Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Momwe Mulungu Amaonera Anthu Akufa

Momwe Mulungu Amaonera Anthu Akufa

Momwe Mulungu Amaonera Anthu Akufa

IMFA ya munthu amene timamukonda imapweteka kwambiri. Munthu umataya mtima kwambiri, umasungulumwa, ndipo umamva kuti wataya winawake wofunika kwambiri. Munthu akafedwa amathedwa nzeru, chifukwa chakuti masiku ano padziko lapansi palibe munthu amene angaukitse wakufa, kaya ali ndi chuma, mphamvu, kapena ulamuliro wotani.

Komabe, Mlengi wathu amaona zinthu mosiyana ndi ife. Popeza anapanga munthu woyamba kuchokera ku fumbi, angathe kulenganso munthu woti anafa kale kukhalanso wamoyo. Pachifukwa chimenechi, Mulungu amaona anthu akufa ngati kuti ali moyo. Ponena za atumiki okhulupirika akale amene anamwalira, Yesu anati: “Onse akhala ndi moyo kwa [Mulungu].” Kunena kwina tingati, Mulungu amawaona onse kuti ndi amoyo.​—Luka 20:38.

Yesu ali padziko lino lapansi, anapatsidwa mphamvu youkitsa akufa. (Yohane 5:21) Choncho, amaona anthu amene anafa ali okhulupirika monga momwe Atate wake amawaonera. Mwachitsanzo, bwenzi lake Lazaro atamwalira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) Kwa anthu, Lazaro anali wakufa, koma kwa Yehova ndi Yesu, anali mtulo.

Mu ulamuliro wa Ufumu wa Yesu, kudzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) M’kupita kwa nthaŵi, oukitsidwawo adzaphunzitsidwa ndi Mulungu ndipo adzayembekezera kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Yohane 5:28, 29.

Inde, imfa ya munthu amene timamukonda ingatisautse maganizo ndiponso ingatiwawe kwambiri, kwa zaka zambiri. Komabe, kuona akufa monga momwe Mulungu amawaonera kungatitonthonze ndiponso kungatipatse chiyembekezo.​—2 Akorinto 1:3, 4.