Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Kuti Okhulupirira Achikulire ndi Ofunika Kwambiri?

Kodi Mumaona Kuti Okhulupirira Achikulire ndi Ofunika Kwambiri?

Kodi Mumaona Kuti Okhulupirira Achikulire ndi Ofunika Kwambiri?

PANTHAŴI imene anthu a mtundu wakale wa Israyeli anali pa pangano ndi Mulungu, anawalamulira kuti: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako.” (Levitiko 19:32) Choncho, kulemekeza achikulire kunali ntchito yopatulika, yogwirizana ndi kugonjera Mulungu. Ngakhale kuti panopa Akristu sakutsatiranso Chilamulo cha Mose, Chilamulocho chimatikumbukutsa kuti Yehova amaona kuti achikulire amene amamutumikira ndi ofunika kwambiri. (Miyambo 16:31; Ahebri 7:18) Kodi ifenso timawaona ngati mmene Yehova amawaonera? Kodi timaona kuti abale ndi alongo athu achikristu ndi ofunika kwambiri?

Anaona Kuti Mnzake Wachikulireyo Anali Wofunika Kwambiri

Nkhani inayake ya m’Baibulo imene imasonyeza munthu akuchitira ulemu munthu wina wachikulire ili m’buku la 2 Mafumu. Imafotokoza mmene mneneri Eliya anasiyira ntchito yake kwa mneneri wachinyamatayo, Elisa. Taonani zimene zinachitika tsiku lomaliza la Eliya kukhala mneneri mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi.

Tsiku limenelo, Yehova anauza mneneri wachikulireyo kuti ayende kuchoka ku Giligala kupita ku Beteli, kuchoka ku Beteli kupita ku Yeriko, ndi kuchoka ku Yeriko kupita ku mtsinje wa Yordano. (2 Mafumu 2:1, 2, 4, 6) Pa ulendo wa makilomita pafupifupi 50 umenewo, Eliya anauza Elisa katatu konse kuti asiye kumulondola. Koma, mofanana ndi mmene Rute yemwe anali wachitsikana anakanira kusiya Naomi zaka mazana angapo m’mbuyomo, Elisa anakana kusiya mneneri wachikulireyo. (Rute 1:16, 17) Katatu konse Elisa anati: “Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani.” (2 Mafumu 2:2, 4, 6) Pa nthaŵi imeneyo n’kuti Elisa atathandiza kale Eliya kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Komabe, iye anafuna kutumikira limodzi ndi Eliya kwa nthaŵi yonse imene akanatha kutero. Inde, nkhaniyo ikupitiriza kunena kuti: “Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, . . . Eliya [a]nakwera kumwamba.” (Vesi 11) Eliya ndi Elisa anali kukambirana mpaka pamapeto penipeni pa utumiki wa Eliya mu Israyeli. Mwachionekere, mneneri wachinyamatayo anali wofunitsitsa kumvetsetsa malangizo ndi mawu onse olimbikitsa amene akanatha kumva amene mneneri wachikulire ndi wanzeruyo anali kulankhula. Zoonadi, anaona kuti mnzake wachikulireyo anali wofunika kwmbiri.

‘Ngati Atate ndi Amayi’

N’zosavuta kuona chifukwa chimene Elisa anakondera mneneri wachikulireyo monga mnzake, komanso, monga atate ake auzimu. (2 Mafumu 2:12) Utumiki wa Eliya mu Israyeli utangotsala pang’ono kutha, iye anati kwa Elisa: “Tapempha chimene ndikuchitire ndisanachotsedwe kwa iwe.” (Vesi 9) Choncho, mpaka kufika pamapeto, Eliya anadera nkhaŵa moyo wauzimu wa wotsatira wake komanso anali wofunitsitsa kuti ntchito ya Mulungu ipitirirebe.

Masiku ano, n’zosangalatsa kuona kuti abale ndi alongo athu achikulire achikristu ali ndi mtima ngati womwewo wotidera nkhaŵa ngati atate ndi amayi athu ndipo amagaŵira achinyamata zinthu zimene akudziŵa komanso nzeru zawo mosaumira. Mwachitsanzo, anthu ongodzipereka amene akhala akutumikira pa maofesi a nthambi a Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali, mwaufulu amathandiza anthu ongobwera kumene pa banja la Beteli kuti adziŵe bwino ntchito yawo. Chimodzimodzinso oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo amene akhala akuyendera mipingo kwa zaka zambiri amasangalala kugaŵana zinthu zochuluka zimene akudziŵa ndi anthu amene akuwaphunzitsa ntchito yoyendayenda. Ndiponso, m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, muli abale ndi alongo achikulire amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri amene amagaŵana nzeru zawo zothandiza komanso zinthu zimene akudziŵa ndi anthu atsopano mu mpingo.​—Miyambo 2:7; Afilipi 3:17; Tito 2:3-5.

Nkhaŵa imene Akristu achikulire okondedwa ameneŵa amakhala nayo pa ife imatichititsa kuti tiziwasonyeza ulemu mosangalala. Choncho, tikufuna kutsanzira chitsanzo cha Elisa choona okhulupirira achikulire ngati anthu ofunika kwambiri. Monga mmene mtumwi Paulo anatikumbutsira, tiyeni tipitirize kuona “mkulu . . . ngati atate” ndi “akazi aakulu ngati amayi.” (1 Timoteo 5:1, 2) Tikamatero timathandiza kuti mpingo wachikristu padziko lonse uziyenda bwino ndiponso uzipita patsogolo.

[Chithunzi patsamba 30]

Elisa anafuna kutumikira ndi Eliya kwa nthaŵi yonse imene akanatha kutero

[Zithunzi patsamba 31]

Achinyamata amathandizidwa kwambiri ndi Akristu achikulire