Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Yesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi Rute anali chitsanzo chabwino m’njira ziti?

Anali wachitsanzo chabwino posonyeza kukonda Yehova, chikondi chokhulupirika kwa Naomi, ndiponso kulimbikira ntchito komanso kudzichepetsa. M’pake kuti anthu anali kumuona monga “mkazi waulemu.” (Rute 3:11)​—4/15, tsamba 23 mpaka 26.

Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amaganizira anthu wamba?

Iye anauza Aisrayeli, amene anazunzidwa mwankhanza ku Igupto kuti asamasautse anthu wamba. (Eksodo 22:21-24) Yesu amene anatsanzira Atate wake, anasonyeza kuganizira anthu wamba, ndipo anasankha anthu “osaphunzira ndi opulukira [“anthu wamba,” NW]” kukhala atumwi ake. (Machitidwe 4:13; Mateyu 9:36) Tingatsanzire Mulungu mwa kukhala oganizira ena, monga achinyamata.​—4/15, tsamba 28 mpaka 31.

• Kodi n’chifukwa chiyani tikutsimikiza kuti Yehova amaona zimene timachita?

Nkhani za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yehova amaona zochita za anthu. Anaona nsembe imene Abele anapereka, ndipo amaona ‘nsembe zathu zoyamika, chipatso cha milomo.’ (Ahebri 13:15) Yehova anali kudziŵa kuti Enoke anayesetsa kuchita zom’sangalatsa mwa kukhala woyera, ndi wamakhalidwe abwino. Ndipo Mulungu anaona zimene mkazi wamasiye wa ku Zarefati yemwe sanali Mwisrayeli anachita pogaŵira mneneri Eliya zinthu zochepa zimene anali nazo. Yehova amaonanso zochita zathu zosonyeza chikhulupiriro.​—5/1, tsamba 28 mpaka 31.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti pambuyo pa Pentekoste wa mu 33 C.E., Ayuda amene anakhala Akristu anafunika kudzipatulira paokha kwa Mulungu?

Mu 1513 B.C.E., Aisrayeli akale analoŵa mu ubwenzi ndi Yehova chifukwa chokhala anthu odzipatulira kwa iye. (Eksodo 19:3-8) Kuyambira pamenepo, Ayuda anali kubadwira mu mtundu wodzipatulirawo umene unali mu pangano la Chilamulo. Koma Yehova anachotsa pangano la Chilamulo ndi imfa ya Kristu mu 33 C.E. (Akolose 2:14) Kuyambira pamenepo, Ayuda ofuna kutumikira Mulungu moyenera anafunika kudzipatulira kwa iye ndi kubatizidwa mu dzina la Yesu Kristu.​—5/15, tsamba 30 ndi 31.

Kodi kufukiza n’kofunika pa kulambira koona masiku ano?

Kufukiza kunali mbali ya kulambira koona mu Israyeli wakale. (Eksodo 30:37, 38; Levitiko 16:12, 13) Koma pangano la Chilamulo, kuphatikizapo kufukiza, kunathera pa imfa ya Kristu. Akristu angasankhe okha kugwiritsa kapena kusagwiritsa ntchito zofukiza pa zinthu zina zosakhala zachipembedzo, koma si kofunika pa kulambira koona masiku ano. Tiziganiziranso mmene ena angaonere zimenezi kuti tisawakhumudwitse.​—6/1, tsamba 28 mpaka 30.

Kodi ndi nkhani yaposachedwa iti imene yapangitsa anthu ambiri kulingalira mofatsa mfundo yakuti Yesu anakhalapo padziko lapansi?

Anthu anena zambiri zokhudza bokosi lamwala losungiramo mafupa lomwe linapezeka ku Israyeli. Zikuoneka kuti bokosili ndi la m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, ndipo panalembedwa kuti: “Yakobo, mwana wa Yosefe, mbale wa Yesu.” Ena amaona kuti umenewu ndi “umboni wosakhala wa m’Baibulo wakale kwambiri umene ofukula m’mabwinja apeza” wakuti Yesu anakhalako.​—6/15, tsamba 3 ndi 4.

Kodi anthu amaphunzira bwanji kukonda ena?

Anthu amayamba kuphunzira chikondi mwa chitsanzo cha makolo ndi zimene akuphunzitsidwa ndi makolowo. Mwamuna ndi mkazi wake akamasonyeza kuti amakondana komanso amalemekezana, ana amaphunzira kukonda ena. (Aefeso 5:28; Tito 2:4) Ngakhale munthu amene anakulira m’banja mopanda chikondi, angaphunzire chikondi mwa kutsatira malangizo autate a Yehova, mwa kuthandizidwa ndi mzimu woyera, ndiponso mwa kupindula ndi thandizo lachikondi la abale achikristu.​—7/1, tsamba 4 mpaka 7.

Kodi Eusebius anali ndani, ndipo tikuphunzira chiyani pa mbiri ya moyo wake?

Eusebius anali wolemba mbiri wakale amene anamaliza kulemba buku la magawo khumi lakuti History of the Christian Church mu 324 C.E. Ngakhale kuti ankakhulupirira kuti Atate anakhalako Mwana asanakhaleko, Eusebius anavomereza chiphunzitso chosiyana ndi chimenechi pamsonkhano wa ku Nesiya. Mwachionekere ananyalanyaza zimene Yesu ananena kuti otsatira Ake ‘sayenera kukhala a dziko lapansi.’ (Yohane 17:16)​—7/15, tsamba 29 mpaka 31.

Kodi Yehova anasintha maganizo ake pa nkhani ya mitala?

Ayi, Yehova sanasinthe maganizo ake pa nkhani ya mitala. (Malaki 3:6) Mulungu anafuna kuti mwamuna woyamba ‘adziphatike kwa mkazi wake’ ndipo akhale thupi limodzi. (Genesis 2:24) Yesu anati kusudzulana osati chifukwa cha chigololo ndi kukwatira kapena kukwatiwanso, n’kuchita chigololo. (Mateyu 19:4-6, 9) Yehova analeka kulolera mitala pamene mpingo wachikristu unapangidwa.​—8/1, tsamba 28.