Kodi Timafunikadi Anthu Ena?
Kodi Timafunikadi Anthu Ena?
“TIKAUONETSESA bwino moyo wathu ndi zochita zathu, timaoneratu kuti pafupifupi zochita ndi zofuna zathu zonse zimadalira anthu ena,” anatero wasayansi wina wotchuka kwambiri dzina lake Albert Einstein. Iye anatinso: “Timadya chakudya cholimidwa ndi anthu ena, timavala zovala zopangidwa ndi anthu ena, timakhala m’nyumba zomangidwa ndi anthu ena. . . . Munthu payekha ndi munthu payekha basi ndipo ndi wofunika osati payekha, koma monga mmodzi wa anthu ambirimbiri, amene zochita zawo zimamuthandiza mwakuthupi ndiponso mwauzimu kuyambira ali mwana mpaka pamene adzamwalira.”
Nthaŵi zambiri, nyama mwachibadwa zimayendera limodzi. Njovu zimayenda m’chigulu ndipo zimateteza kwambiri ana awo. Mikango yaikazi imafunira pamodzi chakudya n’kukadyera limodzi ndi mikango yaimuna. Nyama zotchedwa Dolphins zimaseŵerera pamodzi ndipo zatetezapo nyama zina kapena anthu osambira amene ali pavuto.
Komabe, akatswiri a sayansi ya kakhalidwe ka anthu aona kuti anthu ali ndi chizoloŵezi chimene chikudetsa nkhaŵa kwambiri. Malinga ndi zimene inalemba nyuzipepala ina ya ku Mexico, asayansi ena akuganiza kuti, “zaka zambiri zimene anthu akhala akudzipatula ndiponso kusokonezeka kwa chizoloŵezi chokhalira pamodzi ndi anthu ena zabweretsa mavuto ambiri kwa anthu a ku United States.” Nyuzipepalayo inati “kuti zinthu ziyende bwino m’dzikolo pafunika kuti anthu asinthe kwambiri kakhalidwe kawo, zimene zikuphatikizapo kuti ayambenso kukhalira limodzi ndi anthu ena.”
Vutoli n’lofala kwambiri makamaka kwa anthu a m’mayiko olemera. Pali chizoloŵezi chimene chikukula kwambiri chakuti anthu ambiri amadzipatula. Anthu amafuna ‘kuima paokha’ ndipo safuna n’komwe kuti ena ‘awasokoneze.’ Anthu anena kuti khalidwe limeneli lapangitsa anthu kuvutika maganizo, ndiponso kudzipha.
Pa chifukwa chimenechi, Dr. Daniel Goleman anati: “Kudzipatula, kuganiza kuti munthu ulibe woti ungamuuze za kukhosi kapena kucheza naye momasuka kumapangitsa munthu kudwala kapena kumwalira msanga kusiyana ndi amene sadzipatula.” Lipoti la m’magazini yotchedwa Science linati kudzipatula ‘kungachititse imfa zofanana ndi zimene kusuta, kuthamanga magazi kwambiri, kuchuluka mafuta m’thupi, kunenepa kwambiri, ndiponso kusachita maseŵera olimbitsa thupi kungachititse.’
Chotero, pali zifukwa zambiri zimene timafunikiradi anthu ena. Sitingaime patokha. Choncho kodi vuto lodzipatula lingathetsedwe bwanji? Kodi n’chiyani chimene chapangitsa moyo wa anthu ambiri kukhala watanthauzo? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso ameneŵa.
[Mawu Otsindika patsamba 3]
“Pafupifupi zochita ndi zofuna zathu zonse zimadalira anthu ena.”—Anatero Albert Einstein