Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Asanaphunzire ndi Ataphunzira—Anapeza Mphamvu Kuti Asinthe

Asanaphunzire ndi Ataphunzira—Anapeza Mphamvu Kuti Asinthe

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

Asanaphunzire ndi Ataphunzira​—Anapeza Mphamvu Kuti Asinthe

SANDRA, mayi wa ku Mexico, ankadziona kuti anali munthu woipa m’banja lawo. Pachitsikana chake anali kuona kuti anthu anali kumupatula ndiponso kuti sanali kumukonda. Iye anati: “Pachitsikana changa, ndinkangoganiza kuti ndilibe phindu ndipo ndinkakonda kufunsa kuti n’chifukwa chiyani ndili moyo ndiponso mafunso ena okhudza moyo.”

Sandra ali ku sukulu ya sekondale anayamba kumwa moyo umene bambo ake anali kubweretsa panyumba. Kenako, anayamba kumagula yekha mowawo ndipo anakhala chidakwa. Iye akuti: “Sindinkafuna kukhala ndi moyo.” Sandra atasoŵa kuti agwira mtengo wanji, anayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo. Iye akuti: “Chomwe chinkandithandiza kuiwala mavuto anga ndi zinthu zimene ndinkanyamula m’kachikwama kanga basi: mowa, mapilisi angapo a mankhwala osokoneza bongo, kapena chamba pang’ono.”

Sandra atamaliza maphunziro a zachipatala, analowerera n’kukhala chidakwa chotheratu ntchito. Anafuna kudzipha. Koma anapulumuka.

Sandra analowa m’zipembedzo zosiyanasiyana n’cholinga choti apeze thandizo lauzimu ndiponso kuti zimuthandize maganizo, koma zipembedzo zonsezo zinamulembetsa m’madzi. Atasoŵa chochita ndiponso atataya mtima, nthaŵi zambiri anali kumufunsa Mulungu kuti: “Kodi muli kuti? N’chifukwa chiyani simukundithandiza?” Pamene Mboni za Yehova zinam’fikira kudzalankhula naye, n’kuti maganizo ake odziona kuti ndi wopanda phindu atam’kulira kwambiri. Zimenezi zinapangitsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo. Sandra anakhudzidwa mtima ataphunzira kuti “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka.”​—Salmo 34:18.

Amene anali kuphunzitsa Sandra Baibulo anamuthandiza kuzindikira kuti Yehova Mulungu amadziŵa kuti zimenezi zingatichitikire chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa Adamu. Sandra anazindikira kuti Mulungu amadziŵa kuti sitingatsatire ndendende miyezo yolungama. (Salmo 51:5; Aroma 3:23; 5:12, 18) Anasangalala kuphunzira kuti Yehova sayang’ana zolakwa zathu, ndipo safuna kuti tichite zimene sitingathe. Wamasalmo anafunsa kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?”​—Salmo 130:3.

Mfundo ya m’Baibulo yonena za nsembe ya dipo ya Yesu Kristu inam’khazika mtima pansi Sandra. Kudzera mu nsembeyi, Yehova mwachifundo wapangitsa kuti anthu omvera akhale owongoka ngakhale ndi opanda ungwiro. (1 Yohane 2:2; 4:9, 10) Inde, tingathe ‘kukhululukidwa zochimwa’ zathu ndipo zimenezi zingatithandize kuthetsa maganizo onse odziona ngati wopanda pake.​—Aefeso 1:7.

Sandra anaphunzira maphunziro abwino pa chitsanzo cha mtumwi Paulo. Anayamikira kwambiri kukoma mtima kwa Mulungu pom’khululukira mwachifundo zolakwa zake zimene anachita ndiponso pomuthandiza kumenya nkhondo yaikulu yolimbana ndi zofooka zimene anali kuzibwerezabwereza. (Aroma 7:15-25; 1 Akorinto 15:9, 10) Paulo anasintha moyo wake, ‘anapumpuntha thupi lake, ndi kuliyesa kapolo’ kuti ayanjidwebe ndi Mulungu. (1 Akorinto 9:27) Sanalole kuti zochita zake zauchimo zimuike paukapolo.

Zolakwa za Sandra zinali kumuvutitsa kwambiri, koma anamenyerabe nkhondo kuti azisiye. Anapemphera mochokera pansi pamtima kwa Yehova kuti amuthandize kuthana nazo ndiponso anapempha kuti amuchitire chifundo. (Salmo 55:22; Yakobo 4:8) Sandra atazindikira kuti Mulungu amamukonda, anasintha moyo wake. Iye akuti: “Ndimasangalala kuphunzitsa ena Baibulo nthaŵi zonse.” Sandra anali ndi mwayi wosangalatsa wothandiza mkulu wake ndi mng’ono wake kudziŵa Yehova. Pamene iye ‘akuchita chokoma,’ amadziperekanso kuthandiza ena pamisonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito luso lake la zachipatala.​—Agalatiya 6:10.

Nanga bwanji zizoloŵezi zoipa za Sandra? Iye ndi mtima wonse akuti: “Maganizo anga ndi abwino. Ndinasiya kumwa, kusuta, kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Zimenezi zilibenso ntchito kwa ine. Ndinapeza chimene ndinkafuna.”

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Ndinapeza chimene ndinkafuna”

[Bokosi patsamba 9]

Mfundo za M’Baibulo Zikugwira Ntchito

Zina mwa mfundo za m’Baibulo zimene zathandiza anthu ambiri kusiya zizoloŵezi zoipa ndi izi:

“Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Mulungu amadalitsa amene adziyeretsa kuleka chodetsa, kupeŵa kuchita zinthu zoipa.

“Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa.” (Miyambo 8:13) Kuopa Mulungu ndi kum’patsa ulemu kumathandiza munthu kusiya zizoloŵezi zoipa, monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Kuphatikiza pa kukondweretsa Yehova, munthu amene wasiya zimenezi amatetezekanso ku matenda oopsa.

“Iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera.” (Tito 3:1) M’madera ambiri, kupezeka kapena kugwiritsa ntchito mitundu ina ya mankhwala osokoneza bongo ndi kuphwanya malamulo. Akristu oona sasunga kapena kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa.