufuna kapena sangathe kuwathandiza popanda kuwaika magazi. Koma abale akazindikira kuti pali madokotala a opaleshoni ogwirizanika pa mbali iliyonse ya zamankhwala mu mzinda wa Madrid, mitima yawo imakhala pansi. Ndinaona mmene nkhope ya mbale wina inasinthira kuchoka pa nkhaŵa n’kufika pokhazika mtima pansi, chifukwa choti ife tinali naye limodzi m’chipatala.

Oweruza ndi Malamulo a Zamankhwala

M’zaka zaposachedwapa, a m’Makomiti Olankhulana ndi Chipatala ayenderanso oweruza milandu. Powayendera timawapatsa buku lakuti Family Care and Medical Management for Jehovah’s Witnesses limene linakonzedwa makamaka kuti liwadziŵitse oweruza maganizo athu pankhani yogwiritsa ntchito magazi ndi kuti pali njira zina zamankhwala zosagwiritsa ntchito magazi. Kuwayendera kumeneku kunali kofunika kwambiri chifukwa poyamba sizinali zachilendo ku Spain kuti oweruza apatse mphamvu madokotala zoika magazi ngakhale kuti wodwalayo sanafune.

Maofesi a oweruza ndi ochititsa chidwi kwambiri, ndipo pa ulendo wanga woyamba, ndinadziona ngati wopanda pake pamene ndinali kuyenda m’kanjira pa njinga yanga ya olumala. Zinthu zikatinso ziipe, ndinachita ngozi pang’ono, ndinagwa pa njingayo n’kugwera maondo. Oweruza ndi maloya angapo amene anaona kuvutika kwanga anabwera n’kundithandiza mwachifundo, koma ndinachita manyazi kwambiri.

Ngakhale kuti oweruza anali kukayikira zifukwa zathu zowayendera, ambiri anatithandiza mwachifundo. Woweruza woyamba amene ndinamuyendera anali akuganizira za mmene timaonera nkhani imeneyi, ndipo anati angakonde kulankhula nafe mokwanira ndithu. Paulendo wathu wachiŵiri, anandiyendetsa pa njinga yangayo kuloŵa muofesi yake ndipo anamvetsera mwatcheru. Zotsatira zabwino za maulendo oyamba ameneŵa zinandilimbikitsa pamodzinso ndi anzanga kuti tithetse mantha amene tinali nawo, ndipo posakhalitsa tinaona zotsatira zina zabwino.

M’chaka chomwecho, tinapereka buku lakuti Family Care kwa woweruza wina amene anatilandira bwino ndipo anatilonjeza kuti adzaŵerenga zimene zili m’bukulo. Ndinam’patsa nambala yanga ya telefoni kuti mwina angadzafune kulankhula nafe patachitika zadzidzidzi. Patapita milungu iŵiri, iye anaimba kundiuza kuti dokotala wa opaleshoni wa m’deralo anamupempha kuti am’patse mphamvu zoti aike magazi wa Mboni yemwe anafunikira kuchitidwa opaleshoni. Woweruzayo anatiuza kuti anafuna kuti timuthandize kupeza njira yothetsera vutolo imene ikanalemekeza zofuna za Mboniyo zoti isaikidwe magazi. Sitinavutike kwambiri kupeza chipatala china, kumene madokotala anachita bwinobwino opaleshoniyo popanda kugwiritsa ntchito magazi. Woweruzayo anasangalala atamva zotsatira za opaleshoniyo ndipo anatitsimikizira kuti adzafuna njira zothetsera vutoli zofanana ndi zimenezi m’tsogolo.

Poyendera zipatala, nthaŵi zambiri nkhani ya malamulo a zamankhwala inkatuluka, popeza tinkafuna kuti madokotala aziganizira ufulu ndi chikumbumtima cha wodwala. Chipatala china chimene chinali kutithandiza ku Madrid chinandipempha kutenga nawo mbali pa maphunziro amene anali kuphunzitsa malamulo a zamankhwala. Maphunziro ameneŵa anandithandiza kufotokoza maganizo athu ozikidwa m’Baibulo kwa akatswiri a malamulo a zamankhwala. Anandithandizanso kumvetsa zosankha zovuta kwambiri zimene madokotala amafunika kupanga.

Mmodzi mwa aphunzitsi a maphunziro ameneŵa, Pulofesa Diego Gracia, amakonza nthaŵi zonse maphuziro apamwamba kwambiri a malamulo a zamankhwala kwa madokotala a ku Spain ndipo watithandiza kwambiri pa ufulu wathu wovomereza kulandira chithandizo munthu utadziŵa zonse zokhudza kuikidwa magazi. * Kulankhula naye kwathu nthaŵi zonse kwachititsa kuti tiitane oimira ena a nthambi ya Mboni za Yehova ku Spain kuti adzafotokoze maganizo athu kwa ophunzira a Pulofesa Gracia, omwe ena mwa iwo amatengedwa kuti ndi madokotala abwino kwambiri m’dzikoli.

Kulimbana ndi Matenda Anga

Komabe sikuti ntchito yosangalatsa imeneyi yothandiza okhulupirira anzanga yathetsa mavuto anga onse. Nthenda yanga ikumakulirakulirabe. Komabe mwamwayi, ndimaganiza bwinobwino. Mothandizidwa ndi mkazi wanga ndi mwana wanga, omwe sanyinyirika, ndikutha kukwaniritsabe maudindo anga. Popanda thandizo lawo, zimenezi sizikanatheka. Sindingathe kumanga batani la buluku langa kapena kuvala jasi. Ndimasangalala kwambiri kulalikira Loŵeruka lililonse pamodzi ndi mwana wanga, Ismael, yemwe amandiyendetsa pa njinga yangayo kuti ndilankhule ndi mwininyumba aliyense. Ndiponso ndikutha kusamalira udindo wanga monga mkulu mumpingo.

Panali nthaŵi zina zokhumudwitsa kwambiri m’zaka 12 zimene zapitazi. Nthaŵi zina, kuona mmene kulumala kwanga kumakhudzira banja langa zimandipweteka kwambiri kuposa mmene matenda enieniwo amandipwetekera. Ndimadziŵa kuti amavutika, ngakhale kuti sanena zimenezo. Osati kale kwambiri, apongozi anga ndi bambo anga anamwalira m’chaka chimodzi chokha. M’chaka chomwecho, kunapezeka kuti sindingathe kuyenda popanda njinga ya olumala. Bambo anga, amene anali kukhala m’nyumba yathu, anamwalira ndi matenda ena osachiritsika. Milagros, amene anali kuwasamalira, anakhala ngati akuona zimene zidzandichitikire ine m’tsogolo.

Komabe, nkhani yabwino ndi yakuti banja lathu n’logwirizana pamene tikukumana ndi mavutowa pamodzi. M’malo mokhala pa mpando wa mkulu wa pakampani tsopano ndimakhala pa njinga ya olumala, koma moyo wanga uli bwinopo panopa chifukwa ndadzipereka kwambiri kutumikira ena. Kupatsa kungachepetse mavuto, ndipo Yehova amasunga lonjezo lake loti adzatilimbikitsa pamene tikufunikira kulimbikitsidwa. Mofanana ndi Paulo, ndinganene zoona kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Nthenda ya multiple sclerosis imasokoneza ubongo ndi fupa la msana. Nthaŵi zambiri, matendawa pang’onopang’ono amayambitsa chizungulire, amawononga miyendo ndi mikono, ndiponso nthaŵi zina amamuchititsa munthu kuvutikira kuona, kulankhula, kapena kumvetsa zinthu.

^ ndime 19 Opaleshoni imeneyi amaitcha opaleshoni ya Ross.

^ ndime 27 Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1997, masamba 19-20.

[Bokosi patsamba 24]

Zimene Mkazi Wake Wanena

Kwa mkazi, kukhala ndi mwamuna amene akudwala matenda a multiple sclerosis n’kovutitsa maganizo, mtima, ndiponso thanzi. Ndimafunika kusonyeza nzeru pa zimene ndimakonza kuti ndichite ndiponso kufunitsitsa kusadera nkhaŵa mosayenera za m’tsogolo. (Mateyu 6:34) Komabe, mavuto angasonyeze makhalidwe abwino kwambiri a munthu. Ukwati wathu ndi wolimba kuposa kale, ndipo ubwenzi wanga ndi Yehova walimbanso. Mbiri za moyo wa anthu ena omwe analinso m’mavuto ofanana ndi ameneŵa zandilimbikitsa kwambiri. Ndimasangalala monga mmene akuchitira Julián chifukwa cha kutumikira kwake abale komwe n’kwamtengo wapatali, ndipo ndaona kuti Yehova satisiya, ngakhale kuti tsiku lililonse lingabweretse vuto latsopano.

[Bokosi patsamba 24]

Zimene Mwana Wake Wanena

Kupirira kwa bambo ndiponso kuyembekezera kwawo kuti zinthu zidzakhala bwino, kwandipatsa chitsanzo chabwino kwambiri ndipo ndimaona kuti ndine waphindu ndikamawayendetsa pa njinga ya olumala. Ndikudziŵa kuti sindingachite zimene ndingafune kuchita nthaŵi zonse. Panopa ndine wachinyamata, koma ndikadzakula, ndikufuna kudzakhala m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala. Ndikudziŵa kuchokera m’malonjezo a Baibulo kuti kuvutikaku n’kwanthaŵi yochepa chabe ndipo kuti abale ndi alongo ambiri amavutika kuposa mmene ife tikuvutikira.

[Chithunzi patsamba 22]

Mkazi wanga amandilimbikitsa kwambiri

[Chithunzi patsamba 23]

Kukambirana ndi a Dr. Juan Duarte, dokotala wa opaleshoni ya mtima

[Chithunzi patsamba 25]

Ine ndi mwana wanga timasangalala kugwirira ntchito limodzi mu utumiki