Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vidiyo Imene Imakhudza Mitima ya Achinyamata

Vidiyo Imene Imakhudza Mitima ya Achinyamata

Vidiyo Imene Imakhudza Mitima ya Achinyamata

ACHINYAMATA ambiri ataonera vidiyo yakuti Young People Ask​—How Can I Make Real Friends? * analimbikitsidwa kulingalira mofatsa khalidwe lawo. Vidiyoyi ili ndi malangizo opindulitsa a m’malemba, zimene Akristu achinyamata anena, ndiponso seŵero lolimbikitsa la makono lochokera pa nkhani ya m’Baibulo ya Dina. (Genesis, chaputala 34) Mawu onena za vidiyoyi otsatiraŵa anachokera ku Mexico.

Martha akuti: “Vidiyoyi inandikhudza mtima zedi. Ikuoneka ngati anapangira ine. Ndinkaganiza kuti popeza aphunzitsi anga ndi ana asukulu anzanga ankadziŵa kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova, zimenezi zinali zokwanira. Ndinkalephera kusonyeza zimenezi mwa kuwalalikira. Ndimathokoza chifukwa cha nkhani zonse zimene Yehova amapereka, makamaka zikakhala zokhudza mtima ngati vidiyoyi.”

Juan Carlos anati: “Vidiyo imeneyi ndi yochititsa munthu kuganiza kwambiri. Monga wachinyamata, ndinachitapo zinthu zolakwa, ndipo ndinaona kuti zinali kufanana ndi za anthu ena a m’seŵeroli. Zaka zingapo zapitazo, ndinali ndi moyo wapaŵiri, koma ndinazindikira kuti moyo umenewu ukhoza kundipalamulira mavuto. Nditaonera vidiyoyi, ndinatsimikiza mtima kukhala wokhulupirika kwa Yehova.”

Sulem akuti: “Nditaonera vidiyoyi, inandikhudza mtima kwambiri. M’mbuyomo, ndinasiya kuŵerenga Baibulo, ndipo sindinali kupemphera kwa Yehova kwenikweni. Nditamva zimene achinyamata a m’vidiyoyi ananena, ndinalimbikitsidwa kuyambiranso kuŵerenga Baibulo ndi kupemphera kwa Yehova.”

Achinyamata ambiri masiku ano amakumana ndi mavuto ambiri, ndipo nthaŵi zambiri mabwenzi amene amasankha angakhudze kwambiri zimene amachita pamoyo wawo. (Salmo 26:4; Miyambo 13:20) Vidiyo yakuti Young People Ask​—How Can I Make Real Friends? ikuthandiza anthu ambiri kusankha mabwenzi mwanzeru.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.