Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Lingathandize Ukwati Wanu

Baibulo Lingathandize Ukwati Wanu

Baibulo Lingathandize Ukwati Wanu

ENA amasangalala ndi mawu akuti ukwati. Anthu ena, mawuŵa amawasautsa maganizo. Mkazi wina anadandaula kuti: “Ndimangoona ngati ndinasudzulidwa. Ndimaona kuti sandisamala ndiponso ndimasungulumwa nthaŵi zonse.”

N’chiyani chimachititsa anthu aŵiri amene analumbira kukondana ndi kusamalirana kuti asiye kukondana? Chimodzi mwa izo n’kusadziŵa zofunika mu ukwati. Mtolankhani wina wa zachipatala anati: “Timaloŵa m’banja popanda maphunziro ena alionse.”

Umboni wakuti masiku ano ndi anthu ochepa chabe amene amaphunzira zofunika mu ukwati ukuoneka m’zimene bungwe lofufuza za maukwati la The National Marriage Project, la pa yunivesite ya Rutgers ku New Jersey, m’dziko la America, linapeza pa kafukufuku wina. Oyang’anira kafukufukuyo analemba kuti: “Pa kafukufuku ameneyu anapeza kuti anthu ambiri anakulira m’banja limene bambo ndi mayi anali osasangalala kapena osudzulana. Ukwati woipa amaudziŵa bwino, koma sadziŵa mmene ukwati wabwino umakhalira. Ena amangonena kuti ukwati wabwino ndi umene uli wosiyana ndi ‘wa makolo anga.’”

Kodi Akristu sakhala ndi mavuto mu ukwati? Amakhala nawo. Ndipotu, Akristu ena m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anadzudzulidwa mosapita m’mbali kuti ‘asafune kumasuka’ m’maukwati awo. (1 Akorinto 7:27) Ndithudi, ukwati uliwonse wa anthu opanda ungwiro sungalephere mavuto, koma thandizo lilipo. Amuna ndi akazi angasinthe kuti ukwati wawo uziyenda bwino mwa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Inde, Baibulo sikuti ndi buku lodzaza ndi malangizo a ukwati. Komabe, popeza ndi louziridwa ndi amene anayambitsa ukwati, tingayembekezere mfundo zake kukhala zothandiza. Yehova Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:17, 18.

Kodi chikondi chimene chinali pakati pa inu ndi mnzanu wa muukwati chikuzirala? Kodi mukuona kuti muli mu ukwati wopanda chikondi? Mkazi wina amene wakhala m’banja zaka 26 anati: “Sindingathe kufotokoza mmene zimandiwawira kukhala m’banja lotereli. Zimachitika nthaŵi zonse.” Mmalo mongolekerera ukwati umene sukukwaniritsa zimene mumafuna, n’kumati ndi mmene ulili, bwanji osatsimikiza mtima kuchitapo kanthu? Nkhani yotsatirayi isonyeza amuna ndi akazi momwe mfundo za m’Baibulo zingathandizire ukwati wawo pambali ya kudzipereka.