Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatisamalira Nthaŵi zonse

Yehova Amatisamalira Nthaŵi zonse

Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Amatisamalira Nthaŵi zonse

YOSIMBIDWA NDI ENELESI MZANGA

Munali m’chaka cha 1972 pamene anyamata khumi, a m’gulu la Malawi Youth League (mayufi) analoŵa m’nyumba mwathu, n’kundigwira, ndipo anandikokera m’dimba la nzimbe limene linali chapafupi. Kumeneko, anandimenya n’kundisiya ndili thapsa poganiza kuti ndafa.

Anthu a Mboni za Yehova ambiri ku Malawi anawachitira nkhanza ngati zimenezi. Kodi ankazunzidwa chifukwa chiyani? N’chiyani chinawathandiza kuti apirire? Ndiloleni kuti ndikufotokozereni mbiri ya banja langa.

NDINABADWA pa December 31, 1921, m’banja lopembedza. Bambo anga anali abusa a mpingo wa Church of Central African Presbyterian [C.C.A.P]. Ndinakulira ku Nkhoma, katauni kakang’ono kufupi ndi mzinda wa Lilongwe umene uli likulu la dziko la Malawi. Nditakwanitsa zaka 15, ndinakwatiwa ndi a Emmas Mzanga.

Tsiku lina anzawo a bambo anga, amenenso anali abusa, anabwera kunyumba kwathu. Anali ataona kuti Mboni za Yehova zimakhala pafupi ndi nyumba yathu ndipo anabwera kudzatichenjeza kuti tisamacheze nazo. Anatiuza kuti Amboniwo anali ndi ziwanda ndipo ngati sitisamala nafenso tidzaloŵedwa ziwanda. Chenjezo limenelo linatiopsa kwambiri moti tinasamuka n’kukakhala ku mudzi wina, kumene a Emmas anapeza ntchito yogulitsa m’sitolo. Koma pasanapite nthaŵi yaitali tinadzazindikira kuti nyumba yathu yatsopanoyo inalinso pafupi ndi Mboni za Yehova!

Koma patangopita nthaŵi yochepa, a Emmas, amene anali munthu wokonda Baibulo kwambiri, analankhula ndi mmodzi mwa anthu Amboniwo. Atapeza mayankho omveka bwino a mafunso ambirimbiri amene anali nawo, a Emmas anavomera kuti Amboniwo aziphunzira nawo Baibulo. Poyamba ankachitira phunziro la Baibulolo ku sitolo kumene a Emmas ankagwira ntchito, koma kenaka anayamba kuchita phunziro la mlungu ndi mlungulo m’nyumba mwathu. Nthaŵi zonse a Mboni za Yehova akabwera, ndinkachoka kunyumbako chifukwa ndimawaopa. Koma a Emmas anapitirizabe kuphunzira Baibulo. Patatha pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi kuyambira pamene anayamba kuphunzira Baibulo, anabatizidwa, mu April 1951. Koma sanandiuze zimenezi chifukwa amaopa kuti akandiuza, basi, ukwati wathu uthera pomwepo.

Milungu Itatu Imene Tinakumana ndi Mavuto

Koma tsiku lina, mnzanga, Ellen Kadzalero anandiuza kuti amuna anga anabatizidwa ndipo anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinakwiya kwambiri! Kuyambira tsiku limenelo ndinasiya kuwalankhulitsa kapena kuwaphikira. Ndinasiyanso kuwatungira ndi kuwaphitsira madzi osamba, ntchito imene mkazi amayenera kuchita pa mwambo wathu.

Atapirira zimenezi kwa milungu itatu, a Emmas anandipempha kuti tikambirane, ndipo anandiuza chimene chinawapangitsa kuti akhale a Mboni. Anandiŵerengera komanso kundifotokozera malemba angapo, monga 1 Akorinto 9:16. Zimenezi zinandikhudza mtima kwambiri, ndipo ndinaona kuti nanenso ndiyenera kumalalikira nawo uthenga wabwino. Choncho, ndinaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Madzulo a tsiku lomwelo, ndinawaphikira amuna anga okondedwawo chakudya chabwino kwambiri, zimene zinawasangalatsa zedi.

Kuwauza Choonadi Achibale ndi Anzathu

Makolo athu atamva kuti tayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova, anatitsutsa kwambiri. Makolowo ndi achibale anga anatilembera kalata yotiuza kuti tisadzawayenderenso. Zimenezi zinatimvetsa chisoni, koma tinakhulupirira lonjezo la Yesu loti tidzapeza abale, alongo, atate, ndi amayi ambiri auzimu.​—Mateyu 19:29.

Ndinapita patsogolo mofulumira pa phunziro langa la Baibulo ndipo ndinabatizidwa mu August 1951, patangotha miyezi itatu ndi theka yokha kuchoka pamene amuna anga anabatizidwa. Ndinaganiza kuti ndiyenera kumuuza choonadi mnzanga Ellen. Chosangalatsa n’chakuti analola kuti ndizichita naye phunziro la Baibulo. Mu May 1952, Ellen anabatizidwa ndipo anakhala mlongo wanga wauzimu, zimene zinapangitsa kuti ubwenzi wathu ulimbe kwambiri. Mpaka lero, tikadali pachinzake cha ponda apa m’pondepo.

Mu 1954, a Emmas anasankhidwa kuti aziyendera mipingo monga woyang’anira dera. Pa nthaŵi imeneyo, tinali kale ndi ana asanu ndi mmodzi. Masiku amenewo, woyang’anira woyendayenda wapabanja amatha mlungu umodzi akuyendera mpingo kenako amakhala kunyumba ndi mkazi wake ndi ana ake mlungu winawo. Koma nthaŵi zonse a Emmas akapita koyendera mipingo, amaonetsetsa kuti ndizichititsa phunziro lathu la Baibulo la banja. Tinkayesetsa kuti phunzirolo lizikhala losangalatsa kwa ana athu. Tinkalankhulanso kuchokera pansi pa mtima za chikondi chathu pa Yehova komanso pa choonadi cha m’Mawu ake, ndipo tinkalalikira limodzi monga banja. Maphunziro auzimu ameneŵa analimbitsa chikhulupiriro cha ana athu ndipo anawakonzekeretsa kuti alimbane ndi chizunzo chimene chimabwera m’tsogolo.

Ayamba Kutizunza Chifukwa cha Chipembedzo Chathu

M’chaka cha 1964, dziko la Malawi linalandira ufulu wodzilamulira lokha. Atsogoleri a chipani cholamulira boma atamva zoti ife sititenga nawo mbali m’ndale, anayesera kutikakamiza kuti tigule makadi a chipani. * Chifukwa chakuti a Emmas ndi ine tinakana kugula makadiwo, mayufi anatchetcha chimanga chonse chimene chinali m’munda mwathu, chimene chinali chakudya chathu cha chaka chonse chotsatiracho. Pamene mayufiwo ankadula chimangacho, ankaimba kuti: “Anthu onse okana kugula khadi la Kamuzu [Pulezidenti Banda], chiswe chiwadyera chimanga chawo ndipo adzachilirira chimanga chimenechi.” Komabe, ngakhale kuti chakudya chathu chinaonongedwa motero, sitinataye mtima. Tinaona Yehova akutisamalira. Mwachikondi, iye anatilimbikitsa.​—Afilipi 4:12, 13.

Tsiku lina usiku mu August 1964, ndinali m’nyumba ndi ana athu. Tinali tikugona, koma ndinadzuka nditamva phokoso la nyimbo likuchokera kutali. Anali a Gulewamkulu, gulu lachinsinsi la anthu ovina amene amaopedwa kwambiri ndipo amavutitsa anthu komanso amanamizira kuti ndi mizimu ya makolo athu akufa. Mayufi anatumiza a Gulewamkuluwo kuti adzativutitse. Ndinadzutsa anawo mofulumira ndipo a Gulewamkuluwo asanafike, tinathaŵira kutchire.

Titabisala patchirepo, tinaona kuwala kwakukulu. A Gulewamkuluwo anali atayatsa nyumba yathu yofoleredwa ndi udzu. Yonse inapsa, limodzi ndi katundu wathu yense. Pamene anthu achiwembuwo amachoka pa nyumba yathu yomwe inali kufuka utsi, tinawamva akunena kuti, “Tam’sonkhera moto wabwino Wamboni amene uja kuti aziotha.” Tinathokoza kwambiri Yehova chifukwa tinapulumuka osavulazidwa! N’zoona kuti anaononga katundu wathu yense, koma sanaononge chikhulupiriro chathu choti tiyenera kudalira Yehova m’malo modalira anthu.​—Salmo 118:8.

Tinadzamva kuti a Gulewamkuluwo anaononganso nyumba za mabanja ena asanu a Mboni za Yehova m’dera lathulo. Tinasangalala ndi kuthokoza kwambiri pamene abale a m’mipingo yoyandikana nafe anadzatithandiza! Anatimangiranso nyumba zina ndipo anatipatsa chakudya kwa milungu ingapo.

Chizunzo Chikula

Mu September 1967 munali kalikiliki wofuna kugwira Mboni za Yehova zonse m’Malawi. Kuti atipeze, anyamata ankhanza ayufi ndi a Malawi Young Pioneer [apainiya] atanyamula zikwanje ankayenda khomo ndi khomo kufufuza anthu Amboni. Akawapeza, ankawauza kuti agule makadi achipani.

Atafika kunyumba kwathu, anatifunsa ngati tinali ndi khadi lachipani. Ine ndinati: “Ayi, sindinagule. Sindigula panopa ndipo ngakhale m’tsogolo sindidzagula.” Kenaka, ine ndi amuna anga anatigwira n’kutipititsa ku polisi, osatipatsa n’komwe mpata woti titenge kanthu kalikonse. Pamene ana athu aang’ono anabwera kunyumba kuchokera ku sukulu, sanatipeze, ndipo anayamba kuda nkhaŵa. Mwamwayi, mwana wathu wamkulupo, Daniel, anabwera kunyumba patangopita nthaŵi yochepa ndipo anauzidwa ndi anthu okhala nawo pafupi zimene zinachitika. Nthaŵi yomweyo anatengana ndi abale ake ang’onoang’onowo n’kunyamuka kupita ku polisi kuja. Anafika pamene apolisiwo amatikweza malole kuti apite nafe ku Lilongwe. Anawo anapita nafe.

Titafika ku Lilongwe, ku likulu la a polisi, anatizenga mlandu wabodza. Apolisiwo anatifunsa kuti: “Kodi mupitirizabe kukhala a Mboni za Yehova?” Tinayankha kuti: “Inde!” ngakhale kuti yankho limenelo linatanthauza kuti nthaŵi yomweyo tipatsidwa chilango chokhala m’ndende kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. Kwa “atsogoleri” a gululo, chilangocho chinali zaka 14 m’ndende.

Titachezera usiku wonse ndi njala komanso osagona, apolisiwo anatitengera ku ndende ya Maula. Kumeneko zipinda zogona akaidi zinali zodzaza kwambiri ndi anthu moti sitinapeze malo ogona paliponse, ngakhale pansi! Chimbudzi chake chinali chidebe chimodzi chimene anachiika pakati pa chipinda chilichonse chodzaza ndi akaidi. Zakudya zimene amatipatsa zinali zochepa ndiponso zosapsa. Patatha milungu iŵiri, oyang’anira ndendeyo anazindikira kuti tinali anthu amtendere ndipo anatilola kugwiritsa ntchito bwalo lochitirapo maseŵera olimbitsa thupi la m’ndendeyo. Chifukwa chakuti tinalipo ambirimbiri pamalo amodzi, tsiku lililonse timakhala ndi mpata wolimbikitsana tokhatokha komanso wolalikira akaidi ena m’ndendemo. Tinadabwa kuona kuti titakhala m’ndendemo kwa pafupifupi miyezi itatu, anatitulutsa chifukwa mayiko ena anali kukakamiza boma la Malawi kuti lisiye kuzunza Mboni za Yehova.

Apolisiwo anatiuza kuti tibwerere kwathu, koma anatiuzanso kuti Mboni za Yehova zaletsedwa ndi boma m’Malawi. Chiletso chimenechi chinayamba pa October 20, 1967 ndipo chinatha pa August 12, 1993​—pafupifupi zaka 26. Zaka zimenezo zinali zovuta, koma ndi thandizo la Yehova tinakhalabe olimba ndipo sitinatenge nawo mbali m’ndale.

Tinasakidwa Ngati Nyama

Mu October 1972, lamulo limene boma linapereka linapangitsa kuti tiyambenso kuzunzidwa mwankhanza. Lamulolo linati a Mboni za Yehova onse achotsedwe ntchito ndipo Mboni zonse zimene zinali m’midzi zithamangitsidwe m’makomo mwawo. Mboni zinasakidwa ngati nyama.

Pa nthaŵi imeneyo, mbale wachinyamata wachikristu anabwera kunyumba kwathu kudzawauza a Emmas uthenga wofunika kwambiri wakuti: ‘Mayufi akufuna akuduleni khosi, apachike mutu wanu pa ndodo, ndipo apite nawo kwa mfumu.’ A Emmas anachoka kunyumbako mwamsanga, koma anayamba akonza kaye zoti tiwatsatire pakangopita nthaŵi yochepa. Mofulumira, ndinauza ana athu kuti achoke panyumbapo. Kenaka, nditangotsala pang’ono kuti nanenso ndichoke, mayufi khumi anafika kudzafunafuna a Emmas. Analoŵa m’nyumbamo koma anapeza kuti a Emmas mulibe. Atakwiya, anandikokera m’dimba la nzimbe, ndipo anandimenya mateche komanso anandimenya ndi nzimbe. Kenaka anandisiya ndili thapsa poganiza kuti ndafa. Nditatsitsimuka, ndinakwaŵira kunyumba.

Usiku umenewo, mdima uli bii, a Emmas anaika moyo wawo pachiswe pobwera kunyumbako kuti adzandiyang’ane. Atandipeza nditamenyedwa koopsa chotero, a Emmas ndi anzawo amene anali ndi galimoto anandinyamula n’kundiika m’galimotomo mosamala. Kenaka tinayenda pa galimotopo kupita ku nyumba ya mbale ku Lilongwe, kumene pang’ono ndi pang’ono ndinachira ndipo a Emmas anayamba kukonza zoti tithaŵe m’dziko muno.

Anthu Othaŵa Kwawo Koma Osoŵa Kopita

Mwana wathu wamkazi Dinesi ndi mwamuna wake anali ndi lole yotha kunyamula katundu wa matani asanu. Analemba ntchito dalaivala amene kale anali wapainiya koma pa nthaŵi imeneyi anali kutiikira kumbuyo. Anadzipereka kuti adzatithandiza, limodzi ndi Mboni zinanso. Kwa mausiku angapo, dalaivalayo ananyamula Mboni zimene amazipeza pa malo amene anali atapangana nazo kale. Ankati akanyamula Mbonizo amavala yunifolomu yake yapainiya n’kuyendetsa loleyo kudutsa malodibuloko apolisi angapo. Anadziika pangozi kuti athandize Mboni zambiri kudutsa malire a dziko lino kupita ku Zambia.

Patatha miyezi yochepa, boma la Zambia linatiuza kuti tibwererenso ku Malawi, koma sitikanatha kubwerera kumudzi kwathu. Katundu yense amene tinasiya anali atabedwa. Ngakhale malata amene anali padenga la nyumba yathu anali atakanganulidwa. Posoŵa koloŵera, tinathaŵira ku Mozambique ndipo tinakhala pa msasa wa anthu othaŵa kwawo wa Mlangeni kwa zaka ziŵiri ndi theka. Koma mu June 1975, boma latsopano la ku Mozambique linatseka msasawo ndipo linatikakamiza kubwereranso ku Malawi, kumene zinthu zinali zoipabe kwa anthu a Yehova. Sitikanachitira mwina koma kuthaŵira ku Zambia kachiŵirinso. Kumeneko tinakafika ku msasa wa anthu othaŵa kwawo wa Chigumukire.

Patapita miyezi iŵiri, kunabwera mabasi ambiri ndi malole a asilikali amene anaima m’mphepete mwa msewu ndipo mazana mazana a asilikali a ku Zambia analoŵa mu msasamo atanyamula zida zankhondo zoopsa. Anatiuza kuti ku Malawi atimangira nyumba zabwino ndipo abwera kudzatitenga kuti tipite kumeneko. Tinadziŵa kuti limenelo linali bodza. Asilikaliwo anayamba kukankhira anthu m’mabasi ndi m’malolemo, ndipo panayambika chisokonezo. Asilikaliwo anayamba kuombera m’mwamba ndi mfuti zawo zoopsa, ndipo zikwi za abale ndi alongo athu anangoti balala! chifukwa cha mantha.

Pachisokonezocho, a Emmas mwangozi anagwetsedwa pansi n’kupondedwa, koma mbale wina anawathandiza kuimiriranso. Tinaganiza kuti uku kunali kuyambika kwa chisautso chachikulu. Anthu onsewo anayamba kuthaŵa n’kumaloŵera cha ku Malawi. Tikadali ku Zambia, tinafika pa mtsinje, ndipo abalewo anagwirana manja n’kuthandiza aliyense kuti awoloke. Koma titawolokera tsidya lina la mtsinjewo, asilikali a ku Zambia anatigwira n’kutitumizanso ku Malawi mochita kutikakamiza.

Titabwereranso ku Malawi, tinasoŵa kopita. Tinamva kuti pa misonkhano yachipani ndi m’manyuzipepala, anthu anauzidwa kuti akhale maso kuti aone “nkhope zachilendo” zikamabwera m’midzi mwawo, kutanthauza Mboni za Yehova. Choncho tinaganiza zopita ku likulu la dzikolo, kumene sitikanachita kuonekera poyera kwambiri ngati mmene tikanachitira ku mudzi. Tinapeza nyumba yaing’ono imene tinachita lendi, ndipo a Emmas anayambiranso maulendo awo akabisira oyendera mipingo monga woyang’anira woyendayenda.

Kupezeka pa Misonkhano ya Mpingo

Kodi n’chiyani chinatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika? Misonkhano ya mpingo! Ku misasa yothaŵirako ya ku Mozambique ndi Zambia, tinkasonkhana momasuka m’Nyumba za Ufumu zofoleredwa ndi udzu. Kuti tipezeke pa misonkhano ku Malawi zinali zovuta komanso zoopsa, koma nthaŵi zonse zinali zopindulitsa. Kuti asatigwire, nthaŵi zambiri timachita misonkhano usiku kwambiri ku malo akutali. Kuti anthu asadziŵe kuti tikuchita msonkhano, sitinkaomba m’manja poyamikira wokamba nkhani, koma tinkangotikita m’manja.

Ubatizo unkachitika usiku kwambiri. Mwana wathu wamwamuna, Abiyudi anabatizidwa m’njira yoteroyo. Nkhani ya ubatizo itatha, iye ndi anthu ena okabatizidwa anawalondolera ku dambo linalake usikuwo kumene anakumbako chitsime chosazama kwambiri. Kumeneko n’kumene anabatizidwa.

Nyumba Yathu Yaing’onoyo Inali Malo Obisalirako

M’zaka zakumapeto kwa chiletso cha bomacho, nyumba yathu ku Lilongwe inali malo obisalirako. Makalata ndi mabuku ochokera ku ofesi ya nthambi ku Zambia zimafikira ku nyumba kwathu mwakabisira. Abale amene amagwira ntchito yamtengatenga ya panjinga ankabwera kunyumba kwathu kudzatenga mabuku ndi makalata ochokera ku Zambia n’kupita nazo m’madera onse a m’Malawi. Magazini a Nsanja ya Olonda amene ankagaŵidwa anali opyapyala chifukwa ankalembedwa pa mapepala amene ankagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo. Zimenezi zinathandiza kuti amtengatengawo azitha kunyamula kuŵirikiza kaŵiri magazini amene akanatha kunyamula akanakhala kuti analembedwa pa mapepala olemberapo magazini. Amtengatengawo ankagaŵanso timagazini ting’onoting’ono ta Nsanja ya Olonda, timene timangokhala ndi nkhani zophunzira zokha. Kamagazini kakang’ono kanali kosavuta kubisa m’thumba la shati chifukwa limakhala pepala limodzi lokha.

Amtengatenga ameneŵa anaika pangozi ufulu ndi moyo wawo pamene anali kupalasa njinga zawo m’tchire, nthaŵi zina usiku, atasanjikiza makatoni a mabuku oletsedwa pa njingazo. Ngakhale kuti kunali malodibuloko apolisi ndi zoopsa zina, ankayenda makilomita ambiri m’nyengo zonse kuti akapereke chakudya chauzimu kwa abale awo. Amtengatenga okondedwa amenewo analidi olimba mtima!

Yehova Amasamalira Akazi Amasiye

Mu December 1992, a Emmas anayamba kudwala sitiroko akukamba nkhani ku mpingo umene anali kuyendera. Izi zitachitika, sankathanso kulankhula. Patapita nthaŵi, matendawo anakulirakulira, ndipo mbali imodzi ya thupi lawo inazizira. Ngakhale kuti zinali zovuta kuti alimbane ndi matenda awowo, thandizo limene tinalandira ku mpingo wathu linandichititsa kuti ndisataye mtima. Ndinatha kusamalira amuna anga kunyumba mpaka pamene anamwalira mu November 1994, ali ndi zaka 76. Tinakhala pa banja kwa zaka 57, ndipo a Emmas anaona kutha kwa chiletso asanafe. Koma ndikadalirabe maliro a mnzanga wokhulupirika ameneyu.

Nditakhala mayi wamasiye, mkamwini wanga ananditenga kuti azindisamalira, kuphatikiza pa mkazi wake ndi ana awo asanu. Tsoka ilo, anadwala kwa nthaŵi yochepa n’kumwalira mu August 2000. Kodi mwana wanga wamkazi akanatha bwanji kutipezera chakudya ndi pokhala? Apanso ndinaona kuti Yehova amatisamalira ndipo alidi “atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.” (Salmo 68:5) Yehova, podzera mwa atumiki ake padziko lapansi, anatipatsa nyumba yatsopano yokongola. Kodi zimenezi zinachitika bwanji? Abale ndi alongo a mu mpingo wathu ataona vuto lathu, anatimangira nyumba m’milungu isanu yokha! Abale ochokera m’mipingo ina odziŵa kumanga nyumba anabwera kudzathandiza. Titaona chikondi ndi kukoma mtima kumene Mboni zonsezi zinasonyeza, tinangoti kukamwa yasa!, kusoŵa chonena, chifukwa nyumba imene anatimangirayo ndi yabwino kwambiri kuposa nyumba zimene ambiri a iwo akukhalamo. Chikondi chimene mpingo unasonyezachi chinapereka umboni wabwino kwambiri m’dera lathu. Usiku ndikamagona ndimangoona ngati ndili m’Paradaiso! Inde, nyumba yathu yatsopano yokongolayo inamangidwa ndi njerwa ndi simenti, koma, mogwirizana ndi zimene anthu ambiri anena, ndi nyumba imene inamangidwadi ndi chikondi.​—Agalatiya 6:10.

Yehova Akupitirizabe Kundisamalira

Ngakhale kuti pali nthaŵi zimene ndinatsala pang’ono kutaya mtima, Yehova wandichitira zabwino. Ana asanu ndi aŵiri mwa ana anga asanu ndi anayi akadali moyo, ndipo panopa banja langa lakwana anthu 123. Ndine woyamikira kwambiri kuti ambiri mwa ameneŵa akutumikira Yehova mokhulupirika!

Panopa ndili ndi zaka 82 ndipo ndili ndi chimwemwe chodzaza tsaya poona zimene mzimu wa Mulungu wachita ku Malawi kuno. M’zaka zinayi zokha zapitazi, ndaona Nyumba za Ufumu zikuonjezeka kuchoka pa imodzi kufika pa zopitirira 600. Tilinso ndi ofesi ya nthambi yatsopano ku Lilongwe, ndipo timalandira chakudya chambiri chotilimbitsa mwauzimu mosavutikira. Ndinganenedi kuti ndaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu limene lili pa Yesaya 54:17, pamene akutitsimikizira kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.” Pambuyo potumikira Yehova kwa zaka zopitirira 50, ndine wotsimikiza kuti kaya tikumane ndi mavuto otani, Yehova amatisamalira nthaŵi zonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mumve zambiri zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova m’Malawi, onani bulosha lakuti Mboni za Yehova m’Malaŵi​—Nkhani ya Kukhulupirika Kwawo; kapena buku la 1999 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 149-223, zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 24]

Amuna anga a Emmas anabatizidwa mu April 1951

[Chithunzi patsamba 26]

Gulu la amtengatenga olimba mtima

[Chithunzi patsamba 28]

Nyumba yomangidwa ndi chikondi