Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali ‘Mpingo Woona’ Umodzi Wokha?

Kodi Pali ‘Mpingo Woona’ Umodzi Wokha?

Kodi Pali ‘Mpingo Woona’ Umodzi Wokha?

“MONGA momwe zilili kuti pali Kristu mmodzi, palinso thupi limodzi la Kristu, Mkwatibwi mmodzi wa Kristu: ‘mpingo umodzi wokha wa Chikatolika ndi wa atumwi.’”​—Chinatero chikalata chotchedwa Dominus Iesus.

Mmenemu ndi mmene kadinala wa Roma Katolika, Joseph Ratzinger anafotokozera chiphunzitso cha mpingo wake choti payenera kukhala mpingo umodzi wokha woona. Iye anati mpingo umenewo ndi “Mpingo wa Kristu umodzi, umene ndi Mpingo wa Katolika.”

“Si Mipingo Yeniyeni”

Ngakhale kuti Papa Yohane Paulo wachiŵiri analimbikira kunena kuti m’chikalata chotchedwa Dominus Iesus munalibe mawu “odzitukumula, kapena onyoza zipembedzo zina,” atsogoleri a mipingo ya Chipulotesitanti anaipidwa nacho kwambiri chikalatacho. Mwachitsanzo, pa msonkhano wa Presbyterian General Assembly ku Belfast, Northern Ireland, mu June 2001, mtsogoleri wina wachipembedzo ananena kuti chikalatacho chinalembedwa ndi “kagulu kenakake kamphamvu ka mu mpingo wa Roma Katolika . . . kamene kanachita mantha ndi mtima wololera maganizo a ena umene msonkhano wachiŵiri wa Vatican unakhazikitsa.”

Bishopu wamkulu wa mpingo wa Church of Ireland, dzina lake Robin Eames anati angakhale “wokhumudwa kwambiri ngati chikalatacho chikanayambitsanso maganizo amene Akatolika anali nawo msonkhano wachiŵiri wa Vatican usanachitike.” Poyankhapo pa zomwe ananena pa msonkhanowo zoti mipingo imene imatsutsa ziphunzitso zina za Chikatolika “si mipingo yeniyeni,” Eames anati: “Kwa ine chimenecho n’chipongwe.”

Kodi n’chiyani chinachititsa kuti chikalata cha Dominus Iesus chilembedwe? Zikuoneka kuti atsogoleri a Roma Katolika sanasangalale ndi maganizo akuti zikhulupiriro zachipembedzo zimasinthasintha, malinga ndi mmene munthu kapena gulu la anthu likuzionera. Malinga ndi zimene nyuzipepala ya The Irish Times inanena, “kuyambika kwa maganizo akuti zipembedzo zonse n’zabwino . . . kunadetsa nkhaŵa Kadinala Ratzinger.” Zikuoneka kuti malingaliro ameneŵa ndi amene anam’chititsa kunena kuti pali mpingo umodzi woona.

Kodi Nkhani ya Mpingo Umene Muli Ndi Yofunika Kwambiri?

N’zoona kuti kwa ena, mfundo yoti “zipembedzo zonse n’zabwino” ndi yomveka ndiponso ndi yokopa kusiyana ndi malingaliro akuti payenera kukhala mpingo umodzi wokha woona. Kwa anthu otero, chipembedzo chiyenera kukhala nkhani ya mmene munthu amaonera payekha. Iwo amati, ‘tikaona mfundo zonse, tipeza kuti zilibe kanthu kuti munthu uli mu mpingo uti.’

Amenewo angaoneke ngati maganizo omva za ena ngakhale kuti zimenezi zachititsa kuti pakhale kugaŵanika kwa chipembedzo komwe kwachititsa kuti pakhale mipingo yambiri yosiyanasiyana. Anthu ambiri amati ‘kuchuluka kwa zipembedzo kumeneku kwangokhala njira yabwino yosonyezera ufulu wa anthu.’ Komabe, wolemba nkhani wotchedwa Steve Bruce anati, “kulolera maganizo a ena pa nkhani ya chipembedzo kumeneku” kwenikweni ndi “kusachita chidwi ndi chipembedzo.”​—Buku lotchedwa A House Divided: Protestantism, Schism, and Secularization.

Kodi pamenepa maganizo olondola ndi ati? Kodi pali mpingo woona umodzi wokha? Kodi mpingo woona umodzi wokha umenewo ndi wa Roma Katolika? Kodi mipingo inanso ndi yovomerezeka kwa Mulungu? Popeza kuti mafunso ameneŵa amakhudza unansi wathu ndi Mlengi wathu, n’kofunika kwambiri kudziŵa malingaliro ake pa nkhani imeneyi. Kodi tingachite bwanji zimenezo? Mwa kufufuza m’Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo. (Machitidwe 17:11; 2 Timoteo 3:16, 17) Tiyeni tione zimene limanena pa nkhani imeneyi ya mpingo umodzi woona.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

PACHIKUTO: Mark Gibson/​Index Stock Photography