Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malonjezo Amene Ali Odalirika

Malonjezo Amene Ali Odalirika

Malonjezo Amene Ali Odalirika

MBIRI ili ndi nkhani zochuluka zokhudza malonjezo amene sanakwaniritsidwe. Nthaŵi zambiri mayiko alephera kukwaniritsa zimene anagwirizana zopeŵa kuukirana, ngakhale kuti anachita kusainirana, ndipo zimenezi zachititsa anthu awo kumenya nkhondo zoopsa kwambiri. Nthaŵi ina Napoleon ananena kuti: “Maboma amasunga malonjezo awo pokhapokha ngati akakamizidwa kuchita zimenezo, kapena ngati zimenezo apindule nazo.”

Bwanji za malonjezo a anthu? Si mmene zimakhumudwitsira munthu akalephera kuchita zimene analonjeza, makamaka ngati ali munthu amene mumam’dziŵa ndiponso kum’dalira. N’zoona kuti anthu angalephere kukwaniritsa zimene alonjeza kapena angakhale asakufuna kuchita zimene alonjezazo.

Malonjezo a anthu amasiyana kwambiri ndi a Mulungu! Malonjezo a Mulungu ndi odalirika kwambiri ndiponso oona. Lonjezo lililonse limene Yehova Mulungu amapanga n’lodalirika. N’loti lidzakwaniritsidwadi. Ponena za mawu a Mulungu amene salephereka, Yesaya 55:11 amati: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka mkamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”

Choncho, kodi tiyenera kuwaona bwanji malonjezo a Mulungu a m’Baibulo? Ndithudi tiyenera kuwadalira. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Mungadzapeze madalitso ameneŵa ngati muchita mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”​—Yohane 17:3.