Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”

Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”

Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”

YEHOVA anakonza zoti anthu ake azikhala ndi misonkhano yachikristu kuti akhale olimba mwauzimu. Mwa kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse, timasonyeza kuti timayamikira zimene Yehova watikonzera. Komanso, imatithandiza ‘kufulumiza [abale athu] ku chikondano ndi ntchito zabwino,’ imene ili njira yofunika kwambiri yosonyezera kuti timakondana. (Ahebri 10:24; Yohane 13:35) Koma, kodi tingalimbikitse bwanji abale athu pa misonkhano?

Lankhulani Pagulu

Mfumu Davide, pofotokoza za iye mwini, analemba kuti: “Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga: pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani. Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu.” “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu: m’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.” “Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga.”​—Salmo 22:22, 25; 35:18; 40:9.

Mu nthaŵi ya mtumwi Paulo, Akristu akasonkhana pamodzi kuti alambire Mulungu nawonso amalankhula za chikhulupiriro chawo mwa Yehova ndiponso za ulemerero wake. Mwa kuchita zimenezi anafulumizana ndi kulimbikitsana ku chikondano ndi ntchito zabwino. Masiku ano, zaka mazana ambiri kuchokera pa nthaŵi ya Davide ndi Paulo, ‘tikuonadi tsiku [la Yehova] lili kuyandikira.’ (Ahebri 10:24, 25) Dziko la Satana latsala pang’ono kuonongedwa, ndipo mavuto akungoonjezereka. Kuposa kale lonse, ‘chitisoŵa [“tikufunika,” NW] chipiriro.’ (Ahebri 10:36) Kodi ndi ndaninso kuposa abale athu amene angatilimbikitse kuti tipirire?

Masiku ano, monga mmene zinthu zinalili kale, anthu okhulupirira amapatsidwa mwayi woti azitha kulankhula za chikhulupiriro chawo “pakati pa msonkhano.” Aliyense ali ndi mwayi woyankha mafunso amene amafunsidwa kwa omvetsera pa misonkhano ya mpingo. Musamapeputse mphamvu ya ndemanga zimenezi. Mwachitsanzo, ndemanga zimene zimasonyeza zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto kapena tiwapeŵe zimalimbikitsa abale kuti apitirizebe kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ndemanga zofotokoza malemba a m’Baibulo amene atchulidwa koma sanawagwire mawu pandimepo, kapena zofotokoza mfundo zimene munthu wapeza atachita kafukufuku payekha, zingalimbikitse ena kukulitsa chizoloŵezi chophunzira paokha.

Kudziŵa kuti ifeyo komanso ena adzapindula ngati tipereka ndemanga pa misonkhano kuyenera kulimbikitsa Mboni za Yehova zonse kugonjetsa mantha kapena manyazi. N’zofunika kwambiri kuti makamaka akulu ndi atumiki otumikira azipereka ndemanga pa misonkhano, chifukwa amayenera kutsogolera poyankha ndi popezeka pa misonkhano. Koma kodi munthu angapite patsogolo bwanji ngati akuona kuti mbali imeneyi ya chikristu chake imam’vuta?

Njira Zimene Zingakuthandizeni Kupita Patsogolo

Kumbukirani kuti kuyankha pa misonkhano n’kulambiranso Yehova. Mlongo wina wachikristu amene amakhala ku Germany akufotokoza mmene amaonera ndemanga zake. “Ndi yankho langalanga lotsutsa Satana amene amafuna kulepheretsa anthu a Mulungu kunena za chikhulupiriro chawo.” Mbale wina amene wangobatizidwa kumene wa mu mpingo womwewo anati: “Kuti ndiziyankha pa misonkhano, ndimapemphera kwambiri.”

Konzekerani bwino. Ngati simuŵerengeratu nkhaniyo musanapite ku misonkhano, mudzavutika kuti muyankhe ndipo ndemanga zanu sizidzakhala zogwira mtima. Mfundo zothandiza poyankha pa misonkhano mungazipeze m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, pa tsamba 70. *

Khalani n’cholinga choti musalephere kupereka ndemanga pa msonkhano uliwonse. Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kukonzekeratu kukayankha mafunso angapo, chifukwa chakuti mukamakweza dzanja lanu pafupipafupi, n’zosavuta kuti mbale amene akuchititsa msonkhanowo akutchuleni. Mwina mungamuuziretu mafunso amene mwakonzekera kuyankha. Zimenezi zimathandiza makamaka ngati mukungoyamba kumene kuyankha pa misonkhano. Popeza mungamakayikire kuti mukweze dzanja lanu “mu msonkhano waukulu,” kudziŵa kuti iyi ndi ndime yanu ndipo amene akuchititsa msonkhanoyo akuyang’anayang’ana dzanja lanu, zingakulimbikitseni kuyankha.

Yankhani kumayambiriro. Ntchito yovuta sikuti imasanduka yofeŵerapo mukamangoisunga n’kumati mudzaigwira m’tsogolo. Kuyankha kumayambiriro pa msonkhano kungakuthandizeni. Mukhoza kudabwa kuona mmene zimakhalira zosavuta kuyankhanso kachiŵiri kapena kachitatu mukangothana ndi vuto lopereka ndemanga yoyamba.

Khalani pabwino. Ena amaona kuti zimakhala zosavuta kuti ayankhe akakhala kutsogolo m’Nyumba ya Ufumu. Kumakhala zododometsa zochepa ndipo amene akuchititsa msonkhanowo angawaone n’kuwatchula mosavutikira kuti ayankhe. Ngati muchita zimenezi, kumbukirani kulankhula mokweza bwino kuti aliyense amve, makamaka ngati mu mpingo wanu simugwiritsa ntchito maikolofoni poyankha.

Mvetserani mwatcheru. Zimenezi zidzakuthandizani kupeŵa kunena zimene wina wanena kale. Komanso, ndemanga za ena zingakukumbutseni lemba kapena mfundo imene mungaonjezere pa zimene zangonenedwazo. Nthaŵi zina, mungafotokoze zimene zinachitikira inuyo kapena munthu wina kuti musonyeze mfundo ya zimene mukukambiranazo. Ndemanga zotero n’zothandiza kwambiri.

Phunzirani kuyankha m’mawu anuanu. Kuŵerenga yankho lochokera pa nkhani imene mukuphunzirayo kungasonyeze kuti mwapeza yankho lolondola, ndipo kungakhale njira yabwino yothandiza amene akungoyamba kumene kuyankha pa misonkhano. Koma kuyankha m’mawu anuanu kumasonyeza kuti mwamvetsa mfundoyo. Sitifunikira kunena zinthu ndendende mmene zalembedwera m’mabuku athu. Mboni za Yehova sizimangobwereza zimene mabuku awo amanena.

Muziyankha zogwirizana ndi nkhaniyo. Mayankho osakhudzana ndi nkhaniyo kapena onena zina zosemphana ndi mfundo yaikulu ya nkhani imene mukukambiranayo ndi osayenera. Zimenezi zikutanthauza kuti mayankho anu azikhala ogwirizana ndi nkhani imene mukukambirana. Zikatero ndiye kuti mudzaonjezerapo kanthu kena pa mfundo imene mukukambiranayo ndipo mudzalimbikitsa anthu mwauzimu.

Khalani n’cholinga choti mulimbikitse ena. Chifukwa chakuti cholinga chachikulu choperekera ndemanga n’chakuti tilimbikitse ena, tiyenera kupeŵa kunena zinthu zimene zingawakhumudwitse. Komanso, musamanene mfundo zonse zimene zili pandimepo popanda kusiya kanthu kena koti ena anenepo, kapena kungowasiyira zochepa zokha. Mayankho aatali kapena ozungulirazungulira amavuta kuwamvetsetsa. Mayankho aafupi ongokhala ndi mawu ochepa okha angakhale ogwira mtima kwambiri, ndipo amalimbikitsa anthu atsopano kuti nawonso apereke ndemanga zawo zazifupi zimene akonzekera.

Udindo wa Ochititsa Misonkhano

Pa nkhani yolimbikitsa ena, amene akuchititsa msonkhano ali ndi udindo waukulu. Amasonyeza kuti ali ndi chidwi ndi ndemanga iliyonse imene ikuperekedwa mwa kumvetsera mwatcheru komanso kumuyang’ana munthu amene akuyankhayo m’malo motanganidwa ndi zinthu zina. Zingakhale zosayenera kwambiri ngati atapanda kumvetsera mwatcheru n’kubwerezanso kunena zinthu zimene munthu wina wangomaliza kunena kapena kufunsa funso limene munthu wangomaliza kuyankha!

Zingakhalenso zofooketsa ngati munthu wochititsayo nthaŵi zonse amabwerezanso kunena m’mawu osiyanako pang’ono zimene munthu wina wangonena kumene, ngati kuti akufuna asonyeze kuti yankholo likupereŵera penapake. Koma zimakhala bwino kwambiri ngati ndemanga zikulimbikitsa ena kunena zinthu zina zoonjezera pa mfundo inayake yofunika. Mafunso amene amathandiza anthu kupereka ndemanga zabwino, zimene zimalimbikitsa kwambiri ndi monga aŵa: ‘Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo imeneyi mu mpingo wathu uno?’ kapena, ‘Kodi ndi lemba liti pandimepo limene likugwirizana ndi zimene anena posachedwazo?’

Inde, makamaka anthu atsopano kapena amanyazi muyenera kuwayamikira akayankha. Mungachite zimenezi munthuyo ali yekha mukamaliza phunzirolo kuti asachite manyazi komanso kuti mukhale ndi mpata wom’patsa munthuyo malangizo ena ngati pangafunikire kutero.

Anthu akamacheza, munthu amene amangofuna kulankhula yekha amafooketsa anzake kuti asalankhulepo. Omvetsera akewo saonanso chifukwa choti anenepo maganizo awo. Samvetsera ndi mtima wonse ndipo mwina samvetsera kumene. Zinthu ngati zimenezi zingachitikenso ngati wochititsa msonkhano akulankhula pafupipafupi. Komabe, wochititsa msonkhano nthaŵi zina angalimbikitse anthu amene ali pa msonkhanopo kuti ayankhe komanso kuwathandiza kuganizapo pa nkhani imene mukukambiranayo mwa kufunsa mafunso oonjezera. Mafunso oterowo azikhala ochepa.

Wochititsayo sayenera nthaŵi zonse kutchula munthu amene wayambirira kukweza dzanja lake. Kuchita zimenezo kungafooketse anthu amene amafunikira nthaŵi yochulukirapo kuti aganize mmene angayankhire. Akadikira pang’ono, wochititsayo angapereke mwayi kwa munthu wina amene sanayankhepo kuti ayankhe. Ayeneranso kuchita zinthu mwanzeru popeŵa kutchula ana kuti ayankhe funso lokhudzana ndi nkhani imene sangaimvetsetse.

Nanga bwanji munthu akapereka yankho lolakwa? Wochititsayo ayenera kupeŵa kuchititsa manyazi munthu amene wayankhayo. Ngakhale pamene ndemanga si yolondola, nthaŵi zambiri imakhala ndi mbali zina zoona. Mwa kusankhapo mawu ena amene ali olondola, kufunsanso funsolo m’mawu ena, kapena kufunsa funso lina, wochititsayo angakonze yankholo popanda kuchititsa munthu manyazi.

Pofuna kulimbikitsa anthu kuti ayankhe, wochititsayo azipeŵa kufunsa mafunso amene sakusonyeza mfundo yeniyeni imene akufuna, monga funso lakuti, ‘Kodi pali winanso amene ali ndi ndemanga?’ Funso lakuti ‘Ndani amene sanayankhepo? Uwu ndi mwayi wanu wotsiriza!’ mwina mungalifunse n’cholinga chabwino, koma sililimbikitsa munthu kupereka maganizo ake momasuka. Simuyenera kuwapangitsa abale kumva ngati achita chinthu cholakwa chifukwa chosayankha kumayambiriro kwa phunzirolo. M’malo mwake, muyenera kuwalimbikitsa kuti agaŵane ndi anzawo zimene akudziŵa, chifukwa kugaŵana zinthu ndi ena kumasonyeza chikondi. Ndiponso, wochititsayo akatchula munthu kuti ayankhe, zingakhale bwino kuti asamanene kuti, “Akatha ameneŵa, timva ndemanga ya Mbale uje, kenaka ya Mlongo uje.” Wochititsayo choyamba ayenera kumvetsera ndemangayo ndiyeno n’kuona ngati pangafunike ndemanga ina yoonjezerapo.

Kuyankha pa Misonkhano Ndi Mwayi Wapadera

Kupezeka pa misonkhano yachikristu n’kofunika kwambiri pa moyo wathu wauzimu, ndipo kuyankha pa misonkhano imeneyi ndi mwayi wapadera. Tikamatenga nawo mbali m’njira yapadera imeneyi yotamandira Yehova “pakati pa msonkhano,” ndiye kuti tikutsatira chitsanzo cha Davide ndiponso tikumvera malangizo a Paulo. Kuyankha pa misonkhano kumasonyeza kuti timakonda abale athu ndipo kumasonyezanso kuti ndife mbali ya mpingo waukulu wa Yehova. Kodi n’kutinso kumene mungafune kukhala pamene “muona tsiku lili kuyandikira” koposa pa misonkhano yachikristu?​—Ahebri 10:25.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 20]

Kumvetsera ndi kuyankha n’zofunika pa misonkhano yachikristu

[Chithunzi patsamba 21]

Amene akuchititsa msonkhano amasonyeza kuti ali ndi chidwi ndi ndemanga iliyonse