Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ganizani Bwino Kuti Muchite Zinthu Mwanzeru

Ganizani Bwino Kuti Muchite Zinthu Mwanzeru

Ganizani Bwino Kuti Muchite Zinthu Mwanzeru

YEREKEZERANI kuti mukuona izi: Yesu Kristu akufotokoza kuti adani ake achipembedzo ku Yerusalemu adzam’pweteka kwambiri ndipo adzamupha. Mtumwi Petro yemwe ndi mnzake wapamtima sakukhulupirira zimenezo. Ndipo, akum’tengera Yesu pambali ndi kum’dzudzula. N’zosachita kufunsa kuti Petro ali ndi nkhaŵa yeniyeni ndiponso yochokera pansi pamtima. Koma kodi Yesu akuwaona bwanji maganizo a Petro? Yesu akuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.”​—Mateyu 16:21-23.

Petro ayeneratu kuti anakhumudwa zedi. Pankhaniyi anali ‘chokhumudwitsa’ kwa Mbuye wake wokondedwa, m’malo moti akhale wothandiza ndi wolimbikitsa. Kodi izi zinachitika bwanji? Petro ayenera kuti anapusitsidwa ndi vuto limene anthu ambiri amakhala nalo poganiza, lokhulupirira zimene akufuna kukhulupirira zokha basi.

Musadzidalire Kwambiri

Chimene chingapangitse kuti tisaganize bwino ndi chizoloŵezi chodzidalira kwambiri. Mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake a ku Korinto wakale kuti: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:12) N’chifukwa chiyani Paulo ananena zimenezi? Ayenera kuti anatero chifukwa chakuti ankadziŵa kuti maganizo a anthu sachedwa kupotoka. Ngakhalenso maganizo a Akristu ‘angaipitsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.’​—2 Akorinto 11:3.

Zimenezi zinachitikira mbadwo wonse wa makolo a Paulo. Panthaŵiyo Yehova anawauza kuti: “Maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga.” (Yesaya 55:8) Iwo anali ‘kudziyesa anzeru,’ koma zimenezi zinawapalamulira mavuto zedi. (Yesaya 5:21) N’chifukwa chake, n’koyenera kuona zimene tingachite kuti tiziganiza bwino n’cholinga choti tipeŵe mavuto ofananawo.

Peŵani Maganizo a Anthu

Anthu ena ku Korinto anatengera kwambiri maganizo a anthu. (1 Akorinto 3:1-3) Anali kukonda kwambiri nzeru za anthu kuposa Mawu a Mulungu. Mosakayikira anzeru achigiriki a masiku amenewo anali anthu aluntha zedi. Komabe, kwa Mulungu, anali opusa. Paulo anati: ‘Kwalembedwa, Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha. Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthaŵi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?’ (1 Akorinto 1:19, 20) Anzeru amenewo anali kutsogoleredwa ndi “mzimu wa dziko lapansi” osati mzimu wa Mulungu. (1 Akorinto 2:12) Nzeru zawo ndi maganizo awo zinali zosagwirizana ndi maganizo a Yehova.

Gwero lenileni la maganizo a anthu amenewo ndi Satana Mdyerekezi, amene anagwiritsa ntchito njoka kunyenga Hava. (Genesis 3:1-6; 2 Akorinto 11:3) Kodi ifenso angatinyenge? Inde. Malinga ndi Mawu a Mulungu, Satana ‘wachititsa khungu maganizo’ a anthu moti tsopano ‘akunyenga dziko lonse.’ (2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9) N’kofunika kwambiri kuzindikira machenjera ake.​—2 Akorinto 2:11.

Chenjerani ndi “Chinyengo cha Anthu”

Mtumwi Paulo anachenjezanso za “tsenga la [“chinyengo cha,” NW] anthu.” (Aefeso 4:14) Anakumana ndi “ochita ochenjerera,” amene anali kunamizira kulalikira choonadi koma kwenikweni akupotoza choonadicho. (2 Akorinto 11:12-15) Anthu ameneŵa pokwaniritsa cholinga chawo, angagwiritse ntchito umboni wokhawo umene ukugwirizana ndi maganizo awo, mawu osangalatsa, nkhani zoti mbali ina zoona mbali ina zonama, mawu ofuna kupotoza anthu, ngakhalenso mabodza a m’kunkhuniza.

Nthaŵi zambiri anthu ofuna kupotoza anthu amagwiritsa ntchito mawu ngati akuti “mpatuko” kuti aipitse anthu ena. Pamfundo za pa msonkhano wa kunyumba ya malamulo ya bungwe la Council of Europe, anapereka malangizo akuti akuluakulu a boma ofufuza magulu achipembedzo atsopano “azilangizidwa kupeŵa kugwiritsa ntchito mawu ameneŵa.” Chifukwa chiyani? Chifukwa anaona kuti mawu akuti “mpatuko” ali ndi tanthauzo loipa kwambiri. Mofananamo, anthu anzeru achigiriki ananena molakwa kuti mtumwi Paulo anali “wobwetuka,” kapena kuti “wotola mbewu.” Anali kutanthauza kuti anali wongobwebweta, munthu amene anali kungodziŵa zinthu zochepa chabe n’kumangozibwerezabwereza. Koma kwenikweni, Paulo anali ‘kulalikira za Yesu ndi kuuka kwa akufa.’​—Machitidwe 17:18.

Kodi njira zimene anthu opotoza ena amagwiritsa ntchito zimawayendera? Inde. Ndi amene achititsa kwambiri kuti pakhale udani pakati pa mafuko ndi zipembedzo mwa kuipitsa mmene anthu amaonera mitundu ina ya anthu kapena zipembedzo zina. Anthu ambiri agwiritsa ntchito zimenezi kuponderezera mitundu ing’onoing’ono. Adolf Hitler anagwiritsa ntchito njira zimenezo pamene anasonyeza kuti Ayuda ndi ena anali “otsika,” “oipa,” ndiponso “oukira” Boma, ndipo zinamuyendera. Musalole kuti chinyengo ngati chimenechi chiipitse maganizo anu.​—Machitidwe 28:19-22.

Musadzinyenge Nokha

N’kosavutanso kudzinyenga tokha. Ndipotu, kungakhale kovuta kwambiri kusiya kapena kupenda maganizo amene azika kwambiri mizu mwa ife. Chifukwa chiyani? Chifukwa timakhala kuti tikuwakonda kwambiri maganizo athuwo. Ndiyeno tingadzinyenge tokha poganiza zabodza, kupeza zifukwa zotsimikizira kuti zikhulupiriro zimene zilidi zolakwika ndi zonyenga zikhale zoona.

Izi zinachitika kwa Akristu ena a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Ankadziŵa Mawu a Mulungu, koma sanafune kuti Mawuwo atsogolere maganizo awo. Mapeto ake ‘anadzinyenga okha [ndi maganizo abodza, NW].’ (Yakobo 1:22, 26) Ngati timakwiya kwambiri ena akakayikira zikhulupiriro zathu, n’chizindikiro chimodzi chakuti tili ndi vuto limeneli lodzinyenga tokha. M’malo mokwiya, ndi bwino kukhala ndi maganizo ofuna kumva za ena ndi kumvetsera mosamalitsa zonena zawo ngakhale tikudziŵa kuti zimene tikuganizazo ndizo zoona.​—Miyambo 18:17.

Funafunani “Kum’dziŵadi Mulungu”

Kodi tingatani kuti tiziganiza bwino? Pali zambiri zimene zingatithandize, koma tifunika khama. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kupfuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:1-5) Inde, ngati tiyesetsa kuti maganizo ndi mtima wathu zidzaze ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu, tidzapeza nzeru zenizeni, luntha, ndi kuzindikira. Ndipotu, tidzakhala tikufunafuna zinthu zamtengo wapatali kuposa siliva kapena chuma chilichonse cha mtengo wapatali.​—Miyambo 3:13-15.

Ndithudi, nzeru ndi kudziŵa zinthu n’zofunika poganiza bwino. Mawu a Mulungu amati: “Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m’njira za mdima.”​—Miyambo 2:10-13.

N’kofunika kwambiri kulola maganizo a Mulungu kutsogolera maganizo athu panthaŵi zovuta kapena zoopsa. Zinthu monga mkwiyo kapena mantha zingapangitse kuganiza bwino kukhala kovuta. Solomo anati: “Nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Ndipo n’zothekanso ‘kudandaula pa Yehova.’ (Miyambo 19:3) Motani? Poimba mlandu Mulungu chifukwa cha mavuto athu ndiponso kuwatenga mavutowo kukhala chifukwa chochitira zinthu zosagwirizana ndi malamulo ake ndi mfundo zake. M’malo moganiza kuti timadziŵa zonse, tiyenitu tizimvera modzichepetsa aphungu anzeru amene amafuna kutithandiza pogwiritsa ntchito Malemba. Ndipo ngati n’koyenera, tikhale okonzeka kusiya ngakhale maganizo amene anazika mizu, ngati aonekeratu kuti ndi olakwika.​—Miyambo 1:1-5; 15:22.

‘Pemphani kwa Mulungu’

Tikukhala m’nthaŵi zovuta ndi zoopsa. N’kofunika kupemphera kwa Yehova nthaŵi zonse kuti atitsogolere ngati tikufuna kuti tiziganiza bwino ndi kuchita zinthu mwanzeru. Paulo anati: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Ngati tisoŵa nzeru za mmene tingachitire ndi mavuto kapena mayesero othetsa nzeru, tifunika ‘kupempha kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza.’​—Yakobo 1:5-8.

Chifukwa chakuti mtumwi Petro ankadziŵa kuti Akristu anzake amafunika kukhala anzeru, anafuna ‘kutsitsimutsa mtima wawo woona.’ Anafuna kuti iwo ‘akumbukire mawu onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Mbuye ndi Mpulumutsi,’ Yesu Kristu. (2 Petro 3:1, 2) Ngati tichita zimenezi ndiponso ngati maganizo athu agwirizana ndi Mawu a Yehova, tidzaganiza bwino ndipo tidzachita zinthu mwanzeru.

[Zithunzi patsamba 21]

Akristu oyambirira analola nzeru za Mulungu osati nzeru za anthu, kuumba maganizo awo

[Mawu a Chithunzi]

Philosophers left to right: Epicurus: Photograph taken by courtesy of the British Museum; Cicero: Reproduced from The Lives of the Twelve Caesars; Plato: Roma, Musei Capitolini

[Zithunzi patsamba 23]

Kupemphera ndi kuphunzira Mawu a Mulungu n’kofunika