Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulambira Koona Kugwirizanitsa Banja

Kulambira Koona Kugwirizanitsa Banja

Kulambira Koona Kugwirizanitsa Banja

MARIA anali ndi zaka 13 pamene iye ndi mng’ono wake, Lucy, anamva za Yehova kwa wachibale wawo. Wachibaleyo anawafotokozeranso kuti tikuyembekeza kuti dziko lapansi lidzakhale Paradaiso. Iwo anachita chidwi ndipo anapita naye ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Maria anachitanso chidwi kwambiri ndi malangizo omveka amene anamva kumeneko. Zinali zosiyana kwambiri ndi kutchalitchi kwawo, kumene nthaŵi yambiri ankangokhalira kuimba nyimbo. Patapita nthaŵi pang’ono, ana aja anayamba kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova.

Mchimwene wawo, Hugo, anali kukonda maphunziro a nzeru za anthu ndi chisinthiko. Iyeyo anali kunena kuti sakhulupirira Mulungu. Koma akugwira ntchito yausilikali, anaŵerenga buku lakuti Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? * Anapeza mayankho a mafunso amene chipembedzo china chilichonse sichikanayankha. Atamaliza ntchito yake yausilikali, anayamba kulimbitsa chikhulupiriro chake chatsopanocho mwa Mulungu. Anachita zimenezo mwa kuphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano ndi azichemwali ake aja. Maria ndi Lucy anabatizidwa mu 1992, patatha zaka ziŵiri kuchokera pamene anamva choonadi, ndipo mchimwene wawoyo anabatizidwa patapita zaka ziŵiri.

Panthaŵiyi makolo awo, omwe anali Akatolika odzipereka, analibe chidwi ndi choonadi. Iwo anali kuona kuti Mboni za Yehova n’zovuta, ngakhale kuti anali kusirira makhalidwe abwino ndi mavalidwe aulemu a Mboni zachinyamata zimene ana awo anali kuziitanira kunyumba kwawo. Ndiponso ana awo akamakambirana zinthu zimene aphunzira kumsonkhano, makolo awo anali kuchita chidwi.

Komabe, makolo awo onse anali kukonda zaufiti. Bambo anali chidakwa ndipo anali kumenya amayi. Banjali linali pafupi kutha. Ndiyeno, bambo anakhala kundende milungu iŵiri chifukwa cha khalidwe loipa limene anachita ataledzera. Ali kundende, anayamba kuŵerenga Baibulo. Akuŵerenga, anapeza mawu a Yesu onena za chizindikiro cha masiku otsiriza. Zimenezi zinawapatsa maganizo kwambiri, ndipo bambo ndi mayi onse anapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo anavomera phunziro la Baibulo lapanyumba. Ataphunzira choonadi, anataya mabuku awo onse a zaufiti ndipo ziwanda zinaleka kuwavutitsa chifukwa choitanira pa dzina la Yehova. Anayamba kusintha makhalidwe awo kukhala abwino kwambiri.

Tangolingalirani momwe Maria ndi Lucy anasangalalira kuonerera makolo awo akubatizidwa ndi Hugo pamsonkhano wachigawo ku Bolivia mu 1999. Nthaŵi imeneyi panali patatha zaka zisanu ndi zinayi kuchokera pamene Maria ndi Lucy anamva za Yehova ndi malonjezo ake. Tsopano ali mu utumiki wa nthaŵi zonse pamodzi ndi Hugo. Amasangalala kwambiri kuti kulambira koona kunagwirizanitsa banja lawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.