Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi kukhala ndi “moyo mwa Iye yekha” kumatanthauzanji?

Baibulo limanena kuti Yesu Kristu ali ndi “moyo mwa Iye yekha” ndipo limanenanso kuti otsatira ake ali ndi ‘moyo mwa iwo okha.’ (Yohane 5:26; 6:53) Komatu, sikuti malemba aŵiriŵa ali ndi tanthauzo lofanana.

Yesu anati: “Monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha.” Asananene mfundo yochititsa chidwiyi, Yesu anati: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mawu anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nawo moyo wosatha . . . ikudza nthaŵi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mawu a [Mwana wa] Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.” Apa Yesu anali kunena za mphamvu zapadera zimene Atate anam’patsa, mphamvu zopangitsa anthu kuyanjidwa ndi Mulungu. Komanso, Yesu akhoza kuukitsa anthu omwe ali m’tulo ta imfa ndi kuwapatsa moyo. Kwa Yesu, kukhala ndi “moyo mwa Iye yekha” kukutanthauza kuti iye anapatsidwa mphamvu zimenezi. Mawuŵa angatanthauzenso kuti, mofanana ndi Atate, Mwana nayenso ali ndi “mphatso ya moyo mwa iye yekha.” (Yohane 5:24-26) Nanga bwanji za otsatira ake?

Patatha pafupifupi chaka chimodzi chinenereni mawuŵa, Yesu anauza anthu amene ankam’mvetsera kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.” (Yohane 6:53, 54) Apa Yesu anafananitsa kukhala ndi “moyo mwa inu nokha” ndi kupeza “moyo wosatha.” Mawu olembedwa mofanana ndi mawu akuti kukhala ndi “moyo mwa inu nokha” amapezeka m’malo enanso m’Malemba Achigiriki. “Khalani nawo mchere mwa inu nokha” ndi “analandira mwa iwo okha mphoto,” ndi zitsanzo ziŵiri za mawu otero. (Marko 9:50; Aroma 1:27) M’mavesi ameneŵa, mawuŵa sakunena za kukhala ndi mphamvu yopatsa ena mchere kapena kupatsa wina aliyense mphoto, koma akusonyeza kukwanira. Motero mawu akuti “moyo mwa inu nokha” a pa Yohane 6:53 akungotanthauza kuloŵa m’moyo wokwanira.

Pofotokoza za otsatira ake kuti ali ndi moyo mwa iwo okha, Yesu anatchula za thupi ndi mwazi wake. Kenako, pamene ankakhazikitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, Yesu anafotokozanso za thupi ndi mwazi wake ndipo analamula otsatira ake omwe anali kudzawaloŵetsa m’pangano latsopano, kuti adye mkate wopanda chotupitsa ndi kumwa vinyo zoimira thupi ndi mwaziwo. Kodi izi zikutanthauza kuti Akristu odzozedwa, omwe ali m’pangano latsopano ndi Yehova Mulungu, ndi okhawo amene amaloŵa m’moyo wokwanirawu? Ayi. Yesu anafotokoza mfundo yachiŵiriyi patatha chaka chimodzi chifotokozereni mfundo yoyamba ija. Anthu omwe anamva Yesu akulankhula mawu a pa Yohane 6:53, 54 sankadziŵa za mwambo wapachaka wokhala ndi zinthu zoimira thupi ndi mwazi wa Kristu.

Malinga ndi Yohane chaputala 6, Yesu poyamba anayerekezera thupi lake ndi mana, mwa kunena kuti: “Makolo anu adadya [mana, NW] m’chipululu, ndipo adamwalira. Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha.” Thupi la Yesu, pamodzi ndi mwazi wake, linali lofunika kwambiri kuposa mana. Motani? Chifukwa chakuti thupi lake linaperekedwa chifukwa cha “moyo wa dziko lapansi,” kupangitsa kuti zikhale zotheka kupeza moyo wosatha. * Motero, mawu onena za kukhala ndi “moyo mwa inu nokha” a pa Yohane 6:53 akunena za anthu onse olandira moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padziko lapansi.​—Yohane 6:48-51.

Kodi otsatira Kristu amalandira liti moyo mwa iwo okha, kapena kuloŵa m’moyo wokwanira? Kwa odzozedwa oloŵa Ufumu, izi zimachitika pamene akuukitsidwa kukakhala kumwamba monga zolengedwa zauzimu zomwe sizingafe. (1 Akorinto 15:52, 53; 1 Yohane 3:2) “Nkhosa zina” za Yesu zidzaloŵa m’moyo wokwanira pamene Ulamuliro wake wa Zaka 1000 watha. Nthaŵi imeneyo, iwo adzakhala atayesedwa, n’kupezedwa okhulupirika, ndi kuyesedwa olungama, oyenera moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.​—Yohane 10:16; Chivumbulutso 20:5, 7-10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 M’chipululu, Aisrayeli ndiponso “anthu ambiri [osakanizika, NW]” anafunika kudya mana kuti akhale ndi moyo. (Eksodo 12:37, 38; 16:13-18) Momwemonso, Akristu onse, kaya ndi odzozedwa kapena ayi, kuti akhale ndi moyo wosatha ayenera kudya mana a kumwamba mwa kukhulupirira mphamvu zopulumutsa za thupi ndi mwazi wa Yesu zomwe zinaperekedwa nsembe.​—Onani Nsanja ya Olonda, ya February 1, 1988, masamba 30 mpaka 31.

[Zithunzi patsamba 31]

Akristu onse oona angakhale ndi ‘moyo mwa iwo okha’