Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wonse Panthaŵi za Mavuto

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wonse Panthaŵi za Mavuto

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wonse Panthaŵi za Mavuto

“Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.”​—SALMO 46:1.

1, 2. (a) Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti kungonena kuti timakhulupirira Mulungu n’kosakwanira? (b) N’chifukwa chiyani tifunika kuchita zambiri osati kungonena chabe kuti timakhulupirira Yehova?

N’ZOSAVUTA kunena kuti timakhulupirira Mulungu, koma kusonyeza zimenezo mwa zochita zathu m’pamene pagona nkhani. Mwachitsanzo, mawu akuti “Timakhulupirira Mulungu” akhala akuwalemba pa ndalama za pepala ndi zachitsulo za ku United States. * M’chaka cha 1956, nyumba ya malamulo ya ku United States inapereka lamulo lakuti mawu ameneŵa akhale mawu oimira dzikolo. Koma m’malo mokhulupirira Mulungu, anthu ambiri kumeneko komanso padziko lonse, amakhulupirira kwambiri ndalama ndi katundu amene ali naye.​—Luka 12:16-21.

2 Ife monga Akristu oona tifunika kuchita zambiri osati kungonena chabe kuti timakhulupirira Yehova. Monga mmene zilili kuti “chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa,” kunenanso kuti timakhulupirira Mulungu n’kopanda phindu ngati sitisonyeza zimenezo mwa zochita zathu. (Yakobo 2:26) Mu nkhani yapitayo, tinaphunzira kuti timasonyeza kudalira kwathu Yehova mwa kupemphera kwa iye, kufufuza malangizo m’Mawu ake, ndi kutsatira mfundo za m’gulu lake kuti zititsogolere. Tsopano tiyeni tione mmene tingatsatirire njira zitatu zimenezo panthaŵi za mavuto.

Ntchito Ikatithera Kapena Ngati Ndalama Zimene Timapeza N’zochepa

3. Kodi ndi mavuto a zachuma otani amene atumiki a Yehova amakumana nawo mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, ndipo tikudziŵa bwanji kuti Mulungu ndi wokonzeka kutithandiza?

3 Mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, Akristu timakumana ndi mavuto a zachuma amene anthu enanso akukumana nawo. (2 Timoteo 3:1) Motero, ntchito yathu ikhoza kutithera mwadzidzidzi. Kapena sitingachitire mwina koma kugwira ntchito kwa maola ambiri n’kumalandira malipiro ochepa zedi. M’zochitika ngati zimenezi, tingavutike kuti ‘tidzisungire [“tipezere zosoŵa,” NW] mbumba yathu.’ (1 Timoteo 5:8) Kodi Mulungu Wam’mwambamwamba ndi wokonzeka kutithandiza tikakumana ndi zimenezi? Inde. N’zoona kuti Yehova satiteteza m’mavuto onse amene timakumana nawo m’dzikoli. Komabe, ngati timukhulupirira, mawu a pa Salmo 46:1 adzagwira ntchito kwa ife. Mawu ake ndi akuti: “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova ndi mtima wonse m’nthaŵi za mavuto a zachuma?

4. Tikakumana ndi mavuto a zachuma, kodi tingapempherere chiyani, ndipo Yehova amayankha bwanji mapemphero oterowo?

4 Njira imodzi yosonyezera kuti timakhulupirira Yehova ndiyo kupemphera kwa iye. Koma kodi tingapempherere chiyani? Tikakumana ndi mavuto a zachuma tingafunikire nzeru zenizeni kuposa kale. Choncho tiyenera kupempherera nzeruzo! Mawu a Yehova amatitsimikizira kuti: “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzam’patsa iye.” (Yakobo 1:5) Inde, tiyeni tim’pemphe Yehova nzeru, zomwe zimatanthauza kugwiritsa ntchito bwino zimene tikudziŵa, luntha, ndi kuzindikira, kuti tisankhe zochita zoyenera. Atate wathu wachikondi wakumwamba amatitsimikizira kuti adzamva mapemphero oterowo. Iye ndi wokonzeka kuwongola njira ya anthu amene amamukhulupirira ndi mtima wawo wonse.​—Salmo 65:2; Miyambo 3:5, 6.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani tingafufuze m’Mawu a Mulungu thandizo loti tilimbane ndi mavuto a zachuma? (b) Kodi tingachite chiyani kuti tichepetse nkhaŵa ntchito ikatithera?

5 Njira ina yosonyezera kukhulupirira Yehova ndiyo kufufuza malangizo m’Mawu ake. Mfundo zake zotikumbutsa zimene zimapezeka m’Baibulo ‘n’zovomerezeka [“n’zodalirika,” NW].’ (Salmo 93:5) Ngakhale kuti buku louziridwa limeneli anamaliza kulilemba zaka zoposa 1,900 zapitazo, lili ndi malangizo odalirika ndiponso luntha lenileni limene lingatithandize kulimbana bwino ndi mavuto a zachuma. Taonani zitsanzo zina za nzeru za m’Baibulo.

6 Kalekale, Mfumu ya nzeru Solomo inanena mawu aŵa: “Tulo ta munthu wogwira ntchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.” (Mlaliki 5:12) Zimafuna nthaŵi ndi ndalama kuti tikonze, tiyeretse ndiponso titeteze katundu wathu. Motero, ntchito ikatha, tingapezerepo mpata kuonanso moyo wathu, kusiyanitsa zinthu zofunika kwambiri ndi zosafunika kwenikweni. Pofuna kuchepetsa nkhaŵa, kungakhale kwanzeru kusintha zina ndi zina. Mwachitsanzo, kodi n’zotheka kukhala ndi moyo wosalira zambiri, mwina kusamuka n’kumakakhala m’nyumba yaing’onopo kapena kuchotsa katundu wina wosafunikira kwenikweni?​—Mateyu 6:22.

7, 8. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankadziŵa kuti anthu opanda ungwiro amakonda kudera nkhaŵa mopambanitsa zinthu zakuthupi? (Onani mawu a m’munsi.) (b) Kodi Yesu anapereka malangizo anzeru ati ofotokoza mmene tingapeŵere nkhaŵa zosayenerera?

7 Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu analangiza kuti: “Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala.” * (Mateyu 6:25) Yesu ankadziŵa kuti anthu opanda ungwiro mwachibadwa amafuna kukhala ndi zinthu zofunika pa moyo. Koma kodi tingatani kuti ‘tisamadere nkhaŵa’ zinthu zoterozo? Yesu anati: “Muthange mwafuna Ufumu.” Kaya tikukumana ndi mavuto otani, tiyenera kupitiriza kuika patsogolo kulambira Yehova m’moyo wathu. Tikatero, Atate wathu wakumwamba ‘adzatiwonjezera’ zonse zofunika pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. M’njira ina yake, adzatipatsa zimene tikufunikira.​—Mateyu 6:33.

8 Yesu anaperekanso malangizo ena akuti: “Musadere nkhaŵa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhaŵa iwo okha.” (Mateyu 6:34) Si chinthu chanzeru kudera nkhaŵa kwambiri zimene zingachitike mawa. Katswiri wina anati: “Zinthu za m’tsogolo zimene timada nazo nkhaŵa kaŵirikaŵiri sizikhala zoipa kwambiri monga mmene timaganizira.” Kumvera modzichepetsa malangizo a m’Baibulo oti tiike mtima pa zinthu zofunika kwambiri ndiponso kuti zimene tili nazo patsikulo zizitikwanira kungatithandize kupeŵa nkhaŵa zosayenerera.​—1 Petro 5:6, 7.

9. Tikakumana ndi mavuto azachuma, kodi ndi thandizo lotani limene tingalipeze m’zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

9 Tikakumana ndi mavuto azachuma, tingasonyezenso kukhulupirira Yehova mwa kufufuza m’zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti tipeze thandizo. (Mateyu 24:45) Nthaŵi ndi nthaŵi, magazini a Galamukani! afotokoza nkhani zimene zinali ndi malangizo ndi malingaliro othandiza kwambiri polimbana ndi mavuto a zachuma. Nkhani yakuti, “Mutachotsedwa Ntchito Kodi Mankhwala Ake Nchiyani?” ya mu Galamukani! ya August 8, 1991, inafotokoza malangizo opindulitsa asanu ndi atatu amene athandiza anthu ambiri kukhazika mtima pansi ndi kupeza kangachepe akakhala kuti sali pantchito. * Komabe, n’kofunika kugwirizanitsa malangizo amenewo ndi maganizo oyenera pankhani ya kufunika kwenikweni kwa ndalama. Zimenezi anazifotokoza m’nkhani yakuti “Chinachake Chofunika Koposa Ndalama,” imenenso inatuluka m’magazini yomweyo.​—Mlaliki 7:12.

Mukamadwala

10. Kodi chitsanzo cha Mfumu Davide chikusonyeza bwanji kuti ndi nzeru kukhulupirira Yehova tikamadwala kwambiri?

10 Kodi ndi nzeru kukhulupirira Yehova ngati tikudwala kwambiri? Inde! Yehova amamvera chisoni anthu ake amene akudwala. Ndiponso, iye ndi wokonzeka kuwathandiza. Mwachitsanzo, taganizirani Mfumu Davide. Iye ayenera kuti anadwala kwambiri panthaŵi imene analemba mawu ofotokoza mmene Mulungu amachitira ndi munthu wowongoka mtima amene akudwala. Iye anati: “Yehova adzam’gwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.” (Salmo 41:1, 3, 7, 8) Davide anakhulupirirabe Mulungu molimbika, ndipo kenako mfumuyo inachira. Koma kodi tingasonyeze bwanji kudalira Mulungu ngati tikudwala?

11. Tikamadwala, kodi tingapemphe chiyani kwa Atate wathu wakumwamba?

11 Tikamadwala, njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakhulupirira Yehova ndiyo kupemphera kwa iye kuti atithandize kupirira. Tingam’pemphe kuti atithandize kugwiritsa ntchito “nzeru yeniyeni” kuti tifunefune thandizo loti tipeze bwino mogwirizana ndi zimene zingatheke kwa ife. (Miyambo 3:21) Tingamupemphenso kuti atithandize kukhala oleza mtima ndi kupirira polimbana ndi matendawo. Koposa zonse, tifunika kupempha kuti Yehova atithandize, atipatse mphamvu kuti tikhalebe okhulupirika kwa iye ndi kuti tisataye mtima ngakhale patachitika china chilichonse. (Afilipi 4:13) Kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kupulumutsa moyo umene tili nawowu. Ngati tikhalabe okhulupirika, Wopereka Mphoto Wamkulu adzatipatsa moyo ndi thanzi labwino kwamuyaya. (Ahebri 11:6)

12. Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zingatithandize kusankha mwanzeru pankhani ya chithandizo cha mankhwala?

12 Kukhulupirira kwathu Yehova kumatichititsanso kudalira Mawu ake, Baibulo, kuti tipeze malangizo othandiza. Mfundo za m’Malemba zingatithandize kusankha mwanzeru pankhani ya chithandizo chamankhwala. Mwachitsanzo, podziŵa kuti Baibulo limaletsa “nyanga,” tidzapeŵa njira zodziŵira matenda kapena njira zochiritsira zokhudzana ndi mizimu. (Agalatiya 5:19-21; Deuteronomo 18:10-12) Chitsanzo china cha nzeru zodalirika za m’Baibulo ndi ichi: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Motero, poganizira za thandizo la mankhwala, n’kwanzeru kufufuza mfundo zodalirika m’malo ‘mokhulupirira mawu onse.’ “Kuganiza mwanzeru” koteroko kungatithandize kupenda mosamala njira zosiyanasiyana zimene tingatsatire ndi kusankha zochita titadziŵa mfundo zonse.​—Tito 2:12, NW.

13, 14. (a) Kodi ndi nkhani zothandiza ziti zokhudza zaumoyo zimene zafalitsidwa m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! (Onani bokosi patsamba 17) (b) Kodi mu Galamukani! ya February 8, 2001, anafotokozamo malangizo ati okhudza kupirira matenda osatha?

13 Tingasonyezenso kudalira Yehova mwa kufufuza m’zofalitsa za kapolo wokhulupirika. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthaŵi zina afalitsa nkhani zothandiza zokhudza matenda osiyanasiyana. * Nthaŵi zina, magaziniwa afotokoza nkhanizo posimba za anthu amene akwanitsa kulimbana ndi matenda kapena kulumala. Ndiponso, nkhani zina zapereka malingaliro a m’Malemba ndi malangizo othandiza ofotokoza mmene tingapiririre matenda osatha.

14 Mwachitsanzo, Galamukani! ya February 8, 2001, inali ndi nkhani zoyambira pachikuto zakuti “Kulimbikitsa Odwala.” Nkhanizo zinafotokoza mfundo zothandiza za m’Baibulo pamodzinso ndi mfundo zimene anthu amene akudziŵa bwino za matendawo, amene apirira matenda ofooketsa kwa zaka zambiri, anafotokoza atafunsidwa. Nkhani yakuti “Ndi Motani Mmene Mungakhalire Osangalala Ngakhale Mukudwala?” inapereka malangizo akuti: Dziŵani zonse zimene mungathe zokhudza matenda anuwo. (Miyambo 24:5) Khalani ndi zolinga zabwino, kuphatikizapo kukhala ndi cholinga chothandiza ena, koma kumbukirani kuti simungathe kukwaniritsa zolinga zimene ena angakwanitse. (Machitidwe 20:35; Agalatiya 6:4) Peŵani kudzipatula. (Miyambo 18:1) Chitani zoti anthu azisangalala akabwera kudzakuzondani. (Miyambo 17:22) Koposa zonse, khalanibe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso gwirizanani kwambiri ndi mpingo. (Nahumu 1:7; Aroma 1:11, 12) Kodi sitikuyamikira malangizo odalirika amene Yehova amapereka kudzera m’gulu lake?

Ngati Zikutivuta Kugonjetsa Chofooka Chathu

15. Kodi mtumwi Paulo anatha bwanji kupambana nkhondo yake yolimbana ndi zofooka za thupi lopanda ungwiro, ndipo tingakhale ndi chikhulupiriro chotani?

15 Mtumwi Paulo analemba kuti: “M’thupi langa, simukhala chinthu chabwino.” (Aroma 7:18) Paulo anadzionera yekha mmene zimavutira kulimbana ndi zilakolako ndi zofooka za thupi lopanda ungwiro. Komabe, Paulo analinso ndi chikhulupiriro chakuti angapambane. (1 Akorinto 9:26, 27) Motani? Mwa kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse. N’chifukwa chake iye anati: “Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:24, 25) Bwanji ife? Ifenso tikulimbana ndi zofooka za thupi lathu. Pamene tikulimbana ndi zofooka zimenezo, n’zosavuta kutaya mtima, kuganiza kuti sitidzapambana. Koma Yehova adzatithandiza ngati timudalira ndi mtima wonse monga mmene anachitira Paulo, osati kudalira mphamvu zathu zokha.

16. Ngati zikutivuta kugonjetsa chofooka chathu, kodi tifunika kupempherera chiyani, ndipo tiyenera kutani ngati tabwerezanso chofookacho?

16 Ngati zikutivuta kugonjetsa chofooka chathu, tingasonyeze kuti timakhulupirira Yehova mwa kupemphera kwa iye. Tifunika kum’pempha Yehova kuti atithandize ndi mzimu wake woyera. (Luka 11:9-13) Tingam’pemphe mwachindunji kuti atithandize kukhala odziletsa, yomwe ndi mbali ya chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Kodi tiyenera kutani tikabwereza chofookacho? Tisataye mtima. Tisatope ndi kupemphera modzichepetsa kwa Mulungu wathu wachifundo, kum’pempha kuti atikhululukire ndi kutithandiza. Yehova sadzakana mtima “wosweka ndi woswanyika” umene watero chifukwa chodzimva kuti ndi wolakwa. (Salmo 51:17, NW) Ngati timupempha ndi mtima wonse komanso kusonyeza mtima womva wachisoni, Yehova adzatithandiza kulimbana ndi ziyeso.​—Afilipi 4:6, 7.

17. (a) N’chifukwa chiyani kusinkhasinkha mmene Yehova amaonera chofooka chimene tikulimbana nacho kumathandiza? (b) Kodi ndi malemba ati amene tingaloŵeze ngati tikulimbana ndi kupsa mtima msanga? kulamulira lilime lathu? kukonda zosangalatsa zosayenera?

17 Tingasonyezenso kuti timakhulupirira Yehova mwa kufufuza m’Mawu ake kuti tipeze thandizo. Mwakugwiritsa ntchito buku limene limandandalika mawu a m’Baibulo kapena zisonyezero za nkhani za mu Nsanja ya Olonda zimene zimapezeka mu Nsanja ya Olonda ya December 15 chaka chilichonse kapena za mu Galamukani! zimene zimapezeka mu Galamukani! ya December 8, chaka chilichonse, tingafufuze yankho la funso lakuti, ‘Kodi Yehova amamva bwanji ndi chofooka chimene ndikulimbana nacho?’ Kusinkhasinkha mmene Yehova amaionera nkhaniyo kungalimbitse kufunitsitsa kwathu kumusangalatsa. Motero, tidzayamba kuona mmene iye amaonera, kudana ndi zimene iye amadana nazo. (Salmo 97:10) Ena aona kuti kuloŵeza pamtima malemba ena a m’Baibulo amene amafotokoza chofooka chimene akulimbana nacho n’kothandiza. Kodi tikulimbana ndi vuto la kupsa mtima msanga? Ngati ndi choncho, tingaloŵeze malemba monga Miyambo 14:17 ndi Aefeso 4:31. Kodi zimativuta kulamulira lilime lathu? Tingaloŵeze pamtima malemba monga Miyambo 12:18 ndi Aefeso 4:29. Kodi timakonda zosangalatsa zosayenera? Tingayesetse kukumbukira malemba monga Aefeso 5:3 ndi Akolose 3:5.

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola manyazi kutilepheretsa kupempha thandizo kwa akulu kuti tigonjetse chofooka chathu?

18 Njira ina yosonyeza kukhulupirira Yehova ndiyo mwa kupempha thandizo kwa akulu omwe amaikidwa ndi mzimu. (Machitidwe 20:28) Pajatu Yehova kudzera mwa Kristu ndi amene wapereka “zaufulu [“mphatso mwa amuna,” NW]” zimenezi kuti ziteteze ndi kusamalira nkhosa zake. (Aefeso 4:7, 8, 11-14) N’zoona kuti n’kovuta kupempha thandizo polimbana ndi chofooka chinachake. Tingachite manyazi, kuopa kuti akulu azindikira kufooka kwathu. Koma mosakayika, amuna okhwima mwauzimu ameneŵa adzatilemekeza chifukwa cholimba mtima kupempha thandizo. Ndiponso, akulu amayesetsa kusonyeza makhalidwe a Yehova posamalira nkhosa. Mwina zingakhale kuti malangizo awo olimbikitsa ndiponso othandiza a m’Mawu a Mulungu ndi amene tikufunikira kuti titsimikize mtima kugonjetsa chofooka chathu.​—Yakobo 5:14-16.

19. (a) Kodi Satana amafuna kugwiritsa ntchito motani kupanda pake kwa moyo m’dziko lino? (b) Kodi kukhulupirira Yehova kumafuna chiyani, ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

19 Musaiwale kuti Satana akudziŵa kuti nthaŵi yake yatsala pang’ono. (Chivumbulutso 12:12) Akufuna kugwiritsa ntchito kupanda pake kwa moyo m’dzikoli pofuna kutifooketsa ndi kutitayitsa mtima. Tiyeni tikhulupirire kwambiri mawu amene ali pa Aroma 8:35-39, omwe amati: “Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zowopsa kapena lupanga kodi? . . . Koma m’zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda. Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Ameneŵatu ndi mawu osonyeza kukhulupirira Yehova! Komabe, kukhulupirira Yehova kumeneko sikutanthauza kungomva bwino mumtima chabe ayi. M’malo mwake, kumatanthauza kukhulupirira kumene kumafuna kuti tikamasankha zochita pa moyo wathu tsiku ndi tsiku, tizisankha mwanzeru. Ndiyetu tiyeni titsimikize mtima kwambiri kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse m’nthaŵi za mavuto.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 M’kalata imene analemba pa November 20, 1861, yopita komwe amapanga ndalama zachitsulo ku United States, Nduna ya Zachuma a Salmon P. Chase anati: “Kuti dziko likhale lamphamvu liyenera kudalira mphamvu za Mulungu, ndipo lingakhale lotetezeka ngati Iye aliteteza. Anthu athu amakhulupirira Mulungu ndipo tiyenera kusonyeza zimenezi pa ndalama zachitsulo za dziko lathu.” Chifukwa cha zimenezi, mu 1864 anayamba kulemba mawu akuti “Timakhulupirira Mulungu” pa ndalama zachitsulo za ku United States.

^ ndime 7 Nkhaŵa imene aifotokoza panoyi akuti ndiyo “nkhaŵa yobwera chifukwa cha mantha, imene imamuchotsera munthu chimwemwe chonse.” Kunena kuti “musadere nkhaŵa” kukukhala ngati zikutanthauza kuti sitiyenera kuyamba kuda nkhaŵa. Koma buku lina laumboni limati: “Verebu la Chigirikilo ndi lamulo losonyeza kuti zinthuzo zichitike nthaŵi yomwe ino, kusonyeza kulamula kuti munthu asiye kuchita chinachake chimene wayamba kale kuchichita.”

^ ndime 9 Mfundo zisanu ndi zitatu zimene anazitchula m’nkhaniyo ndi izi: (1) Musakhale Wosakhazikika Mtima; (2) Khalani ndi Maganizo Abwino; (3) Tsegulani Maganizo Anu ku Mitundu Yatsopano ya Ntchito; (4) Dalirani pa Ndalama Zimene Mumapeza​—Osati za Wina; (5) Chenjerani ndi Ngongole; (6) Lisungeni Banja Kukhala Logwirizana; (7) Sungani Ulemu Wanu Waumwini; (8) Pangani Bajeti.

^ ndime 13 Magazini ofotokoza za m’Baibulo ameneŵa salimbikitsa mankhwala a mtundu wina uliwonse chifukwa imeneyi ndi nkhani imene munthu amasankha yekha chochita. M’malo mwake, cholinga cha nkhanizi n’kudziŵitsa anthu amene amaŵerenga magaziniwa mfundo zokhudza matendawo malinga ndi mmene anthu akuzidziŵira pakalipano.

Kodi Mukukumbukira?

• Tikakumana ndi mavuto a zachuma, kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Mulungu ngati tikudwala?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira kwambiri Yehova ngati zikutivuta kugonjetsa chofooka chathu?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 17]

Kodi Mukukumbukira Nkhani Izi?

Tikamavutika maganizo chifukwa cha matenda, zimakhala zolimbikitsa kuŵerenga nkhani za anthu amene akwanitsa kulimbana ndi matenda kapena kulumala. Nkhani zotsatirazi ndi zina mwa nkhani zimene zinafalitsidwa m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

“Kuchita ndi Zofooka Zanga,” nkhani imene inatsindika vuto loona chilichonse ngati choipa ndiponso kuvutika maganizo.​—Nsanja ya Olonda, May 1, 1990.

“Ngakhale Ndili Wolumala Ndine Wosangalala.”​—Galamukani!, December 8, 2000.

“Chipolopolo Chinasintha Moyo Wanga,” nkhani imene ikunena za kupuwala.​—Galamukani!, November 8, 1995.

“Simudziŵa Chimene Chidzagwa Maŵa,” nkhani imene ikufotokoza za kulimbana ndi matenda a kusokonezeka maganizo.​—Nsanja ya Olonda, December 1, 2000.

“Loida Ayamba Kulankhula,” nkhani imene ikufotokoza za matenda aubongo amene amakhudza ziwalo za thupi otchedwa cerebral palsy.​Galamukani!, May 8, 2000.

“Ngakhale Ndili Wakhungu Ndili Wofunika ndi Wachimwemwe.”​—Galamukani!, February 8, 1999.

“Kutumikira Ena Kumachepetsa Mavuto,” nkhani imene ikufotokoza za kulimbana ndi matenda okhudza ubongo otchedwa multiple sclerosis.​Nsanja ya Olonda, July 1, 2003.

“Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka.”​—Galamukani!, August 8, 2002.

[Chithunzi patsamba 15]

Ntchito yathu ikatithera, kungakhale kwanzeru kuonanso moyo wathu

[Chithunzi patsamba 16]

Nkhani ya Loida ikusonyeza mmene kukhulupirira Yehova kumathandizira munthu kupirira. (Onani bokosi pa tsamba 17)

[Chithunzi patsamba 18]

Sitifunika kuchita manyazi kupempha thandizo kuti tigonjetse zofooka zathu