Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilimbikitso kwa Anthu Ofuulira Thandizo

Chilimbikitso kwa Anthu Ofuulira Thandizo

Chilimbikitso kwa Anthu Ofuulira Thandizo

BAIBULO si buku lopereka malangizo othandiza kuti munthu asakhale ndi mavuto okhudza maganizo. Komabe, limatilimbikitsa ndiponso limatithandiza kukhala osangalala ngakhale kuti timavutika. Malemba amanena zoona kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Kupanda kwathu ungwiro ndi kumene kumachititsa mavuto ena amene timakumana nawo. Koma kodi ndani kwenikweni amene amachititsa kuti anthu azivutika?

Baibulo limati ndi mzimu woipa wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana. Iye ‘akunyenga dziko lonse’ ndipo akuchititsa mavuto ambiri amene anthu akuvutika nawo. Komabe, Baibulo limatiuzanso kuti nthaŵi yake ikutha. (Chivumbulutso 12:9, 12) Posachedwapa Mulungu athetsa mavuto onse amene Satana wachitira anthu padziko lapansi. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, m’dziko latsopano lachilungamo limene Mulungu walonjeza simudzakhala kuthedwa nzeru ndiponso kuvutika maganizo.​—2 Petro 3:13.

N’zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti kuvutika kwa anthu kumene kulipoku sikudzakhalapo mpaka kalekale. Mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu, umene uli m’manja mwa Yesu Kristu, chinyengo ndi kuvutika zidzatha. Pofotokoza za Mfumu imene Mulungu waisankha, Malemba amati: “Adzapulumutsa waumphaŵi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”​—Salmo 72:12-14.

Nthaŵi yokwaniritsa mawu aulosi ameneŵa ili pafupi kwambiri. Tikhoza kudzakhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso mmene zinthu zidzakhala bwino kwambiri. (Luka 23:43; Yohane 17:3) Kudziŵa malonjezo a m’Malemba olimbikitsa ameneŵa kumathandiza anthu amene akufuulira thandizo kuyembekezera zabwino m’tsogolo ndiponso kumawalimbikitsa.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Depressed girl: Photo ILO/​J. Maillard