Yehova, Mulungu wa Choonadi
Yehova, Mulungu wa Choonadi
“Mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa choonadi.”—SALMO 31:5.
1. Kodi zinthu zinali bwanji kumwamba ndi padziko lapansi pamene kunalibe bodza?
PA NTHAŴI ina kunja kuno kunalibe bodza. Kumwamba kosaoneka ndi maso kunali zolengedwa zauzimu zangwiro zimene zimatumikira Mlengi wawo, “Mulungu wa choonadi.” (Salmo 31:5) Kunalibe bodza, ndiponso kunalibe chinyengo. Yehova anali kuuza ana ake auzimu zinthu zoona. Anatero chifukwa chakuti anali kuwakonda ndiponso anali kuwafunira zabwino. Padziko lapansi zinthu zinali chimodzimodzi. Yehova analenga mwamuna ndi mkazi woyamba, ndipo pogwiritsa ntchito njira yake yolankhulira imene anakhazikitsa, nthaŵi zonse anali kulankhula nawo momveka bwino, mosapita m’mbali, ndiponso anali kuwauza zoona. Zinthu ziyenera kuti zinali zosangalatsa kwambiri!
2. Kodi ndani anayambitsa bodza, ndipo kodi n’chifukwa chiyani analiyambitsa?
2 Koma patapita nthaŵi, mwana wauzimu wa Mulungu mwamwano anafuna kuti nayenso akhale ngati mulungu kuti azitsutsana ndi Yehova. Mwana wolengedwa wauzimu ameneyu, amene anadzatchedwa Satana Mdyerekezi, anafuna kuti ena azimulambira. Kuti zimenezi zitheke, anayambitsa bodza kuti lim’thandize kulamulira ena. Chifukwa chochita zimenezi, anasanduka “wabodza, ndi atate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.
3. Kodi Adamu ndi Hava anachita chiyani atamva mabodza a Satana, ndipo kodi zotsatirapo zake zinali zotani?
3 Pogwiritsa ntchito njoka, Satana anauza mkazi woyambayo, Hava, kuti ngati samvera lamulo la Mulungu n’kudya chipatso choletsedwacho, sadzafa. Limenelo linali bodza. Anamuuzanso kuti akadya chipatsocho adzakhala ngati Mulungu, wodziŵa zabwino ndi zoipa. Limenelonso linali bodza. Ngakhale kuti Hava anali asananamizidwepo, ayenera kuti anazindikira kuti zimene anamva kwa njokazo zinali zosiyana ndi zimene Mulungu anauza mwamuna wake, Adamu. Komabe, iye anasankha kukhulupirira Satana, osati Yehova. Atanyengedwa kotheratu, anatenga chipatsocho n’kudya. Kenaka, Adamu anadyanso chipatsocho. (Genesis 3:1-6) Mofanana ndi Hava, Adamu anali asanamvepo bodza, koma sananyengedwe. (1 Timoteo 2:14) Pochita zimenezi anasonyeza kuti akum’kana Mlengi wake. Zotsatirapo zake kwa mtundu wonse wa anthu zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Chifukwa cha kusamvera kwa Adamu, uchimo ndi imfa, kuphatikizapo kuipa ndi kuvutika kosaneneka, zinafalikira kwa ana ake onse.—Aroma 5:12.
4. (a) Kodi mabodza amene ananenedwa mu Edene anali otani? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisanyengedwe ndi Satana?
4 Ndiponso bodza linafalikira. Tiyenera kuzindikira kuti mabodza amene ananenedwa m’munda wa Edene aja anatsutsa Yehova kuti sanena zoona. Satana ananena kuti Mulungu mwachinyengo anali kumana anthu aŵiri oyambawo kanthu kena kabwino. Koma tikudziŵa kuti zinthu sizinali choncho. Adamu ndi Hava sanapindule chifukwa cha kusamvera kwawoko. Anafa, monga mmene Yehova ananenera. Komabe, Satana anapitiriza kunamizira Yehova, mpaka kufika poti patapita zaka mazana ambiri mtumwi Yohane anauziridwa kulemba kuti Satana ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9) Kuti tisanyengedwe ndi Satana Mdyerekezi, tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amanena zoona ndiponso kuti Mawu ake ndi oona. Kodi mungalimbitse ndi kukulitsa bwanji chikhulupiriro chanu mwa Yehova komanso kudzitchinjiriza nokha ku chinyengo ndi mabodza amene Mdani wake amafalitsa?
Yehova Amadziŵa Choonadi
5, 6. (a) Kodi Yehova amadziŵa zotani? (b) Kodi zimene anthu amadziŵa tingaziyerekezere bwanji ndi zimene Yehova amadziŵa?
5 Baibulo nthaŵi zonse limanena kuti Yehova ndi amene “[ana]lenga zonse.” (Aefeso 3:9) Iye ndiye “[ana]lenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili mmenemo.” (Machitidwe 4:24) Chifukwa chakuti Yehova ndiye Mlengi, amadziŵa zoona zake za chinthu chilichonse. Mwachitsanzo: Taganizirani za munthu amene wajambula pulani ya nyumba yake, kenaka n’kuimanga yekha, kuyala thabwa lililonse komanso kukhoma msomali uliwonse yekha. Iye adzaidziŵa bwino kwambiri nyumba imeneyo kuposa munthu wina aliyense amene wangoiona chabe. Anthu amadziŵa bwino kwambiri zinthu zimene amazipanga okha. Mofananamo, Mlengi amadziŵa zonse zokhudza zinthu zimene analenga.
6 Mneneri Yesaya anafotokoza bwino kwambiri kuchuluka kwa zinthu zimene Yehova amadziŵa. Timaŵerenga kuti: “Ndani wayesa madzi m’dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m’nsengwa, ndi kuyesa mapiri m’mbale zoyesera, ndi zitunda mu mlingo? Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kum’phunzitsa Iye? Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kum’phunzitsa m’njira ya chiweruzo, ndi kum’phunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?” (Yesaya 40:12-14) Zoonadi, Yehova ndi “Mulungu wodziŵa zinthu” ndipo ‘amadziŵa mwangwiro.’ (1 Samueli 2:3, NW; Yobu 36:4; 37:16) Poyerekezera ndi Yehova, ifeyo timadziŵa zinthu zochepa kwambiri! Anthu akudziŵa zinthu zambiri zochititsa chidwi, koma zimene akudziŵa zokhudza chilengedwe sizifika n’komwe pa “malekezero a njira [za Mulungu].” Zili ngati ‘kunong’ona’ mukakuyerekezera ndi “kugunda kwa mphamvu.”—Yobu 26:14.
7. Kodi Davide anadziŵa chiyani chokhudza zinthu zimene Yehova amadziŵa, ndipo chifukwa cha zimenezi, kodi tiyenera kuvomereza chiyani?
7 Chifukwa chakuti Yehova anatilenga, n’zachidziŵikire kuti amatidziŵa bwino. Mfumu Davide anadziŵa zimenezi. Iye analemba kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziŵa. Inu mudziŵa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Muyesa Salmo 139:1-4) Komabe, Davide anadziŵa kuti anthu ali ndi ufulu wosankha, kapena kuti, Mulungu anatipatsa mphamvu yoti tingasankhe kumumvera kapena kusamumvera. (Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15) Ngakhale zili choncho, Yehova amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziŵira ife eni. Iye amatifunira zabwino, ndipo ndiye amene ayenera kutitsogolera pa moyo wathu. (Yeremiya 10:23) Zoonadi, palibe mphunzitsi, katswiri, kapena mlangizi amene angapose Yehova potiphunzitsa choonadi ndi kutithandiza kukhala anzeru ndi achimwemwe.
popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzoloŵerana nazo. Pakuti asanafike mawu pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziŵa onse.” (Yehova Amanena Zoona
8. Kodi tikudziŵa bwanji kuti Yehova amanena zoona?
8 Munthu akadziŵa choonadi sizitanthauza kuti nthaŵi zonse amanena zoona, kapena kuti ndi woona mtima. Mwachitsanzo, Mdyerekezi anasankha ‘kusaima m’choonadi.’ (Yohane 8:44) Mosiyana ndi zimenezo, Yehova ndi “wachoonadi.” (Eksodo 34:6) Malemba nthaŵi zonse amafotokoza kuti Yehova amanena zoona. Mtumwi Paulo ananena kuti “Mulungu sakhoza kunama,” ndiponso anati Mulungu ndi “wosanamayo.” (Ahebri 6:18; Tito 1:2) Kunena zoona ndi mbali yofunika kwambiri ya khalidwe la Mulungu. Tikhoza kudalira ndi kukhulupirira Yehova chifukwa amanena zoona ndipo sanyenga anthu ake okhulupirika.
9. Kodi dzina la Yehova n’logwirizana bwanji ndi choonadi?
9 Dzina la Yehova lenilenilo limasonyeza kuti amanena zoona. Dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Dzina limeneli limasonyeza kuti Yehova m’kupita kwa nthaŵi amakwaniritsa malonjezo ake onse. Palibe wina aliyense amene angathe kuchita zimenezo. Chifukwa chakuti Yehova ndiye Wamkulukulu, palibe chimene chingamulepheretse kukwaniritsa zolinga zake. Yehova amanena zoona, komanso ndi iye yekha amene ali ndi mphamvu ndi nzeru zofunika kuti zonse zimene amanena zichitikedi.
10. (a) Kodi Yoswa anaona bwanji kuti Yehova amanena zoona? (b) Kodi ndi malonjezo ati a Yehova amene inuyo mwaona akukwaniritsidwa?
10 Yoswa anali mmodzi mwa anthu ambiri amene anaona zinthu zochititsa chidwi zosonyeza kuti Yehova amanena zoona. Yoswa anali ku Igupto pamene Yehova anabweretsa miliri khumi m’dziko limenelo, ndipo Yehova ananeneratu za mliri uliwonse usanachitike. Mwa zina, Yoswa anaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti adzaombola Aisrayeli kuwachotsa ku Igupto n’kuwatsogolera kupita ku Dziko Lolonjezedwa, komanso kugonjetsa magulu ankhondo amphamvu a ku Kanani amene amadana nawo. Atatsala pang’ono kumwalira, Yoswa anauza akulu a mtundu wa Israyeli kuti: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.” (Yoswa 23:14) Ngakhale kuti inuyo simunaone zozizwitsa zimene Yoswa anaona, kodi pamoyo wanu mwaona kuti zimene Mulungu amalonjeza n’zoona?
Yehova Sabisa Choonadi
11. Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuuza anthu choonadi?
11 Tayerekezerani kuti pali kholo limene limadziŵa zinthu zambiri koma nthaŵi zambiri sililankhula ndi ana ake. Kodi simukuthokoza chifukwa chakuti Yehova si wotero? Yehova mwachikondi amalankhula ndi anthu, ndipo amatero mosaumira. Malemba amamutcha “Mlangizi Wamkulu.” (Yesaya 30:20, NW) Chifukwa cha kukoma mtima kwake, amayesetsa kulankhula ngakhale ndi anthu amene safuna kumumvetsera. Mwachitsanzo, Ezekieli anauzidwa kuti akalalikire kwa anthu amene Yehova ankadziŵa kuti sakamvetsera. Yehova anati: “Wobadwa ndi munthu iwe, muka, nufike kwa nyumba ya Israyeli, nunene nawo mawu anga.” Ndiyeno anamuchenjeza kuti: ‘Sadzakumvera; pakuti safuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israyeli ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.’ Imeneyo inali ntchito yovuta, koma Ezekieli anaigwira mokhulupirika, ndipo mwa kuchita zimenezo anasonyeza chifundo chimene Yehova ali nacho. Mwina mungakhale ndi ntchito yolalikira yovuta, koma ngati mudalira Mulungu, adzakupatsani mphamvu monga momwe anachitira ndi mneneri Ezekieli.—Ezekieli 3:4, 7-9.
12, 13. Kodi Mulungu walankhula ndi anthu m’njira zotani?
12 Yehova amafuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Iye walankhula kudzera mwa aneneri, angelo, ndipo ngakhale kudzera mwa Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu. (Ahebri 1:1, 2; 2:2) Polankhula ndi Pilato, Yesu anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mawu anga.” Pilato anali ndi mwayi waukulu kwambiri woti akanatha kumva choonadi chonena za njira yopulumutsira anthu imene Yehova anakonza, kuchokera kwa Mwana wa Mulungu weniweniyo mwachindunji. Koma Pilato sanali kumbali ya choonadi, ndipo sanafune kuphunzira kwa Yesu. M’malo mwake, Pilato anayankha monyoza kuti: “Choonadi n’chiyani?” (Yohane 18:37, 38) Zomvetsa chisoni kwambiri! Komabe, anthu ambiri anamvetsera choonadi chimene Yesu analalikira. Kwa ophunzira ake iye anati: “Maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.”—Mateyu 13:16.
13 Yehova wasunga choonadi m’Baibulo ndipo walipereka kwa anthu kulikonse. Baibulo limafotokoza zinthu monga mmene zilili. Limafotokoza za makhalidwe a Mulungu, zolinga zake, ndi malamulo ake, komanso limafotokoza mmene zinthu zililidi pakati pa anthu. Yesu popemphera kwa Yehova anati: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) N’chifukwa chake Baibulo lili buku lapadera. Ndi buku lokhalo limene linalembedwa mouziridwa ndi Mulungu amene amadziŵa zonse. (2 Timoteo 3:16) Baibulo ndi mphatso ya mtengo wapatali kwa anthu, ndipo atumiki a Mulungu amaliyamikira kwambiri. Ndi chinthu chanzeru kuliŵerenga tsiku lililonse.
Gwiritsitsani Choonadi
14. Kodi zinthu zina zimene Yehova wanena kuti adzachita n’ziti, ndipo kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kum’khulupirira?
14 Tiyenera kukhulupirira zimene Yehova amatiuza m’Mawu ake. Mmene iye amadzifotokozera ndi mmene alilidi, ndipo adzachitadi zimene amanena kuti adzachita. Palibe chifukwa choti tisakhulupirire Mulungu. Tiyenera kukhulupirira pamene Yehova akunena kuti adzabweretsa “chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:8) Tiyeneranso kum’khulupirira Yehova pamene akunena kuti amakonda anthu ochita chilungamo, pamene akunena kuti adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene amachita zinthu zosonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro, ndiponso pamene akunena kuti adzachotsa kupweteka, kulira, ngakhale imfa. Yehova anatsimikizira kuti lonjezo lomalizali n’lodalirikadi mwa kulangiza mtumwi Yohane kuti: “Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:4, 5; Miyambo 15:9; Yohane 3:36.
15. Kodi ena mwa mabodza amene Satana amafalitsa ndi ati?
15 Satana amasiyana kotheratu ndi Yehova. M’malo mowaunikira anthu, Satana amawanyenga. Pofuna kukwaniritsa cholinga chake chosiyitsa anthu kulambira koyera, iye amafalitsa mabodza osiyanasiyana. Mwachitsanzo, Satana amafuna kuti ife tizikhulupirira kuti Mulungu satikonda ndiponso kuti kuvutika kumene kuli padziko lapansi pano Mulungu alibe nako ntchito. Koma Baibulo limasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri zolengedwa zake ndipo amadana ndi zinthu zoipa ndiponso kuvutika. (Machitidwe 17:24-30) Satana amafunanso kuti anthu azikhulupirira kuti kuchita zinthu zauzimu n’kutaya nthaŵi. Mosiyana ndi zimenezo, Malemba amatitsimikizira kuti “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” Komanso, Malemba amanena momveka bwino kuti “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”—Ahebri 6:10; 11:6.
16. Kodi n’chifukwa chiyani Akristu ayenera kukhala maso ndiponso kugwiritsitsa choonadi?
16 Ponena za Satana, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino waulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.” (2 Akorinto 4:4) Mofanana ndi Hava, ena amanyengedwa kotheratu ndi Satana Mdyerekezi. Ena amatsatira Adamu, amene sananyengedwe koma mwadala anasankha kukhala wosamvera. (Yuda 5, 11) Choncho, m’pofunika kwambiri kuti Akristu akhale maso ndiponso kuti agwiritsitse choonadi.
Yehova Amafuna ‘Chikhulupiriro Chopanda Chinyengo’
17. Kodi tiyenera kutani kuti Yehova atiyanje?
17 Chifukwa chakuti Yehova amanena zoona nthaŵi zonse, amafunanso kuti anthu amene amamulambira azinena zoona. Wamasalmo analemba kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mu mtima mwake.” (Salmo 15:1, 2) Ayuda amene ankaimba mawu ameneŵa mwachionekere akamatchula phiri lopatulika la Yehova ankakumbukira Phiri la Ziyoni, kumene Mfumu Davide anapititsako likasa la chipangano n’kuliika mu hema amene anamanga pa phiripo. (2 Samueli 6:12, 17) Kutchula phiri ndi hema kunawakumbutsa za malo amene Yehova anali kukhalapo mophiphiritsira. Kumeneko anthu anatha kuyandikira kwa Mulungu n’kumupempha kuti awayanje.
18. (a) Kodi kuti munthu akhale bwenzi la Mulungu amafunika kuchita chiyani? (b) Kodi nkhani yotsatira ifotokoza chiyani?
18 Aliyense amene akufuna kuti akhale bwenzi 1 Timoteo 1:5; Mateyu 12:34, 35) Bwenzi la Mulungu silikhala labodza kapena lachinyengo, chifukwa “munthu . . . wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.” (Salmo 5:6) Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zimayesetsa kunena zoona potsanzira Mulungu wawo. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zimenezi.
la Yehova ayenera kunena zoona “mu mtima mwake,” osati pakamwa pokha. Mabwenzi oona a Mulungu ayenera kukhala oona mtima ndipo ayenera kusonyeza kuti ali ndi ‘chikhulupiriro chopanda chinyengo,’ chifukwa choonadi chimayambira mu mtima. (Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amadziŵa zoona zake za chinthu chilichonse?
• Kodi n’chiyani chimene chimasonyeza kuti Yehova amanena zoona?
• Kodi Yehova wauza ena choonadi motani?
• Pankhani ya choonadi, kodi n’chiyani chimene tikufunika kuchita?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 10]
Mulungu wa choonadi amadziŵa chilichonse chokhudza zinthu zimene analenga
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Malonjezo a Yehova adzakwaniritsidwa