Wodala Munthu Amene Mulungu Wake ndi Yehova
Mbiri ya Moyo Wanga
Wodala Munthu Amene Mulungu Wake ndi Yehova
YOSIMBIDWA NDI TOM DIDUR
Tinali titalipira kale ndalama kuti tidzagwiritse ntchito holo ya m’mudzimo. Timayembekezera anthu pafupifupi 300 kubwera ku msonkhano kutauni yotchedwa Porcupine Plains, Saskatchewan, ku Canada. Lachitatu kunayamba kugwa chipale chofeŵa, ndipo pofika Lachisanu kunali chimphepo chophatikizana ndi chipale chofeŵa ndipo zinthu sizimaoneka n’komwe. Kunja kunazizira mpaka kufika pa –40 digiri Celsius. Kunabwera anthu 28, kuphatikizapo ana angapo. Uwu unali msonkhano wanga woyamba monga woyang’anira dera, ndipo ndinali woda nkhaŵa chifukwa ndinali mnyamata wa zaka 25 basi. Ndisanakuuzeni zimene zinachitika, ndifotokoze kaye zimene zinachititsa kuti ndikhale ndi mwayi wapadera umenewu.
NDINE wachisanu ndi chiŵiri kubadwa m’banja la ana asanu ndi atatu, amuna okhaokha. Woyamba kubadwa anali Bill, kenaka Metro, John, Fred, Mike, ndi Alex. Ine ndinabadwa m’chaka cha 1925, ndipo Wally ndiye womaliza kubadwa. Tinkakhala pafupi ndi tauni ya Ukraina, ku Manitoba, kumene makolo anga, Michael ndi Anna Didur, anali ndi famu yaing’ono. Bambo ankagwira ntchito yokonza njanji. Tinkakhala pa famupo chifukwa chakuti nyumba ya matabwa m’mphepete mwa njanji sanali malo abwino olerera ana komanso kunali kutali. Bambo sankakhala pakhomo nthaŵi zambiri, choncho Amayi ndi amene anali ndi ntchito yotilera. Nthaŵi ndi nthaŵi Amayi amachoka kupita kumene kunali Bambo kwa mlungu umodzi kapena iŵiri, koma anaonetsetsa kuti tiphunzire kuphika, ngakhale kuphika buledi ndi masikono, ndi kugwira ntchito zapakhomo. Ndipo chifukwa chakuti tinkapemphera Tchalitchi cha Katolika cha Agiriki, chinthu chimodzi mwa zina chimene Amayi anatiphunzitsa tili ana chinali kuloŵeza mapemphero ndi kuchita nawo miyambo ina ndi ina.
Kupeza Choonadi cha m’Baibulo
Ndinayamba ndili mwana kufuna kulimvetsetsa Baibulo. Munthu wina wa Mboni za Yehova amene
amakhala pafupi ndi nyumba yathu ankabwerabwera kwathu kudzaŵerenga mbali zina za m’Baibulo zofotokoza za Ufumu wa Mulungu, Armagedo, ndi madalitso a m’dziko latsopano. Amayi analibe chidwi chilichonse ndi zimene anamvazo, koma uthengawo unasangalatsa Mike ndi Alex. Moti zimene anaphunzirazo zinawapangitsa kukana kupita kunkhondo chifukwa cha chikumbumtima chawo panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Chifukwa cha zimenezi, Mike anaikidwa m’ndende kwa nthaŵi yochepa, pamene Alex anatumizidwa ku msasa wolangirako anthu ku Ontario. Patapita nthaŵi, Fred ndi Wally nawonso anakhulupirira choonadi. Koma akulu anga atatu sanakhulupirire. Kwa zaka zingapo, Amayi anali kutsutsa choonadi koma kenaka anadzatidabwitsa tonsefe poima kumbali ya Yehova. Anabatizidwa ali ndi zaka 83. Amayi anamwalira ali ndi zaka 96. Bambo nawonso anayamba kumasangalala ndi choonadi atatsala pang’ono kumwalira.Nditakwanitsa zaka 17 ndinapita ku Winnipeg kukafuna ntchito komanso kuti ndizikakhala ndi anthu amene angandithandize kuphunzira Baibulo. Panthaŵi imeneyi n’kuti Mboni za Yehova zili zoletsedwa ndi boma, koma misonkhano imachitika mokhazikika. Msonkhano woyamba umene ndinapitako unachitikira m’nyumba. Chifukwa chakuti ndinaleredwa m’chipembedzo cha Katolika cha Agiriki, zimene ndinamva kumeneko poyamba zinali zachilendo kwa ine. Koma pang’ono ndi pang’ono ndinamvetsa chifukwa chake kukhala ndi magulu aŵiri osiyana a atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba sikunali kochokera m’Malemba ndiponso chifukwa chake Mulungu sasangalala akamaona atsogoleri achipembedzo akudalitsa nkhondo. (Yesaya 2:4; Mateyu 23:8-10; Aroma 12:17, 18) Zoti anthu adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi zinali zomveka komanso zimaoneka zotheka kusiyana n’zopita kumalo akutali kukakhala kumeneko kosatha.
Nditakhulupirira kuti choonadi n’chimenechi, ndinadzipatulira kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa mu 1942 ku Winnipeg. Pofika mu 1943, ntchito ya Mboni za Yehova ku Canada inatsegulidwanso ndipo ntchito yolalikira inayamba kufulumira. Komanso, choonadi cha m’Baibulo chinayamba kukhudza mtima wanga kwambiri. Ndinali ndi mwayi wotumikira monga mkulu mu mpingo komanso ndinkapita nawo m’madera osiyanasiyana kukakamba nkhani za onse ndi kukalalikira m’gawo losagaŵiridwa mpingo uliwonse. Kupezeka pa misonkhano ikuluikulu ku United States kunandithandiza kwambiri kuti ndipite patsogolo mwauzimu.
Kuonjezera Utumiki Wanga kwa Yehova
Mu 1950 ndinalembetsa upainiya, ndipo mu December chaka chimenecho anandiuza kuti ndikhale woyang’anira dera. Ndinali ndi mwayi wophunzira ntchito imeneyi kufupi ndi ku Toronto pophunzitsidwa ndi Charlie Hepworth, mbale wodziŵa bwino zinthu komanso wokhulupirika. Ndinasangalalanso kwambiri chifukwa chothera mlungu womaliza wa maphunziro anga ndi mchimwene wanga Alex, amene panthaŵi imeneyi anali kale woyang’anira dera ku Winnipeg.
Msonkhano wanga wadera woyamba, monga ndafotokozera poyamba paja, sindidzauiŵala. Mwachidziŵikire, ndinkada nkhaŵa kuti zinthu ziyenda bwanji. Koma woyang’anira chigawo wathu, Mbale Jack Nathan anatithandiza tonsefe kukhala otanganidwa ndi osangalala. Tinakambirana pulogalamu ya msonkhanowo mwachidule ndi anthu okamba nkhani amene analipo. Aliyense anafotokozapo zinthu zimene anakumana nazo, anayeseza kuchita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, kuchita maulendo obwereza, ndi kusonyeza mmene tingachititsire maphunziro a Baibulo apanyumba. Tinaimba nyimbo za Ufumu. Panali zakudya zambiri. Tinamwa khofi ndi kudya makeke pafupifupi maola aŵiri alionse. Ena anagona pamabenchi ndi papulatifomu, pamene ena anagona pansi. Pofika Lamlungu chipale chofeŵa chija chinali chitachepako ndipo anthu 96 anabwera kudzamvera nkhani ya onse. Zimene zinachitikazi zinandiphunzitsa kupirira pamavuto.
Kenaka ananditumiza kukayang’anira dera kumpoto kwa Alberta, ku British Columbia, ndi ku Yukon Territory, kudera limene dzuŵa sililoŵa. Kuti tiyende pa msewu woipa wa Alaska Highway kuchoka
ku Dawson Creek, British Columbia, kupita ku Whitehorse, Yukon (ulendo wa makilomita 1,477), n’kumalalikira m’njiramo tinafunika kupirira ndi kusamala. Panali zinthu zambiri zimene tinalimbana nazo monga chipale chofeŵa chogumuka, njira zoterera zodutsa m’mphepete mwa mapiri, komanso kuona movutikira chifukwa cha chipale chofeŵa chouluka ndi mphepo.Ndinadabwa kuona kuti choonadi chinafika mpaka ku Far North. Panthaŵi ina ndili ndi Walter Lewkowicz tinapita ku nyumba yaing’ono kufupi ndi mudzi wa Lower Post, ku British Columbia, m’mphepete mwa msewu wa Alaska Highway kufupi ndi malire a Yukon Territory. Tinadziŵa kuti m’kanyumbako munali munthu chifukwa tinaona kuwala pa zenera laling’ono. Nthaŵi inali pafupifupi 9 koloko usiku ndipo tinagogoda pachitseko. Tinamva mawu achimuna akutiuza kuti tiloŵe, ndipo tinaloŵa. Zinali zodabwitsa kwambiri kuona bambo wokalamba atagona pa bedi losanjikizana ndi linzake akuŵerenga magazini ya Nsanja ya Olonda. Ndipo anali ndi magazini yatsopano kwambiri kuposa imene tinali kugaŵira anthu. Anatifotokozera kuti makalata ake amabwera pandege. Chifukwa chakuti tinali titachoka ku mpingo wathu kwa masiku oposa asanu ndi atatu tsopano, tinalibe magazini atsopano. Bamboyo anatiuza kuti dzina lake ndi Fred Berg, ndipo ngakhale kuti anali kulandira magazini pa positi kwa zaka zingapo, aka kanali koyamba kuti Mboni za Yehova zimuyendere. Fred anatiuza kuti tigone. Tinakambirana naye mfundo zambiri za choonadi cha m’Malemba ndipo tinakonza zoti Mboni zina zimene zimadutsa m’dera limenelo nthaŵi ndi nthaŵi zizimuyendera.
Kwa zaka zingapo ndinatumikira madera aang’ono atatu. Dera lake limayambira ku Grande Prairie, Alberta, kum’maŵa mpaka ku Kodiak, Alaska, kumadzulo, ulendo wa makilomita 3,500.
Ndinasangalala kwambiri kuzindikira kuti kumadera akutali, mofanana ndi kwina kulikonse, Yehova amakomera mtima anthu onse ndipo mzimu wa Mulungu umakhudza mitima ndi maganizo a anthu ofuna moyo wosatha. Munthu mmodzi wotero anali Henry Lepine wa ku Dawson City, ku Yukon, kumene tsopano kumatchedwa ku Dawson. Henry ankakhala kudera lakutali. Ndipo iye anali atatha zaka 60 asanapiteko kwina kulikonse kukayenda kuchoka ku dera la kwawo la migodi ya golide. Komabe, mzimu wa Yehova unapangitsa bambo wa zaka 84 ameneyu kuyenda ulendo wopitirira makilomita 1,600 kupita kokha kukafika ku Anchorage
kuti akachite nawo msonkhano wadera, ngakhale kuti anali asanapiteko ku msonkhano uliwonse wa mpingo. Anasangalala kwambiri ndi pulogalamuyo komanso macheza amene anali kumeneko. Atabwerera ku Dawson City, Henry anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa. Anthu ambiri amene ankamudziŵa Henry anadabwa kuti n’chiyani chinapangitsa bambo wokalambayu kuyenda ulendo wautali choncho. Kudabwa kumeneku kunapangitsa okalamba ena angapo kukhulupirira choonadi. Choncho, ngakhale kuti sanalalikire mwachindunji, Henry anatha kuchitira umboni wabwino.Yehova Anandikomera Mtima
M’chaka cha 1955, ndinasangalala kwambiri pamene ndinaitanidwa kukakhala nawo m’kalasi la nambala 26 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Maphunziro ameneŵa analimbitsa chikhulupiriro changa ndipo anandithandiza kuyandikana kwambiri ndi Yehova. Nditamaliza maphunzirowo, ndinauzidwa kukapitiriza ntchito yoyang’anira dera ku Canada.
Kwa pafupifupi chaka chimodzi, ndinatumikira kuchigawo cha Ontario. Kenaka ndinatumizidwa kukatumikira ku dera lokongola la North. M’maganizo mwangamu, mpaka pano ndimathabe kuona misewu yokongola yodutsa m’mphepete mwa nyanja za madzi oyera bwino, yokwera m’mapiri a nsonga zokutidwa ndi chipale chofeŵa. M’chilimwe, zigwa ndi madambo zimakutidwa ndi maluŵa owala bwino. Mpweya ndi madzi ake n’zabwino. Zimbalangondo, nkhandwe, moose, caribou, ndi nyama zina zakutchire zimayendayenda popanda chilichonse chozisokoneza m’dera lawo lachilengedwe.
Koma kutumikira ku Alaska kuli ndi mavuto ake, osati chifukwa cha nyengo yosinthasintha yokha komanso chifukwa cha kukula kwa deralo. Dera langa linali lalitali makilomita 3,200 kuchoka kum’maŵa kukafika kumadzulo. Kalelo panalibe zoti woyang’anira dera azikhala ndi galimoto. Abale anadzipereka kunditenga pagalimoto zawo kuchoka ku mpingo umodzi kupita ku mpingo wina. Koma nthaŵi zina ndinafunika kukwera matola pa mathiraki kapena pa magalimoto a alendo odzaona malo.
Nthaŵi imodzi imene ndinachita zimenezi inali pamene ndinali pa msewu wa Alaska Highway pakati pa malo otchedwa Tok Junction, ku Alaska ndi malo otchedwa Mile 1202, kapena kuti dera la Scotty Creek. Maofesi a kasitomu pamalo aŵiri ameneŵa anali otalikirana makilomita 160. Ndinadutsa ofesi ya kasitomu ya ku United States pa Tok n’kukwera matola kwa ulendo wotalika makilomita 50. Kenaka, sipanadutsenso galimoto lililonse, ndipo ndinayenda pansi kwa maola pafupifupi khumi, ulendo wa makilomita opitirira 40. Pambuyo pake m’pamene ndinadzauzidwa kuti nditangodutsa ofesi ya kasitomu ija, magalimoto onse anawaletsa kudutsa mu msewuwo chifukwa cha chipale chofeŵa chimene chinagumuka penapake kungopitirira pang’ono ofesi ya kasitomuyo. Pofika pakati pa usiku kunja kunazizira mpaka kufika –23 digiri Celsius, ndipo malo apafupi amene ndikanausirapo anali pamtunda wa makilomita pafupifupi 80 kuchoka pamene ndinalipo. Ndinafunikira kupeza malo mwamsanga kuti ndipumuleko.
Ndikuyenda chotsimphina, ndinaona galimoto yotayidwa ili m’mphepete mwa msewu, itakutidwa pang’ono ndi chipale chofeŵa. Ndinaganiza kuti ngati ndingaloŵe m’kati mwa galimotoyo n’kugona pamipando yake, ndingapulumuke usiku wozizirawo. Ndinatha kukankha chipale chofeŵacho n’kutsegula chitseko, koma ndinapeza kuti m’kati monsemo anali atakanganulamo chilichonse n’kungosiya zitsulo zokhazokha. Mwamwayi, chapafupiko
pang’ono m’mphepete mwa msewuwo ndinapeza kanyumba kakang’ono kopanda kanthu. Ndinavutika kwambiri kuti ndikatsegule n’kuloŵamo komanso kuti ndiyatse moto, koma kenaka ndinatha kupumulako kwa maola angapo. M’maŵa mwake, ndinapeza matola okafika ku nyumba ya alendo yapafupi ndi kumene ndinaliko, ndipo kumeneko ndinapeza chakudya komanso ndinamanga zala zanga zimene zinali zitang’ambikang’ambika.Yehova Akulitsa Choonadi Kumpoto
Ulendo wanga woyamba wopita ku Fairbanks unali wolimbikitsa kwambiri. Zinatiyendera bwino kwambiri mu utumiki ndipo anthu pafupifupi 50 anabwera kudzamvera nkhani ya onse Lamlungu. Tinasonkhana m’nyumba yaing’ono ya amishonale kumene Vernor ndi Lorraine Davis anali kukhala. Anthu m’nyumbamo anakhala m’khitchini, kuchipinda chogona, ndi m’tinjira ta m’nyumbamo ndipo ankachita kusuzumira kuti amve nkhaniyo. Poona mmene anthu anasangalalira ndi nkhaniyo, tinadziŵa kuti kumanga Nyumba ya Ufumu ku Fairbanks kukanalimbikitsa ntchito yolalikira. Choncho, ndi thandizo la Yehova, tinagula nyumba yokulirapo ndithu imene kale ankaigwiritsa ntchito ngati holo yoviniramo, ndipo tinaisamutsira pa malo ena abwino. Tinakumba chitsime, ndipo tinaika mabafa ndi makina otenthetsera mpweya m’nyumbamo. Pamene chaka chimatha, tinali tili ndi Nyumba ya Ufumu yabwino ku Fairbanks. Titaonjezeramo khitchini, tinagwiritsa ntchito holoyo kuchitiramo msonkhano wachigawo m’chaka cha 1958 ndipo kunabwera anthu 330.
M’chilimwe cha 1960, ndinayenda ulendo wautali pagalimoto kupita ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku New York, kumene ndinakachita nawo maphunziro oonjezera a oyang’anira oyendayenda a ku United States ndi Canada. Ndili kumeneko, Mbale Nathan Knorr ndi abale ena amaudindo anandifunsa maganizo anga pa nkhani yokhazikitsa ofesi ya nthambi ku Alaska. Patapita miyezi yochepa, tinasangalala kumva kuti kuyambira pa September 1, 1961, ku Alaska kudzakhala ofesi ya nthambi yakeyake. Mbale Andrew K. Wagner anaikidwa kuti aziyang’anira ntchito za panthambi. Iye ndi mkazi wake Vera anali atatumikira ku Brooklyn kwa zaka 20 ndipo anali atagwiraponso ntchito ya woyang’anira woyendayenda. Tinayamikira kwambiri kukhazikitsidwa kwa ofesi ya nthambi ya Alaska chifukwa kunachepetsa ulendo umene woyang’anira dera amayenda, ndipo zimenezi zinathandiza kuti woyang’anira dera azithera nthaŵi yake yambiri akusamalira zosoŵa za mipingo ndi za magawo akutali.
Chilimwe cha 1962 chinali chosangalatsa kwambiri ku North. Nthambi ya Alaska anaipatulira, ndipo ku Juneau, Alaska, kunachitika msonkhano wachigawo. Ku Juneau ndi ku Whitehorse, Yukon, kunamangidwa Nyumba za Ufumu zatsopano ndipo magulu akutali angapo anakhazikitsidwa.
Kubwerera ku Canada
Kwa zaka zingapo ndinali kulemberana makalata ndi Margareta Petras wa ku Canada. Reta, monga mmene amadziŵikira, anayamba upainiya mu 1947, anamaliza maphunziro a Gileadi mu 1955, ndipo anali akuchita upainiya kum’maŵa kwa Canada. Ndinamfunsa kuti tikwatirane, ndipo anandilola. Tinakwatirana ku Whitehorse mu February 1963. Pofika m’nyengo ya phukuto (nyengo imene mitengo ina imayoyola masamba ake), ndinatumizidwa kukagwira ntchito yoyang’anira dera kumadzulo kwa Canada, ndipo tinasangalala kutumikira kumeneko kwa zaka 25.
Chifukwa cha kudwala, mu 1988 tinatumizidwa ku Winnipeg, Manitoba, kukachita upainiya wapadera. Kumeneko tinalinso ndi ntchito yoyang’anira Nyumba ya Msonkhano kwa zaka pafupifupi zisanu. Tikupitirizabe kugwira nawo ntchito yosangalatsa yopanga ophunzira mogwirizana ndi mmene tingathere. Pamene timagwira ntchito yoyang’anira dera, tinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri n’kusiyira ena kuti apitirize kuwachititsa. Panopa, chifukwa cha kukoma mtima kwa Yehova, timayambitsa maphunziro komanso timakhala ndi chimwemwe choonjezereka poona ophunzirawo akupita patsogolo mpaka kudzipatulira ndi kubatizidwa.
Ndikukhulupirira kuti moyo wotumikira Yehova ndiye wabwino kwambiri kuposa moyo wina uliwonse. Ndi moyo watanthauzo komanso wokhutiritsa, ndipo umakulitsa chikondi chathu pa Yehova tsiku lililonse. Zimenezi n’zimene zimabweretsa chimwemwe chenicheni. Kaya tikugwira ntchito yotani yotumikira Mulungu, kapena tikutumikira kuti, timavomerezana ndi wamasalmo amene ananena kuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15.
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Ndili mu ntchito yadera
[Chithunzi patsamba 25]
Titapita kukacheza ndi Henry Lepine ku Dawson City. Ine ndili kumanzere
[Chithunzi patsamba 26]
Nyumba ya Ufumu yoyamba ku Anchorage
[Chithunzi patsamba 26]
Ine ndi Reta mu 1998