Anali Wokoma Mtima
Anali Wokoma Mtima
MILTON G. HENSCHEL, yemwe wakhala m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali, anamaliza moyo wake wa padziko lapansi Loŵeruka, pa March 22, 2003. Anali ndi zaka 82.
Milton Henschel ali mnyamata, anapita kulikulu la Mboni za Yehova ndipo anatumikira mokhulupirika kwa zaka zoposa 60. Anadziŵika mwamsanga chifukwa cha luntha lake ndi kukonda kwake ntchito yolalikira Ufumu. Mu 1939 anakhala mlembi wa N. H. Knorr, amene panthaŵiyo anali woyang’anira nyumba yosindikizira mabuku ya Mboni za Yehova ku Brooklyn. Mbale Knorr atayamba kutsogolera pakati pa Mboni padziko lonse mu 1942, Mbale Henschel anakhalabe wachiŵiri wake. Mbale Henschel anakwatira Lucille Bennett mu 1956, ndipo anasangalala ndi kuvutikira limodzi pamoyo wawo wonse.
Mbale Henschel anagwira ntchito kwambiri ndi Mbale Knorr mpaka pamene a Knorr anamwalira mu 1977. Mbale Henschel ndi Mbale Knorr anafika m’mayiko oposa 150, kuyendera ndi kulimbikitsa Mboni za Yehova padziko lonse, makamaka amishonale ndi abale amene ali m’maofesi a nthambi. Nthaŵi zina maulendo ameneŵa anali ovuta, ngakhalenso oopsa. Mbale Henschel akuyendera msonkhano wa ku Liberia mu 1963, anazunzidwa mwankhanza chifukwa chokana kuchita nawo mwambo wosonyeza kukonda dzikolo. * Patangotha miyezi ingapo izi zitachitika, Mbale Henschel mosaopa anapitanso ku Liberia kukakambirana ndi pulezidenti wa dzikolo kuti Mboni za Yehova kumeneko zikhale ndi ufulu waukulu wolambira.
Posamalira mavuto akuluakulu, Mbale Henschel anali kudziŵika monga munthu wopereka mfundo zothandiza, sanali woumirira zinthu, ndipo anali wololera. Ogwira naye ntchito anali kumuyamikira kwambiri kuti anali wadongosolo, wodzichepetsa, ndiponso wanthabwala. Popeza anali ndi luso lokumbukira zinthu, anali kusangalatsa amishonale ambiri padziko lonse chifukwa chokumbukira msanga mayina awo, kunena mawu amodzi kapena angapo a m’chinenero cha kumeneko, ndiponso kuseŵerako ndi mawu—zimene anali kuchita mwanthabwala ndithu.
Mika 6:8, amatikumbutsa kuti Yehova Mulungu amafuna kuti ‘tikonde chifundo,’ kapena kuti tikhale okoma mtima. Abale sadzaiŵala chitsanzo chabwino chimene Milton Henschel anapereka pankhani imeneyi. Ngakhale kuti anali ndi udindo waukulu, anali wochezeka, wofatsa, ndi wokoma mtima. Ankakonda kunena kuti, “Ngati mukukayika, kumbukirani kuti chinthu chabwino kuchita ndicho kukoma mtima basi.” Ngakhale kuti tili ndi chisoni chifukwa chotaya mbale wathu wokondedwa ameneyu, tikusangalala kuti anapirira mokhulupirika mpaka mapeto, ali wotsimikiza kulandira mphoto yake, “korona wa moyo.”—Chivumbulutso 2:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Onani 1977 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 171-7.
[Chithunzi patsamba 31]
M. G. Henschel ali ndi N. H. Knorr
[Chithunzi patsamba 31]
Ali ndi mkazi wake, Lucille